Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 136 - البَقَرَة - Page - Juz 1
﴿قُولُوٓاْ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ وَمَآ أُنزِلَ إِلَيۡنَا وَمَآ أُنزِلَ إِلَىٰٓ إِبۡرَٰهِـۧمَ وَإِسۡمَٰعِيلَ وَإِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَ وَٱلۡأَسۡبَاطِ وَمَآ أُوتِيَ مُوسَىٰ وَعِيسَىٰ وَمَآ أُوتِيَ ٱلنَّبِيُّونَ مِن رَّبِّهِمۡ لَا نُفَرِّقُ بَيۡنَ أَحَدٖ مِّنۡهُمۡ وَنَحۡنُ لَهُۥ مُسۡلِمُونَ ﴾
[البَقَرَة: 136]
﴿قولوا آمنا بالله وما أنـزل إلينا وما أنـزل إلى إبراهيم وإسماعيل وإسحاق﴾ [البَقَرَة: 136]
Khaled Ibrahim Betala “Nenani (inu Asilamu kuwauza Ayuda ndi Akhrisitu); “Takhulupirira Allah ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa ife, ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa Ibrahim, Ismail, Ishâq, Ya’qub ndi zidzukulu (zake) ndi zimene adapatsidwa Mûsa, Isa (Yesu), ndiponso zimene adapatsidwa aneneri (ena) kuchokera kwa Mbuye wawo. Sitilekanitsa pakati pa mmodzi wa iwo (koma onse tikuwakhulupirira). Ndipo ife kwa Iye tili Asilamu (ogonjera).” |