Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ahzab ayat 51 - الأحزَاب - Page - Juz 22
﴿۞ تُرۡجِي مَن تَشَآءُ مِنۡهُنَّ وَتُـٔۡوِيٓ إِلَيۡكَ مَن تَشَآءُۖ وَمَنِ ٱبۡتَغَيۡتَ مِمَّنۡ عَزَلۡتَ فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكَۚ ذَٰلِكَ أَدۡنَىٰٓ أَن تَقَرَّ أَعۡيُنُهُنَّ وَلَا يَحۡزَنَّ وَيَرۡضَيۡنَ بِمَآ ءَاتَيۡتَهُنَّ كُلُّهُنَّۚ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ مَا فِي قُلُوبِكُمۡۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلِيمًا حَلِيمٗا ﴾
[الأحزَاب: 51]
﴿ترجي من تشاء منهن وتؤوي إليك من تشاء ومن ابتغيت ممن عزلت﴾ [الأحزَاب: 51]
Khaled Ibrahim Betala “Ukhoza kumchedwetsa (posagona m’nyumba mwake) amene wam’funa pakati pa iwo ndi kumuyandikitsa kwa iwe amene wam’funa. Ndipo amene wam’funa mwa amene udawapatuka, palibe tchimo pa iwe. Kuchita izi kuchititsa kuti maso awo atonthole (mitima yawo ikondwe) ndipo asadandaule; ndi kuyanjana nacho chimene wawapatsa onse. Ndipo Allah akudziwa zimene zili m’mitima mwanu. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri, Ngoleza, (salanga mwachangu) |