Quran with Chichewa translation - Surah Al-Muddaththir ayat 31 - المُدثر - Page - Juz 29
﴿وَمَا جَعَلۡنَآ أَصۡحَٰبَ ٱلنَّارِ إِلَّا مَلَٰٓئِكَةٗۖ وَمَا جَعَلۡنَا عِدَّتَهُمۡ إِلَّا فِتۡنَةٗ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ لِيَسۡتَيۡقِنَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ وَيَزۡدَادَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِيمَٰنٗا وَلَا يَرۡتَابَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡمُؤۡمِنُونَ وَلِيَقُولَ ٱلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٞ وَٱلۡكَٰفِرُونَ مَاذَآ أَرَادَ ٱللَّهُ بِهَٰذَا مَثَلٗاۚ كَذَٰلِكَ يُضِلُّ ٱللَّهُ مَن يَشَآءُ وَيَهۡدِي مَن يَشَآءُۚ وَمَا يَعۡلَمُ جُنُودَ رَبِّكَ إِلَّا هُوَۚ وَمَا هِيَ إِلَّا ذِكۡرَىٰ لِلۡبَشَرِ ﴾
[المُدثر: 31]
﴿وما جعلنا أصحاب النار إلا ملائكة وما جعلنا عدتهم إلا فتنة للذين﴾ [المُدثر: 31]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo sitidaike oyang’anira ku Moto (kukhala anthu) koma angelo; ndipo sitidaike chiwerengero chawo koma ndimayesero kwa amene sadakhulupirire, kuti atsimikize amene adapatsidwa mabuku (zimene Qur’an ikunena za chiwerengero cha angelo a ku Moto) ndiponso kuti chionjezeke chikhulupiliro kwa amene akhulupirira, ndikuti asapeneke amene adapatsidwa mabuku pamodzi ndi okhulupirira. Ndiponso kuti amene m’mitima mwawo muli matenda (matenda achinyengo) komanso osakhulupirira anene: “Kodi Allah akulinganji pa fanizo limeneli?” Momwemo Allah akumulekelera kusokera amene wamfuna, ndipo akumuongola amene wamfuna ndipo palibe amene angadziwe magulu a nkhondo a Mbuye wako kupatula Iye mwini. (Kutchula moto ndi zam’kati mwake) sichina koma ndichenjezo kwa anthu |