Quran with Chichewa translation - Surah AT-Talaq ayat 6 - الطَّلَاق - Page - Juz 28
﴿أَسۡكِنُوهُنَّ مِنۡ حَيۡثُ سَكَنتُم مِّن وُجۡدِكُمۡ وَلَا تُضَآرُّوهُنَّ لِتُضَيِّقُواْ عَلَيۡهِنَّۚ وَإِن كُنَّ أُوْلَٰتِ حَمۡلٖ فَأَنفِقُواْ عَلَيۡهِنَّ حَتَّىٰ يَضَعۡنَ حَمۡلَهُنَّۚ فَإِنۡ أَرۡضَعۡنَ لَكُمۡ فَـَٔاتُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ وَأۡتَمِرُواْ بَيۡنَكُم بِمَعۡرُوفٖۖ وَإِن تَعَاسَرۡتُمۡ فَسَتُرۡضِعُ لَهُۥٓ أُخۡرَىٰ ﴾
[الطَّلَاق: 6]
﴿أسكنوهن من حيث سكنتم من وجدكم ولا تضاروهن لتضيقوا عليهن وإن كن﴾ [الطَّلَاق: 6]
Khaled Ibrahim Betala “Akhazikeni (osiyidwawo) m’mene mukukhala inumo monga momwe kulili kupeza kwanu (ndi mphamvu zanu ngakhale kuti mwawasiya ukwati). Musawavute ndi cholinga chowapana (kuti athawe okha). Ngati ali ndi pakati, apatseni zonse zofunika pa moyo mpaka adzabereke. Ngati akukuyamwitsirani ana anu apatseni malipiro awo mokwanira; gwirizanani pakati panu mwa ubwino ndi mofatsa. Ngati wina apereka mavuto kwa mnzake (ndiye kuti mwanayo) adzamuyamwitsira (mkazi) wina |