Quran with Chichewa translation - Surah Al-A‘raf ayat 160 - الأعرَاف - Page - Juz 9
﴿وَقَطَّعۡنَٰهُمُ ٱثۡنَتَيۡ عَشۡرَةَ أَسۡبَاطًا أُمَمٗاۚ وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ إِذِ ٱسۡتَسۡقَىٰهُ قَوۡمُهُۥٓ أَنِ ٱضۡرِب بِّعَصَاكَ ٱلۡحَجَرَۖ فَٱنۢبَجَسَتۡ مِنۡهُ ٱثۡنَتَا عَشۡرَةَ عَيۡنٗاۖ قَدۡ عَلِمَ كُلُّ أُنَاسٖ مَّشۡرَبَهُمۡۚ وَظَلَّلۡنَا عَلَيۡهِمُ ٱلۡغَمَٰمَ وَأَنزَلۡنَا عَلَيۡهِمُ ٱلۡمَنَّ وَٱلسَّلۡوَىٰۖ كُلُواْ مِن طَيِّبَٰتِ مَا رَزَقۡنَٰكُمۡۚ وَمَا ظَلَمُونَا وَلَٰكِن كَانُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ ﴾
[الأعرَاف: 160]
﴿وقطعناهم اثنتي عشرة أسباطا أمما وأوحينا إلى موسى إذ استسقاه قومه أن﴾ [الأعرَاف: 160]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo tidawagawa iwo m’mafuko khumi ndi awiri (osiyanasiyana) monga mitundu ikuluikulu. Ndipo tidamuvumbulutsira Mûsa pamene anthu ake adampempha madzi, kuti: “Menya mwala ndi ndodo yakoyo.” Ndipo mudatuluka akasupe khumi ndi awiri mwakuti fuko lililonse lidadziwa malo ake omwera. Ndipo tidawaphimba ndi mthunzi wa mtambo, ndi kuwatumizira mana ndi salwa (mbalame). (Tidawauza): “Idyani zinthu zabwinozi zomwe takupatsani.” Komatu sadatichitire choipa (pamene adachita zamphulupulu), koma adadzichitira okha zoipa |