يَا أَيُّهَا النَّبِيُّ إِذَا طَلَّقْتُمُ النِّسَاءَ فَطَلِّقُوهُنَّ لِعِدَّتِهِنَّ وَأَحْصُوا الْعِدَّةَ ۖ وَاتَّقُوا اللَّهَ رَبَّكُمْ ۖ لَا تُخْرِجُوهُنَّ مِن بُيُوتِهِنَّ وَلَا يَخْرُجْنَ إِلَّا أَن يَأْتِينَ بِفَاحِشَةٍ مُّبَيِّنَةٍ ۚ وَتِلْكَ حُدُودُ اللَّهِ ۚ وَمَن يَتَعَدَّ حُدُودَ اللَّهِ فَقَدْ ظَلَمَ نَفْسَهُ ۚ لَا تَدْرِي لَعَلَّ اللَّهَ يُحْدِثُ بَعْدَ ذَٰلِكَ أَمْرًا (1) Oh iwe Mtumwi! Ngati usudzula akazi ako, asudzule potsatira nthawi zawo. Ndipo werenga bwino bwino masiku awo. Ndipo opani Mulungu Ambuye wanu ndipo musawapirikitse m’nyumba zawo ndipo iwo asachoke pokhapokha ngati iwo apalamula mlandu wachigololo. Amenewa ndiwo malamulo amene akhazikitsidwa ndi Mulungu. Ndipo aliyense amene aphwanya malamulo a Mulungu, ndithudi, amapondereza mzimu wake. Inu Al Talaq 605 simudziwa kuti, mwina, Mulungu adzakukumanizaninso |
فَإِذَا بَلَغْنَ أَجَلَهُنَّ فَأَمْسِكُوهُنَّ بِمَعْرُوفٍ أَوْ فَارِقُوهُنَّ بِمَعْرُوفٍ وَأَشْهِدُوا ذَوَيْ عَدْلٍ مِّنكُمْ وَأَقِيمُوا الشَّهَادَةَ لِلَّهِ ۚ ذَٰلِكُمْ يُوعَظُ بِهِ مَن كَانَ يُؤْمِنُ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ ۚ وَمَن يَتَّقِ اللَّهَ يَجْعَل لَّهُ مَخْرَجًا (2) Ndipo ngati iwo ali pafupi kukwaniritsa nthawi yawo, mukhoza kuwasunga mwaubwino kapena kuwasiya mwaulemu. Ndipo itanani mboni ziwiri za chilungamo kuchokera pakati panu. Ndipo perekani umboni wanu chifukwa cha Mulungu. Limeneli ndi langizo limene laperekedwa kwa iye amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza. Ndipo aliyense amene aopa Mulungu, Iye adzamupulumutsa |
وَيَرْزُقْهُ مِنْ حَيْثُ لَا يَحْتَسِبُ ۚ وَمَن يَتَوَكَّلْ عَلَى اللَّهِ فَهُوَ حَسْبُهُ ۚ إِنَّ اللَّهَ بَالِغُ أَمْرِهِ ۚ قَدْ جَعَلَ اللَّهُ لِكُلِّ شَيْءٍ قَدْرًا (3) Ndipo Iye adzamupatsa zinthu kuchokera ku mbali imene sanali kuyembekeza. Ndipo aliyense amene amakhulupirira mwa Mulungu, Iye adzamupatsa chili chonse. Mulungu, ndithudi, adzamupatsa iye zofuna zake zonse. Ndithudi Mulungu adakhazikitsa muyeso wa chilichonse |
وَاللَّائِي يَئِسْنَ مِنَ الْمَحِيضِ مِن نِّسَائِكُمْ إِنِ ارْتَبْتُمْ فَعِدَّتُهُنَّ ثَلَاثَةُ أَشْهُرٍ وَاللَّائِي لَمْ يَحِضْنَ ۚ وَأُولَاتُ الْأَحْمَالِ أَجَلُهُنَّ أَن يَضَعْنَ حَمْلَهُنَّ ۚ وَمَن يَتَّقِ اللَّهَ يَجْعَل لَّهُ مِنْ أَمْرِهِ يُسْرًا (4) Ndipo ena akazi anu amene adasiya kupita kumwezi, kwa iwo nthawi yawo yodikira, ngati inu mukaika, ndi miyezi itatu ndipo iwo amene anasiyiratu, nthawi yawo idzakhala chimodzimodzi. Ndipo iwo amene ali ndi akazi odwala pakati, nthawi yawo idzakhala mpaka pamene abereka. Ndipo aliyense amene amaopa Mulungu, Iye adzamuchepetsera mavuto ake |
ذَٰلِكَ أَمْرُ اللَّهِ أَنزَلَهُ إِلَيْكُمْ ۚ وَمَن يَتَّقِ اللَّهَ يُكَفِّرْ عَنْهُ سَيِّئَاتِهِ وَيُعْظِمْ لَهُ أَجْرًا (5) Uwu ndi ulamuliro wa Mulungu umene wakutumizirani inu. Ndipo aliyense amene aopa Mulungu, Iye adzamuchotsera zoipa zake. Ndipo Iye adzamuchulukitsira mphotho yake |
أَسْكِنُوهُنَّ مِنْ حَيْثُ سَكَنتُم مِّن وُجْدِكُمْ وَلَا تُضَارُّوهُنَّ لِتُضَيِّقُوا عَلَيْهِنَّ ۚ وَإِن كُنَّ أُولَاتِ حَمْلٍ فَأَنفِقُوا عَلَيْهِنَّ حَتَّىٰ يَضَعْنَ حَمْلَهُنَّ ۚ فَإِنْ أَرْضَعْنَ لَكُمْ فَآتُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ ۖ وَأْتَمِرُوا بَيْنَكُم بِمَعْرُوفٍ ۖ وَإِن تَعَاسَرْتُمْ فَسَتُرْضِعُ لَهُ أُخْرَىٰ (6) Khalani nawo monga momwe inu muli kukhalira, molingana ndi kupeza kwanu. Musawazunze ndi cholinga chowasowetsa mtendere. Ngati iwo ali ndi pakati, asamalireni mpaka pamene iwo abereka. Ndipo ngati iwo ali kuyamwitsa, apatseni malipiro awo ndipo lemekezanani. Ndipo ngati pali mavuto oti simuli kugwirizana m’banja, pezani Mayi wina kuti ayamwitse mwana m’malo mwake |
لِيُنفِقْ ذُو سَعَةٍ مِّن سَعَتِهِ ۖ وَمَن قُدِرَ عَلَيْهِ رِزْقُهُ فَلْيُنفِقْ مِمَّا آتَاهُ اللَّهُ ۚ لَا يُكَلِّفُ اللَّهُ نَفْسًا إِلَّا مَا آتَاهَا ۚ سَيَجْعَلُ اللَّهُ بَعْدَ عُسْرٍ يُسْرًا (7) Mulekeni munthu wolemera kuti apereke molingana ndi chuma chake ndipo munthu wosauka molingana ndi mmene Mulungu adamupatsira iye. Mulungu sakhazika mtulo wolemera pa munthu umene sangathe kuunyamula. Mulungu adzapereka mtendere mavuto akatha |
وَكَأَيِّن مِّن قَرْيَةٍ عَتَتْ عَنْ أَمْرِ رَبِّهَا وَرُسُلِهِ فَحَاسَبْنَاهَا حِسَابًا شَدِيدًا وَعَذَّبْنَاهَا عَذَابًا نُّكْرًا (8) Ndipo ndi mizinda yambiri imene idaukira malamulo a Mulungu ndi Atumwi ndipo Ife tidayilanga iyo ndipo tidzailanga ndi chilango choopsa zedi |
فَذَاقَتْ وَبَالَ أَمْرِهَا وَكَانَ عَاقِبَةُ أَمْرِهَا خُسْرًا (9) Motero iyo idalawa mphotho ya kusakhulupilira kwake ndipo mapeto a kusakhulupilira adali chionongeko |
أَعَدَّ اللَّهُ لَهُمْ عَذَابًا شَدِيدًا ۖ فَاتَّقُوا اللَّهَ يَا أُولِي الْأَلْبَابِ الَّذِينَ آمَنُوا ۚ قَدْ أَنزَلَ اللَّهُ إِلَيْكُمْ ذِكْرًا (10) Mulungu wawakonzeraiwochilangochoopsa. Moteroopani Mulungu oh inu anthu ozindikira! Inu amene mwakhulupirira, ndithudi, Mulungu watumiza chikumbutso kwa inu |
رَّسُولًا يَتْلُو عَلَيْكُمْ آيَاتِ اللَّهِ مُبَيِّنَاتٍ لِّيُخْرِجَ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ مِنَ الظُّلُمَاتِ إِلَى النُّورِ ۚ وَمَن يُؤْمِن بِاللَّهِ وَيَعْمَلْ صَالِحًا يُدْخِلْهُ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا أَبَدًا ۖ قَدْ أَحْسَنَ اللَّهُ لَهُ رِزْقًا (11) Mtumwi amene ali kukuuzani zizindikiro zooneka za Mulungu ndi cholinga choti atsogolere onse amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino kuchokera ku mdima kupita kowala. Ndipo aliyense amene amakhulupirira mwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino, Iye adzamulowetsa m’minda imene pansi pake pamayenda mitsinje kuti adzakhaleko mpaka kalekale. Ndithudi Mulungu wawapatsa iwo mphotho yabwino kwambiri |
اللَّهُ الَّذِي خَلَقَ سَبْعَ سَمَاوَاتٍ وَمِنَ الْأَرْضِ مِثْلَهُنَّ يَتَنَزَّلُ الْأَمْرُ بَيْنَهُنَّ لِتَعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ وَأَنَّ اللَّهَ قَدْ أَحَاطَ بِكُلِّ شَيْءٍ عِلْمًا (12) Ndi Mulungu amene adalenga miyamba isanu ndi iwiri ndi dziko lapansi lolingana nayo. Malamulo ake amatsatiridwa ndi izo kuti inu mukhoza kudziwa kuti Mulungu ali ndi mphamvu pa zinthu zonse ndipo kuti Mulungu amadziwa chilichonse |