Quran with Chichewa translation - Surah AT-Talaq ayat 1 - الطَّلَاق - Page - Juz 28
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ إِذَا طَلَّقۡتُمُ ٱلنِّسَآءَ فَطَلِّقُوهُنَّ لِعِدَّتِهِنَّ وَأَحۡصُواْ ٱلۡعِدَّةَۖ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ رَبَّكُمۡۖ لَا تُخۡرِجُوهُنَّ مِنۢ بُيُوتِهِنَّ وَلَا يَخۡرُجۡنَ إِلَّآ أَن يَأۡتِينَ بِفَٰحِشَةٖ مُّبَيِّنَةٖۚ وَتِلۡكَ حُدُودُ ٱللَّهِۚ وَمَن يَتَعَدَّ حُدُودَ ٱللَّهِ فَقَدۡ ظَلَمَ نَفۡسَهُۥۚ لَا تَدۡرِي لَعَلَّ ٱللَّهَ يُحۡدِثُ بَعۡدَ ذَٰلِكَ أَمۡرٗا ﴾
[الطَّلَاق: 1]
﴿ياأيها النبي إذا طلقتم النساء فطلقوهن لعدتهن وأحصوا العدة واتقوا الله ربكم﴾ [الطَّلَاق: 1]
Khaled Ibrahim Betala “E iwe Mneneri (s.a.w) ngati mufuna kusudzula akazi ukwati, asudzuleni mnyengo yowerengera Edda yawo (kuwerengera Edda kumayambika mkazi akakhala ndi Twahara akachira matenda akumwezi), ndipo werengerani nyengo ya Edda. Ndipo muopeni Allah Mbuye wanu. Ndipo musawatulutse m’nyumba zawo ndiponso asatuluke kupatula akachita tchimo lalikulu loonekera (loyenera chilango, apo atha kutulutsidwa). Ndipo amenewa ndiwo malire a Allah (amene wawakhazikitsa kwa anthu Ake). Ndipo amene apyola malire a Allah wadzichitira yekha zoipa. Sukudziwa (cholinga cha malamulo amenewa) mwina Allah adzadzetsa chinthu pambuyo pake (chosonyeza kuyanjana) |