Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 249 - البَقَرَة - Page - Juz 2
﴿فَلَمَّا فَصَلَ طَالُوتُ بِٱلۡجُنُودِ قَالَ إِنَّ ٱللَّهَ مُبۡتَلِيكُم بِنَهَرٖ فَمَن شَرِبَ مِنۡهُ فَلَيۡسَ مِنِّي وَمَن لَّمۡ يَطۡعَمۡهُ فَإِنَّهُۥ مِنِّيٓ إِلَّا مَنِ ٱغۡتَرَفَ غُرۡفَةَۢ بِيَدِهِۦۚ فَشَرِبُواْ مِنۡهُ إِلَّا قَلِيلٗا مِّنۡهُمۡۚ فَلَمَّا جَاوَزَهُۥ هُوَ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥ قَالُواْ لَا طَاقَةَ لَنَا ٱلۡيَوۡمَ بِجَالُوتَ وَجُنُودِهِۦۚ قَالَ ٱلَّذِينَ يَظُنُّونَ أَنَّهُم مُّلَٰقُواْ ٱللَّهِ كَم مِّن فِئَةٖ قَلِيلَةٍ غَلَبَتۡ فِئَةٗ كَثِيرَةَۢ بِإِذۡنِ ٱللَّهِۗ وَٱللَّهُ مَعَ ٱلصَّٰبِرِينَ ﴾
[البَقَرَة: 249]
﴿فلما فصل طالوت بالجنود قال إن الله مبتليكم بنهر فمن شرب منه﴾ [البَقَرَة: 249]
Khaled Ibrahim Betala “Choncho, Taluti pamene adapita ndi magulu (ake) a nkhondo, adati: “Allah akuyesani mayeso ndi mtsinje (womwe mukumane nawo panjira komwe mukupitako). Choncho amene akamwe mmenemo sali nane. Koma amene sakamwa adzakhala pamodzi nane kupatula amene watunga ndi dzanja lake (ndikumwa; iyeyo ndiye kuti sadalakwe). Koma (iwo) adamwa m’menemo kupatula ochepa mwa iwo. Choncho pamene adaoloka iye pamodzi ndi aja omwe adakhulupirira limodzi naye, (iwo) adati: “Lero sitingamuthe Jaluti ndi magulu ake a nkhondo.” Omwe adali ndi chitsimikizo chokumana ndi Allah adati: “Kodi ndimagulu angati ochepa amene adagonjetsa magulu ambiri mwa chilolezo cha Allah! Ndipo Allah Ali pamodzi ndi opirira |