يُسَبِّحُ لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۖ لَهُ الْمُلْكُ وَلَهُ الْحَمْدُ ۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (1) Chilichonse chili mlengalenga ndi padziko lapansi chimatamanda ndi kulemekeza Mulungu. Iye ndiye Mwini ufumu ndipo kwake ndi kuyamikidwa ndipo Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse |
هُوَ الَّذِي خَلَقَكُمْ فَمِنكُمْ كَافِرٌ وَمِنكُم مُّؤْمِنٌ ۚ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (2) Ndiye amene adakulengani inu ndipo ena a inu ndi osakhulupirira pamene ena ndi okhulupirira. Mulungu amaona zonse zimene mumachita |
خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ بِالْحَقِّ وَصَوَّرَكُمْ فَأَحْسَنَ صُوَرَكُمْ ۖ وَإِلَيْهِ الْمَصِيرُ (3) Iye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwa chilungamo ndipo Iye adakulengani ndi kukupatsani maonekedwe abwino ndipo kwa Iye ndi kumene mudzabwerera |
يَعْلَمُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَيَعْلَمُ مَا تُسِرُّونَ وَمَا تُعْلِنُونَ ۚ وَاللَّهُ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (4) Iye amadziwa chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi ndipo amadziwa zonse zimene mumabisa ndi zimene mumaulula. Ndithudi Mulungu amadziwa bwino lomwe zinsinsi za m’mitima mwanu |
أَلَمْ يَأْتِكُمْ نَبَأُ الَّذِينَ كَفَرُوا مِن قَبْلُ فَذَاقُوا وَبَالَ أَمْرِهِمْ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (5) Kodi inu simudamve za iwo amene sadakhulupirire kale? Ndipo iwo adalawa chilango chifukwa chosakhulupilira, ndipo chawo chidzakhala chilango chowawa kwambiri |
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُ كَانَت تَّأْتِيهِمْ رُسُلُهُم بِالْبَيِّنَاتِ فَقَالُوا أَبَشَرٌ يَهْدُونَنَا فَكَفَرُوا وَتَوَلَّوا ۚ وَّاسْتَغْنَى اللَّهُ ۚ وَاللَّهُ غَنِيٌّ حَمِيدٌ (6) Ichi ndi chifukwa chakuti kunadza kwa iwo Atumwi amene adali ndi zizindikiro zooneka koma iwo adati: “Kodi ife tizitsogozedwa ndi anthu anzathu?” Kotero iwo sanakhulupilire ndipo anabwerera m’mbuyo. Koma Mulungu sasowa kanthu. Ndithudi Mulungu ndi Mwini wa chilichonse ndi Mwini ulemerero wonse. Al Taghabun |
زَعَمَ الَّذِينَ كَفَرُوا أَن لَّن يُبْعَثُوا ۚ قُلْ بَلَىٰ وَرَبِّي لَتُبْعَثُنَّ ثُمَّ لَتُنَبَّؤُنَّ بِمَا عَمِلْتُمْ ۚ وَذَٰلِكَ عَلَى اللَّهِ يَسِيرٌ (7) Anthu osakhulupirira amaganiza kuti sadzaukitsidwa kwa akufa. Nena: “Inde! Pali Ambuye wanga! Inu, ndithudi, mudzaukitsidwa kwa akufa ndipo mudzauzidwa zimene mudachita. Zimenezo ndi za pafupi ndi Mulungu.” |
فَآمِنُوا بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ وَالنُّورِ الَّذِي أَنزَلْنَا ۚ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌ (8) Motero khulupirirani mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi wake ndi mu Muuni umene Ife tatumiza. Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse chimene mumachita |
يَوْمَ يَجْمَعُكُمْ لِيَوْمِ الْجَمْعِ ۖ ذَٰلِكَ يَوْمُ التَّغَابُنِ ۗ وَمَن يُؤْمِن بِاللَّهِ وَيَعْمَلْ صَالِحًا يُكَفِّرْ عَنْهُ سَيِّئَاتِهِ وَيُدْخِلْهُ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا أَبَدًا ۚ ذَٰلِكَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ (9) Patsiku limene Iye adzakusonkhanitsani inu nonse, tsiku losonkhana, tsiku limeneli lidzakhala tsiku la mavuto ndi la mtendere kwa ena a inu. Ndipo iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino, Iye adzawakhululukira machimo awo ndipo adzawaika m’minda imene imathiriridwa ndi mitsinje yoyenda madzi pansi pake kuti akhale m’menemo mpaka kalekale. Kumeneko ndiko kupambana kwenikweni |
وَالَّذِينَ كَفَرُوا وَكَذَّبُوا بِآيَاتِنَا أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ خَالِدِينَ فِيهَا ۖ وَبِئْسَ الْمَصِيرُ (10) Koma iwo amene sakhulupirira ndipo amakana ulangizi wathu, iwo adzakhala ku moto nthawi zonse omwe ndi malo oipitsitsa kukhalako |
مَا أَصَابَ مِن مُّصِيبَةٍ إِلَّا بِإِذْنِ اللَّهِ ۗ وَمَن يُؤْمِن بِاللَّهِ يَهْدِ قَلْبَهُ ۚ وَاللَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (11) Palibe vuto limene limadza popanda chilolezo cha Mulungu ndipo aliyense amene amakhulupirira mwa Mulungu, Iye amatsogolera mtima wake ndipo Mulungu amadziwa chilichonse |
وَأَطِيعُوا اللَّهَ وَأَطِيعُوا الرَّسُولَ ۚ فَإِن تَوَلَّيْتُمْ فَإِنَّمَا عَلَىٰ رَسُولِنَا الْبَلَاغُ الْمُبِينُ (12) Mverani Mulungu ndipo mverani Mtumwi wake. Koma ngati inu mukana, udindo wa Mtumwi wathu ndi kukuuzani uthenga wathu momveka ndi poyera |
اللَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۚ وَعَلَى اللَّهِ فَلْيَتَوَكَّلِ الْمُؤْمِنُونَ (13) Mulungu! Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha ndipo mwa Mulungu onse okhulupirira aike chikhulupiriro chawo |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِنَّ مِنْ أَزْوَاجِكُمْ وَأَوْلَادِكُمْ عَدُوًّا لَّكُمْ فَاحْذَرُوهُمْ ۚ وَإِن تَعْفُوا وَتَصْفَحُوا وَتَغْفِرُوا فَإِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (14) Oh inu okhulupirira! Ndithudi pakati pa akazi ndi ana anu alipo ena amene ndi adani anu, motero chenjerani! Koma ngati inu muwakhululukira ndipo simulabadira zoipa zawo, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira nthawi zonse ndi Mwini chisoni chosatha |
إِنَّمَا أَمْوَالُكُمْ وَأَوْلَادُكُمْ فِتْنَةٌ ۚ وَاللَّهُ عِندَهُ أَجْرٌ عَظِيمٌ (15) Chuma chanu ndipo ana anu ndi mayesero pamene Mulungu ndiye amene ali ndi mphotho yaikulu |
فَاتَّقُوا اللَّهَ مَا اسْتَطَعْتُمْ وَاسْمَعُوا وَأَطِيعُوا وَأَنفِقُوا خَيْرًا لِّأَنفُسِكُمْ ۗ وَمَن يُوقَ شُحَّ نَفْسِهِ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (16) Kotero kwaniritsani udindo wanu kwa Mulungu ndipo muopeni Iye kwambiri. Mverani ndipo mumvere. Ndipo perekani chopereka chaulere. Chimenecho ndi chabwino kwa inu. Ndipo aliyense amene asiya umbombo adzakhala wopambana |
إِن تُقْرِضُوا اللَّهَ قَرْضًا حَسَنًا يُضَاعِفْهُ لَكُمْ وَيَغْفِرْ لَكُمْ ۚ وَاللَّهُ شَكُورٌ حَلِيمٌ (17) Ngati mukongoza Mulungu ngongole yabwino, Iye adzaichulukitsa ndipo adzakukhululukirani machimo anu. Ndipo Mulungu ndi wokonzeka kuyamika ndi kulipira ndipo ndi wopilira kwambiri |
عَالِمُ الْغَيْبِ وَالشَّهَادَةِ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (18) Wodziwa zonse zobisika ndi zooneka ndipo ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse |