Quran with Chichewa translation - Surah Al-A‘raf ayat 156 - الأعرَاف - Page - Juz 9
﴿۞ وَٱكۡتُبۡ لَنَا فِي هَٰذِهِ ٱلدُّنۡيَا حَسَنَةٗ وَفِي ٱلۡأٓخِرَةِ إِنَّا هُدۡنَآ إِلَيۡكَۚ قَالَ عَذَابِيٓ أُصِيبُ بِهِۦ مَنۡ أَشَآءُۖ وَرَحۡمَتِي وَسِعَتۡ كُلَّ شَيۡءٖۚ فَسَأَكۡتُبُهَا لِلَّذِينَ يَتَّقُونَ وَيُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَٱلَّذِينَ هُم بِـَٔايَٰتِنَا يُؤۡمِنُونَ ﴾
[الأعرَاف: 156]
﴿واكتب لنا في هذه الدنيا حسنة وفي الآخرة إنا هدنا إليك قال﴾ [الأعرَاف: 156]
Khaled Ibrahim Betala ““Ndipo tilembereni zabwino pa dziko lino lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro, ndithudi tibwerera kwa inu!” (Allah) adati: “Chilango changa ndichifikitsa kwa yemwe ndamfuna (mwa anthu oipa); ndipo chifundo Changa chakwanira pa chilichonse (pa abwino ndi oipa). Choncho ndiwalembera (kuti mtendere umenewu udzakhale wawowawo pa tsiku lachimaliziro) amene akupewa (zoletsedwa) ndi kumapereka Zakaat, ndi kumakhulupirira zizindikiro Zathu;” |