Quran with Chichewa translation - Surah Al-hajj ayat 5 - الحج - Page - Juz 17
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِن كُنتُمۡ فِي رَيۡبٖ مِّنَ ٱلۡبَعۡثِ فَإِنَّا خَلَقۡنَٰكُم مِّن تُرَابٖ ثُمَّ مِن نُّطۡفَةٖ ثُمَّ مِنۡ عَلَقَةٖ ثُمَّ مِن مُّضۡغَةٖ مُّخَلَّقَةٖ وَغَيۡرِ مُخَلَّقَةٖ لِّنُبَيِّنَ لَكُمۡۚ وَنُقِرُّ فِي ٱلۡأَرۡحَامِ مَا نَشَآءُ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗى ثُمَّ نُخۡرِجُكُمۡ طِفۡلٗا ثُمَّ لِتَبۡلُغُوٓاْ أَشُدَّكُمۡۖ وَمِنكُم مَّن يُتَوَفَّىٰ وَمِنكُم مَّن يُرَدُّ إِلَىٰٓ أَرۡذَلِ ٱلۡعُمُرِ لِكَيۡلَا يَعۡلَمَ مِنۢ بَعۡدِ عِلۡمٖ شَيۡـٔٗاۚ وَتَرَى ٱلۡأَرۡضَ هَامِدَةٗ فَإِذَآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡهَا ٱلۡمَآءَ ٱهۡتَزَّتۡ وَرَبَتۡ وَأَنۢبَتَتۡ مِن كُلِّ زَوۡجِۭ بَهِيجٖ ﴾
[الحج: 5]
﴿ياأيها الناس إن كنتم في ريب من البعث فإنا خلقناكم من تراب﴾ [الحج: 5]
Khaled Ibrahim Betala “E inu anthu! Ngati muli m’chikaiko za kuuka ku imfa, (ndipo mukuona kuti nzosatheka, yang’anani mmene tidakulengerani). Ndithu Ife tidakulengani ndi dothi, ndipo (timakulengani) ndi dontho la umuna, komanso (umunawo udasanduka) gawo lamagazi, kenako gawo la mnofti woumbidwa (chithunzi cha munthu) ndi wosaumbidwa, kuti tikulongosolereni (kukhoza Kwathu;) ndipo Ife timachikhazikitsa mchiberekero; chimene tifuna kufikira nthawi yake yoyikidwa kenako timakutulutsani muli khanda, (tsono timakulerani) kuti mufike pa nsinkhu wanu. Ndipo ena mwa inu amamwalira (asanakule), pomwe ena mwa inu amabwezedwa ku moyo wofooka (waukalamba) kotero kuti asadziwe chilichonse pambuyo pakuti adali wodziwa. Ndipo umaiona nthaka ili chetee, koma tikatsitsa madzi pamwamba pake, imagwedezeka ndi kufufuma, ndi kumeretsa mtundu uliwonse wa mmera wokongola |