×

Ndipo Mose adasankha, pakati pa anthu ake, amuna makumi asanu ndi awiri 7:155 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Al-A‘raf ⮕ (7:155) ayat 155 in Chichewa

7:155 Surah Al-A‘raf ayat 155 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Al-A‘raf ayat 155 - الأعرَاف - Page - Juz 9

﴿وَٱخۡتَارَ مُوسَىٰ قَوۡمَهُۥ سَبۡعِينَ رَجُلٗا لِّمِيقَٰتِنَاۖ فَلَمَّآ أَخَذَتۡهُمُ ٱلرَّجۡفَةُ قَالَ رَبِّ لَوۡ شِئۡتَ أَهۡلَكۡتَهُم مِّن قَبۡلُ وَإِيَّٰيَۖ أَتُهۡلِكُنَا بِمَا فَعَلَ ٱلسُّفَهَآءُ مِنَّآۖ إِنۡ هِيَ إِلَّا فِتۡنَتُكَ تُضِلُّ بِهَا مَن تَشَآءُ وَتَهۡدِي مَن تَشَآءُۖ أَنتَ وَلِيُّنَا فَٱغۡفِرۡ لَنَا وَٱرۡحَمۡنَاۖ وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلۡغَٰفِرِينَ ﴾
[الأعرَاف: 155]

Ndipo Mose adasankha, pakati pa anthu ake, amuna makumi asanu ndi awiri kuti adzakumane nafe ndipo pamene nthaka idagwedezeka pamapazi pawo, Mose adati: “Chikadakhala chifuniro chanu, Ambuye, mukadawaononga iwo ndi ine kale. Kodi inu mungationonge chifukwa cha ntchito za anthu amene ali pakati pathu? Awa ndi mayesero anu, amene Inu mumasocheretsa aliyense amene mwamufuna ndi kutsogolera yemwe mwamufuna. Inu nokha ndinu Mtetezi wathu ndipo tichitireni chisoni chifukwa Inu ndinu wopambana onse amene amakhululukira.”

❮ Previous Next ❯

ترجمة: واختار موسى قومه سبعين رجلا لميقاتنا فلما أخذتهم الرجفة قال رب لو, باللغة نيانجا

﴿واختار موسى قومه سبعين رجلا لميقاتنا فلما أخذتهم الرجفة قال رب لو﴾ [الأعرَاف: 155]

Khaled Ibrahim Betala
“Ndipo Mûsa adasankha anthu ake makumi asanu ndi awiri (omwe adali amakhalidwe abwino) kuti akafike kumalo a chipangano chathu (chimene tidamuuza kuti akabwere nawo pa phiripo kuti akapemphe chikhululuko pa machimo awo omwe adachitidwa ndi anzawo oipa). Ndipo pamene chivomerezi chachikulu chidawafika (adatsala pang’ono kufa). (Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ngati mukadafuna mukadawaononga iwo ndi ine kale (pamaso pa anzawo onse kuti adzionere okha kuti amwalira ndi mphamvu za Allah, osati pakuwapha ine). Kodi mutiononga chifukwa cha zochita za mbuli zathu? Izi sichina koma ndi mayesero anu. Kupyolera m’mayeserowo mumamlekelera kusokera amene mwamfuna, ndi kumtsogolera amene mwamfuna. Inu ndiye Mtetezi wathu; choncho, tikhululukireni ndi kutimvera chifundo. Inu ndinu Abwino mwa okhululuka onse.”
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek