×

Surah At-Taghabun in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Taghabun

Translation of the Meanings of Surah Taghabun in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Taghabun translated into Chichewa, Surah At-Taghabun in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Taghabun in Chichewa - نيانجا, Verses 18 - Surah Number 64 - Page 556.

بسم الله الرحمن الرحيم

يُسَبِّحُ لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۖ لَهُ الْمُلْكُ وَلَهُ الْحَمْدُ ۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (1)
Chilichonse chili mlengalenga ndi padziko lapansi chimatamanda ndi kulemekeza Mulungu. Iye ndiye Mwini ufumu ndipo kwake ndi kuyamikidwa ndipo Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse
هُوَ الَّذِي خَلَقَكُمْ فَمِنكُمْ كَافِرٌ وَمِنكُم مُّؤْمِنٌ ۚ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (2)
Ndiye amene adakulengani inu ndipo ena a inu ndi osakhulupirira pamene ena ndi okhulupirira. Mulungu amaona zonse zimene mumachita
خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ بِالْحَقِّ وَصَوَّرَكُمْ فَأَحْسَنَ صُوَرَكُمْ ۖ وَإِلَيْهِ الْمَصِيرُ (3)
Iye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwa chilungamo ndipo Iye adakulengani ndi kukupatsani maonekedwe abwino ndipo kwa Iye ndi kumene mudzabwerera
يَعْلَمُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَيَعْلَمُ مَا تُسِرُّونَ وَمَا تُعْلِنُونَ ۚ وَاللَّهُ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (4)
Iye amadziwa chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi ndipo amadziwa zonse zimene mumabisa ndi zimene mumaulula. Ndithudi Mulungu amadziwa bwino lomwe zinsinsi za m’mitima mwanu
أَلَمْ يَأْتِكُمْ نَبَأُ الَّذِينَ كَفَرُوا مِن قَبْلُ فَذَاقُوا وَبَالَ أَمْرِهِمْ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (5)
Kodi inu simudamve za iwo amene sadakhulupirire kale? Ndipo iwo adalawa chilango chifukwa chosakhulupilira, ndipo chawo chidzakhala chilango chowawa kwambiri
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُ كَانَت تَّأْتِيهِمْ رُسُلُهُم بِالْبَيِّنَاتِ فَقَالُوا أَبَشَرٌ يَهْدُونَنَا فَكَفَرُوا وَتَوَلَّوا ۚ وَّاسْتَغْنَى اللَّهُ ۚ وَاللَّهُ غَنِيٌّ حَمِيدٌ (6)
Ichi ndi chifukwa chakuti kunadza kwa iwo Atumwi amene adali ndi zizindikiro zooneka koma iwo adati: “Kodi ife tizitsogozedwa ndi anthu anzathu?” Kotero iwo sanakhulupilire ndipo anabwerera m’mbuyo. Koma Mulungu sasowa kanthu. Ndithudi Mulungu ndi Mwini wa chilichonse ndi Mwini ulemerero wonse. Al Taghabun
زَعَمَ الَّذِينَ كَفَرُوا أَن لَّن يُبْعَثُوا ۚ قُلْ بَلَىٰ وَرَبِّي لَتُبْعَثُنَّ ثُمَّ لَتُنَبَّؤُنَّ بِمَا عَمِلْتُمْ ۚ وَذَٰلِكَ عَلَى اللَّهِ يَسِيرٌ (7)
Anthu osakhulupirira amaganiza kuti sadzaukitsidwa kwa akufa. Nena: “Inde! Pali Ambuye wanga! Inu, ndithudi, mudzaukitsidwa kwa akufa ndipo mudzauzidwa zimene mudachita. Zimenezo ndi za pafupi ndi Mulungu.”
فَآمِنُوا بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ وَالنُّورِ الَّذِي أَنزَلْنَا ۚ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌ (8)
Motero khulupirirani mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi wake ndi mu Muuni umene Ife tatumiza. Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse chimene mumachita
يَوْمَ يَجْمَعُكُمْ لِيَوْمِ الْجَمْعِ ۖ ذَٰلِكَ يَوْمُ التَّغَابُنِ ۗ وَمَن يُؤْمِن بِاللَّهِ وَيَعْمَلْ صَالِحًا يُكَفِّرْ عَنْهُ سَيِّئَاتِهِ وَيُدْخِلْهُ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا أَبَدًا ۚ ذَٰلِكَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ (9)
Patsiku limene Iye adzakusonkhanitsani inu nonse, tsiku losonkhana, tsiku limeneli lidzakhala tsiku la mavuto ndi la mtendere kwa ena a inu. Ndipo iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino, Iye adzawakhululukira machimo awo ndipo adzawaika m’minda imene imathiriridwa ndi mitsinje yoyenda madzi pansi pake kuti akhale m’menemo mpaka kalekale. Kumeneko ndiko kupambana kwenikweni
وَالَّذِينَ كَفَرُوا وَكَذَّبُوا بِآيَاتِنَا أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ خَالِدِينَ فِيهَا ۖ وَبِئْسَ الْمَصِيرُ (10)
Koma iwo amene sakhulupirira ndipo amakana ulangizi wathu, iwo adzakhala ku moto nthawi zonse omwe ndi malo oipitsitsa kukhalako
مَا أَصَابَ مِن مُّصِيبَةٍ إِلَّا بِإِذْنِ اللَّهِ ۗ وَمَن يُؤْمِن بِاللَّهِ يَهْدِ قَلْبَهُ ۚ وَاللَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (11)
Palibe vuto limene limadza popanda chilolezo cha Mulungu ndipo aliyense amene amakhulupirira mwa Mulungu, Iye amatsogolera mtima wake ndipo Mulungu amadziwa chilichonse
وَأَطِيعُوا اللَّهَ وَأَطِيعُوا الرَّسُولَ ۚ فَإِن تَوَلَّيْتُمْ فَإِنَّمَا عَلَىٰ رَسُولِنَا الْبَلَاغُ الْمُبِينُ (12)
Mverani Mulungu ndipo mverani Mtumwi wake. Koma ngati inu mukana, udindo wa Mtumwi wathu ndi kukuuzani uthenga wathu momveka ndi poyera
اللَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۚ وَعَلَى اللَّهِ فَلْيَتَوَكَّلِ الْمُؤْمِنُونَ (13)
Mulungu! Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha ndipo mwa Mulungu onse okhulupirira aike chikhulupiriro chawo
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِنَّ مِنْ أَزْوَاجِكُمْ وَأَوْلَادِكُمْ عَدُوًّا لَّكُمْ فَاحْذَرُوهُمْ ۚ وَإِن تَعْفُوا وَتَصْفَحُوا وَتَغْفِرُوا فَإِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (14)
Oh inu okhulupirira! Ndithudi pakati pa akazi ndi ana anu alipo ena amene ndi adani anu, motero chenjerani! Koma ngati inu muwakhululukira ndipo simulabadira zoipa zawo, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira nthawi zonse ndi Mwini chisoni chosatha
إِنَّمَا أَمْوَالُكُمْ وَأَوْلَادُكُمْ فِتْنَةٌ ۚ وَاللَّهُ عِندَهُ أَجْرٌ عَظِيمٌ (15)
Chuma chanu ndipo ana anu ndi mayesero pamene Mulungu ndiye amene ali ndi mphotho yaikulu
فَاتَّقُوا اللَّهَ مَا اسْتَطَعْتُمْ وَاسْمَعُوا وَأَطِيعُوا وَأَنفِقُوا خَيْرًا لِّأَنفُسِكُمْ ۗ وَمَن يُوقَ شُحَّ نَفْسِهِ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (16)
Kotero kwaniritsani udindo wanu kwa Mulungu ndipo muopeni Iye kwambiri. Mverani ndipo mumvere. Ndipo perekani chopereka chaulere. Chimenecho ndi chabwino kwa inu. Ndipo aliyense amene asiya umbombo adzakhala wopambana
إِن تُقْرِضُوا اللَّهَ قَرْضًا حَسَنًا يُضَاعِفْهُ لَكُمْ وَيَغْفِرْ لَكُمْ ۚ وَاللَّهُ شَكُورٌ حَلِيمٌ (17)
Ngati mukongoza Mulungu ngongole yabwino, Iye adzaichulukitsa ndipo adzakukhululukirani machimo anu. Ndipo Mulungu ndi wokonzeka kuyamika ndi kulipira ndipo ndi wopilira kwambiri
عَالِمُ الْغَيْبِ وَالشَّهَادَةِ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (18)
Wodziwa zonse zobisika ndi zooneka ndipo ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas