المص (1) Alif Lam Mim Sad |
كِتَابٌ أُنزِلَ إِلَيْكَ فَلَا يَكُن فِي صَدْرِكَ حَرَجٌ مِّنْهُ لِتُنذِرَ بِهِ وَذِكْرَىٰ لِلْمُؤْمِنِينَ (2) Buku ili lavumbulutsidwa kwa iwe, mtima wako usavutike ndi kuti uchenjeze ndi ilo ndipo ndi chikumbutso kwa anthu okhulupirira |
اتَّبِعُوا مَا أُنزِلَ إِلَيْكُم مِّن رَّبِّكُمْ وَلَا تَتَّبِعُوا مِن دُونِهِ أَوْلِيَاءَ ۗ قَلِيلًا مَّا تَذَكَّرُونَ (3) Tsatirani zonse zimene zadza kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu ndipo musatsatire wina powonjezerapa Iye. Ndizochepazimenemumakumbukira |
وَكَم مِّن قَرْيَةٍ أَهْلَكْنَاهَا فَجَاءَهَا بَأْسُنَا بَيَاتًا أَوْ هُمْ قَائِلُونَ (4) Ndipo mizinda ndi yambiri imene Ife tidaononga! Chilango chathu chidadza pa iwo usiku kapena pamene iwo adali kugona nthawi ya masana |
فَمَا كَانَ دَعْوَاهُمْ إِذْ جَاءَهُم بَأْسُنَا إِلَّا أَن قَالُوا إِنَّا كُنَّا ظَالِمِينَ (5) Iwo sadalire mwa mtundu wina uli wonse pamene chilango chathu chinadza kupatula kuti: “Ndithudi ife tidali anthu olakwa.” |
فَلَنَسْأَلَنَّ الَّذِينَ أُرْسِلَ إِلَيْهِمْ وَلَنَسْأَلَنَّ الْمُرْسَلِينَ (6) Ndithudi Ife tidzawafunsa onse amene uthenga wathu udatumizidwa ndipo, ndithudi, Ife tidzafunsa Atumwi |
فَلَنَقُصَّنَّ عَلَيْهِم بِعِلْمٍ ۖ وَمَا كُنَّا غَائِبِينَ (7) Ndipo, ndithudi, tidzawauza modziwa ndipo, ndithudi, sikuti Ife padalibe |
وَالْوَزْنُ يَوْمَئِذٍ الْحَقُّ ۚ فَمَن ثَقُلَتْ مَوَازِينُهُ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (8) Pa tsiku limenelo muyeso udzakhala wachilungamo. Motero iwo amene muyeso wawo udzakhala wolemera amenewo adzakhala opambana |
وَمَنْ خَفَّتْ مَوَازِينُهُ فَأُولَٰئِكَ الَّذِينَ خَسِرُوا أَنفُسَهُم بِمَا كَانُوا بِآيَاتِنَا يَظْلِمُونَ (9) Koma iwo amene muyeso wawo udzakhala wopepuka amenewo ndi olephera chifukwa ankakana chivumbulutso chathu |
وَلَقَدْ مَكَّنَّاكُمْ فِي الْأَرْضِ وَجَعَلْنَا لَكُمْ فِيهَا مَعَايِشَ ۗ قَلِيلًا مَّا تَشْكُرُونَ (10) Ndipo Ife tidakupatsani ulamuliro padziko ndipo tidakuikirani zofunikira mu moyo wanu koma kuthokoza kwanu ndi kochepa |
وَلَقَدْ خَلَقْنَاكُمْ ثُمَّ صَوَّرْنَاكُمْ ثُمَّ قُلْنَا لِلْمَلَائِكَةِ اسْجُدُوا لِآدَمَ فَسَجَدُوا إِلَّا إِبْلِيسَ لَمْ يَكُن مِّنَ السَّاجِدِينَ (11) Ndithudi ife tidakulengani inu ndipo tidakupatsani maonekedwe ndipo Ife tidati kwa angelo: “Mugwadireni Adamu” ndipo onse adamugwadira iye kupatula Iblis amene adakana kukhala mmodzi mwa ogwada |
قَالَ مَا مَنَعَكَ أَلَّا تَسْجُدَ إِذْ أَمَرْتُكَ ۖ قَالَ أَنَا خَيْرٌ مِّنْهُ خَلَقْتَنِي مِن نَّارٍ وَخَلَقْتَهُ مِن طِينٍ (12) Mulungu adati: “Kodi chakuletsa ndi chiyani kuti umugwadire iye pamene Ine nditakulamula kutero?” Iye adati: “Ine ndine wolemekezeka kuposa Adamu. Inu mudandilenga ine kuchokera ku moto pamene iye mudamulenga kuchokera ku dothi.” |
قَالَ فَاهْبِطْ مِنْهَا فَمَا يَكُونُ لَكَ أَن تَتَكَبَّرَ فِيهَا فَاخْرُجْ إِنَّكَ مِنَ الصَّاغِرِينَ (13) Mulungu adati: “Choka kumene kuno. Ano simalo okhalako munthu wa mtudzu ayi. Choka! Chifukwa iwe ndiwe mmodzi wa anthu onyozedwa.” |
قَالَ أَنظِرْنِي إِلَىٰ يَوْمِ يُبْعَثُونَ (14) Satana adati, “Mundisunge mpaka pa tsiku la kuuka kwa akufa.” |
قَالَ إِنَّكَ مِنَ الْمُنظَرِينَ (15) Mulungu adati, “Iwe ndiwe mmodzi wa iwo amene apatsidwa nthawi.” |
قَالَ فَبِمَا أَغْوَيْتَنِي لَأَقْعُدَنَّ لَهُمْ صِرَاطَكَ الْمُسْتَقِيمَ (16) Satana adati: “Chifukwa chakuti Inu mwandisocheretsa, ine ndidzawadikira pa njira yanu yoyenera.” |
ثُمَّ لَآتِيَنَّهُم مِّن بَيْنِ أَيْدِيهِمْ وَمِنْ خَلْفِهِمْ وَعَنْ أَيْمَانِهِمْ وَعَن شَمَائِلِهِمْ ۖ وَلَا تَجِدُ أَكْثَرَهُمْ شَاكِرِينَ (17) “Ndipo ine ndidzabuka patsogolo ndi pambuyo pawo ndipo kuchokera ku mbali ya dzanja lamanja ndi mbali ya dzanja lamanzere ndipo Inu simudzawapeza ambiri a iwo ali othokoza.” |
قَالَ اخْرُجْ مِنْهَا مَذْءُومًا مَّدْحُورًا ۖ لَّمَن تَبِعَكَ مِنْهُمْ لَأَمْلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنكُمْ أَجْمَعِينَ (18) Mulungu adati: “Tuluka muno wonyozedwa ndi wothamangitsidwa. Ndipo aliyense amene adzakutsata iwe ndithudi ndidzadzadza Gahena ndi inu nonse.” |
وَيَا آدَمُ اسْكُنْ أَنتَ وَزَوْجُكَ الْجَنَّةَ فَكُلَا مِنْ حَيْثُ شِئْتُمَا وَلَا تَقْرَبَا هَٰذِهِ الشَّجَرَةَ فَتَكُونَا مِنَ الظَّالِمِينَ (19) “O iwe Adamu! Khala iwe ndi mkazi wako ku Paradiso ndipo idyani mmenemo monga mungafunire, koma inu musadzayandikire mtengo uwu chifukwa nonse mungadzakhale odzipondereza nokha.” |
فَوَسْوَسَ لَهُمَا الشَّيْطَانُ لِيُبْدِيَ لَهُمَا مَا وُورِيَ عَنْهُمَا مِن سَوْآتِهِمَا وَقَالَ مَا نَهَاكُمَا رَبُّكُمَا عَنْ هَٰذِهِ الشَّجَرَةِ إِلَّا أَن تَكُونَا مَلَكَيْنِ أَوْ تَكُونَا مِنَ الْخَالِدِينَ (20) Ndipo Satana anawanong’oneza iwo onse ndi cholinga choti chionekere kwa iwo chimene chinali chobisika ndi chochititsa manyazi ndipo Satana adati: “Ambuye wanu adakuletsani kuti musayandikire mtengo uwu chifukwa sadafune kuti mukhale angelo kapena anthu a muyaya.” |
وَقَاسَمَهُمَا إِنِّي لَكُمَا لَمِنَ النَّاصِحِينَ (21) Ndipo iye adalumbira pali Mulungu nati: “Ndithudi ine ndi mmodzi wa iwo amene amakufunirani inu zabwino.” |
فَدَلَّاهُمَا بِغُرُورٍ ۚ فَلَمَّا ذَاقَا الشَّجَرَةَ بَدَتْ لَهُمَا سَوْآتُهُمَا وَطَفِقَا يَخْصِفَانِ عَلَيْهِمَا مِن وَرَقِ الْجَنَّةِ ۖ وَنَادَاهُمَا رَبُّهُمَا أَلَمْ أَنْهَكُمَا عَن تِلْكُمَا الشَّجَرَةِ وَأَقُل لَّكُمَا إِنَّ الشَّيْطَانَ لَكُمَا عَدُوٌّ مُّبِينٌ (22) Motero iye adawanyenga iwo. Ndipo pamene iwo adalawa mtengo uja, maliseche awo adaonekera poyera ndipo onse anayamba kuvala masamba a ku Paradiso. Ndipo Ambuye wawo adawaitana nati: “Kodi Ine sindidakuletseni mtengo uwu ndiponso kukuuzani kuti: ‘Ndithudi Satana ndi mdani wanu weniweni?” |
قَالَا رَبَّنَا ظَلَمْنَا أَنفُسَنَا وَإِن لَّمْ تَغْفِرْ لَنَا وَتَرْحَمْنَا لَنَكُونَنَّ مِنَ الْخَاسِرِينَ (23) Iwo adati: “Ambuye wathu! Ife tachimwa tokha. Ngati Inu simutikhululukira ndikutimvera chisoni, ndithudi ife tidzakhala m’gulu la anthu olephera |
قَالَ اهْبِطُوا بَعْضُكُمْ لِبَعْضٍ عَدُوٌّ ۖ وَلَكُمْ فِي الْأَرْضِ مُسْتَقَرٌّ وَمَتَاعٌ إِلَىٰ حِينٍ (24) Iye adati: “Tsikani pansi, aliyense wa inu adzakhala mdani wa mnzake. Padziko lapansi padzakhala malo anu okhala ndi a chisangalalo cha kanthawi kochepa.” |
قَالَ فِيهَا تَحْيَوْنَ وَفِيهَا تَمُوتُونَ وَمِنْهَا تُخْرَجُونَ (25) Iye anati, “Kumeneko mudzakhala ndi moyo, kumeneko mudzafa ndipo kuchokera kumeneko mudzaukitsidwa.” |
يَا بَنِي آدَمَ قَدْ أَنزَلْنَا عَلَيْكُمْ لِبَاسًا يُوَارِي سَوْآتِكُمْ وَرِيشًا ۖ وَلِبَاسُ التَّقْوَىٰ ذَٰلِكَ خَيْرٌ ۚ ذَٰلِكَ مِنْ آيَاتِ اللَّهِ لَعَلَّهُمْ يَذَّكَّرُونَ (26) Oh inu ana a Adamu! Ife takupatsani zovala kuti mubise umaliseche wanu ndi zovala zokukongoletsani ndi chobvala cha chilungamo chimene chili chabwino. Zimenezo ndi zina mwa zizindikiro za Mulungu kuti akhale okumbuka |
يَا بَنِي آدَمَ لَا يَفْتِنَنَّكُمُ الشَّيْطَانُ كَمَا أَخْرَجَ أَبَوَيْكُم مِّنَ الْجَنَّةِ يَنزِعُ عَنْهُمَا لِبَاسَهُمَا لِيُرِيَهُمَا سَوْآتِهِمَا ۗ إِنَّهُ يَرَاكُمْ هُوَ وَقَبِيلُهُ مِنْ حَيْثُ لَا تَرَوْنَهُمْ ۗ إِنَّا جَعَلْنَا الشَّيَاطِينَ أَوْلِيَاءَ لِلَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ (27) oh inu ana a Adamu! Musalole Satana kuti akunyengeni inu monga momwe anawatulutsitsa makolo anu ku Paradiso, kuwavula nsalu zawo ndi kuwaonetsa maliseche awo. Ndithudi iye pamodzi ndi gulu lake, amakuonani inu kuchokera kumalo amene inu simungathe kuwaona. Ndithudi Ife tidawapanga a Satana kukhala othandiza anthu osakhulupirira |
وَإِذَا فَعَلُوا فَاحِشَةً قَالُوا وَجَدْنَا عَلَيْهَا آبَاءَنَا وَاللَّهُ أَمَرَنَا بِهَا ۗ قُلْ إِنَّ اللَّهَ لَا يَأْمُرُ بِالْفَحْشَاءِ ۖ أَتَقُولُونَ عَلَى اللَّهِ مَا لَا تَعْلَمُونَ (28) Ndipo pamene iwo achita chinthu chochititsa manyazi amati: “Tinapeza makolo athu ali kuchita ndipo Mulungu watilamula ife kutero.” Nena: “Iyayi; Mulungu salamula chinthu chimene chili chonyansa. Kodi inu muli kunena za Mulungu zimene simuzidziwa?” |
قُلْ أَمَرَ رَبِّي بِالْقِسْطِ ۖ وَأَقِيمُوا وُجُوهَكُمْ عِندَ كُلِّ مَسْجِدٍ وَادْعُوهُ مُخْلِصِينَ لَهُ الدِّينَ ۚ كَمَا بَدَأَكُمْ تَعُودُونَ (29) Nena, “Ambuye wanga walamula chilungamo ndi kuti muzimupembedza Iye yekha. Mpembedzeni Iye. Monga momwe adakulengerani poyamba kwa Iye mudzabwerera.” |
فَرِيقًا هَدَىٰ وَفَرِيقًا حَقَّ عَلَيْهِمُ الضَّلَالَةُ ۗ إِنَّهُمُ اتَّخَذُوا الشَّيَاطِينَ أَوْلِيَاءَ مِن دُونِ اللَّهِ وَيَحْسَبُونَ أَنَّهُم مُّهْتَدُونَ (30) Gulu lina adalitsogolera ndipo gulu lina liyenera kusochera chifukwa, ndithudi, iwo adasankha a Satana kuti akhale owathandiza ndi atetezi awo m’malo mwa Mulungu ndipo anali kuganizira kuti adali otsogolera |
۞ يَا بَنِي آدَمَ خُذُوا زِينَتَكُمْ عِندَ كُلِّ مَسْجِدٍ وَكُلُوا وَاشْرَبُوا وَلَا تُسْرِفُوا ۚ إِنَّهُ لَا يُحِبُّ الْمُسْرِفِينَ (31) oh inu ana a Adamu! Valani moyenera pamene muli kupemphera ndi kuzungulira Kaaba, idyani ndi kumwa koma musapyole muyeso ayi. Iye sakonda anthu owononga |
قُلْ مَنْ حَرَّمَ زِينَةَ اللَّهِ الَّتِي أَخْرَجَ لِعِبَادِهِ وَالطَّيِّبَاتِ مِنَ الرِّزْقِ ۚ قُلْ هِيَ لِلَّذِينَ آمَنُوا فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا خَالِصَةً يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۗ كَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ الْآيَاتِ لِقَوْمٍ يَعْلَمُونَ (32) Nena, “Kodi ndani adaletsa kuvala zovala zoyenera zimene Mulungu adapatsa akapolo ake ndiponso zakudya zabwino?” Nena, “Zimenezo ndi zololedwa kwa anthu okhulupirira Mulungu pa moyo uno, ndipo zidzakhala zawo zokha pa tsiku la kuuka kwa akufa.” Mmenemo ndi mmene timaululira poyera chivumbulutso chathu kwa anthu ozindikira |
قُلْ إِنَّمَا حَرَّمَ رَبِّيَ الْفَوَاحِشَ مَا ظَهَرَ مِنْهَا وَمَا بَطَنَ وَالْإِثْمَ وَالْبَغْيَ بِغَيْرِ الْحَقِّ وَأَن تُشْرِكُوا بِاللَّهِ مَا لَمْ يُنَزِّلْ بِهِ سُلْطَانًا وَأَن تَقُولُوا عَلَى اللَّهِ مَا لَا تَعْلَمُونَ (33) Nena, “Ambuye wanga adaletsa ntchito zonse zonyansa kaya zooneka poyera kapena zobisika, machimo, kuponderezana popanda chilungamo, kumphatikiza Mulungu ndi zimene sadalamulire ndi kunena za Mulungu zimene inu simuli kuzidziwa.” |
وَلِكُلِّ أُمَّةٍ أَجَلٌ ۖ فَإِذَا جَاءَ أَجَلُهُمْ لَا يَسْتَأْخِرُونَ سَاعَةً ۖ وَلَا يَسْتَقْدِمُونَ (34) Mtundu uliwonse uli ndi nthawi yake ya chiweruzo, ndipo ngati nthawi yawo ikwana, iwo sangachedwetse kapena kuonjezera ola limodzi |
يَا بَنِي آدَمَ إِمَّا يَأْتِيَنَّكُمْ رُسُلٌ مِّنكُمْ يَقُصُّونَ عَلَيْكُمْ آيَاتِي ۙ فَمَنِ اتَّقَىٰ وَأَصْلَحَ فَلَا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (35) oh inu ana a Adamu! Ngati Atumwi a mtundu wanu adzadza kwa inu kudzakulalikirani chivumbulutso changa ndipo aliyense amene akhala olungama ndi kumachita zabwino, iwo sadzaopa china chilichonse kapena kuda nkhawa |
وَالَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا وَاسْتَكْبَرُوا عَنْهَا أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (36) Ndipo onse amene akana chivumbulutso chathu ndi kuchinyoza, iwo adzakhala eni ake a ku moto ndipo adzakhala kumeneko mpaka kalekale |
فَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّنِ افْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ كَذِبًا أَوْ كَذَّبَ بِآيَاتِهِ ۚ أُولَٰئِكَ يَنَالُهُمْ نَصِيبُهُم مِّنَ الْكِتَابِ ۖ حَتَّىٰ إِذَا جَاءَتْهُمْ رُسُلُنَا يَتَوَفَّوْنَهُمْ قَالُوا أَيْنَ مَا كُنتُمْ تَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ ۖ قَالُوا ضَلُّوا عَنَّا وَشَهِدُوا عَلَىٰ أَنفُسِهِمْ أَنَّهُمْ كَانُوا كَافِرِينَ (37) Kodi wochimwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu kapena amene akana chivumbulutso chake? Anthu otere adzalandira gawo lawo lokonzedwera iwo kuchokera m’Buku mpaka pamene angelo adzadza kudzachotsa miyoyo yawo ndipo iwo adzawauza kuti, “Kodi mafano anu aja ali kuti tsopano, amene mudali kuwapembedza yowonjezera pa Mulungu?” Iwo adzati: “Atithawira.” Ndipo iwo adzadzichitira umboni okha kuti iwo adali anthu osakhulupirira |
قَالَ ادْخُلُوا فِي أُمَمٍ قَدْ خَلَتْ مِن قَبْلِكُم مِّنَ الْجِنِّ وَالْإِنسِ فِي النَّارِ ۖ كُلَّمَا دَخَلَتْ أُمَّةٌ لَّعَنَتْ أُخْتَهَا ۖ حَتَّىٰ إِذَا ادَّارَكُوا فِيهَا جَمِيعًا قَالَتْ أُخْرَاهُمْ لِأُولَاهُمْ رَبَّنَا هَٰؤُلَاءِ أَضَلُّونَا فَآتِهِمْ عَذَابًا ضِعْفًا مِّنَ النَّارِ ۖ قَالَ لِكُلٍّ ضِعْفٌ وَلَٰكِن لَّا تَعْلَمُونَ (38) Mulungu adzati: “Lowani, mgulu la mitundu amene adalipo inu musanadze, anthu ndi majin, kupita ku moto, ndipo pamene uzidzalowa mtundu uliwonse udzakhala uli kutemberera mtundu umene udalipo iwo usanadze mpaka pamene adzasonkhanitsidwa onse m’moto ndipo mtundu womaliza udzati kwa mtundu woyambirira, ‘Ambuye wathu! Awa ndiwo anthu amene adatisokoneza ife motero apatseni chilango choonjezedwa kawiri m’moto.” Iye adzati: “Kwa aliyense kuli chilango chowilikiza koma inu simudziwa.” |
وَقَالَتْ أُولَاهُمْ لِأُخْرَاهُمْ فَمَا كَانَ لَكُمْ عَلَيْنَا مِن فَضْلٍ فَذُوقُوا الْعَذَابَ بِمَا كُنتُمْ تَكْسِبُونَ (39) Ndipo m’badwo woyamba udzati kwa m’badwo womaliza, “Inu simunachite zabwino kuposa ife motero lawani chilango cha ntchito zanu zimene mudali kuchita.” |
إِنَّ الَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا وَاسْتَكْبَرُوا عَنْهَا لَا تُفَتَّحُ لَهُمْ أَبْوَابُ السَّمَاءِ وَلَا يَدْخُلُونَ الْجَنَّةَ حَتَّىٰ يَلِجَ الْجَمَلُ فِي سَمِّ الْخِيَاطِ ۚ وَكَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُجْرِمِينَ (40) Ndithudi amene amati zizindikiro zathu ndi zabodza ndipo amazinyoza izo, makomo a kumwamba sadzatsegulidwa kwa iwo ndipo iwo sadzalowa ku Paradiso pokhapokha ngati ngamira italowa pa diso la zingano. Mmenemo ndi mmene timalipirira anthu ochita zoipa malipiro awo |
لَهُم مِّن جَهَنَّمَ مِهَادٌ وَمِن فَوْقِهِمْ غَوَاشٍ ۚ وَكَذَٰلِكَ نَجْزِي الظَّالِمِينَ (41) Wawo adzakhala kama wa moto ndipo pamwamba pawo padzakhala malawi a moto. M’menemo ndi m’mene tidzawalipirira anthu ochita zoipa |
وَالَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ لَا نُكَلِّفُ نَفْسًا إِلَّا وُسْعَهَا أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ الْجَنَّةِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (42) Koma iwo amene anakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino; Ife sitisenzetsa munthu katundu amene sangathe kumunyamula; iwo ndi anthu a ku Paradiso. Ndipo adzakhalako mpaka kalekale |
وَنَزَعْنَا مَا فِي صُدُورِهِم مِّنْ غِلٍّ تَجْرِي مِن تَحْتِهِمُ الْأَنْهَارُ ۖ وَقَالُوا الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي هَدَانَا لِهَٰذَا وَمَا كُنَّا لِنَهْتَدِيَ لَوْلَا أَنْ هَدَانَا اللَّهُ ۖ لَقَدْ جَاءَتْ رُسُلُ رَبِّنَا بِالْحَقِّ ۖ وَنُودُوا أَن تِلْكُمُ الْجَنَّةُ أُورِثْتُمُوهَا بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (43) Ndipo Ife tidzachotsa chidani m’mitima mwawo ndipo mitsinje idzayenda pansi pa mapazi awo ndipo iwo adzati: “Kuyamikidwa ndi kwa Mulungu amene watitsogolera ife ku izi ndipo ife sitikadakhala otsogozedwa pakadapanda Mulungu kutitsogolera! Ndithudi Atumwi a Ambuye wathu adadza ndi choonadi.” Ndipo zidzanenedwa kwa iwo kuti: “Iyi ndiyo Paradiso imene mwailandira chifukwa cha ntchito zanu zimene mudali kuchita.” |
وَنَادَىٰ أَصْحَابُ الْجَنَّةِ أَصْحَابَ النَّارِ أَن قَدْ وَجَدْنَا مَا وَعَدَنَا رَبُّنَا حَقًّا فَهَلْ وَجَدتُّم مَّا وَعَدَ رَبُّكُمْ حَقًّا ۖ قَالُوا نَعَمْ ۚ فَأَذَّنَ مُؤَذِّنٌ بَيْنَهُمْ أَن لَّعْنَةُ اللَّهِ عَلَى الظَّالِمِينَ (44) Ndipo anthu okhala ku Paradiso adzaitana anthu a ku Moto. “Ndithudi chimene adatilonjeza ife Ambuye wathu tachipeza kuti ndi choona. Kodi inu mwapeza chomwe adakulonjezani Ambuye wanu kuti ndi choona?” Iwo adzati: Inde. Ndipo wofuula adzanena pakati pawo: “Matemberero a Mulungu ali pa anthu olakwa.” |
الَّذِينَ يَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ اللَّهِ وَيَبْغُونَهَا عِوَجًا وَهُم بِالْآخِرَةِ كَافِرُونَ (45) Iwo amene anali kuletsa anzawo kutsatira njira ya Mulungu ndipo amafuna kuti iyo ikhale yokhotakhota ndipo adalibe chikhulupiriro m’moyo umene uli nkudza |
وَبَيْنَهُمَا حِجَابٌ ۚ وَعَلَى الْأَعْرَافِ رِجَالٌ يَعْرِفُونَ كُلًّا بِسِيمَاهُمْ ۚ وَنَادَوْا أَصْحَابَ الْجَنَّةِ أَن سَلَامٌ عَلَيْكُمْ ۚ لَمْ يَدْخُلُوهَا وَهُمْ يَطْمَعُونَ (46) Ndipo pakati pawo padzakhala chotchinga ndi chipupa mmene mudzakhala anthu amene adzazindikira wina aliyense poona zizindikiro zawo. Iwo adzaitana anthu a ku Paradiso: Mtendere ukhale pa inu. Koma panthawi imeneyo iwo adzakhala asadalowe ku Paradiso koma iwo adzakhala ndi chikhulupiriro choti adzalowanso mopanda chikaiko |
۞ وَإِذَا صُرِفَتْ أَبْصَارُهُمْ تِلْقَاءَ أَصْحَابِ النَّارِ قَالُوا رَبَّنَا لَا تَجْعَلْنَا مَعَ الْقَوْمِ الظَّالِمِينَ (47) Ndipo pamene iwo adzaona iwo amene adzakhala ku moto, iwo adzati: “Oh Ambuye wathu! Musatiike ife malo a anthu oipa.” |
وَنَادَىٰ أَصْحَابُ الْأَعْرَافِ رِجَالًا يَعْرِفُونَهُم بِسِيمَاهُمْ قَالُوا مَا أَغْنَىٰ عَنكُمْ جَمْعُكُمْ وَمَا كُنتُمْ تَسْتَكْبِرُونَ (48) Ndipo anthu a m’chipupa adzawaitana anthu omwe adzawadziwa ndi zizindikiro zawo ndipo adzati: “Kodi kuchuluka kwanu, kwakuthandizani chiani ndiponso mwano umene mumaonetsa ku chipembedzo?” |
أَهَٰؤُلَاءِ الَّذِينَ أَقْسَمْتُمْ لَا يَنَالُهُمُ اللَّهُ بِرَحْمَةٍ ۚ ادْخُلُوا الْجَنَّةَ لَا خَوْفٌ عَلَيْكُمْ وَلَا أَنتُمْ تَحْزَنُونَ (49) Kodi awa ndi anthu amene munkalumbira kuti sadzalandira chisomo cha Mulungu? “Lowani ku Paradiso, inu simudzachita mantha ndiponso simudzada nkhawa ayi.” |
وَنَادَىٰ أَصْحَابُ النَّارِ أَصْحَابَ الْجَنَّةِ أَنْ أَفِيضُوا عَلَيْنَا مِنَ الْمَاءِ أَوْ مِمَّا رَزَقَكُمُ اللَّهُ ۚ قَالُوا إِنَّ اللَّهَ حَرَّمَهُمَا عَلَى الْكَافِرِينَ (50) Ndipo anthu a ku Moto adzaitana anthu a ku Paradiso kuti, “Tithireni madzi kapena china chilichonse chimene Mulungu wakupatsani inu!” Anthu a ku Paradiso adzati, “Mulungu adaletsa zonse ziwiri kuti anthu osakhulupirira alandire.” |
الَّذِينَ اتَّخَذُوا دِينَهُمْ لَهْوًا وَلَعِبًا وَغَرَّتْهُمُ الْحَيَاةُ الدُّنْيَا ۚ فَالْيَوْمَ نَنسَاهُمْ كَمَا نَسُوا لِقَاءَ يَوْمِهِمْ هَٰذَا وَمَا كَانُوا بِآيَاتِنَا يَجْحَدُونَ (51) “Iwo amene adasandutsa chipembedzo chawo ngatinthabwalandichoseweretsandipoadalikunyengedwa ndi zokoma za m’moyo wa padziko lapansi. Motero lero Ife tiwaiwala monga mmene adaiwalira za kukumana kwa tsiku lawoli ndi chifukwa chokana zizindikiro zathu.” |
وَلَقَدْ جِئْنَاهُم بِكِتَابٍ فَصَّلْنَاهُ عَلَىٰ عِلْمٍ هُدًى وَرَحْمَةً لِّقَوْمٍ يُؤْمِنُونَ (52) Ndithudi Ifetawabweretsera Bukum’menetalongosola za nzeru, chilangizo ndi madalitso kwa anthu okhulupirira kwenikweni |
هَلْ يَنظُرُونَ إِلَّا تَأْوِيلَهُ ۚ يَوْمَ يَأْتِي تَأْوِيلُهُ يَقُولُ الَّذِينَ نَسُوهُ مِن قَبْلُ قَدْ جَاءَتْ رُسُلُ رَبِّنَا بِالْحَقِّ فَهَل لَّنَا مِن شُفَعَاءَ فَيَشْفَعُوا لَنَا أَوْ نُرَدُّ فَنَعْمَلَ غَيْرَ الَّذِي كُنَّا نَعْمَلُ ۚ قَدْ خَسِرُوا أَنفُسَهُمْ وَضَلَّ عَنْهُم مَّا كَانُوا يَفْتَرُونَ (53) Kodi iwo akudikira kuti chikwaniritsidwe? Patsiku limene chidzakwaniritsidwe iwo amene adaliiwala kale adzati, “Ndithudi,Atumwi aAmbuye wathu adadza ndi choonadi. Kodi palibe wina amene akhoza kutilankhulira m’malo mwathu? Kapena kuti tibwezedwe kupitanso ku dziko lapansi kuti tikachite nthito zabwino osati zoipa zimene timachita?” Ndithudi iwo adadziononga okha ndipo chonse chimene adali kupeka chawathawira iwo |
إِنَّ رَبَّكُمُ اللَّهُ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ ثُمَّ اسْتَوَىٰ عَلَى الْعَرْشِ يُغْشِي اللَّيْلَ النَّهَارَ يَطْلُبُهُ حَثِيثًا وَالشَّمْسَ وَالْقَمَرَ وَالنُّجُومَ مُسَخَّرَاتٍ بِأَمْرِهِ ۗ أَلَا لَهُ الْخَلْقُ وَالْأَمْرُ ۗ تَبَارَكَ اللَّهُ رَبُّ الْعَالَمِينَ (54) Ndithudi Ambuye wanu ndi Mulungu, amene m’masiku asanu ndi limodzi adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo atatero adabuka pamwamba pa Mpando wake wa Chifumu. Iye amavundikira usiku ndi usana ndipo mofulumira usiku umatsata usana. Ndipo dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zimayenda motsatira malamulo ake. Ndithudi zake ndi zolengedwa zonse ndi ulamuliro. Olemekezeka akhale Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse |
ادْعُوا رَبَّكُمْ تَضَرُّعًا وَخُفْيَةً ۚ إِنَّهُ لَا يُحِبُّ الْمُعْتَدِينَ (55) Pemphani kwa Ambuye wanu modzichepetsa ndi mwamseri. Iye sakonda anthu oswa malamulo |
وَلَا تُفْسِدُوا فِي الْأَرْضِ بَعْدَ إِصْلَاحِهَا وَادْعُوهُ خَوْفًا وَطَمَعًا ۚ إِنَّ رَحْمَتَ اللَّهِ قَرِيبٌ مِّنَ الْمُحْسِنِينَ (56) Ndipo musayambitse chisokonezo padziko ilo litakonzedwa ndipo pemphani kwa Iye mwamantha ndi chikhulupiriro; ndithudi, chifundo cha Mulungu chili pafupi ndi anthu ochita zabwino |
وَهُوَ الَّذِي يُرْسِلُ الرِّيَاحَ بُشْرًا بَيْنَ يَدَيْ رَحْمَتِهِ ۖ حَتَّىٰ إِذَا أَقَلَّتْ سَحَابًا ثِقَالًا سُقْنَاهُ لِبَلَدٍ مَّيِّتٍ فَأَنزَلْنَا بِهِ الْمَاءَ فَأَخْرَجْنَا بِهِ مِن كُلِّ الثَّمَرَاتِ ۚ كَذَٰلِكَ نُخْرِجُ الْمَوْتَىٰ لَعَلَّكُمْ تَذَكَّرُونَ (57) Iye ndi amene amatumiza mphepo ngati yobweretsa uthenga wabwino umene umadza pambuyo pa chisomo chake. Mpaka pamene iyo isonkhanitsa mitambo yolemera, timaiyendetsa kupita ku nthaka yakufa ndipo timatumiza mvula kuti igwe pa iyo. Ndipo timameretsa zipatso za mitundu mitundu. Mmenemu ndi mmene tidzadzutsire anthu akufa kuti mwina mukhoza ku chenjezedwa |
وَالْبَلَدُ الطَّيِّبُ يَخْرُجُ نَبَاتُهُ بِإِذْنِ رَبِّهِ ۖ وَالَّذِي خَبُثَ لَا يَخْرُجُ إِلَّا نَكِدًا ۚ كَذَٰلِكَ نُصَرِّفُ الْآيَاتِ لِقَوْمٍ يَشْكُرُونَ (58) Nthaka yabwino imabereka zipatso mwachifuniro cha Mulungu. Nthaka yoipa siibereka chilichonse pokhapokha movutikira. Motero timafotokoza zivumbulutso zathu poyera kwa anthu amene amathokoza |
لَقَدْ أَرْسَلْنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوْمِهِ فَقَالَ يَا قَوْمِ اعْبُدُوا اللَّهَ مَا لَكُم مِّنْ إِلَٰهٍ غَيْرُهُ إِنِّي أَخَافُ عَلَيْكُمْ عَذَابَ يَوْمٍ عَظِيمٍ (59) Ndithudi Ife tidatumiza Nowa kwa anthu ake ndipo iye adati: “Oh anthu anga! Pembedzani Mulungu! Inu mulibe mulungu wina kupatula Iye yekha. Ndithudi ine ndili kuchita mantha ndi chilango chowawa chimene chidzadza pa inu patsiku lalikulu.” |
قَالَ الْمَلَأُ مِن قَوْمِهِ إِنَّا لَنَرَاكَ فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (60) Atsogoleri a anthu ake adati: “Ndithudi ife tili kuona kuti iwe wasochera kwambiri.” |
قَالَ يَا قَوْمِ لَيْسَ بِي ضَلَالَةٌ وَلَٰكِنِّي رَسُولٌ مِّن رَّبِّ الْعَالَمِينَ (61) Iye adati: “oh anthu anga! Ine sindine wosochera, koma ndine Mtumwi wochokera kwa Ambuye wazolengedwa zonse.” |
أُبَلِّغُكُمْ رِسَالَاتِ رَبِّي وَأَنصَحُ لَكُمْ وَأَعْلَمُ مِنَ اللَّهِ مَا لَا تَعْلَمُونَ (62) “Ndipo ndili kukulalikirani uthenga wa Ambuye wanga ndi kukulangizani inu. Ndipo ndili kudziwa kuchokera kwa Mulungu zimene inu simukudziwa ayi.” |
أَوَعَجِبْتُمْ أَن جَاءَكُمْ ذِكْرٌ مِّن رَّبِّكُمْ عَلَىٰ رَجُلٍ مِّنكُمْ لِيُنذِرَكُمْ وَلِتَتَّقُوا وَلَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ (63) “Kodi inu mukudabwa kuti kwadza kwa inu chenjezo lochokera kwa Ambuye wanu kudzera mwa munthu amene ali pakati panu kuti akuchenjezeni kuti mukhale anthu oopa Mulungu ndi kuti mupeze chisomo chake?” |
فَكَذَّبُوهُ فَأَنجَيْنَاهُ وَالَّذِينَ مَعَهُ فِي الْفُلْكِ وَأَغْرَقْنَا الَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا ۚ إِنَّهُمْ كَانُوا قَوْمًا عَمِينَ (64) Koma iwo adamutsutsa ndipo Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi amene adali ndi iye M’chombo ndipo tidawamiza onse amene adakana chivumbulutso chathu. Ndithudi iwo adali anthu akhungu |
۞ وَإِلَىٰ عَادٍ أَخَاهُمْ هُودًا ۗ قَالَ يَا قَوْمِ اعْبُدُوا اللَّهَ مَا لَكُم مِّنْ إِلَٰهٍ غَيْرُهُ ۚ أَفَلَا تَتَّقُونَ (65) Ndipo kwa Ad tidatumiza m’bale wawo Hud. Iye adati: “Oh anthu anga! Pembedzani Mulungu! Inu mulibe mulungu wina koma Iye yekha basi. Kodi simuopa?” |
قَالَ الْمَلَأُ الَّذِينَ كَفَرُوا مِن قَوْمِهِ إِنَّا لَنَرَاكَ فِي سَفَاهَةٍ وَإِنَّا لَنَظُنُّكَ مِنَ الْكَاذِبِينَ (66) Atsogoleri a anthu osakhulupirira ochokera ku mtundu wa Hudadati:“Ifetilikukuonakutiiwendiwewopusandipo ife tili kuganiza kuti ndiwe mmodzi wa anthu a bodza.” |
قَالَ يَا قَوْمِ لَيْسَ بِي سَفَاهَةٌ وَلَٰكِنِّي رَسُولٌ مِّن رَّبِّ الْعَالَمِينَ (67) Iye adati: “oh anthu anga! Ine sindine wopusa koma ndine Mtumwi wochokera kwa Ambuye wazolengedwa zonse.” |
أُبَلِّغُكُمْ رِسَالَاتِ رَبِّي وَأَنَا لَكُمْ نَاصِحٌ أَمِينٌ (68) “Ine ndili kukulalikirani Uthenga wa Ambuye wanga ndipo ndine mchenjezi wanu wokhulupirika.” |
أَوَعَجِبْتُمْ أَن جَاءَكُمْ ذِكْرٌ مِّن رَّبِّكُمْ عَلَىٰ رَجُلٍ مِّنكُمْ لِيُنذِرَكُمْ ۚ وَاذْكُرُوا إِذْ جَعَلَكُمْ خُلَفَاءَ مِن بَعْدِ قَوْمِ نُوحٍ وَزَادَكُمْ فِي الْخَلْقِ بَسْطَةً ۖ فَاذْكُرُوا آلَاءَ اللَّهِ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ (69) “Kodimukudabwakutikwadzachikumbutsochochokera kwa Ambuye kudzera mwa munthu wa mtundu wanu kuti akhale okuchenjezani inu? Ndipo kumbukirani kuti adakupangani inu kukhala alowam’malo a anthu a Nowa ndipo adakuonjezerani mphamvu pachilengedwe. Motero kumbukirani madalitso a Mulungu kuti mupambane.” |
قَالُوا أَجِئْتَنَا لِنَعْبُدَ اللَّهَ وَحْدَهُ وَنَذَرَ مَا كَانَ يَعْبُدُ آبَاؤُنَا ۖ فَأْتِنَا بِمَا تَعِدُنَا إِن كُنتَ مِنَ الصَّادِقِينَ (70) Iwo adati: “Iwe wadza kuti ife tizingopembedza Mulungu yekha ndi kusiya milungu imene makolo athu adali kupembedza. Motero bweretsa chimene ukutiopseza nacho ngati zimene uli kunena ndi zoona.” |
قَالَ قَدْ وَقَعَ عَلَيْكُم مِّن رَّبِّكُمْ رِجْسٌ وَغَضَبٌ ۖ أَتُجَادِلُونَنِي فِي أَسْمَاءٍ سَمَّيْتُمُوهَا أَنتُمْ وَآبَاؤُكُم مَّا نَزَّلَ اللَّهُ بِهَا مِن سُلْطَانٍ ۚ فَانتَظِرُوا إِنِّي مَعَكُم مِّنَ الْمُنتَظِرِينَ (71) Iye adati: “Mkwiyo wa Ambuye wanu ndiponso chilango chake chadza kale pa inu. Kodi inu mukutsutsana ndi ine pa mayina amene inu ndi makolo anu mudapeka, opanda chilolezo cha Mulungu? Dikirani nanenso ndili mmodzi mwa odikira.” |
فَأَنجَيْنَاهُ وَالَّذِينَ مَعَهُ بِرَحْمَةٍ مِّنَّا وَقَطَعْنَا دَابِرَ الَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا ۖ وَمَا كَانُوا مُؤْمِنِينَ (72) Ife tidamupulumutsa iye ndi onse amene adali naye mwa chifundo chathu ndipo tidadula maziko ya onse amene anatsutsa chivumbulutso chathu ndipo iwo adali osakhulupirira |
وَإِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمْ صَالِحًا ۗ قَالَ يَا قَوْمِ اعْبُدُوا اللَّهَ مَا لَكُم مِّنْ إِلَٰهٍ غَيْرُهُ ۖ قَدْ جَاءَتْكُم بَيِّنَةٌ مِّن رَّبِّكُمْ ۖ هَٰذِهِ نَاقَةُ اللَّهِ لَكُمْ آيَةً ۖ فَذَرُوهَا تَأْكُلْ فِي أَرْضِ اللَّهِ ۖ وَلَا تَمَسُّوهَا بِسُوءٍ فَيَأْخُذَكُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (73) Ndipo kwa anthu a Thamud, Ife tidawatumizira m’bale wawo Saleh. Iye adati: “Oh anthu anga! Pembedzani Mulungu. Inu mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Ndithudi wadza umboni wokhulupirika kuchokera kwa Ambuye wanu. Iyi ndi Ngamira yaikazi ya Mulungu, chizindikiro kwa inu. Motero ilekeni kuti izidya m’dziko la Mulungu ndipo musaizunze ayi chifukwa mungapute chilango chowawa.” |
وَاذْكُرُوا إِذْ جَعَلَكُمْ خُلَفَاءَ مِن بَعْدِ عَادٍ وَبَوَّأَكُمْ فِي الْأَرْضِ تَتَّخِذُونَ مِن سُهُولِهَا قُصُورًا وَتَنْحِتُونَ الْجِبَالَ بُيُوتًا ۖ فَاذْكُرُوا آلَاءَ اللَّهِ وَلَا تَعْثَوْا فِي الْأَرْضِ مُفْسِدِينَ (74) “Ndipo kumbukirani pamene Iye adakupangani inu kuti mukhale alowa m’malo a Ad, ndipo adakupatsani malo okhala m’dziko lino. Inu mwamanga nyumba zolemekezeka m’chidikha chake ndiponso mwaboola nyumba pakati pa mapiri ake. Motero kumbukirani zokoma za Mulungu ndipo musachulukitse kuwononga padziko lapansi.” |
قَالَ الْمَلَأُ الَّذِينَ اسْتَكْبَرُوا مِن قَوْمِهِ لِلَّذِينَ اسْتُضْعِفُوا لِمَنْ آمَنَ مِنْهُمْ أَتَعْلَمُونَ أَنَّ صَالِحًا مُّرْسَلٌ مِّن رَّبِّهِ ۚ قَالُوا إِنَّا بِمَا أُرْسِلَ بِهِ مُؤْمِنُونَ (75) Atsogoleri a anthu amene amadzikweza mu anthu ake anati kwa anthu ofoka amene adakhulupirira mwa iwo: “Kodi mukudziwa kuti Saleh ndi wotumidwa kuchokera kwa Ambuye wake?” Iwo adati: “Ndithudi ife takhulupirira mzimene iye watumidwa.” |
قَالَ الَّذِينَ اسْتَكْبَرُوا إِنَّا بِالَّذِي آمَنتُم بِهِ كَافِرُونَ (76) Iwo amene adali odzikuza adati: “Ndithudi ife tili kuzikanazonsezimeneinumulikuzikhulupirira.” |
فَعَقَرُوا النَّاقَةَ وَعَتَوْا عَنْ أَمْرِ رَبِّهِمْ وَقَالُوا يَا صَالِحُ ائْتِنَا بِمَا تَعِدُنَا إِن كُنتَ مِنَ الْمُرْسَلِينَ (77) Motero iwo adapha ngamira yaikazi ija ndipo ananyoza lamulo la Ambuye wawo ndipo adati: “Iwe Saleh! Bweretsa chimene udatiopseza nacho ngati iwe ndiwe Mtumwi woona.” |
فَأَخَذَتْهُمُ الرَّجْفَةُ فَأَصْبَحُوا فِي دَارِهِمْ جَاثِمِينَ (78) Motero nthawi yomweyo chivomerezi chidagwa pa iwo ndipo pamene kumacha m’mawa onse adali lambilambi m’nyumba zawo atafa |
فَتَوَلَّىٰ عَنْهُمْ وَقَالَ يَا قَوْمِ لَقَدْ أَبْلَغْتُكُمْ رِسَالَةَ رَبِّي وَنَصَحْتُ لَكُمْ وَلَٰكِن لَّا تُحِبُّونَ النَّاصِحِينَ (79) Motero Saleh adachoka nati, “oh anthu anga! Ine, ndithudi, ndapereka uthenga wa Ambuye wanga ndipo ndakupatsani chilangizo chabwino koma inu simukonda anthu okuchenjezani.” |
وَلُوطًا إِذْ قَالَ لِقَوْمِهِ أَتَأْتُونَ الْفَاحِشَةَ مَا سَبَقَكُم بِهَا مِنْ أَحَدٍ مِّنَ الْعَالَمِينَ (80) Ndi pamene Loti adanena kwa anthu ake, “Kodi inu mukuchita zinthu zonyansa zimene palibe mtundu wa anthu umene udachitapo ndi kale lomwe?” |
إِنَّكُمْ لَتَأْتُونَ الرِّجَالَ شَهْوَةً مِّن دُونِ النِّسَاءِ ۚ بَلْ أَنتُمْ قَوْمٌ مُّسْرِفُونَ (81) “Ndithudi inu mufuna kukwaniritsa zilakolako za matupi anu ndi amuna anzanu m’malo mwa akazi? Iyayi, ndithudi, inu ndinu anthu ochimwa kwambiri.” |
وَمَا كَانَ جَوَابَ قَوْمِهِ إِلَّا أَن قَالُوا أَخْرِجُوهُم مِّن قَرْيَتِكُمْ ۖ إِنَّهُمْ أُنَاسٌ يَتَطَهَّرُونَ (82) Ndipo yankho la anthu ake silinali lina koma adati: “Achotseni iwo mu Mzinda wanu. Awa ndi anthu amene afuna kukhala angwiro.” |
فَأَنجَيْنَاهُ وَأَهْلَهُ إِلَّا امْرَأَتَهُ كَانَتْ مِنَ الْغَابِرِينَ (83) Ndipo Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi omutsatira ake kupatula mkazi wake amene adali mmodzi mwa otsalira m’mbuyo |
وَأَمْطَرْنَا عَلَيْهِم مَّطَرًا ۖ فَانظُرْ كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الْمُجْرِمِينَ (84) Ndipo tidagwetsa pa iwo mvula yambiri. Onani mapeto a anthu ochita zoipa |
وَإِلَىٰ مَدْيَنَ أَخَاهُمْ شُعَيْبًا ۗ قَالَ يَا قَوْمِ اعْبُدُوا اللَّهَ مَا لَكُم مِّنْ إِلَٰهٍ غَيْرُهُ ۖ قَدْ جَاءَتْكُم بَيِّنَةٌ مِّن رَّبِّكُمْ ۖ فَأَوْفُوا الْكَيْلَ وَالْمِيزَانَ وَلَا تَبْخَسُوا النَّاسَ أَشْيَاءَهُمْ وَلَا تُفْسِدُوا فِي الْأَرْضِ بَعْدَ إِصْلَاحِهَا ۚ ذَٰلِكُمْ خَيْرٌ لَّكُمْ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (85) Kwa anthu a ku Midiyani tidatumiza m’bale wawo Shaibu. Iye anati: “Oh anthu anga! Pembedzani Mulungu, inu mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Ndithudi chizindikiro chooneka chadza kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu motero perekani muyeso woyenera ndipo yesani zonse moyenera ndipo musachite chinyengo kwa anthu pa katundu wawo ndipo musawononge dziko lapansi pambuyo poti layeretsedwa kale. Chimenecho ndicho chinthu chabwino kwa inu ngati inu ndinu okhulupirira kwenikweni.” |
وَلَا تَقْعُدُوا بِكُلِّ صِرَاطٍ تُوعِدُونَ وَتَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ اللَّهِ مَنْ آمَنَ بِهِ وَتَبْغُونَهَا عِوَجًا ۚ وَاذْكُرُوا إِذْ كُنتُمْ قَلِيلًا فَكَثَّرَكُمْ ۖ وَانظُرُوا كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الْمُفْسِدِينَ (86) “Ndipo musakhale mu msewu uliwonse ndi kumaopseza anthu okhulupirira ndi kuwaletsa kutsatira njira ya Mulungu ndi kufunafuna njira yoti mukhotetsere njirayo. Kumbukirani mmene adakuchulukitsirani inu pamene mudali ochepa. Ndipo onani mmene adalili mapeto a anthu ochita zoipa.” |
وَإِن كَانَ طَائِفَةٌ مِّنكُمْ آمَنُوا بِالَّذِي أُرْسِلْتُ بِهِ وَطَائِفَةٌ لَّمْ يُؤْمِنُوا فَاصْبِرُوا حَتَّىٰ يَحْكُمَ اللَّهُ بَيْنَنَا ۚ وَهُوَ خَيْرُ الْحَاكِمِينَ (87) “Ndipo ngati lilipo gulu lina pakati panu limene lidakhulupirira mu Uthenga umene ndidatumizidwa ndi gulu limene silidakhulupirire motero pilira mpaka pamene Mulungu aweruza pakati pathu. Iye ndiye wabwino mwa oweruza onse.” |
۞ قَالَ الْمَلَأُ الَّذِينَ اسْتَكْبَرُوا مِن قَوْمِهِ لَنُخْرِجَنَّكَ يَا شُعَيْبُ وَالَّذِينَ آمَنُوا مَعَكَ مِن قَرْيَتِنَا أَوْ لَتَعُودُنَّ فِي مِلَّتِنَا ۚ قَالَ أَوَلَوْ كُنَّا كَارِهِينَ (88) Mafumu odzikweza a gulu lina la mtundu wake adati: “Iwe Shaibu! Ndithudi ife tidzakuthamangitsa iwe mu mzinda wathu pamodzi ndi iwo amene akhulupirira ndi iwe kapena kuti mubwerere ku chipembedzo chathu.” Iye adati: “Chiyani! Ngakhale kuti zikutinyansa?” |
قَدِ افْتَرَيْنَا عَلَى اللَّهِ كَذِبًا إِنْ عُدْنَا فِي مِلَّتِكُم بَعْدَ إِذْ نَجَّانَا اللَّهُ مِنْهَا ۚ وَمَا يَكُونُ لَنَا أَن نَّعُودَ فِيهَا إِلَّا أَن يَشَاءَ اللَّهُ رَبُّنَا ۚ وَسِعَ رَبُّنَا كُلَّ شَيْءٍ عِلْمًا ۚ عَلَى اللَّهِ تَوَكَّلْنَا ۚ رَبَّنَا افْتَحْ بَيْنَنَا وَبَيْنَ قَوْمِنَا بِالْحَقِّ وَأَنتَ خَيْرُ الْفَاتِحِينَ (89) “Ndithudi ife timpekera Mulungu bodza ngati tibwerera ku chipembedzo chanu pamene Mulungu watipulumutsa ife ku icho. Ndipo ife sitikadatha mwa njira iliyonse kubwerera ku icho pokhapokha ndi chifuniro cha Mulungu. Ambuye wathu amadziwa chili chonse. Mwa Mulungu ife taika chikhulupiriro chathu. Ambuye wathu! Weruzani pakati pa ife ndi anthu athu mwachoonadi chifukwa Inu ndinu wodziwa kuweruza.” |
وَقَالَ الْمَلَأُ الَّذِينَ كَفَرُوا مِن قَوْمِهِ لَئِنِ اتَّبَعْتُمْ شُعَيْبًا إِنَّكُمْ إِذًا لَّخَاسِرُونَ (90) Ndipo mafumu a iwo amene sadakhulupirire a mtundu wa Shaibu adati: “Ngati inu mutsatira Shaibu ndithudi, mudzakhala olephera pa zochita zanu.” |
فَأَخَذَتْهُمُ الرَّجْفَةُ فَأَصْبَحُوا فِي دَارِهِمْ جَاثِمِينَ (91) Ndipo nthawi yomweyo chivomerezi chidagwa pa iwo ndipo onse adali lambilambi m’nyumba zawo |
الَّذِينَ كَذَّبُوا شُعَيْبًا كَأَن لَّمْ يَغْنَوْا فِيهَا ۚ الَّذِينَ كَذَّبُوا شُعَيْبًا كَانُوا هُمُ الْخَاسِرِينَ (92) onse amene adatsutsa Shaibu adakhala ngati sadakhalenso malo amenewa. onse amene sadakhulupirire mwa Shaibu adali otaika |
فَتَوَلَّىٰ عَنْهُمْ وَقَالَ يَا قَوْمِ لَقَدْ أَبْلَغْتُكُمْ رِسَالَاتِ رَبِّي وَنَصَحْتُ لَكُمْ ۖ فَكَيْفَ آسَىٰ عَلَىٰ قَوْمٍ كَافِرِينَ (93) Motero Shaibu adawasiya iwo nati: “Oh inu anthu anga! Ndithudi ine ndidakuuzani uthenga wa Ambuye wanga ndipo ndakupatsani ulangizi wabwino. Kodi ine ndingamvere bwanji chisoni anthu osakhulupirira?” |
وَمَا أَرْسَلْنَا فِي قَرْيَةٍ مِّن نَّبِيٍّ إِلَّا أَخَذْنَا أَهْلَهَا بِالْبَأْسَاءِ وَالضَّرَّاءِ لَعَلَّهُمْ يَضَّرَّعُونَ (94) Ndipo Ife sitimatumiza Mtumwi ku mzinda wina uli wonse koma timagwetsa pa anthu ake umphawi, matenda ndi matsoka kuti akhoza kudzichepetsa |
ثُمَّ بَدَّلْنَا مَكَانَ السَّيِّئَةِ الْحَسَنَةَ حَتَّىٰ عَفَوا وَّقَالُوا قَدْ مَسَّ آبَاءَنَا الضَّرَّاءُ وَالسَّرَّاءُ فَأَخَذْنَاهُم بَغْتَةً وَهُمْ لَا يَشْعُرُونَ (95) Ndipo tidasanduliza matsoka kukhala mwayi mpaka pamene iwo adachuluka ndikukhala ndi chuma ndipo adayamba kunena kuti: “Makolo athu nawonso adali kuona zosangalatsa ndiponso mavuto.” Ndipo Ife tidawapatsa chilango mwadzidzidzi pamene iwo sadali kudziwa |
وَلَوْ أَنَّ أَهْلَ الْقُرَىٰ آمَنُوا وَاتَّقَوْا لَفَتَحْنَا عَلَيْهِم بَرَكَاتٍ مِّنَ السَّمَاءِ وَالْأَرْضِ وَلَٰكِن كَذَّبُوا فَأَخَذْنَاهُم بِمَا كَانُوا يَكْسِبُونَ (96) Ndipo anthu a m’Mizinda imeneyi akadakhulupirira ndi kuopa uchimo, tikadawatsegulira madalitso kuchokera kumwamba ndi padziko lapansi. Koma iwo adakana choonadi. Motero Ife tidawalanga chifukwa cha zimene adali kuchita |
أَفَأَمِنَ أَهْلُ الْقُرَىٰ أَن يَأْتِيَهُم بَأْسُنَا بَيَاتًا وَهُمْ نَائِمُونَ (97) Kodi anthu a m’mizinda amaganiza kuti adali wotetezedwa ku chilango chathu ngati chikanadza kwa iwo nthawi ya usiku pamene iwo adali kugona |
أَوَأَمِنَ أَهْلُ الْقُرَىٰ أَن يَأْتِيَهُم بَأْسُنَا ضُحًى وَهُمْ يَلْعَبُونَ (98) Kapena anthu a m’Mizinda amaganiza kuti anali otetezedwa ku chilango chathu chimene chingadze kwa iwo masana pamene ali kusewera |
أَفَأَمِنُوا مَكْرَ اللَّهِ ۚ فَلَا يَأْمَنُ مَكْرَ اللَّهِ إِلَّا الْقَوْمُ الْخَاسِرُونَ (99) Kodi iwo amaganiza kuti ndi otetezedwa ku chiweruzo cha Mulungu? Palibe amene angaganize kuti ndiotetezedwa kuchilango cha Mulungu, kupatula anthu otayika |
أَوَلَمْ يَهْدِ لِلَّذِينَ يَرِثُونَ الْأَرْضَ مِن بَعْدِ أَهْلِهَا أَن لَّوْ نَشَاءُ أَصَبْنَاهُم بِذُنُوبِهِمْ ۚ وَنَطْبَعُ عَلَىٰ قُلُوبِهِمْ فَهُمْ لَا يَسْمَعُونَ (100) Kodi m’badwo uno, umene wadza pambuyo pa wina, siuzindikira kuti ngati Ife titafuna, tikhoza kuulanga chifukwa cha machimo awo? Ndipo timaika chimatiro m’mitima mwawo kuti asamve |
تِلْكَ الْقُرَىٰ نَقُصُّ عَلَيْكَ مِنْ أَنبَائِهَا ۚ وَلَقَدْ جَاءَتْهُمْ رُسُلُهُم بِالْبَيِّنَاتِ فَمَا كَانُوا لِيُؤْمِنُوا بِمَا كَذَّبُوا مِن قَبْلُ ۚ كَذَٰلِكَ يَطْبَعُ اللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِ الْكَافِرِينَ (101) Imeneyo ndi mizinda imene nkhani zake tili kukuuza iwe. Ndithudi kudadza kwa iwo Atumwi awo ndi zizindikiro zooneka. Koma iwo sadakhulupirire zimene adazikana kale. Kotero Mulungu amamata mitima ya anthu osakhulupirira |
وَمَا وَجَدْنَا لِأَكْثَرِهِم مِّنْ عَهْدٍ ۖ وَإِن وَجَدْنَا أَكْثَرَهُمْ لَفَاسِقِينَ (102) Ife sitidaone ambiri mwa iwo amene adasunga malonjezo koma Ife tidawapeza, ndithudi, ambiri a iwo ali anthu ochita zoipa |
ثُمَّ بَعَثْنَا مِن بَعْدِهِم مُّوسَىٰ بِآيَاتِنَا إِلَىٰ فِرْعَوْنَ وَمَلَئِهِ فَظَلَمُوا بِهَا ۖ فَانظُرْ كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الْمُفْسِدِينَ (103) Atapita awa, Ife tidatumiza Mose ndi zizindikiro zathu kwa Farao ndi mafumu ake koma iwo adazikana. Motero taona mapeto a anthu ochita zoipa |
وَقَالَ مُوسَىٰ يَا فِرْعَوْنُ إِنِّي رَسُولٌ مِّن رَّبِّ الْعَالَمِينَ (104) Ndipo Mose adati: “oh Farao! Ine ndine Mtumwi wochokera kwa Ambuye wazolengedwa zonse |
حَقِيقٌ عَلَىٰ أَن لَّا أَقُولَ عَلَى اللَّهِ إِلَّا الْحَقَّ ۚ قَدْ جِئْتُكُم بِبَيِّنَةٍ مِّن رَّبِّكُمْ فَأَرْسِلْ مَعِيَ بَنِي إِسْرَائِيلَ (105) Ndithudi ine sindidzanena china chilichonse chokhudza Mulungu kupatula choonadi. Ndithudi ine ndakubweretserani chizindikiro chosakaikitsa kuchokera kwa Ambuye wanu. Motero alole ana a Israyeli kuti apite ndi ine.” |
قَالَ إِن كُنتَ جِئْتَ بِآيَةٍ فَأْتِ بِهَا إِن كُنتَ مِنَ الصَّادِقِينَ (106) Farao adati: “Ngati wabwera ndi chizindikiro, chionetse msanga ngati uli kunena zoona.” |
فَأَلْقَىٰ عَصَاهُ فَإِذَا هِيَ ثُعْبَانٌ مُّبِينٌ (107) Ndipo Mose adaponya pansi ndodo yake ndipo nthawi yomweyo idasanduka njoka yeniyeni |
وَنَزَعَ يَدَهُ فَإِذَا هِيَ بَيْضَاءُ لِلنَّاظِرِينَ (108) Ndipo iye adatulutsa dzanja lake ndipo nthawi yomweyo lidasanduka loyera kwa iwo amene adaliona |
قَالَ الْمَلَأُ مِن قَوْمِ فِرْعَوْنَ إِنَّ هَٰذَا لَسَاحِرٌ عَلِيمٌ (109) Mafumu a anthu a Farao adati: “Ndithudi munthu uyu ndi wodziwa matsenga kwambiri |
يُرِيدُ أَن يُخْرِجَكُم مِّنْ أَرْضِكُمْ ۖ فَمَاذَا تَأْمُرُونَ (110) Iye akufuna kukutulutsani inu mu dziko lanu, nanga inu mukuti bwanji?” |
قَالُوا أَرْجِهْ وَأَخَاهُ وَأَرْسِلْ فِي الْمَدَائِنِ حَاشِرِينَ (111) Iwo adati: “Bamusungani pa kanthawi, iye pamodzi ndi m’bale wake ndipo tumizani anthu ku mizinda kuti akasonkhanitse.” |
يَأْتُوكَ بِكُلِّ سَاحِرٍ عَلِيمٍ (112) Ndipo kuti abweretse kwa iwe onse odziwa matsenga.” |
وَجَاءَ السَّحَرَةُ فِرْعَوْنَ قَالُوا إِنَّ لَنَا لَأَجْرًا إِن كُنَّا نَحْنُ الْغَالِبِينَ (113) Ndipo anthu a matsenga adadza kwa Farao. Iwo adati: “Ndithudi ife tidzapeza malipiro abwino ngati ife tipambana.” |
قَالَ نَعَمْ وَإِنَّكُمْ لَمِنَ الْمُقَرَّبِينَ (114) Iye adati: “Inde ndipo inu mudzakhala pafupi ndi ine.” |
قَالُوا يَا مُوسَىٰ إِمَّا أَن تُلْقِيَ وَإِمَّا أَن نَّكُونَ نَحْنُ الْمُلْقِينَ (115) Iwo adati: “oh iwe Mose! Kapena uyambe ndiwe kuponya ndodo yako kapena tiyambe ndife?” |
قَالَ أَلْقُوا ۖ فَلَمَّا أَلْقَوْا سَحَرُوا أَعْيُنَ النَّاسِ وَاسْتَرْهَبُوهُمْ وَجَاءُوا بِسِحْرٍ عَظِيمٍ (116) Iye adati: “Yambani ndinu.” Ndipo pamene iwo adaponya, iwo adalodza maso a anthu ndi kuwachititsa mantha ndipo adaonetsa matsenga akulu |
۞ وَأَوْحَيْنَا إِلَىٰ مُوسَىٰ أَنْ أَلْقِ عَصَاكَ ۖ فَإِذَا هِيَ تَلْقَفُ مَا يَأْفِكُونَ (117) Ndipo ife tidati kwa Mose: “Tsopano ponya pansi ndodo yako.” Ndipo nthawi yomweyo ndodo yake idameza zonse za matsenga zimene iwo amaonetsa |
فَوَقَعَ الْحَقُّ وَبَطَلَ مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (118) Motero choonadi chidakhazikitsidwa ndipo zochita zawo zidakhala zopanda pake |
فَغُلِبُوا هُنَالِكَ وَانقَلَبُوا صَاغِرِينَ (119) Motero iwo adagonjetsedwa nthawi yomweyo ndipo anachititsidwa manyazi |
وَأُلْقِيَ السَّحَرَةُ سَاجِدِينَ (120) Ndipo anthu a matsenga onse adagwetsa mphumi zawo pansi ndi kulambira |
قَالُوا آمَنَّا بِرَبِّ الْعَالَمِينَ (121) Iwo adati, “Ife takhulupirira mwa Ambuye wa zolengedwa zonse.” |
رَبِّ مُوسَىٰ وَهَارُونَ (122) “Ambuye wa Mose ndi Aroni.” |
قَالَ فِرْعَوْنُ آمَنتُم بِهِ قَبْلَ أَنْ آذَنَ لَكُمْ ۖ إِنَّ هَٰذَا لَمَكْرٌ مَّكَرْتُمُوهُ فِي الْمَدِينَةِ لِتُخْرِجُوا مِنْهَا أَهْلَهَا ۖ فَسَوْفَ تَعْلَمُونَ (123) Ndipo Farao adati, “Kodi inu mwakhulupirira mwa iye popanda chilolezo changa? Ndithudi chimenechi ndi chiwembu chimene inu mwakonza mu mzinda ndi cholinga chotulutsa anthu ake koma posachedwapa mudzadziwa.” |
لَأُقَطِّعَنَّ أَيْدِيَكُمْ وَأَرْجُلَكُم مِّنْ خِلَافٍ ثُمَّ لَأُصَلِّبَنَّكُمْ أَجْمَعِينَ (124) “Ndithudi ine ndidzadula manja anu ndi mapazi anu mosiyanitsa ndipo ndidzakupachikani nonse.” |
قَالُوا إِنَّا إِلَىٰ رَبِّنَا مُنقَلِبُونَ (125) Iwo adamuyankha: “Ndithudi ife tili kubwerera kwa Ambuye wathu.” |
وَمَا تَنقِمُ مِنَّا إِلَّا أَنْ آمَنَّا بِآيَاتِ رَبِّنَا لَمَّا جَاءَتْنَا ۚ رَبَّنَا أَفْرِغْ عَلَيْنَا صَبْرًا وَتَوَفَّنَا مُسْلِمِينَ (126) “Ndipo inu mufuna kubwezera kwa ife chifukwa cha kuti takhulupirira mu zizindikiro za Ambuye wathu pamene zalangizidwa kwa ife! Ambuye wathu! Tipatseni kupirira ndipo konzani kuti ife tife ngati Asilamu.” |
وَقَالَ الْمَلَأُ مِن قَوْمِ فِرْعَوْنَ أَتَذَرُ مُوسَىٰ وَقَوْمَهُ لِيُفْسِدُوا فِي الْأَرْضِ وَيَذَرَكَ وَآلِهَتَكَ ۚ قَالَ سَنُقَتِّلُ أَبْنَاءَهُمْ وَنَسْتَحْيِي نِسَاءَهُمْ وَإِنَّا فَوْقَهُمْ قَاهِرُونَ (127) Mafumu a anthu a Farao adati: “Kodi inu mukumusiya Mose ndi anthu ake kuti azichita zoipa m’dziko ndi kukusiya iwe ndi milungu yako?” Iye adayankha, “Ife tidzapha ana awo amuna ndi kusiya ana awo akazi ndi moyo ndipo Ife ndithudi tili ndi mphamvu pa iwo.” |
قَالَ مُوسَىٰ لِقَوْمِهِ اسْتَعِينُوا بِاللَّهِ وَاصْبِرُوا ۖ إِنَّ الْأَرْضَ لِلَّهِ يُورِثُهَا مَن يَشَاءُ مِنْ عِبَادِهِ ۖ وَالْعَاقِبَةُ لِلْمُتَّقِينَ (128) Mose adawauza anthu ake kuti, “Pemphani thandizo kwa Mulungu ndipo mupirire. Ndithudi Mwini wake wa dziko lino ndi Mulungu. Iye amalipereka ngati mokhalamo kwa iwo, akapolo ake, amene Iye wawasankha ndipo mapeto abwino adzakhala kwa anthu angwiro.” |
قَالُوا أُوذِينَا مِن قَبْلِ أَن تَأْتِيَنَا وَمِن بَعْدِ مَا جِئْتَنَا ۚ قَالَ عَسَىٰ رَبُّكُمْ أَن يُهْلِكَ عَدُوَّكُمْ وَيَسْتَخْلِفَكُمْ فِي الْأَرْضِ فَيَنظُرَ كَيْفَ تَعْمَلُونَ (129) Iwo adati, “Ife tidali kuzunzidwa iwe usadadze kwa ife ndipo tikuzunzidwabe pamene iwe wadza.” Iye adati: “Mwina Ambuye wanu akhoza kuwononga adani anu ndi kukupangani inu kukhala olamulira m’dziko kuti Iye aone mmene muzidzachitira.” |
وَلَقَدْ أَخَذْنَا آلَ فِرْعَوْنَ بِالسِّنِينَ وَنَقْصٍ مِّنَ الثَّمَرَاتِ لَعَلَّهُمْ يَذَّكَّرُونَ (130) Ndithudi Ife tidawalanga anthu a Farao ndi chilala cha zaka zambiri ndi kuchepa kwa zipatso kuti mwina akhoza kukumbuka |
فَإِذَا جَاءَتْهُمُ الْحَسَنَةُ قَالُوا لَنَا هَٰذِهِ ۖ وَإِن تُصِبْهُمْ سَيِّئَةٌ يَطَّيَّرُوا بِمُوسَىٰ وَمَن مَّعَهُ ۗ أَلَا إِنَّمَا طَائِرُهُمْ عِندَ اللَّهِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (131) Koma pamene zabwino zinali kudza kwa iwo, iwo amati: “Zimenezi ndi zotiyenera.” Koma ngati choipa chimadza pa iwo, adali kunena kuti chadza chifukwa cha Mose ndi anthu ake. Dziwani! Ndithudi zoipa zawo zimachokera kwa Mulungu koma ambiri a iwo sadziwa |
وَقَالُوا مَهْمَا تَأْتِنَا بِهِ مِنْ آيَةٍ لِّتَسْحَرَنَا بِهَا فَمَا نَحْنُ لَكَ بِمُؤْمِنِينَ (132) Iwo adati: “Zodabwitsa zina zilizonse zimene ungabweretse ndi cholinga chotizunguza ife sitidzakukhulupirira ayi.” |
فَأَرْسَلْنَا عَلَيْهِمُ الطُّوفَانَ وَالْجَرَادَ وَالْقُمَّلَ وَالضَّفَادِعَ وَالدَّمَ آيَاتٍ مُّفَصَّلَاتٍ فَاسْتَكْبَرُوا وَكَانُوا قَوْمًا مُّجْرِمِينَ (133) Motero ife tidawatumizira chigumula ndi dzombe, nsabwe, achule, ndi magazi kukhala zizindikiro zoonadi zosiyanasiyana zooneka komabe iwo adazikana izo chifukwa chakuti adali anthu ochimwa |
وَلَمَّا وَقَعَ عَلَيْهِمُ الرِّجْزُ قَالُوا يَا مُوسَى ادْعُ لَنَا رَبَّكَ بِمَا عَهِدَ عِندَكَ ۖ لَئِن كَشَفْتَ عَنَّا الرِّجْزَ لَنُؤْمِنَنَّ لَكَ وَلَنُرْسِلَنَّ مَعَكَ بَنِي إِسْرَائِيلَ (134) Ndipo pamene mlili unali kudza pa iwo, iwo amati: “Oh Mose! Chonde, pempha kwa Ambuye wako, m’malo mwathu, chifukwa cha lonjezo lake kwa iwe. Ngati iwe utichotsera mliliwu, ndithudi, ife tidzakhulupirira mwa iwe ndipo tidzawalola ana a Israyeli kuti apite nawe.” |
فَلَمَّا كَشَفْنَا عَنْهُمُ الرِّجْزَ إِلَىٰ أَجَلٍ هُم بَالِغُوهُ إِذَا هُمْ يَنكُثُونَ (135) Koma pamene Ife tidachotsa mlili pa iwo mpaka nthawi yokhazikika, imene adzaifika, taona! Iwo adaphwanya lonjezo |
فَانتَقَمْنَا مِنْهُمْ فَأَغْرَقْنَاهُمْ فِي الْيَمِّ بِأَنَّهُمْ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا وَكَانُوا عَنْهَا غَافِلِينَ (136) Motero ife tidawabwezera chipongwe chawo. Ndipo tidawamiza m’nyanja chifukwa chakuti iwo adakana zizindikiro zathu ndipo sadafune kulabadira |
وَأَوْرَثْنَا الْقَوْمَ الَّذِينَ كَانُوا يُسْتَضْعَفُونَ مَشَارِقَ الْأَرْضِ وَمَغَارِبَهَا الَّتِي بَارَكْنَا فِيهَا ۖ وَتَمَّتْ كَلِمَتُ رَبِّكَ الْحُسْنَىٰ عَلَىٰ بَنِي إِسْرَائِيلَ بِمَا صَبَرُوا ۖ وَدَمَّرْنَا مَا كَانَ يَصْنَعُ فِرْعَوْنُ وَقَوْمُهُ وَمَا كَانُوا يَعْرِشُونَ (137) Ndipo Ife tidawapatsa anthu amene amati ndi ofooka ulamuliro wa maiko a ku m’mawa ndi ku madzulo, amene tidawadalitsa. Ndipo Mau olemekezeka Ambuye wako kwa ana a Israyeli, adakwaniritsidwa chifukwa cha kupirira kwawo. Ndipo Ife tidaononga zinthu zonse zomwe Farao ndi anthu ake adapanga ndi zimene anali kumanga |
وَجَاوَزْنَا بِبَنِي إِسْرَائِيلَ الْبَحْرَ فَأَتَوْا عَلَىٰ قَوْمٍ يَعْكُفُونَ عَلَىٰ أَصْنَامٍ لَّهُمْ ۚ قَالُوا يَا مُوسَى اجْعَل لَّنَا إِلَٰهًا كَمَا لَهُمْ آلِهَةٌ ۚ قَالَ إِنَّكُمْ قَوْمٌ تَجْهَلُونَ (138) Ndipo Ife tidawatsogolera ana a Israyeli powoloka nyanja ndipo iwo adapeza anthu omwe anali kupembedza mafano awo. Iwo adati, “Mose tipangire ife mulungu wolingana ndi milungu yawo.” Mose anayankha: “Ndithudi inu ndinu anthu osadziwa.” |
إِنَّ هَٰؤُلَاءِ مُتَبَّرٌ مَّا هُمْ فِيهِ وَبَاطِلٌ مَّا كَانُوا يَعْمَلُونَ (139) Ndithudi anthu awa adzawonongeka chifukwa chopembedza mafano. Ndipo ntchito zawo zonse ndi zopanda pake |
قَالَ أَغَيْرَ اللَّهِ أَبْغِيكُمْ إِلَٰهًا وَهُوَ فَضَّلَكُمْ عَلَى الْعَالَمِينَ (140) Iye anati: “Kodi ndikufunireni mulungu wina kupatula Mulungu weniweni pamene Iye wakulemekezani inu kuposa mitundu yonse.” |
وَإِذْ أَنجَيْنَاكُم مِّنْ آلِ فِرْعَوْنَ يَسُومُونَكُمْ سُوءَ الْعَذَابِ ۖ يُقَتِّلُونَ أَبْنَاءَكُمْ وَيَسْتَحْيُونَ نِسَاءَكُمْ ۚ وَفِي ذَٰلِكُم بَلَاءٌ مِّن رَّبِّكُمْ عَظِيمٌ (141) Ndi pamene Ife tidakupulumutsani inu kwa anthu a Farao, amene adali kukuzunzani kwambiri, kupha ana anu amuna ndi kusiya ana anu akazi a moyo. Ndipo mmenemo munali mayesero akulu ochokera kwa Ambuye wanu |
۞ وَوَاعَدْنَا مُوسَىٰ ثَلَاثِينَ لَيْلَةً وَأَتْمَمْنَاهَا بِعَشْرٍ فَتَمَّ مِيقَاتُ رَبِّهِ أَرْبَعِينَ لَيْلَةً ۚ وَقَالَ مُوسَىٰ لِأَخِيهِ هَارُونَ اخْلُفْنِي فِي قَوْمِي وَأَصْلِحْ وَلَا تَتَّبِعْ سَبِيلَ الْمُفْسِدِينَ (142) Ife tidamusankhira Mose masiku makumi atatu ndipo tinaonjeza masiku khumi ena, motero iye adakwaniritsa nthawi imene adasankhidwa ndi Ambuye wake ya masiku makumi anayi ndipo Mose anamuuza m’bale wake Aroni kuti: Lowa m’malo mwanga pakati pa anthu anga. Uchite zinthu za ngwiro ndipo usatsatire njira ya anthu ochita zoipa |
وَلَمَّا جَاءَ مُوسَىٰ لِمِيقَاتِنَا وَكَلَّمَهُ رَبُّهُ قَالَ رَبِّ أَرِنِي أَنظُرْ إِلَيْكَ ۚ قَالَ لَن تَرَانِي وَلَٰكِنِ انظُرْ إِلَى الْجَبَلِ فَإِنِ اسْتَقَرَّ مَكَانَهُ فَسَوْفَ تَرَانِي ۚ فَلَمَّا تَجَلَّىٰ رَبُّهُ لِلْجَبَلِ جَعَلَهُ دَكًّا وَخَرَّ مُوسَىٰ صَعِقًا ۚ فَلَمَّا أَفَاقَ قَالَ سُبْحَانَكَ تُبْتُ إِلَيْكَ وَأَنَا أَوَّلُ الْمُؤْمِنِينَ (143) Ndipo pamene Mose adabwera panthawi ndi malo osankhidwa ndi Ife, Ambuye wake adalankhula naye ndipo iye adati: “Oh Ambuye wanga! Dzionetseni inu kwa ine kuti ndikuoneni.” Mulungu adati: “Iwe siudzandiona Ine ayi. Koma uone kuphiri ndipo ngati ilo lingakhalebe chikhalire ndiye kuti ukhoza kundiona Ine.” Ndipo pamene Ambuye wake anadzionetsera pa phiri, phiri lidaphwanyika ndi kusanduka fumbi lokhalokha ndipo Mose adagwa pansi ndipo adakomoka koma pamene anatsitsimuka iye adati: “Ulemerero ukhale kwa Inu. Ine ndalapa kwa Inu ndipo ine ndine woyamba wa anthu okhulupirira.” |
قَالَ يَا مُوسَىٰ إِنِّي اصْطَفَيْتُكَ عَلَى النَّاسِ بِرِسَالَاتِي وَبِكَلَامِي فَخُذْ مَا آتَيْتُكَ وَكُن مِّنَ الشَّاكِرِينَ (144) Mulungu adati: “oh iwe Mose! Ine ndakusankha iwe kukhala wapamwamba pakati pa anthu a mitundu yonse polankhula nawe. Motero gwiritsa zimene takupatsa ndipo khala othokoza.” |
وَكَتَبْنَا لَهُ فِي الْأَلْوَاحِ مِن كُلِّ شَيْءٍ مَّوْعِظَةً وَتَفْصِيلًا لِّكُلِّ شَيْءٍ فَخُذْهَا بِقُوَّةٍ وَأْمُرْ قَوْمَكَ يَأْخُذُوا بِأَحْسَنِهَا ۚ سَأُرِيكُمْ دَارَ الْفَاسِقِينَ (145) Ndipo tidamulembera iye, pa matabwa, malamulo osiyanasiyana ndi malangizo okhudza zinthu zonse ndipo tidati kwa iye, “Gwiritsa malamulo awa mwamphamvu ndiponso lamulira anthu ako kuti awatsatire bwinobwino. Ine ndidzakuonetsa midzi ya anthu oswa malamulo.” |
سَأَصْرِفُ عَنْ آيَاتِيَ الَّذِينَ يَتَكَبَّرُونَ فِي الْأَرْضِ بِغَيْرِ الْحَقِّ وَإِن يَرَوْا كُلَّ آيَةٍ لَّا يُؤْمِنُوا بِهَا وَإِن يَرَوْا سَبِيلَ الرُّشْدِ لَا يَتَّخِذُوهُ سَبِيلًا وَإِن يَرَوْا سَبِيلَ الْغَيِّ يَتَّخِذُوهُ سَبِيلًا ۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا وَكَانُوا عَنْهَا غَافِلِينَ (146) Ine ndidzawabisila zizindikiro zanga anthu a odzikweza ndi ochita zoipa mopanda chilungamo padziko ngakhale kuti iwo ataona chizindikiro china chilichonse, sadzachikhulupirira. Ngati aona njira yoyenera, iwo sadzaitsata, koma akaona njira yopotoka, iwo adzaitsatira iyo; chifukwa chakuti iwo adakana zizindikiro zathu ndipo sadafune kuzimvera ayi |
وَالَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا وَلِقَاءِ الْآخِرَةِ حَبِطَتْ أَعْمَالُهُمْ ۚ هَلْ يُجْزَوْنَ إِلَّا مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (147) Iwo amene akana zizindikiro zathu ndi kukumana kwa patsiku la chiweruzo ntchito zawo ndi zopanda pake. Kodi iwo amayembekeza kuti adzalipidwa kuposa zimene amachita |
وَاتَّخَذَ قَوْمُ مُوسَىٰ مِن بَعْدِهِ مِنْ حُلِيِّهِمْ عِجْلًا جَسَدًا لَّهُ خُوَارٌ ۚ أَلَمْ يَرَوْا أَنَّهُ لَا يُكَلِّمُهُمْ وَلَا يَهْدِيهِمْ سَبِيلًا ۘ اتَّخَذُوهُ وَكَانُوا ظَالِمِينَ (148) Ndipo anthu ake a Mose adaumba, iye atachoka, kuchokera ku mphete ndi ndolo zawo, chifanizo cha mwana wa ng’ombe amene adali ndi mawu. Kodi iwo sadathe kuona kuti iyo siinathe kuwalankhula kapena kuwalondolera njira? Iwo adaipembedza iyo, kotero adalakwa |
وَلَمَّا سُقِطَ فِي أَيْدِيهِمْ وَرَأَوْا أَنَّهُمْ قَدْ ضَلُّوا قَالُوا لَئِن لَّمْ يَرْحَمْنَا رَبُّنَا وَيَغْفِرْ لَنَا لَنَكُونَنَّ مِنَ الْخَاسِرِينَ (149) Koma pamene iwo adazindikira ndi kuona kuti adalakwa, iwo adati: “Ngati Ambuye wathu sakhala ndi chifundo ndi ife ndi kutikhululukira, ndithudi, ife tidzakhala anthu otayika.” |
وَلَمَّا رَجَعَ مُوسَىٰ إِلَىٰ قَوْمِهِ غَضْبَانَ أَسِفًا قَالَ بِئْسَمَا خَلَفْتُمُونِي مِن بَعْدِي ۖ أَعَجِلْتُمْ أَمْرَ رَبِّكُمْ ۖ وَأَلْقَى الْأَلْوَاحَ وَأَخَذَ بِرَأْسِ أَخِيهِ يَجُرُّهُ إِلَيْهِ ۚ قَالَ ابْنَ أُمَّ إِنَّ الْقَوْمَ اسْتَضْعَفُونِي وَكَادُوا يَقْتُلُونَنِي فَلَا تُشْمِتْ بِيَ الْأَعْدَاءَ وَلَا تَجْعَلْنِي مَعَ الْقَوْمِ الظَّالِمِينَ (150) Ndipo pamene Mose adabwerera kwa anthu ake, wokwiya ndi wachisoni, iye adati: “Kodi ndi chinthu choipa bwanji chimene mwachita pamene ine kudalibe! Kodi inu munafulumira ndi kusiya kupembedza Ambuye wanu?” Ndipo iye adaponya pansi matabwa a malamulo, nagwira mutu wa m’bale wake ndi kumukokera kwa iye. Aroni adati: “Iwe mwana wa Amayi anga! Ndithu anthu awa adandiposa mphamvu ndipo adakhala pang’ono kundipha ndipo usalole kuti adani anga asangalale pa ine ndipo usandiike pa gulu la anthu ochita zoipa.” |
قَالَ رَبِّ اغْفِرْ لِي وَلِأَخِي وَأَدْخِلْنَا فِي رَحْمَتِكَ ۖ وَأَنتَ أَرْحَمُ الرَّاحِمِينَ (151) Mose adati: “Ambuye wanga! Ndikhululukireni ine pamodzi ndi m’bale wanga ndipo tilowetseni m’chisoni chanu chifukwa Inu ndinu oonetsa chisoni kwambiri kuposa onse omwe amaonetsa chisoni.” |
إِنَّ الَّذِينَ اتَّخَذُوا الْعِجْلَ سَيَنَالُهُمْ غَضَبٌ مِّن رَّبِّهِمْ وَذِلَّةٌ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ۚ وَكَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُفْتَرِينَ (152) Ndithudi iwo amene adapembedza ng’ombe, mkwiyo wa Ambuye wawo ndi kupeputsidwa kudzadza kwa iwo m’moyo uno. Mmenemo ndi mmene timalipirira anthu opeka mabodza |
وَالَّذِينَ عَمِلُوا السَّيِّئَاتِ ثُمَّ تَابُوا مِن بَعْدِهَا وَآمَنُوا إِنَّ رَبَّكَ مِن بَعْدِهَا لَغَفُورٌ رَّحِيمٌ (153) Koma iwo amene anachita zoipa ndipo pambuyo pake adalapa ndi kukhala ndi chikhulupiriro, ndithu Ambuye wako pambuyo pa izo ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha |
وَلَمَّا سَكَتَ عَن مُّوسَى الْغَضَبُ أَخَذَ الْأَلْوَاحَ ۖ وَفِي نُسْخَتِهَا هُدًى وَرَحْمَةٌ لِّلَّذِينَ هُمْ لِرَبِّهِمْ يَرْهَبُونَ (154) Ndipo pamene mkwiyo wake udatha, Mose adatenga matabwa a malamulo, amene m’zolembedwa zake mudali chilangizo ndi chifundo kwa anthu amene amaopa Ambuye wawo |
وَاخْتَارَ مُوسَىٰ قَوْمَهُ سَبْعِينَ رَجُلًا لِّمِيقَاتِنَا ۖ فَلَمَّا أَخَذَتْهُمُ الرَّجْفَةُ قَالَ رَبِّ لَوْ شِئْتَ أَهْلَكْتَهُم مِّن قَبْلُ وَإِيَّايَ ۖ أَتُهْلِكُنَا بِمَا فَعَلَ السُّفَهَاءُ مِنَّا ۖ إِنْ هِيَ إِلَّا فِتْنَتُكَ تُضِلُّ بِهَا مَن تَشَاءُ وَتَهْدِي مَن تَشَاءُ ۖ أَنتَ وَلِيُّنَا فَاغْفِرْ لَنَا وَارْحَمْنَا ۖ وَأَنتَ خَيْرُ الْغَافِرِينَ (155) Ndipo Mose adasankha, pakati pa anthu ake, amuna makumi asanu ndi awiri kuti adzakumane nafe ndipo pamene nthaka idagwedezeka pamapazi pawo, Mose adati: “Chikadakhala chifuniro chanu, Ambuye, mukadawaononga iwo ndi ine kale. Kodi inu mungationonge chifukwa cha ntchito za anthu amene ali pakati pathu? Awa ndi mayesero anu, amene Inu mumasocheretsa aliyense amene mwamufuna ndi kutsogolera yemwe mwamufuna. Inu nokha ndinu Mtetezi wathu ndipo tichitireni chisoni chifukwa Inu ndinu wopambana onse amene amakhululukira.” |
۞ وَاكْتُبْ لَنَا فِي هَٰذِهِ الدُّنْيَا حَسَنَةً وَفِي الْآخِرَةِ إِنَّا هُدْنَا إِلَيْكَ ۚ قَالَ عَذَابِي أُصِيبُ بِهِ مَنْ أَشَاءُ ۖ وَرَحْمَتِي وَسِعَتْ كُلَّ شَيْءٍ ۚ فَسَأَكْتُبُهَا لِلَّذِينَ يَتَّقُونَ وَيُؤْتُونَ الزَّكَاةَ وَالَّذِينَ هُم بِآيَاتِنَا يُؤْمِنُونَ (156) “Ndipo tipatseni ife zabwino m’moyo uno ndiponso m’moyo umene uli nkudza. Ndithudi ife tabwerera kwa Inu.” Mulungu adati: “Ine ndidzaonetsa chilango changa kwa aliyense amene ndimufuna ndipo chifundo changa chimakwanira zinthu zonse. Ine ndidzaonetsa chisoni kwa onse amene amalewa zoipa ndipo amapereka chaulere ndi iwo amene amakhulupirirazizindikirozathu.” |
الَّذِينَ يَتَّبِعُونَ الرَّسُولَ النَّبِيَّ الْأُمِّيَّ الَّذِي يَجِدُونَهُ مَكْتُوبًا عِندَهُمْ فِي التَّوْرَاةِ وَالْإِنجِيلِ يَأْمُرُهُم بِالْمَعْرُوفِ وَيَنْهَاهُمْ عَنِ الْمُنكَرِ وَيُحِلُّ لَهُمُ الطَّيِّبَاتِ وَيُحَرِّمُ عَلَيْهِمُ الْخَبَائِثَ وَيَضَعُ عَنْهُمْ إِصْرَهُمْ وَالْأَغْلَالَ الَّتِي كَانَتْ عَلَيْهِمْ ۚ فَالَّذِينَ آمَنُوا بِهِ وَعَزَّرُوهُ وَنَصَرُوهُ وَاتَّبَعُوا النُّورَ الَّذِي أُنزِلَ مَعَهُ ۙ أُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (157) Iwoameneamatsatira Mtumwi kapena Mneneri amene sadziwa kulemba ndi kuwerenga, amene mbiri yake inalembedwa m’Buku la chipangano chakale ndi mu chipangano chatsopano. Iye amawalamulira kuchita zabwino ndipo amawaletsa kuchita zoipa. Ndipo amawaloleza zabwino ndi kuwaletsa zonyansa. Iye amawapeputsira katundu wolemera amene adali pa iwo. Motero iwo amene akhulupirira mwa iye ndi kumulemekeza, ndi kumuthandiza iye ndi kutsata kuunika kumene kwatumizidwa ndi iye, ndi okhawo amene adzakhala opambana |
قُلْ يَا أَيُّهَا النَّاسُ إِنِّي رَسُولُ اللَّهِ إِلَيْكُمْ جَمِيعًا الَّذِي لَهُ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ يُحْيِي وَيُمِيتُ ۖ فَآمِنُوا بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ النَّبِيِّ الْأُمِّيِّ الَّذِي يُؤْمِنُ بِاللَّهِ وَكَلِمَاتِهِ وَاتَّبِعُوهُ لَعَلَّكُمْ تَهْتَدُونَ (158) Nena, “Oh inu anthu! Ndithudi ine ndatumizidwa ngati Mtumwi wa Mulungu kwa inu nonse, yemwe ali Mwini ufumu wakumwamba ndi wa padziko lapansi. Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Iye amapereka moyo ndi imfa. Motero khulupilirani mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi wake, Mtumwi yemwe sadziwa kuwerenga ndi kulemba, amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi m’Mawu ake. Ndipo mutsatireni iye kuti mukhale otsogozedwa.” |
وَمِن قَوْمِ مُوسَىٰ أُمَّةٌ يَهْدُونَ بِالْحَقِّ وَبِهِ يَعْدِلُونَ (159) Pakati pa anthu a Mose, pali anthu ena amene amatsogolera mwa choonadi ndipo anali kuchita chilungamo |
وَقَطَّعْنَاهُمُ اثْنَتَيْ عَشْرَةَ أَسْبَاطًا أُمَمًا ۚ وَأَوْحَيْنَا إِلَىٰ مُوسَىٰ إِذِ اسْتَسْقَاهُ قَوْمُهُ أَنِ اضْرِب بِّعَصَاكَ الْحَجَرَ ۖ فَانبَجَسَتْ مِنْهُ اثْنَتَا عَشْرَةَ عَيْنًا ۖ قَدْ عَلِمَ كُلُّ أُنَاسٍ مَّشْرَبَهُمْ ۚ وَظَلَّلْنَا عَلَيْهِمُ الْغَمَامَ وَأَنزَلْنَا عَلَيْهِمُ الْمَنَّ وَالسَّلْوَىٰ ۖ كُلُوا مِن طَيِّبَاتِ مَا رَزَقْنَاكُمْ ۚ وَمَا ظَلَمُونَا وَلَٰكِن كَانُوا أَنفُسَهُمْ يَظْلِمُونَ (160) Ndipo Ifetidawagawakukhalamafukokhumindiiwiri. Ndipo Ife tidamupatsa Mau Mose, ndipo tidati: “Menya thanthwe ndi ndodo yako.” Pomwepo a kasupe khumi ndi awiri anatumphuka kuchokera m’thanthwe ndipo gulu lililonse lidadziwa chitsime chake. Ife tidawavundikira ndi mitambo ndipo tidawatumizira Manna ndi mbalame ndipo tidati: “Idyani zinthu zabwino zimene takupatsani inu.” Iwo sadatilakwire Ife koma analakwira mizimu yawo |
وَإِذْ قِيلَ لَهُمُ اسْكُنُوا هَٰذِهِ الْقَرْيَةَ وَكُلُوا مِنْهَا حَيْثُ شِئْتُمْ وَقُولُوا حِطَّةٌ وَادْخُلُوا الْبَابَ سُجَّدًا نَّغْفِرْ لَكُمْ خَطِيئَاتِكُمْ ۚ سَنَزِيدُ الْمُحْسِنِينَ (161) Ndi pamene zidanenedwa kwa iwo: “Khalani mu Mzinda uwu ndipo idyani mmene mungafunire ndipo munene kuti: ‘Tikhululukireni machimo athu; ndipo lowani pa khomo modzichepetsa.’ Ife tidzakukhululukirani machimo anu. Ndipo tidzaonjezera mphotho ya iwo amene achita zabwino.” |
فَبَدَّلَ الَّذِينَ ظَلَمُوا مِنْهُمْ قَوْلًا غَيْرَ الَّذِي قِيلَ لَهُمْ فَأَرْسَلْنَا عَلَيْهِمْ رِجْزًا مِّنَ السَّمَاءِ بِمَا كَانُوا يَظْلِمُونَ (162) Koma anthu oipa amene adali pakati pawo, adasintha mawu amene adapatsidwa, motero Ife tidawatumizira chilango kuchokera kumwamba chifukwa cha kulakwa kwawo |
وَاسْأَلْهُمْ عَنِ الْقَرْيَةِ الَّتِي كَانَتْ حَاضِرَةَ الْبَحْرِ إِذْ يَعْدُونَ فِي السَّبْتِ إِذْ تَأْتِيهِمْ حِيتَانُهُمْ يَوْمَ سَبْتِهِمْ شُرَّعًا وَيَوْمَ لَا يَسْبِتُونَ ۙ لَا تَأْتِيهِمْ ۚ كَذَٰلِكَ نَبْلُوهُم بِمَا كَانُوا يَفْسُقُونَ (163) Ndipo afunse iwo za Mzinda umene udali pa mbali pa nyanja pamene iwo adaphwanya malamulo a tsiku la Sabata pamene nsomba zinali kusewera pafupi ndi kumatulutsa mitu yawo pamene sizidali kutero pa masiku ena. Motero Ife tidawayesa chifukwa iwo adali anthu oswa malamulo |
وَإِذْ قَالَتْ أُمَّةٌ مِّنْهُمْ لِمَ تَعِظُونَ قَوْمًا ۙ اللَّهُ مُهْلِكُهُمْ أَوْ مُعَذِّبُهُمْ عَذَابًا شَدِيدًا ۖ قَالُوا مَعْذِرَةً إِلَىٰ رَبِّكُمْ وَلَعَلَّهُمْ يَتَّقُونَ (164) Ndi pamene gulu lina lidati, “Kodi ndi chifukwa chiyani uli kulalikira kwa anthu amene Mulungu ali pafupi kuwaononga kapena kuwalanga kwambiri?” Iwo adayankha kuti; “Ife tisadzakhale ndi mlandu kwa Ambuye wanu ndiponso kuti mwina iwo angaope Mulungu.” |
فَلَمَّا نَسُوا مَا ذُكِّرُوا بِهِ أَنجَيْنَا الَّذِينَ يَنْهَوْنَ عَنِ السُّوءِ وَأَخَذْنَا الَّذِينَ ظَلَمُوا بِعَذَابٍ بَئِيسٍ بِمَا كَانُوا يَفْسُقُونَ (165) Ndipo pamaso pa iwo amene adaiwala chikumbutso chimene chidaperekedwa kwa iwo, Ife tidapulumutsa iwo amene amaletsa zoipa ndipo Ife tidawalanga amene adali olakwa ndi chilango chowawa chifukwa cha machimo awo |
فَلَمَّا عَتَوْا عَن مَّا نُهُوا عَنْهُ قُلْنَا لَهُمْ كُونُوا قِرَدَةً خَاسِئِينَ (166) Ndipo pa nthawi imene iwo adapitiriza kuchita zinthu zimene adaletsedwa kuchita, Ife tidati kwa iwo! “Khalani anyani, onyozeka ndi okanidwa.” |
وَإِذْ تَأَذَّنَ رَبُّكَ لَيَبْعَثَنَّ عَلَيْهِمْ إِلَىٰ يَوْمِ الْقِيَامَةِ مَن يَسُومُهُمْ سُوءَ الْعَذَابِ ۗ إِنَّ رَبَّكَ لَسَرِيعُ الْعِقَابِ ۖ وَإِنَّهُ لَغَفُورٌ رَّحِيمٌ (167) Ndi pamene Ambuye wako adalamula kuti adzawatumizira, mpaka tsiku la chiweruzo, iwo amene azibweretsa mazunzo ndi mnyozo pa iwo. Ndithudi Ambuye wako ndi wachangu polanga. Ndipo, ndithudi, Iye ndi wokhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha |
وَقَطَّعْنَاهُمْ فِي الْأَرْضِ أُمَمًا ۖ مِّنْهُمُ الصَّالِحُونَ وَمِنْهُمْ دُونَ ذَٰلِكَ ۖ وَبَلَوْنَاهُم بِالْحَسَنَاتِ وَالسَّيِّئَاتِ لَعَلَّهُمْ يَرْجِعُونَ (168) Ife tidawamwaza pa dziko lapansi m’magulu osiyanasiyana. Ena adali anthu angwiro pamene ena ndi anthu oipa. Ndipo Ife tidawayesa powapatsa madalitso ndi matsoka kuti mwina akhoza kubwerera |
فَخَلَفَ مِن بَعْدِهِمْ خَلْفٌ وَرِثُوا الْكِتَابَ يَأْخُذُونَ عَرَضَ هَٰذَا الْأَدْنَىٰ وَيَقُولُونَ سَيُغْفَرُ لَنَا وَإِن يَأْتِهِمْ عَرَضٌ مِّثْلُهُ يَأْخُذُوهُ ۚ أَلَمْ يُؤْخَذْ عَلَيْهِم مِّيثَاقُ الْكِتَابِ أَن لَّا يَقُولُوا عَلَى اللَّهِ إِلَّا الْحَقَّ وَدَرَسُوا مَا فِيهِ ۗ وَالدَّارُ الْآخِرَةُ خَيْرٌ لِّلَّذِينَ يَتَّقُونَ ۗ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (169) Ndipo lidalowa m’malo gulu lina loipa limene linatenga Buku, koma iwo adasankha zinthu zopanda pake za pa dziko lapansi. Ndipo iwo adati “Tidzakhululukidwa.” Koma zitawapezanso zinthu zopanda pake za mtundu womwewo iwo akadazilandira. Kodi lonjezo la m’Buku silinalandiridwe kuchokera kwa iwo kuti sadzanena chili chonse chokhudza Mulungu kupatula choonadi? Ndipo iwo aphunzira zomwe zili m’menemo. Ndipo dziko limene lili nkudza ndi labwino kwa anthu oopa Mulungu. Kodi inu mulibe nzeru |
وَالَّذِينَ يُمَسِّكُونَ بِالْكِتَابِ وَأَقَامُوا الصَّلَاةَ إِنَّا لَا نُضِيعُ أَجْرَ الْمُصْلِحِينَ (170) Akakhala iwo amene amatsatira moona Mau a Mulungu ndi kupitiriza mapemphero, ndithudi, Ife sitidzaononga mphotho za anthu ochita ntchito zabwino |
۞ وَإِذْ نَتَقْنَا الْجَبَلَ فَوْقَهُمْ كَأَنَّهُ ظُلَّةٌ وَظَنُّوا أَنَّهُ وَاقِعٌ بِهِمْ خُذُوا مَا آتَيْنَاكُم بِقُوَّةٍ وَاذْكُرُوا مَا فِيهِ لَعَلَّكُمْ تَتَّقُونَ (171) Ndi pamene tidakweza phiri ndikuliika pamwamba pawo kukhala ngati mthunzi ndipo iwo amaganiza kuti liwagwera. Ndipo Ife tidati, “Gwiritsani chimene takupatsani inu ndipo kumbukirani zimene zili m’kati mwake kuti mukhale oopa Mulungu ndi kumumvera Iye.” |
وَإِذْ أَخَذَ رَبُّكَ مِن بَنِي آدَمَ مِن ظُهُورِهِمْ ذُرِّيَّتَهُمْ وَأَشْهَدَهُمْ عَلَىٰ أَنفُسِهِمْ أَلَسْتُ بِرَبِّكُمْ ۖ قَالُوا بَلَىٰ ۛ شَهِدْنَا ۛ أَن تَقُولُوا يَوْمَ الْقِيَامَةِ إِنَّا كُنَّا عَنْ هَٰذَا غَافِلِينَ (172) Ndi pamene Ambuye wako adabweretsa kuchokera kwa ana a Adamu, kuchokera m’misana mwawo mbeu yawo ndipo adawapanga kuti alumbire okha. Iye adati, “Kodi ine sindine Ambuye wanu?” Iwo adayankha: “Indedi! Ife tili kuchitira umboni.” Kuti mwina mungadzanene, pa tsiku louka kwa akufa kuti: “Ndithudi ife sitimadziwa china chilichonse cha izi.” |
أَوْ تَقُولُوا إِنَّمَا أَشْرَكَ آبَاؤُنَا مِن قَبْلُ وَكُنَّا ذُرِّيَّةً مِّن بَعْدِهِمْ ۖ أَفَتُهْلِكُنَا بِمَا فَعَلَ الْمُبْطِلُونَ (173) Kapena mwina mungadzanene kuti, “Ndi makolo athu akale amene amapembedza milungu ina pambali pa Mulungu. Ife tidali m’badwo wapambuyo pawo. Kodi inu mutiononga chifukwa cha zimene adachita anthu oipa?” |
وَكَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ الْآيَاتِ وَلَعَلَّهُمْ يَرْجِعُونَ (174) Motero Ife tili kulongosola chivumbulutso chathu kuti iwo abwerere |
وَاتْلُ عَلَيْهِمْ نَبَأَ الَّذِي آتَيْنَاهُ آيَاتِنَا فَانسَلَخَ مِنْهَا فَأَتْبَعَهُ الشَّيْطَانُ فَكَانَ مِنَ الْغَاوِينَ (175) Ndipo awerengere iwo za nkhani ya munthu amene Ife tidamupatsa zizindikiro zathu koma iye adazikana, ndipo Satana adamutsatira ndipo iye adali mmodzi wa anthu osochera |
وَلَوْ شِئْنَا لَرَفَعْنَاهُ بِهَا وَلَٰكِنَّهُ أَخْلَدَ إِلَى الْأَرْضِ وَاتَّبَعَ هَوَاهُ ۚ فَمَثَلُهُ كَمَثَلِ الْكَلْبِ إِن تَحْمِلْ عَلَيْهِ يَلْهَثْ أَوْ تَتْرُكْهُ يَلْهَث ۚ ذَّٰلِكَ مَثَلُ الْقَوْمِ الَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا ۚ فَاقْصُصِ الْقَصَصَ لَعَلَّهُمْ يَتَفَكَّرُونَ (176) Ndipo tikadafuna Ife tikadamukweza iye, koma iye adaumirira moyo wa pa dziko lino lapansi ndi kutsatira zilakolako zake. Motero iye akhoza kufanizidwa ndi galu, amene ngati umupilikitsa, amatulutsa lilime lake, kaya umusiya yekha iye amalitulutsabe. Limenelo ndi fanizo la anthu amene amakana zizindikiro zathu. Motero auze nkhanizi kuti mwina iwo akhoza kuganiza bwino |
سَاءَ مَثَلًا الْقَوْمُ الَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا وَأَنفُسَهُمْ كَانُوا يَظْلِمُونَ (177) Choipa ndicho chifanizo cha anthu amene amakana chivumbulutso chathu, ndipo iwo amachimwira mizimu yawo yomwe |
مَن يَهْدِ اللَّهُ فَهُوَ الْمُهْتَدِي ۖ وَمَن يُضْلِلْ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْخَاسِرُونَ (178) Aliyense amene Mulungu amamutsogolera, iye amatsogozedwa bwino ndipo aliyense amene Iye amusocheretsa, iye ndi olephera |
وَلَقَدْ ذَرَأْنَا لِجَهَنَّمَ كَثِيرًا مِّنَ الْجِنِّ وَالْإِنسِ ۖ لَهُمْ قُلُوبٌ لَّا يَفْقَهُونَ بِهَا وَلَهُمْ أَعْيُنٌ لَّا يُبْصِرُونَ بِهَا وَلَهُمْ آذَانٌ لَّا يَسْمَعُونَ بِهَا ۚ أُولَٰئِكَ كَالْأَنْعَامِ بَلْ هُمْ أَضَلُّ ۚ أُولَٰئِكَ هُمُ الْغَافِلُونَ (179) Ndithudi, Ife tanalenga majini ndi anthu ambiri kuti akalowe ku Gahena. Iwo ali ndi mitima imene sangathe kuzindikira, ali ndi maso amene sangathe kuona, ali ndi makutu amene sangathe kumva ayi. Iwo ali ngati ng’ombe. Iyai! Iwo ndi osochera kwambiri. Amenewa! Ndi nkhutukumve |
وَلِلَّهِ الْأَسْمَاءُ الْحُسْنَىٰ فَادْعُوهُ بِهَا ۖ وَذَرُوا الَّذِينَ يُلْحِدُونَ فِي أَسْمَائِهِ ۚ سَيُجْزَوْنَ مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (180) Mulungu ali ndi mayina abwino kwambiri. Motero muitaneni pa mayina amenewo ndipo asiyeni iwo amene amaononga ulemerero wa mayina ake. Iwo adzalangidwa chifukwa cha zimene adali kuchita |
وَمِمَّنْ خَلَقْنَا أُمَّةٌ يَهْدُونَ بِالْحَقِّ وَبِهِ يَعْدِلُونَ (181) Ndipo pakati pa iwo amene tidawalenga, alipo anthu amene amalangiza choonadi ndipo amachita chilungamo |
وَالَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا سَنَسْتَدْرِجُهُم مِّنْ حَيْثُ لَا يَعْلَمُونَ (182) Iwo amene amakana chivumbulutso chathu, Ife tidzawagwira pang’onopang’ono ndi chilango chathu popanda iwo kuzindikira |
وَأُمْلِي لَهُمْ ۚ إِنَّ كَيْدِي مَتِينٌ (183) Ndimawapatsa nthawi, ndithudi, chikonzero changa ndi chokhwima |
أَوَلَمْ يَتَفَكَّرُوا ۗ مَا بِصَاحِبِهِم مِّن جِنَّةٍ ۚ إِنْ هُوَ إِلَّا نَذِيرٌ مُّبِينٌ (184) Kodi iwo saganizira? Mulibe misala mwa m’bale wawo. Iye ndi mchenjezi basi |
أَوَلَمْ يَنظُرُوا فِي مَلَكُوتِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَمَا خَلَقَ اللَّهُ مِن شَيْءٍ وَأَنْ عَسَىٰ أَن يَكُونَ قَدِ اقْتَرَبَ أَجَلُهُمْ ۖ فَبِأَيِّ حَدِيثٍ بَعْدَهُ يُؤْمِنُونَ (185) Kodi iwo sayang’ana mu Ufumu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi ndi zonse zimene Mulungu adazilenga kuti aone ngati ndi mapeto a moyo wawo? Kodi ndi uthenga uti pambuyo pa uwu umene iwo adzakhulupirire |
مَن يُضْلِلِ اللَّهُ فَلَا هَادِيَ لَهُ ۚ وَيَذَرُهُمْ فِي طُغْيَانِهِمْ يَعْمَهُونَ (186) Aliyense amene Mulungu wamusocheza palibe wina amene angamutsogolere ndipo Iye amawasiya kuchita zinthu mwakhungu poswa malamulo |
يَسْأَلُونَكَ عَنِ السَّاعَةِ أَيَّانَ مُرْسَاهَا ۖ قُلْ إِنَّمَا عِلْمُهَا عِندَ رَبِّي ۖ لَا يُجَلِّيهَا لِوَقْتِهَا إِلَّا هُوَ ۚ ثَقُلَتْ فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ لَا تَأْتِيكُمْ إِلَّا بَغْتَةً ۗ يَسْأَلُونَكَ كَأَنَّكَ حَفِيٌّ عَنْهَا ۖ قُلْ إِنَّمَا عِلْمُهَا عِندَ اللَّهِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَعْلَمُونَ (187) Iwo amakufunsa iwe za ola lomaliza kuti lidzadza liti? Nena, “Amene adziwa za tsikuli ndi Ambuye wanga. Palibe amene adzaulule nthawi yake kupatula Iye yekha.” Lidzalemetsa kumwamba ndi dziko lapansi. Ilo silidzadza kwa inu kupatula mwadzidzidzi. Iwo alikufunsa ngati iwe umadziwa zambiri za olali. Nena, “Kuzindikira za tsikuli kuli kwa Mulungu yekha koma anthu ambiri sadziwa.” |
قُل لَّا أَمْلِكُ لِنَفْسِي نَفْعًا وَلَا ضَرًّا إِلَّا مَا شَاءَ اللَّهُ ۚ وَلَوْ كُنتُ أَعْلَمُ الْغَيْبَ لَاسْتَكْثَرْتُ مِنَ الْخَيْرِ وَمَا مَسَّنِيَ السُّوءُ ۚ إِنْ أَنَا إِلَّا نَذِيرٌ وَبَشِيرٌ لِّقَوْمٍ يُؤْمِنُونَ (188) Nena, “Ine ndilibe mphamvu yopeza zinthu, kapena kupewa mavuto kupatula ndi chifuniro cha Mulungu. Ine ndikadakhala wodziwa chilichonse chobisika ndikadadzichulukitsira chuma ndipo palibe choipa chimene chikadandipeza. Ine sindine wina aliyense ayi koma wopereka chenjezo ndi wobweretsa nkhani yabwino kwa anthu okhulupirira.” |
۞ هُوَ الَّذِي خَلَقَكُم مِّن نَّفْسٍ وَاحِدَةٍ وَجَعَلَ مِنْهَا زَوْجَهَا لِيَسْكُنَ إِلَيْهَا ۖ فَلَمَّا تَغَشَّاهَا حَمَلَتْ حَمْلًا خَفِيفًا فَمَرَّتْ بِهِ ۖ فَلَمَّا أَثْقَلَت دَّعَوَا اللَّهَ رَبَّهُمَا لَئِنْ آتَيْتَنَا صَالِحًا لَّنَكُونَنَّ مِنَ الشَّاكِرِينَ (189) Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo kuchokera kwa munthu ameneyu adamulengera mkazi wake, kuti akhoza kupeza chisangalalo pokhala naye. Ndipo pamene iye amagona naye, iye adatenga pakati pamene ananyamula mosavutika. Koma pamene panakula, onse awiri amapempha Ambuye wawo: “Ngati Inu mutatipatsa mwana wabwino ndithudi ife tidzakhala othokoza.” |
فَلَمَّا آتَاهُمَا صَالِحًا جَعَلَا لَهُ شُرَكَاءَ فِيمَا آتَاهُمَا ۚ فَتَعَالَى اللَّهُ عَمَّا يُشْرِكُونَ (190) Koma pamene akawapatsa mwana wabwino, iwo amakhazikitsa milungu ina pambali pa Iye kuthokoza pa zimene wawapatsa. Alemekezeke Mulungu kuposa zimene akumphatikiza nazo |
أَيُشْرِكُونَ مَا لَا يَخْلُقُ شَيْئًا وَهُمْ يُخْلَقُونَ (191) Kodi iwo akukhazikitsa milungu ina pambali pa Mulungu weni weni imene siingathe kulenga zina zilizonse koma kuti nayonso ndi yolengedwa |
وَلَا يَسْتَطِيعُونَ لَهُمْ نَصْرًا وَلَا أَنفُسَهُمْ يَنصُرُونَ (192) Palibe chimene ingawathandize ayi ndiponso iyo siingathe kudzithandiza yokha |
وَإِن تَدْعُوهُمْ إِلَى الْهُدَىٰ لَا يَتَّبِعُوكُمْ ۚ سَوَاءٌ عَلَيْكُمْ أَدَعَوْتُمُوهُمْ أَمْ أَنتُمْ صَامِتُونَ (193) Ndipo ngati iwe uwaitana kunjira yoyenera iwo sadzakutsatira ayi. Ndi chimodzimodzi kwa iwe kaya uwaitana kapena ukhala chete |
إِنَّ الَّذِينَ تَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ عِبَادٌ أَمْثَالُكُمْ ۖ فَادْعُوهُمْ فَلْيَسْتَجِيبُوا لَكُمْ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (194) Ndithudi iwo amene mumawapembedza powonjezera pa Mulungu weniweni ndi akapolo ngati inu nomwe. Motero aitaneni ndipo akuyankheni ngati zimene munena ndi zoonadi |
أَلَهُمْ أَرْجُلٌ يَمْشُونَ بِهَا ۖ أَمْ لَهُمْ أَيْدٍ يَبْطِشُونَ بِهَا ۖ أَمْ لَهُمْ أَعْيُنٌ يُبْصِرُونَ بِهَا ۖ أَمْ لَهُمْ آذَانٌ يَسْمَعُونَ بِهَا ۗ قُلِ ادْعُوا شُرَكَاءَكُمْ ثُمَّ كِيدُونِ فَلَا تُنظِرُونِ (195) Kodi iwo ali ndi miyendo yoti angayendere? Kodi ali ndi manja oti angagwire china chilichonse? Kapena ali ndi maso oti angaonere? Kapena ali ndi makutu oti angamvere? Nena, “Itanani milungu yanu yabodza ndipo pangani chiwembu chanu pa ine ndipo musandipatse mpumulo ayi.” |
إِنَّ وَلِيِّيَ اللَّهُ الَّذِي نَزَّلَ الْكِتَابَ ۖ وَهُوَ يَتَوَلَّى الصَّالِحِينَ (196) Ndithudi Mtetezi wanga ndi Mulungu amene wavumbulutsa Buku ndipo Iye ndi Mtetezi wa anthu a chilungamo |
وَالَّذِينَ تَدْعُونَ مِن دُونِهِ لَا يَسْتَطِيعُونَ نَصْرَكُمْ وَلَا أَنفُسَهُمْ يَنصُرُونَ (197) Ndipo iwo amene mumawapembedza powonjezera pa Iye sangathe kukuthandizani inu ndiponso sangathe kudzithandiza iwo eni |
وَإِن تَدْعُوهُمْ إِلَى الْهُدَىٰ لَا يَسْمَعُوا ۖ وَتَرَاهُمْ يَنظُرُونَ إِلَيْكَ وَهُمْ لَا يُبْصِرُونَ (198) Ndipo ngati iwe uwaitanira ku njira yoyenera, sakumva ayi ndipo udzawaona ali kukuyang’ana iwe koma sakuona ai |
خُذِ الْعَفْوَ وَأْمُرْ بِالْعُرْفِ وَأَعْرِضْ عَنِ الْجَاهِلِينَ (199) Onetsa kukhululukira, lamulira zabwino ndipo uwapewe anthu osadziwa |
وَإِمَّا يَنزَغَنَّكَ مِنَ الشَّيْطَانِ نَزْغٌ فَاسْتَعِذْ بِاللَّهِ ۚ إِنَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (200) Ndipo ngati Satana akuyesa iwe, thawira kwa Mulungu. Ndithudi Iye ndi wakumva ndi wodziwa |
إِنَّ الَّذِينَ اتَّقَوْا إِذَا مَسَّهُمْ طَائِفٌ مِّنَ الشَّيْطَانِ تَذَكَّرُوا فَإِذَا هُم مُّبْصِرُونَ (201) Ndithudi iwo amene amaopa Mulungu, ngati maganizo oipa adza kwa iwo kuchokera kwa Satana, iwo amakumbukira ndipo amaona kuunika |
وَإِخْوَانُهُمْ يَمُدُّونَهُمْ فِي الْغَيِّ ثُمَّ لَا يُقْصِرُونَ (202) Koma abale awo, iwo amawalowetsa mu uchimo ndipo salekerera |
وَإِذَا لَمْ تَأْتِهِم بِآيَةٍ قَالُوا لَوْلَا اجْتَبَيْتَهَا ۚ قُلْ إِنَّمَا أَتَّبِعُ مَا يُوحَىٰ إِلَيَّ مِن رَّبِّي ۚ هَٰذَا بَصَائِرُ مِن رَّبِّكُمْ وَهُدًى وَرَحْمَةٌ لِّقَوْمٍ يُؤْمِنُونَ (203) Ndipo ngati iwe siubweretsa chozizwitsa iwo amati, “Kodi ndi chifukwa chiani siunabweretse?” Nena, “Ine ndimatsatira chokhacho chimene chavumbulutsidwa kwa ine kuchokera kwa Ambuye wanga.” Uwu ndi umboni wochokera kwa Ambuye wanu, malangizo ndi madalitso kwa anthu okhulupirira |
وَإِذَا قُرِئَ الْقُرْآنُ فَاسْتَمِعُوا لَهُ وَأَنصِتُوا لَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ (204) Ndipo pamene Korani ilakatulidwa, mverani ndipo khalani chete kuti mulandire madalitso |
وَاذْكُر رَّبَّكَ فِي نَفْسِكَ تَضَرُّعًا وَخِيفَةً وَدُونَ الْجَهْرِ مِنَ الْقَوْلِ بِالْغُدُوِّ وَالْآصَالِ وَلَا تَكُن مِّنَ الْغَافِلِينَ (205) Ndipo kumbukira Ambuye wako ndi lilime lako, mwa iwe wekha, modzichepetsa ndi mwamantha ndiponso mosakweza mawu m’mawa ndi masana ndipo usakhale ngati iwo a unyizi |
إِنَّ الَّذِينَ عِندَ رَبِّكَ لَا يَسْتَكْبِرُونَ عَنْ عِبَادَتِهِ وَيُسَبِّحُونَهُ وَلَهُ يَسْجُدُونَ ۩ (206) Ndithudi iwo amene ali ndi Ambuye wako sanyada pogwira ntchito yopembedza Mulungu koma amamulemekeza Iye ndipo amagunditsa phumi zawo pamaso pake |