×

Surah At-Tahreem in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Tahrim

Translation of the Meanings of Surah Tahrim in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Tahrim translated into Chichewa, Surah At-Tahreem in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Tahrim in Chichewa - نيانجا, Verses 12 - Surah Number 66 - Page 560.

بسم الله الرحمن الرحيم

يَا أَيُّهَا النَّبِيُّ لِمَ تُحَرِّمُ مَا أَحَلَّ اللَّهُ لَكَ ۖ تَبْتَغِي مَرْضَاتَ أَزْوَاجِكَ ۚ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (1)
Oh iwe Mtumwi! Bwanji ukudziletsa zinthu zimene Mulungu adakuloleza kuti uchite ndipo iwe ufuna kukondweretsa akazi ako? Ndipo Mulungu ndi wokhululukira nthawi zonse, Mwini chisoni chosatha
قَدْ فَرَضَ اللَّهُ لَكُمْ تَحِلَّةَ أَيْمَانِكُمْ ۚ وَاللَّهُ مَوْلَاكُمْ ۖ وَهُوَ الْعَلِيمُ الْحَكِيمُ (2)
Mulungu wakulolezani kuti mukhoza kumasula malonjezo anu. Ndipo Mulungu ndiye Mtetezi wanu, ndipo ndi wodziwa ndi Mwini nzeru zonse
وَإِذْ أَسَرَّ النَّبِيُّ إِلَىٰ بَعْضِ أَزْوَاجِهِ حَدِيثًا فَلَمَّا نَبَّأَتْ بِهِ وَأَظْهَرَهُ اللَّهُ عَلَيْهِ عَرَّفَ بَعْضَهُ وَأَعْرَضَ عَن بَعْضٍ ۖ فَلَمَّا نَبَّأَهَا بِهِ قَالَتْ مَنْ أَنبَأَكَ هَٰذَا ۖ قَالَ نَبَّأَنِيَ الْعَلِيمُ الْخَبِيرُ (3)
Ndi pamene Mtumwi anamuuza nkhani ya chinsinsi wina wa akazi ake ndipo iye adaulula kwa mnzake wina ndipo Mulungu adamuuza iye za izo, Iye anamuuza gawo la nkhani ndipo anasiya gawo lina. Ndipo pamene iye adamuuza mkaziyo za izo, iye adati: “Ndani wakuuzani izi?” Iye adati: “Wandiuza ndi amene amadziwa chilichonse ndi Mwini kuzindikira.”
إِن تَتُوبَا إِلَى اللَّهِ فَقَدْ صَغَتْ قُلُوبُكُمَا ۖ وَإِن تَظَاهَرَا عَلَيْهِ فَإِنَّ اللَّهَ هُوَ مَوْلَاهُ وَجِبْرِيلُ وَصَالِحُ الْمُؤْمِنِينَ ۖ وَالْمَلَائِكَةُ بَعْدَ ذَٰلِكَ ظَهِيرٌ (4)
Ngati inu awiri mulapa machimo anu kwa Mulungu ndipo mitima yanu itsimikiza kutero, koma ngati inu mugwirizana kulimbana naye, ndithudi, Mulungu ndiye Mtetezi wake, ndi Gabriele ndipo aliyense wolungama amene ali pakati pa anthu amene akhulupirira ndi angelo. Onse ndi omuthandiza iye
عَسَىٰ رَبُّهُ إِن طَلَّقَكُنَّ أَن يُبْدِلَهُ أَزْوَاجًا خَيْرًا مِّنكُنَّ مُسْلِمَاتٍ مُّؤْمِنَاتٍ قَانِتَاتٍ تَائِبَاتٍ عَابِدَاتٍ سَائِحَاتٍ ثَيِّبَاتٍ وَأَبْكَارًا (5)
Zingatheke kuti pamene iye akusudzulani inu, Mulungu adzamupatsa m’malo mwanu, akazi ena abwino oposa inu amene amadzipereka kwa Mulungu, amene ali okhulupirira, opirira, olapa kwa Mulungu, opembedza modzichepetsa, osala zifuniro zawo, kapena obwera amene anakwatiwapo kale kapena a namwali
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا قُوا أَنفُسَكُمْ وَأَهْلِيكُمْ نَارًا وَقُودُهَا النَّاسُ وَالْحِجَارَةُ عَلَيْهَا مَلَائِكَةٌ غِلَاظٌ شِدَادٌ لَّا يَعْصُونَ اللَّهَ مَا أَمَرَهُمْ وَيَفْعَلُونَ مَا يُؤْمَرُونَ (6)
oh inu okhulupirira! Dzitetezeni nokha ndi mabanja anu ku moto umene nkhuni zake ndi anthu ndi miyala ndipo oyang’anira ake ndi angelo a mphamvu a maonekedwe oopsa amene sakana kumvera malamulo amene amalandira kuchokera kwa Mulungu ndipo amachita, mwamsanga, chilichonse chimene Mulungu wawalamula
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ كَفَرُوا لَا تَعْتَذِرُوا الْيَوْمَ ۖ إِنَّمَا تُجْزَوْنَ مَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (7)
oh inu osakhulupirira! Musawiringule lero! Inu muli kulandira mphotho yolingana ndi zimene mudachita
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا تُوبُوا إِلَى اللَّهِ تَوْبَةً نَّصُوحًا عَسَىٰ رَبُّكُمْ أَن يُكَفِّرَ عَنكُمْ سَيِّئَاتِكُمْ وَيُدْخِلَكُمْ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ يَوْمَ لَا يُخْزِي اللَّهُ النَّبِيَّ وَالَّذِينَ آمَنُوا مَعَهُ ۖ نُورُهُمْ يَسْعَىٰ بَيْنَ أَيْدِيهِمْ وَبِأَيْمَانِهِمْ يَقُولُونَ رَبَّنَا أَتْمِمْ لَنَا نُورَنَا وَاغْفِرْ لَنَا ۖ إِنَّكَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (8)
oh inu anthu okhulupirira! Lapani kwa Mulungu mwachoonadi! Mwina Ambuye wanu angakuchotserani machimo anu ndi kukulowetsani inu m’minda imene pansi pake pamayenda mitsinje. Tsiku limene Mulungu sadzalola kuti Mtumwi ndi iwo amene amamutsatira kuti azunzidwe, nyali yawo idzayaka patsogolo pawo ndi Buku ku dzanja lamanja lawo. Iwo adzati: “Ambuye wathu walitsani nyali yathu ndipo tikhululukireni. Ndithudi inu muli ndi mphamvu pa zinthu zonse.”
يَا أَيُّهَا النَّبِيُّ جَاهِدِ الْكُفَّارَ وَالْمُنَافِقِينَ وَاغْلُظْ عَلَيْهِمْ ۚ وَمَأْوَاهُمْ جَهَنَّمُ ۖ وَبِئْسَ الْمَصِيرُ (9)
oh iwe Mtumwi! Limbika kwambiri pogonjetsa anthu osakhulupirira ndi anthu a chinyengo ndipo chita nawo mwankhanza, malo awo ndi kumoto, omwe ndi malo oipa kwambiri kukhalako
ضَرَبَ اللَّهُ مَثَلًا لِّلَّذِينَ كَفَرُوا امْرَأَتَ نُوحٍ وَامْرَأَتَ لُوطٍ ۖ كَانَتَا تَحْتَ عَبْدَيْنِ مِنْ عِبَادِنَا صَالِحَيْنِ فَخَانَتَاهُمَا فَلَمْ يُغْنِيَا عَنْهُمَا مِنَ اللَّهِ شَيْئًا وَقِيلَ ادْخُلَا النَّارَ مَعَ الدَّاخِلِينَ (10)
Mulungu ali kupereka chitsanzo kwa anthu osakhulupirira cha nkhani ya mkazi wa Nowa ndi mkazi wa Loti. Iwo adali akazi a Atumiki athu awiri a ngwiro, koma onse adanyenga amuna awo. Iwo sadalandire kuchokera kwa Mulungu chabwino china chilichonse chifukwa chamakhalidwe awo. Koma iwo adauzidwa kuti: “Lowani inu kumoto pamodzi ndi ena amene ali kulowako.”
وَضَرَبَ اللَّهُ مَثَلًا لِّلَّذِينَ آمَنُوا امْرَأَتَ فِرْعَوْنَ إِذْ قَالَتْ رَبِّ ابْنِ لِي عِندَكَ بَيْتًا فِي الْجَنَّةِ وَنَجِّنِي مِن فِرْعَوْنَ وَعَمَلِهِ وَنَجِّنِي مِنَ الْقَوْمِ الظَّالِمِينَ (11)
Ndipo Mulungu wapereka chitsanzo kwa anthu okhulupirira, nkhani ya mkazi wa Farao. Pamene iye adati: “oh Ambuye wanga! Ndimangireni pafupi ndi Inu, nyumba ya ulemu ku Paradiso, ndipo ndipulumutseni kwa Farao ndi ntchito zake ndipo ndipulumutseni ine kwa athu amene amachita zoipa.”
وَمَرْيَمَ ابْنَتَ عِمْرَانَ الَّتِي أَحْصَنَتْ فَرْجَهَا فَنَفَخْنَا فِيهِ مِن رُّوحِنَا وَصَدَّقَتْ بِكَلِمَاتِ رَبِّهَا وَكُتُبِهِ وَكَانَتْ مِنَ الْقَانِتِينَ (12)
Ndi Maria mwana wa Imran, amene adadzisunga wosadulaunamwaliwakendipo Ifetidauziram’thupimwake mzimu wathu ndipo Iye adachitira umboni wachilungamo cha Ambuye wake ndi chivumbulutso chake. Ndipo iye adali mmodzi wa odzipereka kwa Mulungu
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas