Quran with Chichewa translation - Surah An-Nisa’ ayat 43 - النِّسَاء - Page - Juz 5
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَقۡرَبُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَأَنتُمۡ سُكَٰرَىٰ حَتَّىٰ تَعۡلَمُواْ مَا تَقُولُونَ وَلَا جُنُبًا إِلَّا عَابِرِي سَبِيلٍ حَتَّىٰ تَغۡتَسِلُواْۚ وَإِن كُنتُم مَّرۡضَىٰٓ أَوۡ عَلَىٰ سَفَرٍ أَوۡ جَآءَ أَحَدٞ مِّنكُم مِّنَ ٱلۡغَآئِطِ أَوۡ لَٰمَسۡتُمُ ٱلنِّسَآءَ فَلَمۡ تَجِدُواْ مَآءٗ فَتَيَمَّمُواْ صَعِيدٗا طَيِّبٗا فَٱمۡسَحُواْ بِوُجُوهِكُمۡ وَأَيۡدِيكُمۡۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَفُوًّا غَفُورًا ﴾
[النِّسَاء: 43]
﴿ياأيها الذين آمنوا لا تقربوا الصلاة وأنتم سكارى حتى تعلموا ما تقولون﴾ [النِّسَاء: 43]
Khaled Ibrahim Betala “E inu amene mwakhulupirira! Musayandikire Swala uku muli oledzera, mpaka mudziwe chimene mukunena; ngakhalenso pamene muli ndi janaba (musapemphere kufikira mutasamba) kupatula amene ali pa ulendo (achite Tayammam). Ndipo ngati muli odwala, kapena muli pa ulendo, kapena m’modzi wanu wadza kuchokera kuchimbudzi, kapena mwakhudza akazi (m’njira ya ukwati) ndipo simunapeze madzi (osamba) chitani Tayammam ndi dothi labwino; lipakeni kunkhope kwanu ndi m’mikono mwanu. Ndithudi, Allah Ngofafaniza machimo, Ngokhululuka kwambiri |