يَا أَيُّهَا النَّاسُ اتَّقُوا رَبَّكُمُ الَّذِي خَلَقَكُم مِّن نَّفْسٍ وَاحِدَةٍ وَخَلَقَ مِنْهَا زَوْجَهَا وَبَثَّ مِنْهُمَا رِجَالًا كَثِيرًا وَنِسَاءً ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ الَّذِي تَسَاءَلُونَ بِهِ وَالْأَرْحَامَ ۚ إِنَّ اللَّهَ كَانَ عَلَيْكُمْ رَقِيبًا (1) oh inu anthu! Muopeni Ambuye wanu amene anakulengani inu kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo kuchokera kwa munthu ameneyu, Iye analenga mkazi wake. Ndipo kudzera mwa iwo, Iye adadzadza dziko lonse lapansi ndi anthu amuna ndi akazi osawerengeka. Opani Mulungu, dzina limene mumadandaulirana wina ndi mnzake. Ndipo lemekezani chibale. Ndithudi Mulungu amakuyang’anirani nthawi zonse |
وَآتُوا الْيَتَامَىٰ أَمْوَالَهُمْ ۖ وَلَا تَتَبَدَّلُوا الْخَبِيثَ بِالطَّيِّبِ ۖ وَلَا تَأْكُلُوا أَمْوَالَهُمْ إِلَىٰ أَمْوَالِكُمْ ۚ إِنَّهُ كَانَ حُوبًا كَبِيرًا (2) Apatseni ana a masiye chuma chawo akafika msinkhu woyenera. Musasinthitse choipa ndi chabwino ndipo musadye chuma chawo pamodzi ndi chanu chifukwa kutero, ndithudi, ndi tchimo lalikulu |
وَإِنْ خِفْتُمْ أَلَّا تُقْسِطُوا فِي الْيَتَامَىٰ فَانكِحُوا مَا طَابَ لَكُم مِّنَ النِّسَاءِ مَثْنَىٰ وَثُلَاثَ وَرُبَاعَ ۖ فَإِنْ خِفْتُمْ أَلَّا تَعْدِلُوا فَوَاحِدَةً أَوْ مَا مَلَكَتْ أَيْمَانُكُمْ ۚ ذَٰلِكَ أَدْنَىٰ أَلَّا تَعُولُوا (3) Ngati inu muopa kuti simungathe kuchita chilungamo ndi ana a masiye, kwatirani mkazi amene mungamukonde awiri, atatu kapena anayi. Koma ngati inu muopa kuti simudzatha kuchita chilungamo, kukwaniritsa zonse bwinobwino, kwatirani mmodzi yekha kapena wina wa a kapolo a chitsikana amene muli nawo. Chimenechi chidzakhala chapafupi kwa inu kuti musalephere kutsata njira ya chilungamo |
وَآتُوا النِّسَاءَ صَدُقَاتِهِنَّ نِحْلَةً ۚ فَإِن طِبْنَ لَكُمْ عَن شَيْءٍ مِّنْهُ نَفْسًا فَكُلُوهُ هَنِيئًا مَّرِيئًا (4) Apatseni akazi mphatso yawo monga mphatso yaulere. Koma ngati iwo, mwa chifuniro chawo, asankha kukugawiraniko gawo la mphatsoyi, idyani mosangalala ndi mwa ubwino |
وَلَا تُؤْتُوا السُّفَهَاءَ أَمْوَالَكُمُ الَّتِي جَعَلَ اللَّهُ لَكُمْ قِيَامًا وَارْزُقُوهُمْ فِيهَا وَاكْسُوهُمْ وَقُولُوا لَهُمْ قَوْلًا مَّعْرُوفًا (5) Musawapatse anthu ozerezeka katundu amene Mulungu wakupatsani kuti muziwathandizira, koma inu muyenera kuwasamala ndi kuwaveka kuchokera ku phindu la katunduyu ndipo lankhulani nawo mawu abwino a chifundo |
وَابْتَلُوا الْيَتَامَىٰ حَتَّىٰ إِذَا بَلَغُوا النِّكَاحَ فَإِنْ آنَسْتُم مِّنْهُمْ رُشْدًا فَادْفَعُوا إِلَيْهِمْ أَمْوَالَهُمْ ۖ وَلَا تَأْكُلُوهَا إِسْرَافًا وَبِدَارًا أَن يَكْبَرُوا ۚ وَمَن كَانَ غَنِيًّا فَلْيَسْتَعْفِفْ ۖ وَمَن كَانَ فَقِيرًا فَلْيَأْكُلْ بِالْمَعْرُوفِ ۚ فَإِذَا دَفَعْتُمْ إِلَيْهِمْ أَمْوَالَهُمْ فَأَشْهِدُوا عَلَيْهِمْ ۚ وَكَفَىٰ بِاللَّهِ حَسِيبًا (6) Aikeni ana a masiye pa mayesero mpakana pamene afika poti atha msinkhu. Ngati inu muona kuti ndi a maganizo okhazikika, apatseni chuma chawo ndipo musawaonongere iwo chuma chawo asanathe msinkhu. Munthu amene ali olemera asagwiritse ntchito katundu wa ana a masiye amene ali kumuyang’anira ndipo munthu osauka agwiritse ntchito chuma cha ana a masiye mosamala ndi mwa chilungamo. Pamene inu muwapatsa chuma chawo, itanani ena kuti akhale mboni; Mulungu ndi wokwana kukhala mboni pa zonse zimene muchita |
لِّلرِّجَالِ نَصِيبٌ مِّمَّا تَرَكَ الْوَالِدَانِ وَالْأَقْرَبُونَ وَلِلنِّسَاءِ نَصِيبٌ مِّمَّا تَرَكَ الْوَالِدَانِ وَالْأَقْرَبُونَ مِمَّا قَلَّ مِنْهُ أَوْ كَثُرَ ۚ نَصِيبًا مَّفْرُوضًا (7) Amuna adzakhala ndi gawo mu katundu amene makolo ndi abale awo asiya ndipo akazi adzakhala ndi gawo mu katunduamenemakolondiabaleawoasiya. Kayakatunduyo ndi wochepa kapena wambiri, onse ayenera kulandira gawo lawo malinga ndi malamulo |
وَإِذَا حَضَرَ الْقِسْمَةَ أُولُو الْقُرْبَىٰ وَالْيَتَامَىٰ وَالْمَسَاكِينُ فَارْزُقُوهُم مِّنْهُ وَقُولُوا لَهُمْ قَوْلًا مَّعْرُوفًا (8) Ngati a chibale, a masiye kapena osauka alipo pamene ali kugawa chuma cha masiye, agawireniko nawonso ndipo alankhuleni ndi mawu abwino |
وَلْيَخْشَ الَّذِينَ لَوْ تَرَكُوا مِنْ خَلْفِهِمْ ذُرِّيَّةً ضِعَافًا خَافُوا عَلَيْهِمْ فَلْيَتَّقُوا اللَّهَ وَلْيَقُولُوا قَوْلًا سَدِيدًا (9) Alekeni iwo amene amafunira zabwino ana awo, pamene iwo akufa, kuti asamale posawalakwira ana amasiye. Alekeni kuti aope Mulungu ndi kunena zinthu zokhazikitsa choonadi |
إِنَّ الَّذِينَ يَأْكُلُونَ أَمْوَالَ الْيَتَامَىٰ ظُلْمًا إِنَّمَا يَأْكُلُونَ فِي بُطُونِهِمْ نَارًا ۖ وَسَيَصْلَوْنَ سَعِيرًا (10) Kwa iwo amene amadya chuma cha ana a masiye mopanda chilungamo amameza moto m’mimba mwawo ndipo iwo adzalowa m’malawi a moto wa ku Gahena |
يُوصِيكُمُ اللَّهُ فِي أَوْلَادِكُمْ ۖ لِلذَّكَرِ مِثْلُ حَظِّ الْأُنثَيَيْنِ ۚ فَإِن كُنَّ نِسَاءً فَوْقَ اثْنَتَيْنِ فَلَهُنَّ ثُلُثَا مَا تَرَكَ ۖ وَإِن كَانَتْ وَاحِدَةً فَلَهَا النِّصْفُ ۚ وَلِأَبَوَيْهِ لِكُلِّ وَاحِدٍ مِّنْهُمَا السُّدُسُ مِمَّا تَرَكَ إِن كَانَ لَهُ وَلَدٌ ۚ فَإِن لَّمْ يَكُن لَّهُ وَلَدٌ وَوَرِثَهُ أَبَوَاهُ فَلِأُمِّهِ الثُّلُثُ ۚ فَإِن كَانَ لَهُ إِخْوَةٌ فَلِأُمِّهِ السُّدُسُ ۚ مِن بَعْدِ وَصِيَّةٍ يُوصِي بِهَا أَوْ دَيْنٍ ۗ آبَاؤُكُمْ وَأَبْنَاؤُكُمْ لَا تَدْرُونَ أَيُّهُمْ أَقْرَبُ لَكُمْ نَفْعًا ۚ فَرِيضَةً مِّنَ اللَّهِ ۗ إِنَّ اللَّهَ كَانَ عَلِيمًا حَكِيمًا (11) Mulungu wakulamulirani motere pankhani za ana anu: Mwana wa mwamuma adzalandira magawo awiri kuposa mwana wa mkazi. Ndipo ngati ana a akazi apitirira awiri, iwo adzalandira magawo awiri pa magawo atatu a katundu wosiyidwa koma ngati alipo mwana mmodzi yekha wamkazi, adzalandila theka ndipo makolo ake awiri, aliyense mwa iwo adzalandira gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi – muzimene adasiya malemuyo ngati malemuyo ali ndi mwana. Koma ngati alibe mwana ndipo makolo ake ndiwo amene ayenera kulandira katundu wake, amayi ake adzalandira gawo limodzi la magawo atatu. Ngati iye ali ndi abale ake, amayi ake adzalandira gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi atatha kukwaniritsa lonjezo la malemu ndiponso kubweza ngongole. Inu simudziwa kuti pakati pa makolo anu ndi ana anu amene ali wa phindu ndi inu. Ili ndi lamulo la Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wanzeru ndi wodziwa chilichonse |
۞ وَلَكُمْ نِصْفُ مَا تَرَكَ أَزْوَاجُكُمْ إِن لَّمْ يَكُن لَّهُنَّ وَلَدٌ ۚ فَإِن كَانَ لَهُنَّ وَلَدٌ فَلَكُمُ الرُّبُعُ مِمَّا تَرَكْنَ ۚ مِن بَعْدِ وَصِيَّةٍ يُوصِينَ بِهَا أَوْ دَيْنٍ ۚ وَلَهُنَّ الرُّبُعُ مِمَّا تَرَكْتُمْ إِن لَّمْ يَكُن لَّكُمْ وَلَدٌ ۚ فَإِن كَانَ لَكُمْ وَلَدٌ فَلَهُنَّ الثُّمُنُ مِمَّا تَرَكْتُم ۚ مِّن بَعْدِ وَصِيَّةٍ تُوصُونَ بِهَا أَوْ دَيْنٍ ۗ وَإِن كَانَ رَجُلٌ يُورَثُ كَلَالَةً أَوِ امْرَأَةٌ وَلَهُ أَخٌ أَوْ أُخْتٌ فَلِكُلِّ وَاحِدٍ مِّنْهُمَا السُّدُسُ ۚ فَإِن كَانُوا أَكْثَرَ مِن ذَٰلِكَ فَهُمْ شُرَكَاءُ فِي الثُّلُثِ ۚ مِن بَعْدِ وَصِيَّةٍ يُوصَىٰ بِهَا أَوْ دَيْنٍ غَيْرَ مُضَارٍّ ۚ وَصِيَّةً مِّنَ اللَّهِ ۗ وَاللَّهُ عَلِيمٌ حَلِيمٌ (12) Inu mudzalandira theka la chuma chimene akazi anu adasiya, ngati iwo alibe mwana. Ngati ali ndi mwana, inu mudzalandira gawo limodzi la magawo anayi la zimene mkaziyo wasiya pambuyo popereka zimene analonjeza ndi kubwezera ngongole. Nawo akazi anu adzapeza gawo limodzi m’magawo anayi muzimene mwasiya ngati mulibe mwana. Koma ngati muli ndi mwana, iwo, akaziwo, adzapeza gawo limodzi la magawo asanu ndi atatu a zimene mwasiya, pambuyo popereka zimene mudalonjeza ndi kubwezera ngongole. Ngati mwamuna kapena mkazi ndi yemwe wasiya katundu ndipo alibe mwana kapena mdzukulu, koma ali ndi mchimwene wake kapena mchemwali wake, aliyense wa iwo adzapeza gawo limodzi m’magawo asanu ndi limodzi, ndipo ngati adali ambiri koposa apo adzagawana gawo limodzi la magawo atatu pambuyo popereka zimene analonjeza kapena kubwezera ngongole mosabweretsa mavuto. Limeneli ndi lamulo lochokera kwa Mulungu, Mulungu ndi wodziwa ndi woleza mtima |
تِلْكَ حُدُودُ اللَّهِ ۚ وَمَن يُطِعِ اللَّهَ وَرَسُولَهُ يُدْخِلْهُ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا ۚ وَذَٰلِكَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ (13) Awa ndi malire a Mulungu. Ndipo aliyense amene amvera Mulungu ndi Mtumwi wake adzaikidwa m’minda yoyenda mitsinje pansi pake kumene adzakhalako nthawi zonse. Ndipo kumeneko ndiko kupambana kwakukulu |
وَمَن يَعْصِ اللَّهَ وَرَسُولَهُ وَيَتَعَدَّ حُدُودَهُ يُدْخِلْهُ نَارًا خَالِدًا فِيهَا وَلَهُ عَذَابٌ مُّهِينٌ (14) Koma iye amene amanyoza Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo amalumpha malire ake, adzamuponya ku moto wa ku Gahena ndipo adzakhala komweko mpaka kalekale ndipo iye adzalandira chilango chochititsa manyazi |
وَاللَّاتِي يَأْتِينَ الْفَاحِشَةَ مِن نِّسَائِكُمْ فَاسْتَشْهِدُوا عَلَيْهِنَّ أَرْبَعَةً مِّنكُمْ ۖ فَإِن شَهِدُوا فَأَمْسِكُوهُنَّ فِي الْبُيُوتِ حَتَّىٰ يَتَوَفَّاهُنَّ الْمَوْتُ أَوْ يَجْعَلَ اللَّهُ لَهُنَّ سَبِيلًا (15) Ndipo iwo, mwa akazi anu, amene achita chigololo, pezani mboni zokwanira zinayi zochokera pakati panu ndipo ngati iwo apereka umboni wotsimikiza, asungeni kunyumba zawo mpaka pamene imfa iwapeza kapena mpaka pamene Mulungu alamula kwa iwo njira ina |
وَاللَّذَانِ يَأْتِيَانِهَا مِنكُمْ فَآذُوهُمَا ۖ فَإِن تَابَا وَأَصْلَحَا فَأَعْرِضُوا عَنْهُمَا ۗ إِنَّ اللَّهَ كَانَ تَوَّابًا رَّحِيمًا (16) Ndipo ngati anthu awiri achita chigololo pakati panu, alangeni onse awiri. Ngati iwo alapa ndi kusiya njira zawo zoipa, asiyeni. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wa chisoni chosatha |
إِنَّمَا التَّوْبَةُ عَلَى اللَّهِ لِلَّذِينَ يَعْمَلُونَ السُّوءَ بِجَهَالَةٍ ثُمَّ يَتُوبُونَ مِن قَرِيبٍ فَأُولَٰئِكَ يَتُوبُ اللَّهُ عَلَيْهِمْ ۗ وَكَانَ اللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمًا (17) Mulungu amavomera kulapa kwa amene achita zoipa mosazindikira ngati alapa mwamsanga. Ndi iwo amene Mulungu adzawakhululukira ndipo Mulungu ndi wodziwa ndiponso wanzeru |
وَلَيْسَتِ التَّوْبَةُ لِلَّذِينَ يَعْمَلُونَ السَّيِّئَاتِ حَتَّىٰ إِذَا حَضَرَ أَحَدَهُمُ الْمَوْتُ قَالَ إِنِّي تُبْتُ الْآنَ وَلَا الَّذِينَ يَمُوتُونَ وَهُمْ كُفَّارٌ ۚ أُولَٰئِكَ أَعْتَدْنَا لَهُمْ عَذَابًا أَلِيمًا (18) Kulibe phindu kulapa kwa iwo amene amachita zinthu zoipa mpaka pamene imfa imupeza wina wa iwo ndipo ati: “Tsopano ndalapa,” kapena kwa iwo amene amafa ali osakhulupirira. Kwa iwo Ife tawakonzera chilango chowawa |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا يَحِلُّ لَكُمْ أَن تَرِثُوا النِّسَاءَ كَرْهًا ۖ وَلَا تَعْضُلُوهُنَّ لِتَذْهَبُوا بِبَعْضِ مَا آتَيْتُمُوهُنَّ إِلَّا أَن يَأْتِينَ بِفَاحِشَةٍ مُّبَيِّنَةٍ ۚ وَعَاشِرُوهُنَّ بِالْمَعْرُوفِ ۚ فَإِن كَرِهْتُمُوهُنَّ فَعَسَىٰ أَن تَكْرَهُوا شَيْئًا وَيَجْعَلَ اللَّهُ فِيهِ خَيْرًا كَثِيرًا (19) oh inu anthu okhulupirira! Inu simuloledwa kulowa chokolo chokakamiza ndipo musawazunze ndi cholinga choti muwalande zina zimene mudawapatsa pokhapokha ngati achita chigololo. Ndipo khalani nawo mwa mtendere. Ngati simukuwafuna, mwina mungachide chinthu chimene Mulungu waikamo zabwino zambiri |
وَإِنْ أَرَدتُّمُ اسْتِبْدَالَ زَوْجٍ مَّكَانَ زَوْجٍ وَآتَيْتُمْ إِحْدَاهُنَّ قِنطَارًا فَلَا تَأْخُذُوا مِنْهُ شَيْئًا ۚ أَتَأْخُذُونَهُ بُهْتَانًا وَإِثْمًا مُّبِينًا (20) Koma ngati inu mufuna kusudzula mkazi ndi cholinga chokwatira mkazi wina ndipo mutampatsa mmodzi mwa iwo chuma chochuluka, ngati mphatso ya ukwati, musatenge chilichonse mwa chumacho. Kodi inu mungakhale mopanda chilungamo ndikuwonetsa kuchimwa poyera |
وَكَيْفَ تَأْخُذُونَهُ وَقَدْ أَفْضَىٰ بَعْضُكُمْ إِلَىٰ بَعْضٍ وَأَخَذْنَ مِنكُم مِّيثَاقًا غَلِيظًا (21) Kodi inu mungalande bwanji chuma pamene munali kugonera limodzi, ndipo iwo adakupatsani chipangano chotsimikizika |
وَلَا تَنكِحُوا مَا نَكَحَ آبَاؤُكُم مِّنَ النِّسَاءِ إِلَّا مَا قَدْ سَلَفَ ۚ إِنَّهُ كَانَ فَاحِشَةً وَمَقْتًا وَسَاءَ سَبِيلًا (22) Ndipo musakwatire mkazi amene adakwatiwapo ndi abambo anu, kupatula zimene zidatha kale. Ndithudi zinali zochititsa manyazi; zonyansa ndiponso njira yauchimo |
حُرِّمَتْ عَلَيْكُمْ أُمَّهَاتُكُمْ وَبَنَاتُكُمْ وَأَخَوَاتُكُمْ وَعَمَّاتُكُمْ وَخَالَاتُكُمْ وَبَنَاتُ الْأَخِ وَبَنَاتُ الْأُخْتِ وَأُمَّهَاتُكُمُ اللَّاتِي أَرْضَعْنَكُمْ وَأَخَوَاتُكُم مِّنَ الرَّضَاعَةِ وَأُمَّهَاتُ نِسَائِكُمْ وَرَبَائِبُكُمُ اللَّاتِي فِي حُجُورِكُم مِّن نِّسَائِكُمُ اللَّاتِي دَخَلْتُم بِهِنَّ فَإِن لَّمْ تَكُونُوا دَخَلْتُم بِهِنَّ فَلَا جُنَاحَ عَلَيْكُمْ وَحَلَائِلُ أَبْنَائِكُمُ الَّذِينَ مِنْ أَصْلَابِكُمْ وَأَن تَجْمَعُوا بَيْنَ الْأُخْتَيْنِ إِلَّا مَا قَدْ سَلَفَ ۗ إِنَّ اللَّهَ كَانَ غَفُورًا رَّحِيمًا (23) Inu mwaletsedwa kukwatira awa: Amayi anu, ana anu a akazi, alongo anu, azakhali anu, achemwali amayi anu, ana akazi achimwene anu, ana akazi a alongo anu, amayi amene adakuyamwitsani, akazi amene mudayamwitsidwa nawo bere limodzi, apongozi anu, ndi ana a akazi owapeza amene muli kuwasunga amene anabereka akazi amene mwawakwatira. Koma ngati simunagonepo ndi amai awo palibe choletsa kwa inu kuwakwatira atsikanawo. Kukwatiraakaziaanaanuamunaamenemudaberekainundi akazi awiri amimba imodzi nthawi imodzi ndi koletsedwa kupatula zimene zinachitika kale. Ndithudi Mulungu ndi okhululukira ndi wa chisoni chosatha |
۞ وَالْمُحْصَنَاتُ مِنَ النِّسَاءِ إِلَّا مَا مَلَكَتْ أَيْمَانُكُمْ ۖ كِتَابَ اللَّهِ عَلَيْكُمْ ۚ وَأُحِلَّ لَكُم مَّا وَرَاءَ ذَٰلِكُمْ أَن تَبْتَغُوا بِأَمْوَالِكُم مُّحْصِنِينَ غَيْرَ مُسَافِحِينَ ۚ فَمَا اسْتَمْتَعْتُم بِهِ مِنْهُنَّ فَآتُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ فَرِيضَةً ۚ وَلَا جُنَاحَ عَلَيْكُمْ فِيمَا تَرَاضَيْتُم بِهِ مِن بَعْدِ الْفَرِيضَةِ ۚ إِنَّ اللَّهَ كَانَ عَلِيمًا حَكِيمًا (24) Ndipo ndikoletsedwa kukwatira akazi okwatiwa kupatula amene ali m’manja mwanu ngati akapolo. Limeneli ndi lamulo la Mulungu kwa inu. Ndipo ndi kololedwa kwa inu kukwatira wina aliyense amene sanatchulidwe pamwambapa ngati inu muwapatsa mphatso ya ukwati kuchokera ku chuma chanu mu njira yabwino osati ya chiwerewere. Amene muwakwatira , apatseni mphatso yawo ya ukwati motsatira malamulo. Koma pamene mphatso itchulidwa, sizolakwika kwa inu ngati mugwirizana. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa, ndi Waluntha |
وَمَن لَّمْ يَسْتَطِعْ مِنكُمْ طَوْلًا أَن يَنكِحَ الْمُحْصَنَاتِ الْمُؤْمِنَاتِ فَمِن مَّا مَلَكَتْ أَيْمَانُكُم مِّن فَتَيَاتِكُمُ الْمُؤْمِنَاتِ ۚ وَاللَّهُ أَعْلَمُ بِإِيمَانِكُم ۚ بَعْضُكُم مِّن بَعْضٍ ۚ فَانكِحُوهُنَّ بِإِذْنِ أَهْلِهِنَّ وَآتُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ بِالْمَعْرُوفِ مُحْصَنَاتٍ غَيْرَ مُسَافِحَاتٍ وَلَا مُتَّخِذَاتِ أَخْدَانٍ ۚ فَإِذَا أُحْصِنَّ فَإِنْ أَتَيْنَ بِفَاحِشَةٍ فَعَلَيْهِنَّ نِصْفُ مَا عَلَى الْمُحْصَنَاتِ مِنَ الْعَذَابِ ۚ ذَٰلِكَ لِمَنْ خَشِيَ الْعَنَتَ مِنكُمْ ۚ وَأَن تَصْبِرُوا خَيْرٌ لَّكُمْ ۗ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (25) Ndipo ngati wina wa inu alibe mwayi woti nkukwatira mkazi wokhulupirira amene ndi mfulu, mukhoza kukwatira mwa atsikana anu wokhulupirira kuchokera kugulu la akapolo amene muli nawo, ndipo Mulungu amadziwa zonse za chikhulupiriro chanu ndipo inu ndinu amodzi. Akwatitseni ndi chilolezo cha ambuye awo ndipo muwapatse mphatso yawo ya ukwati mwa chilungamo. Iwo ayenera kudzisunga, osati a chiwerewere kapena wochita chibwenzi. Ndipo ngati akwatiwa ndipo achita chigololo, chilango chawo ndi theka la chilango chimene mfulu ya ikazi ingalandire. Ichi chikhudza iye amene aopa kupwetekeka pakati pa inu. Koma ndi kwabwino ngati inu mudziletsa ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha |
يُرِيدُ اللَّهُ لِيُبَيِّنَ لَكُمْ وَيَهْدِيَكُمْ سُنَنَ الَّذِينَ مِن قَبْلِكُمْ وَيَتُوبَ عَلَيْكُمْ ۗ وَاللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ (26) Mulungu afuna kuti akufotokozereni inu ndi kukutsogolerani ku njira za iwo amene adalipo inu musanadze ndi kukukhululukirani inu. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi wanzeru |
وَاللَّهُ يُرِيدُ أَن يَتُوبَ عَلَيْكُمْ وَيُرِيدُ الَّذِينَ يَتَّبِعُونَ الشَّهَوَاتِ أَن تَمِيلُوا مَيْلًا عَظِيمًا (27) Mulungu afuna kukukhululukirani inu koma iwo amene amatsatira zilakolako zawo amafunisitsa mutasiya njira yoyenera |
يُرِيدُ اللَّهُ أَن يُخَفِّفَ عَنكُمْ ۚ وَخُلِقَ الْإِنسَانُ ضَعِيفًا (28) Mulungu afuna kukupeputsirani malamulo ake chifukwa munthu analengedwa wofoka |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَأْكُلُوا أَمْوَالَكُم بَيْنَكُم بِالْبَاطِلِ إِلَّا أَن تَكُونَ تِجَارَةً عَن تَرَاضٍ مِّنكُمْ ۚ وَلَا تَقْتُلُوا أَنفُسَكُمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ كَانَ بِكُمْ رَحِيمًا (29) oh inu anthu okhulupirira! Musadye chuma cha anzanu mopanda chilungamo ngakhale kuti ndi malonda amene mwagwirizana pakati panu. Ndipo musawonongane wina ndi mzake. Ndithudi Mulungu ndi wa chifundo chosatha kwa inu |
وَمَن يَفْعَلْ ذَٰلِكَ عُدْوَانًا وَظُلْمًا فَسَوْفَ نُصْلِيهِ نَارًا ۚ وَكَانَ ذَٰلِكَ عَلَى اللَّهِ يَسِيرًا (30) Ndipo aliyense amene achita izi mwamtopola kapena mwakusowa chilungamo, Ife tidzamulowetsa kumoto ndipo kutero si chinthu chovuta kwa Mulungu |
إِن تَجْتَنِبُوا كَبَائِرَ مَا تُنْهَوْنَ عَنْهُ نُكَفِّرْ عَنكُمْ سَيِّئَاتِكُمْ وَنُدْخِلْكُم مُّدْخَلًا كَرِيمًا (31) Ngati inu mupewa machimo akuluakulu amene mukuletsedwa, Ife tidzakukhululukirani machimo anu ndipo tidzakulowetsani kukhomo lolemekezeka |
وَلَا تَتَمَنَّوْا مَا فَضَّلَ اللَّهُ بِهِ بَعْضَكُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ ۚ لِّلرِّجَالِ نَصِيبٌ مِّمَّا اكْتَسَبُوا ۖ وَلِلنِّسَاءِ نَصِيبٌ مِّمَّا اكْتَسَبْنَ ۚ وَاسْأَلُوا اللَّهَ مِن فَضْلِهِ ۗ إِنَّ اللَّهَ كَانَ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمًا (32) Ndipo musasirire zokoma zimene Mulungu wawapatsa ena a inu kuposa anzawo. Kwa amuna kuli gawo kuzimene amachita, nawonso akazi ali ndi gawo muzimene amachita ndipo mupempheni Mulungu kuti akupatseni zabwino zake. Ndithudi Mulungu amadziwa chinthu chilichonse |
وَلِكُلٍّ جَعَلْنَا مَوَالِيَ مِمَّا تَرَكَ الْوَالِدَانِ وَالْأَقْرَبُونَ ۚ وَالَّذِينَ عَقَدَتْ أَيْمَانُكُمْ فَآتُوهُمْ نَصِيبَهُمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ كَانَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ شَهِيدًا (33) Ndipo kwa aliyense tamuikira abale olandira chuma chimene chasiyidwa ndi makolo ndi abale. Ndipo iwo amene mwachita nawo chipangano, apatseni gawo lawo nawonso kuti alandire. Ndithudi Mulungu ndi mboni pa zinthu zonse |
الرِّجَالُ قَوَّامُونَ عَلَى النِّسَاءِ بِمَا فَضَّلَ اللَّهُ بَعْضَهُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ وَبِمَا أَنفَقُوا مِنْ أَمْوَالِهِمْ ۚ فَالصَّالِحَاتُ قَانِتَاتٌ حَافِظَاتٌ لِّلْغَيْبِ بِمَا حَفِظَ اللَّهُ ۚ وَاللَّاتِي تَخَافُونَ نُشُوزَهُنَّ فَعِظُوهُنَّ وَاهْجُرُوهُنَّ فِي الْمَضَاجِعِ وَاضْرِبُوهُنَّ ۖ فَإِنْ أَطَعْنَكُمْ فَلَا تَبْغُوا عَلَيْهِنَّ سَبِيلًا ۗ إِنَّ اللَّهَ كَانَ عَلِيًّا كَبِيرًا (34) Anthu amuna ndi atetezi ndi osamala anthu akazi chifukwa Mulungu wawalemekeza ena kuposa anzawo ndiponso chifukwa cha chuma chawo chimene amagwiritsa ntchito. Motero akazi ochita zabwino ndipo amene amamvera, amasunga pamene amuna awo palibe, ndi zimene Mulungu awalamulira kuti azisunge. Ndipo akazi amene mukuona kuti samvera achenjezeni ndipo ngati iwo sasintha asiyeni agone pa okha ndipo ngati sasinthabe amenyeni. Koma ngati iwo akumverani, musawafunire njira yachabe. Ndithudi Mulungu ndi wapamwamba ndi wamkulu |
وَإِنْ خِفْتُمْ شِقَاقَ بَيْنِهِمَا فَابْعَثُوا حَكَمًا مِّنْ أَهْلِهِ وَحَكَمًا مِّنْ أَهْلِهَا إِن يُرِيدَا إِصْلَاحًا يُوَفِّقِ اللَّهُ بَيْنَهُمَا ۗ إِنَّ اللَّهَ كَانَ عَلِيمًا خَبِيرًا (35) Ndipo ngati inu muopa kuti asiyana, sankhani nkhoswe kuchokera kwa m’bale wa mwamuna ndiponso nkhoswe kuchokera kwa m’bale wa mkazi ngati iwo akufuna kuyanjanitsidwa, ndipo Mulungu adzawayanjanitsa pakati pawo. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa ndi wozindikira |
۞ وَاعْبُدُوا اللَّهَ وَلَا تُشْرِكُوا بِهِ شَيْئًا ۖ وَبِالْوَالِدَيْنِ إِحْسَانًا وَبِذِي الْقُرْبَىٰ وَالْيَتَامَىٰ وَالْمَسَاكِينِ وَالْجَارِ ذِي الْقُرْبَىٰ وَالْجَارِ الْجُنُبِ وَالصَّاحِبِ بِالْجَنبِ وَابْنِ السَّبِيلِ وَمَا مَلَكَتْ أَيْمَانُكُمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ لَا يُحِبُّ مَن كَانَ مُخْتَالًا فَخُورًا (36) Pembedzani Mulungu ndipo musamuphatikize Iye ndi china chilichonse ndipo chitani zabwino kwa makolo anu ndi achibale, kwa a masiye ndi kwa osauka, ndi kwa anzanu amene muli nawo pafupi kapena kutali ndi anzanu okhala nawo pafupi, ndi kwa a paulendo ndi kwa akapolo anu. Ndithudi Mulungu sakonda anthu a mtudzu ndi odzikundikira |
الَّذِينَ يَبْخَلُونَ وَيَأْمُرُونَ النَّاسَ بِالْبُخْلِ وَيَكْتُمُونَ مَا آتَاهُمُ اللَّهُ مِن فَضْلِهِ ۗ وَأَعْتَدْنَا لِلْكَافِرِينَ عَذَابًا مُّهِينًا (37) Iwo amene ndi oumira ndipo amauza anzawo kuti akhalenso oumira, amene amabisa chuma chimene Mulungu adawapatsa mwachifundo chake. Ndipo Ife tawakonzera anthu osakhulupirira chilango chochititsa manyazi |
وَالَّذِينَ يُنفِقُونَ أَمْوَالَهُمْ رِئَاءَ النَّاسِ وَلَا يُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَلَا بِالْيَوْمِ الْآخِرِ ۗ وَمَن يَكُنِ الشَّيْطَانُ لَهُ قَرِينًا فَسَاءَ قَرِينًا (38) Ndi iwo amene amaononga chuma chawo modzionetsera kwa anthu, ndipo sakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku la chiweruzo; ndipo aliyense amene asankha Satana kukhala bwenzi lake, wasankha bwenzi loopsya |
وَمَاذَا عَلَيْهِمْ لَوْ آمَنُوا بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ وَأَنفَقُوا مِمَّا رَزَقَهُمُ اللَّهُ ۚ وَكَانَ اللَّهُ بِهِمْ عَلِيمًا (39) Kodi iwo akadataya chiyani ngati akadakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku la chiweruzo ndi kupereka muzinthu zimene Mulungu adawapatsa iwo kuti ziziwathandiza? Mulungu amawadziwa onse |
إِنَّ اللَّهَ لَا يَظْلِمُ مِثْقَالَ ذَرَّةٍ ۖ وَإِن تَكُ حَسَنَةً يُضَاعِفْهَا وَيُؤْتِ مِن لَّدُنْهُ أَجْرًا عَظِيمًا (40) Ndithudi! Mulungu sapondereza malipiro ngakhale a kanthu kochepa, ndipo ngati muli zabwino Iye adzakaonjezera malipiro ake ndipo amapereka kuchokera kwa Iye malipiro ochuluka |
فَكَيْفَ إِذَا جِئْنَا مِن كُلِّ أُمَّةٍ بِشَهِيدٍ وَجِئْنَا بِكَ عَلَىٰ هَٰؤُلَاءِ شَهِيدًا (41) Kodi zidzakhala bwanji pamene tidzabweretsa mboni kuchokera ku anthu a mtundu uliwonse ndipo tikubweretsa iwe kuti uzakhale mboni yowatsutsa |
يَوْمَئِذٍ يَوَدُّ الَّذِينَ كَفَرُوا وَعَصَوُا الرَّسُولَ لَوْ تُسَوَّىٰ بِهِمُ الْأَرْضُ وَلَا يَكْتُمُونَ اللَّهَ حَدِيثًا (42) Patsikulo onse amene sadakhulupilire ndipo sanamvere Mtumwi adzafunitsitsa akadaundiridwa m’nthaka koma iwo sadzabisa china chilichonse kwa Mulungu |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَقْرَبُوا الصَّلَاةَ وَأَنتُمْ سُكَارَىٰ حَتَّىٰ تَعْلَمُوا مَا تَقُولُونَ وَلَا جُنُبًا إِلَّا عَابِرِي سَبِيلٍ حَتَّىٰ تَغْتَسِلُوا ۚ وَإِن كُنتُم مَّرْضَىٰ أَوْ عَلَىٰ سَفَرٍ أَوْ جَاءَ أَحَدٌ مِّنكُم مِّنَ الْغَائِطِ أَوْ لَامَسْتُمُ النِّسَاءَ فَلَمْ تَجِدُوا مَاءً فَتَيَمَّمُوا صَعِيدًا طَيِّبًا فَامْسَحُوا بِوُجُوهِكُمْ وَأَيْدِيكُمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ كَانَ عَفُوًّا غَفُورًا (43) oh inu anthu okhulupirira! Musayandikire mapemphero pamene muli oledzera mpaka pamene mudziwa tanthauzo la zimene muli nkunena ndiponso pamene mwakhala malo ndi a kunyumba kwanu ndipo simunasambe kupatula pamene muli pa ulendo. Ndipo ngati muli nkudwala kapena muli pa ulendo kapena mmodzi mwa inu wachokera ku chimbudzi kapena mwagona limodzi ndi akazi anu, ndipo simudapeze madzi, tapani dothi labwino ndipo mupukute nkhope ndi manja anu. Ndithudi Mulungu ndi wa chifundo ndi okhululukira |
أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ أُوتُوا نَصِيبًا مِّنَ الْكِتَابِ يَشْتَرُونَ الضَّلَالَةَ وَيُرِيدُونَ أَن تَضِلُّوا السَّبِيلَ (44) Kodi iwe siunawaone iwo amene adapatsidwa gawo la Buku ali kusochera ndipo akufuna kuti iwe usochere ku njira yabwino |
وَاللَّهُ أَعْلَمُ بِأَعْدَائِكُمْ ۚ وَكَفَىٰ بِاللَّهِ وَلِيًّا وَكَفَىٰ بِاللَّهِ نَصِيرًا (45) Mulungu amawadziwa bwino adani anu ndipo Mulungu ndi wokwana kukhala Mtetezi ndipo ndi wokwana kukhala Mthandizi |
مِّنَ الَّذِينَ هَادُوا يُحَرِّفُونَ الْكَلِمَ عَن مَّوَاضِعِهِ وَيَقُولُونَ سَمِعْنَا وَعَصَيْنَا وَاسْمَعْ غَيْرَ مُسْمَعٍ وَرَاعِنَا لَيًّا بِأَلْسِنَتِهِمْ وَطَعْنًا فِي الدِّينِ ۚ وَلَوْ أَنَّهُمْ قَالُوا سَمِعْنَا وَأَطَعْنَا وَاسْمَعْ وَانظُرْنَا لَكَانَ خَيْرًا لَّهُمْ وَأَقْوَمَ وَلَٰكِن لَّعَنَهُمُ اللَّهُ بِكُفْرِهِمْ فَلَا يُؤْمِنُونَ إِلَّا قَلِيلًا (46) Pakati pa Ayuda pali ena amene amasinthitsa mawu m’malo mwake ndipo amati: “Ife tamva mau ako koma sitikumvera ndipo imva koma usamve chili chonse” ndipo amati: ‘Chenjera, timvere ife ndipo ife tidzakumvera’ ali kupotoza malirime awo ndi cholinga chotukwana chipembedzo. Koma iwo akadati: “Tamva ndipo tatsatira; tiphunzitse ife”; zikadawakhalira bwino kwambiri, koma Mulungu wawatemberera iwo chifukwa chosakhulupirira kwawo motero iwo sakhulupilira koma pang’ono |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ آمِنُوا بِمَا نَزَّلْنَا مُصَدِّقًا لِّمَا مَعَكُم مِّن قَبْلِ أَن نَّطْمِسَ وُجُوهًا فَنَرُدَّهَا عَلَىٰ أَدْبَارِهَا أَوْ نَلْعَنَهُمْ كَمَا لَعَنَّا أَصْحَابَ السَّبْتِ ۚ وَكَانَ أَمْرُ اللَّهِ مَفْعُولًا (47) oh inu anthu amene mudapatsidwa Buku! Khulupirirani zimene tavumbulutsa zimene zitsimikizira Maua Mulunguamenemulinawo, tisadatembenuzenkhope ndikuzibwezera kumbuyo kwake kapena kuwatemberera monga mmene tidawatemberera anthu ophwanya tsiku la Sabata. Ndipo lamulo la Mulungu limatsatidwa ndipo limakwaniritsidwa |
إِنَّ اللَّهَ لَا يَغْفِرُ أَن يُشْرَكَ بِهِ وَيَغْفِرُ مَا دُونَ ذَٰلِكَ لِمَن يَشَاءُ ۚ وَمَن يُشْرِكْ بِاللَّهِ فَقَدِ افْتَرَىٰ إِثْمًا عَظِيمًا (48) Ndithudi Mulungu sakhululukira kuti milungu izipembedzedwa yowonjezera pa Iye koma Iye amakhululukira aliyense amene wamufuna pa machimo ena. Ndipo aliyense amene amapembedza milungu ina yowonjezera pa Iye, iye, ndithudi, wapeka bodza loopsya |
أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ يُزَكُّونَ أَنفُسَهُم ۚ بَلِ اللَّهُ يُزَكِّي مَن يَشَاءُ وَلَا يُظْلَمُونَ فَتِيلًا (49) Kodi simunaone amene amadziyeretsa okha? Iyayi! Koma Mulungu amayeretsa aliyense amene Iye wamufuna ndipo iwo sadzaponderezedwa ngakhale ndi pang’ono pomwe |
انظُرْ كَيْفَ يَفْتَرُونَ عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ ۖ وَكَفَىٰ بِهِ إِثْمًا مُّبِينًا (50) Taona mmene iwo amapekera bodza lokhudza Mulungu ndipo zimenezi zikukwanira kukhala tchimo looneka |
أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ أُوتُوا نَصِيبًا مِّنَ الْكِتَابِ يُؤْمِنُونَ بِالْجِبْتِ وَالطَّاغُوتِ وَيَقُولُونَ لِلَّذِينَ كَفَرُوا هَٰؤُلَاءِ أَهْدَىٰ مِنَ الَّذِينَ آمَنُوا سَبِيلًا (51) Kodi siunaone iwo amene adapatsidwa gawo la Buku la Mulungu? Iwo amakhulupirira mafano ndi milungu yabodza ndipo amawauza osakhulupilira kuti ndi otsogozedwa bwino kuposa anthu okhulupirira |
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ لَعَنَهُمُ اللَّهُ ۖ وَمَن يَلْعَنِ اللَّهُ فَلَن تَجِدَ لَهُ نَصِيرًا (52) Amenewa ndiwo anthu amene Mulungu wawatemberera ndipo aliyense amene atembereredwa ndi Mulungu iwe siungamupezere womuthandiza |
أَمْ لَهُمْ نَصِيبٌ مِّنَ الْمُلْكِ فَإِذًا لَّا يُؤْتُونَ النَّاسَ نَقِيرًا (53) Kodi kapena iwo ali ndi gawo mu Ufumu? Zikadatero, iwo sakadawapatsa anthu ngakhale kanthu kakang’ono |
أَمْ يَحْسُدُونَ النَّاسَ عَلَىٰ مَا آتَاهُمُ اللَّهُ مِن فَضْلِهِ ۖ فَقَدْ آتَيْنَا آلَ إِبْرَاهِيمَ الْكِتَابَ وَالْحِكْمَةَ وَآتَيْنَاهُم مُّلْكًا عَظِيمًا (54) Kodi kapena iwo amachitira kaduka anthu mu zinthu zabwino zimene Mulungu wawapatsa? Ife tidawapatsa ana a Abrahamu Buku ndi luntha ndipo tidawapatsa Ufumu waukulu |
فَمِنْهُم مَّنْ آمَنَ بِهِ وَمِنْهُم مَّن صَدَّ عَنْهُ ۚ وَكَفَىٰ بِجَهَنَّمَ سَعِيرًا (55) Ena mwa iwo adakhulupirira iye koma ena a iwo anayang’ana kumbali ndipo Moto ukukwanira kukhala chilango chawo |
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا بِآيَاتِنَا سَوْفَ نُصْلِيهِمْ نَارًا كُلَّمَا نَضِجَتْ جُلُودُهُم بَدَّلْنَاهُمْ جُلُودًا غَيْرَهَا لِيَذُوقُوا الْعَذَابَ ۗ إِنَّ اللَّهَ كَانَ عَزِيزًا حَكِيمًا (56) Ndithudi iwo amene adakana zizindikiro zathu tidzawaotcha ku moto. Nthawi zonse pamene makungu awo azidzapsya, Ife tidzawapatsa makungu ena kuti iwo alawe chilango. Ndithudi Mulungu ndi wamphamvu nthawi zonse ndi Wanzeru |
وَالَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ سَنُدْخِلُهُمْ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا أَبَدًا ۖ لَّهُمْ فِيهَا أَزْوَاجٌ مُّطَهَّرَةٌ ۖ وَنُدْخِلُهُمْ ظِلًّا ظَلِيلًا (57) Koma iwo amene amakhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, Ife tidzawalowetsa m’minda yothiriridwa ndi mitsinje yoyenda pansi pake, ndipo adzakhalako mpaka kalekale. Ndipo kumeneko adzakhala ndi akazi oyera ndipo Ife tidzawalowetsa ku mthunzi wabwino kwambiri |
۞ إِنَّ اللَّهَ يَأْمُرُكُمْ أَن تُؤَدُّوا الْأَمَانَاتِ إِلَىٰ أَهْلِهَا وَإِذَا حَكَمْتُم بَيْنَ النَّاسِ أَن تَحْكُمُوا بِالْعَدْلِ ۚ إِنَّ اللَّهَ نِعِمَّا يَعِظُكُم بِهِ ۗ إِنَّ اللَّهَ كَانَ سَمِيعًا بَصِيرًا (58) Ndithudi Mulungu ali kukulamulirani kuti mubwezere katundu amene mwasunga kwa eni ake ndipo ngati muweruza pakati pa anthu, weruzani mwachilungamo. Ndithudi chilangizo chimene Mulungu akukulangizani ndi chabwino kwambiri. Ndithudi Mulungu amamva nthawi zonse ndipo amaona zinthu zonse |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا أَطِيعُوا اللَّهَ وَأَطِيعُوا الرَّسُولَ وَأُولِي الْأَمْرِ مِنكُمْ ۖ فَإِن تَنَازَعْتُمْ فِي شَيْءٍ فَرُدُّوهُ إِلَى اللَّهِ وَالرَّسُولِ إِن كُنتُمْ تُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ ۚ ذَٰلِكَ خَيْرٌ وَأَحْسَنُ تَأْوِيلًا (59) oh inu anthu okhulupirira! Mverani Mulungu ndipo mverani Mtumwi wake ndiponso iwo amene ali ndi udindo pakati panu. Ndipo ngati mutsutsana pa chinthu china chilichonse, chiperekeni icho kwa Mulungu ndi Mtumwi wake ngati inu mumakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza. Zimenezi zidzakhala zabwino ndi zolungama pomaliza |
أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ يَزْعُمُونَ أَنَّهُمْ آمَنُوا بِمَا أُنزِلَ إِلَيْكَ وَمَا أُنزِلَ مِن قَبْلِكَ يُرِيدُونَ أَن يَتَحَاكَمُوا إِلَى الطَّاغُوتِ وَقَدْ أُمِرُوا أَن يَكْفُرُوا بِهِ وَيُرِيدُ الشَّيْطَانُ أَن يُضِلَّهُمْ ضَلَالًا بَعِيدًا (60) Kodi iwe wawaona amene amanena kuti amakhulupirira mu zimene zavumbulitsidwa kwa iwe ndi kwa Atumwi ena amene adalipo iwe usanadze ndipo iwo amafunafuna chiweruzo cha oweruza abodza, pamene iwo adalamulidwa kuti awakane iwo? Koma chofuna cha Satana ndi kuwasokeretsa iwo ku njira yoyenera |
وَإِذَا قِيلَ لَهُمْ تَعَالَوْا إِلَىٰ مَا أَنزَلَ اللَّهُ وَإِلَى الرَّسُولِ رَأَيْتَ الْمُنَافِقِينَ يَصُدُّونَ عَنكَ صُدُودًا (61) Ndipo pamene auzidwa “Bwerani ku zimene Mulungu wavumbulutsa ndiponso kwa Mtumwi,” iwe umaona anthu a chinyengo ali kukukana iwe mwamwano |
فَكَيْفَ إِذَا أَصَابَتْهُم مُّصِيبَةٌ بِمَا قَدَّمَتْ أَيْدِيهِمْ ثُمَّ جَاءُوكَ يَحْلِفُونَ بِاللَّهِ إِنْ أَرَدْنَا إِلَّا إِحْسَانًا وَتَوْفِيقًا (62) Kodi bwanji, ngati vuto ligwa pa iwo chifukwa cha ntchito zimene adatsogoza manja awo, amadza kwa iwe, kulumbira m’dzina la Mulungu kuti: “Ife sitifuna china chilichonse koma zabwino ndi chigwirizano!” |
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ يَعْلَمُ اللَّهُ مَا فِي قُلُوبِهِمْ فَأَعْرِضْ عَنْهُمْ وَعِظْهُمْ وَقُل لَّهُمْ فِي أَنفُسِهِمْ قَوْلًا بَلِيغًا (63) Awa ndiwo amene Mulungu amadziwa zimene zili m’mitima mwawo. Motero asiye koma uwachenjeze ndipo uwauze mawu ogwira mtima |
وَمَا أَرْسَلْنَا مِن رَّسُولٍ إِلَّا لِيُطَاعَ بِإِذْنِ اللَّهِ ۚ وَلَوْ أَنَّهُمْ إِذ ظَّلَمُوا أَنفُسَهُمْ جَاءُوكَ فَاسْتَغْفَرُوا اللَّهَ وَاسْتَغْفَرَ لَهُمُ الرَّسُولُ لَوَجَدُوا اللَّهَ تَوَّابًا رَّحِيمًا (64) IfesitidatumizeMtumwialiyense,komakutiatsatiridwe mwa lamulo la Mulungu. Ngati iwo adadzilakwitsa, akanadza kwa iwe kupempha chikhululukiro cha Mulungu ndipo Mtumwi akadawapemphera chikhululukiro cha Mulungu. Iwo akadamupeza Iye wokhululuka ndi wa chisoni |
فَلَا وَرَبِّكَ لَا يُؤْمِنُونَ حَتَّىٰ يُحَكِّمُوكَ فِيمَا شَجَرَ بَيْنَهُمْ ثُمَّ لَا يَجِدُوا فِي أَنفُسِهِمْ حَرَجًا مِّمَّا قَضَيْتَ وَيُسَلِّمُوا تَسْلِيمًا (65) Koma iyayi, pali Ambuye wako, iwo sadzakhala okhulupirira mpaka pamene akusankha iwe kukhala oweruza pa mikangano ya pakati pawo ndipo satsutsa chiweruzo chako, ndipo achivomeleza kwathunthu |
وَلَوْ أَنَّا كَتَبْنَا عَلَيْهِمْ أَنِ اقْتُلُوا أَنفُسَكُمْ أَوِ اخْرُجُوا مِن دِيَارِكُم مَّا فَعَلُوهُ إِلَّا قَلِيلٌ مِّنْهُمْ ۖ وَلَوْ أَنَّهُمْ فَعَلُوا مَا يُوعَظُونَ بِهِ لَكَانَ خَيْرًا لَّهُمْ وَأَشَدَّ تَثْبِيتًا (66) Zikadakhala kuti Ife tidawalamulira kuti: “Mudziphe nokha kapena tulukani m’nyumba zanu,” sakadachita kupatula owerengeka okha. Koma ngati iwo akadachita zimene auzidwa zikadakhala bwino kwa iwo, ndipo zikadaonjezera chikhulupiriro |
وَإِذًا لَّآتَيْنَاهُم مِّن لَّدُنَّا أَجْرًا عَظِيمًا (67) Ndipo ndithudi Ife tikadawapatsa iwo, kuchokera kwa Ife, dipo lalikulu |
وَلَهَدَيْنَاهُمْ صِرَاطًا مُّسْتَقِيمًا (68) Ndithudi Ife tikadawatsogolera ku njira yoyenera |
وَمَن يُطِعِ اللَّهَ وَالرَّسُولَ فَأُولَٰئِكَ مَعَ الَّذِينَ أَنْعَمَ اللَّهُ عَلَيْهِم مِّنَ النَّبِيِّينَ وَالصِّدِّيقِينَ وَالشُّهَدَاءِ وَالصَّالِحِينَ ۚ وَحَسُنَ أُولَٰئِكَ رَفِيقًا (69) Ndipo aliyense amene amvera Mulungu ndi Mtumwi wake, ameneyo ndi amene ali pamodzi ndi anthu amene Mulungu wawadalitsa kuchokera ku gulu la Atumwi, anthu a chilungamo, anthu ofera ku nkhondo m’njira ya Mulungu ndi anthu ochita zabwino. Ati bwanji kukoma kukhala mgulu lotere |
ذَٰلِكَ الْفَضْلُ مِنَ اللَّهِ ۚ وَكَفَىٰ بِاللَّهِ عَلِيمًا (70) Ichi ndi chisomo chochokera kwa Mulungu, ndipo Mulungu ndi wokwanira kukhala wodziwa chili chonse |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا خُذُوا حِذْرَكُمْ فَانفِرُوا ثُبَاتٍ أَوِ انفِرُوا جَمِيعًا (71) Oh inu anthu okhulupirira! Khalani okonzeka ndipo yendani m’magulu m’magulu kapena pa gulu limodzi lokha |
وَإِنَّ مِنكُمْ لَمَن لَّيُبَطِّئَنَّ فَإِنْ أَصَابَتْكُم مُّصِيبَةٌ قَالَ قَدْ أَنْعَمَ اللَّهُ عَلَيَّ إِذْ لَمْ أَكُن مَّعَهُمْ شَهِيدًا (72) Alipo wina pakati panu amene adzatsalira m’mbuyo. Amene ngati choipa chioneka kwa inu amanena kuti: “Ndithudi Mulungu wandionetsera ine chifundo chifukwa sindinali nawo.” |
وَلَئِنْ أَصَابَكُمْ فَضْلٌ مِّنَ اللَّهِ لَيَقُولَنَّ كَأَن لَّمْ تَكُن بَيْنَكُمْ وَبَيْنَهُ مَوَدَّةٌ يَا لَيْتَنِي كُنتُ مَعَهُمْ فَأَفُوزَ فَوْزًا عَظِيمًا (73) Koma ngati mtendere wochokera kwa Mulungu ukupezani, ndithudi iye adzanena ngati kuti padalibe ubwenzi pakati pa iye ndi inu ndipo iwo adzati: “Ndikadakhala nawo limodzi, ndithudi ndikadakhala ndi mwayi waukulu.” |
۞ فَلْيُقَاتِلْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ الَّذِينَ يَشْرُونَ الْحَيَاةَ الدُّنْيَا بِالْآخِرَةِ ۚ وَمَن يُقَاتِلْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ فَيُقْتَلْ أَوْ يَغْلِبْ فَسَوْفَ نُؤْتِيهِ أَجْرًا عَظِيمًا (74) Kotero alekeni iwo amene amagulitsa moyo uno ndi moyo umene uli nkudza kuti amenye nkhondo mu njira ya Mulungu. Aliyense amene amenya nkhondo m’njira ya Mulungu ndipo aphedwa kapena apambana, Ife tidzamupatsa dipo lalikulu |
وَمَا لَكُمْ لَا تُقَاتِلُونَ فِي سَبِيلِ اللَّهِ وَالْمُسْتَضْعَفِينَ مِنَ الرِّجَالِ وَالنِّسَاءِ وَالْوِلْدَانِ الَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَا أَخْرِجْنَا مِنْ هَٰذِهِ الْقَرْيَةِ الظَّالِمِ أَهْلُهَا وَاجْعَل لَّنَا مِن لَّدُنكَ وَلِيًّا وَاجْعَل لَّنَا مِن لَّدُنكَ نَصِيرًا (75) Kodi ndi chifukwa chiyani inu simukumenya nkhondo m’njira ya Mulungu pamene anthu ofoka mwa anthu amuna, akazi ndi ana amati: “Ambuye wathu! Tipulumutseni kuchoka kumzinda uwu wa anthu wochita zoipa ndipo tidzutsireni mtetezi wochokera kwa Inu amene adzatithandiza ife.” |
الَّذِينَ آمَنُوا يُقَاتِلُونَ فِي سَبِيلِ اللَّهِ ۖ وَالَّذِينَ كَفَرُوا يُقَاتِلُونَ فِي سَبِيلِ الطَّاغُوتِ فَقَاتِلُوا أَوْلِيَاءَ الشَّيْطَانِ ۖ إِنَّ كَيْدَ الشَّيْطَانِ كَانَ ضَعِيفًا (76) Iwo amene akhulupirira amamenya nkhondo m’njira ya Mulungu koma amene sakhulupilira amamenya mu njira ya Satana. Kotero inu menyanani ndi abwenzi a Satana, ndithudi chikonzero cha Satana ndi chopanda mphamvu |
أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ قِيلَ لَهُمْ كُفُّوا أَيْدِيَكُمْ وَأَقِيمُوا الصَّلَاةَ وَآتُوا الزَّكَاةَ فَلَمَّا كُتِبَ عَلَيْهِمُ الْقِتَالُ إِذَا فَرِيقٌ مِّنْهُمْ يَخْشَوْنَ النَّاسَ كَخَشْيَةِ اللَّهِ أَوْ أَشَدَّ خَشْيَةً ۚ وَقَالُوا رَبَّنَا لِمَ كَتَبْتَ عَلَيْنَا الْقِتَالَ لَوْلَا أَخَّرْتَنَا إِلَىٰ أَجَلٍ قَرِيبٍ ۗ قُلْ مَتَاعُ الدُّنْيَا قَلِيلٌ وَالْآخِرَةُ خَيْرٌ لِّمَنِ اتَّقَىٰ وَلَا تُظْلَمُونَ فَتِيلًا (77) Kodi siunaone anthu amene amauzidwa kuti: “Musamenye nkhondo, pempherani mwandondomeko ndipo perekani msonkho wothandizira anthu osauka,” koma pamene iwo adalamulidwa kuti amenye nkhondo, taona; enaaiwoamaopaanthumongamomweamamuopera Mulungu kapenanso kuposa apa. Iwo amati: “Ambuye wathu! Kodi ndi chifukwa chiyani mwatilamula kuti timenye nkhondo? Kodi simungatipatse nthawi yopumula ngakhale yochepa” Nena: “Chisangalalo cha moyo uno ndi chochepa kwambiri. Moyo umene uli nkudza ndi wabwino kwambiri kwa iye amene amaopa Mulungu ndipo inu simudzaponderezedwa ndi pang’onong’ono pomwe.” |
أَيْنَمَا تَكُونُوا يُدْرِككُّمُ الْمَوْتُ وَلَوْ كُنتُمْ فِي بُرُوجٍ مُّشَيَّدَةٍ ۗ وَإِن تُصِبْهُمْ حَسَنَةٌ يَقُولُوا هَٰذِهِ مِنْ عِندِ اللَّهِ ۖ وَإِن تُصِبْهُمْ سَيِّئَةٌ يَقُولُوا هَٰذِهِ مِنْ عِندِكَ ۚ قُلْ كُلٌّ مِّنْ عِندِ اللَّهِ ۖ فَمَالِ هَٰؤُلَاءِ الْقَوْمِ لَا يَكَادُونَ يَفْقَهُونَ حَدِيثًا (78) Pali ponse pomwe mungakhale, imfa idzakupezani, ngakhale inu mutadzitsekera mkati mwa nsanja zolimba. Ndipo ngati zabwino ziwapeza, iwo amati: “Izi zachokera kwa Mulungu” koma ngati choipa chiwagwera, iwo amati: “Ichi ndi chochokera kwa iwe.” Nena: “Zinthu zonse zimachokera kwa Mulungu.” Kodi ndi chiani chawapeza anthu awa kuti sangathe kuzindikira china chiri chonse |
مَّا أَصَابَكَ مِنْ حَسَنَةٍ فَمِنَ اللَّهِ ۖ وَمَا أَصَابَكَ مِن سَيِّئَةٍ فَمِن نَّفْسِكَ ۚ وَأَرْسَلْنَاكَ لِلنَّاسِ رَسُولًا ۚ وَكَفَىٰ بِاللَّهِ شَهِيدًا (79) Chilichonse chabwino chimene chidza pa iwe ndi chochokera kwa Mulungu, ndipo choipa chimene chikupeza ndi chochokera kwa iwe mwini. Ndipo Ife takutumiza iwe ngati Mtumwi kwa anthu onse. Ndipo Mulungu akwana kukhala mboni |
مَّن يُطِعِ الرَّسُولَ فَقَدْ أَطَاعَ اللَّهَ ۖ وَمَن تَوَلَّىٰ فَمَا أَرْسَلْنَاكَ عَلَيْهِمْ حَفِيظًا (80) Aliyense amene amvera Mtumwi ndithudi amvera Mulungu ndipo iye amene safuna kukumvera iwe, Ife sitidakutumize kuti ukhale wowayang’anira ayi |
وَيَقُولُونَ طَاعَةٌ فَإِذَا بَرَزُوا مِنْ عِندِكَ بَيَّتَ طَائِفَةٌ مِّنْهُمْ غَيْرَ الَّذِي تَقُولُ ۖ وَاللَّهُ يَكْتُبُ مَا يُبَيِّتُونَ ۖ فَأَعْرِضْ عَنْهُمْ وَتَوَكَّلْ عَلَى اللَّهِ ۚ وَكَفَىٰ بِاللَّهِ وَكِيلًا (81) Iwo amati: “Ife ndife omvera” koma iwo akangochoka kwa iwe, ambiri a iwo amachita chiwembu usiku pochita zinthu zimene siukunena. Koma Mulungu amalemba ziwembu zawo zonse zomwe amachita usiku. Kotero aleke okha ndipo ika chikhulupiliro chako mwa Mulungu. Ndipo Mulungu ndi okwana kukhala Mtetezi |
أَفَلَا يَتَدَبَّرُونَ الْقُرْآنَ ۚ وَلَوْ كَانَ مِنْ عِندِ غَيْرِ اللَّهِ لَوَجَدُوا فِيهِ اخْتِلَافًا كَثِيرًا (82) Kodi iwo salingalira za Korani? Ilo likadakhala kuti silinachokere kwa Mulungu, iwo akadapeza mu ilo kusemphana kwambiri |
وَإِذَا جَاءَهُمْ أَمْرٌ مِّنَ الْأَمْنِ أَوِ الْخَوْفِ أَذَاعُوا بِهِ ۖ وَلَوْ رَدُّوهُ إِلَى الرَّسُولِ وَإِلَىٰ أُولِي الْأَمْرِ مِنْهُمْ لَعَلِمَهُ الَّذِينَ يَسْتَنبِطُونَهُ مِنْهُمْ ۗ وَلَوْلَا فَضْلُ اللَّهِ عَلَيْكُمْ وَرَحْمَتُهُ لَاتَّبَعْتُمُ الشَّيْطَانَ إِلَّا قَلِيلًا (83) Pamene iwo amva nkhani iliyonse ya mtendere kapena yochititsa mantha, iwo amaiulutsa koma iwo akanaipereka kwa Mtumwi kapena kwa amene ali ndi udindo pakati pawo kapena anthu amene amafufuza bwino nkhani, akadadziwa. Ndipo pakadapanda chisomo ndi chisoni cha Mulungu pa inu, inu mukanatsatira Satana kupatula anthu ochepa okha |
فَقَاتِلْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ لَا تُكَلَّفُ إِلَّا نَفْسَكَ ۚ وَحَرِّضِ الْمُؤْمِنِينَ ۖ عَسَى اللَّهُ أَن يَكُفَّ بَأْسَ الَّذِينَ كَفَرُوا ۚ وَاللَّهُ أَشَدُّ بَأْسًا وَأَشَدُّ تَنكِيلًا (84) Motero menya nkhondo mu njira ya Mulungu, iwe siudzafunsidwa za munthu wina ayi koma za iwe wekha ndipo alimbikitse okhulupirira kuti mwina Mulungu adzagonjetsa anthu osakhulupirira. Mulungu ndi wamphamvu kwambiri ndi Waukali polanga |
مَّن يَشْفَعْ شَفَاعَةً حَسَنَةً يَكُن لَّهُ نَصِيبٌ مِّنْهَا ۖ وَمَن يَشْفَعْ شَفَاعَةً سَيِّئَةً يَكُن لَّهُ كِفْلٌ مِّنْهَا ۗ وَكَانَ اللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ مُّقِيتًا (85) Aliyense amene amathandiza kuchita ntchito zabwino adzalandira gawo lake la ntchitoyo, ndipo aliyense amene amathandiza kuchita ntchito zoipa naye adzakhala ndi gawo la uchimo. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu yochita chinthu china chilichonse |
وَإِذَا حُيِّيتُم بِتَحِيَّةٍ فَحَيُّوا بِأَحْسَنَ مِنْهَا أَوْ رُدُّوهَا ۗ إِنَّ اللَّهَ كَانَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ حَسِيبًا (86) Ngati munthu akulonjerani onetsetsani kuti malonje anu ndi abwino kuposa malonje ake kapena mumubwezere monga momwe wakulonjererani. Ndithudi Mulungu amasunga chiwerengero cha zinthu zonse |
اللَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۚ لَيَجْمَعَنَّكُمْ إِلَىٰ يَوْمِ الْقِيَامَةِ لَا رَيْبَ فِيهِ ۗ وَمَنْ أَصْدَقُ مِنَ اللَّهِ حَدِيثًا (87) Mulungu! Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Ndithudi Iye adzakusonkhanitsani nonse pamodzi patsiku louka kwa akufa, tsiku lopanda chikaiko. Kodi ndani amalankhula zoona kuposa Mulungu |
۞ فَمَا لَكُمْ فِي الْمُنَافِقِينَ فِئَتَيْنِ وَاللَّهُ أَرْكَسَهُم بِمَا كَسَبُوا ۚ أَتُرِيدُونَ أَن تَهْدُوا مَنْ أَضَلَّ اللَّهُ ۖ وَمَن يُضْلِلِ اللَّهُ فَلَن تَجِدَ لَهُ سَبِيلًا (88) Kodi mwatani kuti mukhale ogawikana magulu awiri pa nkhani ya anthu a chinyengo? Mulungu, mwini wake wawataya chifukwa cha ntchito zawo zoipa. Kodi inu mufuna kumutsogolera iye amene Mulungu wamusokeretsa? Inu simudzapeza njira ina iliyonse |
وَدُّوا لَوْ تَكْفُرُونَ كَمَا كَفَرُوا فَتَكُونُونَ سَوَاءً ۖ فَلَا تَتَّخِذُوا مِنْهُمْ أَوْلِيَاءَ حَتَّىٰ يُهَاجِرُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ ۚ فَإِن تَوَلَّوْا فَخُذُوهُمْ وَاقْتُلُوهُمْ حَيْثُ وَجَدتُّمُوهُمْ ۖ وَلَا تَتَّخِذُوا مِنْهُمْ وَلِيًّا وَلَا نَصِيرًا (89) Iwo afuna kuti iwe usakhulupirire monga momwe iwo sadakhulupirire kuti mulingane. Iwe usapalane nawo ubwenzi ayi mpaka pamene asiya nyumba zawo chifukwa cha njira ya Mulungu. Koma ngati iwo akuthawani, agwireni ndipo muwaphe pali ponse pamene muwapeze ndipo musafune abwenzi kapena okuthandizani pakati pawo |
إِلَّا الَّذِينَ يَصِلُونَ إِلَىٰ قَوْمٍ بَيْنَكُمْ وَبَيْنَهُم مِّيثَاقٌ أَوْ جَاءُوكُمْ حَصِرَتْ صُدُورُهُمْ أَن يُقَاتِلُوكُمْ أَوْ يُقَاتِلُوا قَوْمَهُمْ ۚ وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ لَسَلَّطَهُمْ عَلَيْكُمْ فَلَقَاتَلُوكُمْ ۚ فَإِنِ اعْتَزَلُوكُمْ فَلَمْ يُقَاتِلُوكُمْ وَأَلْقَوْا إِلَيْكُمُ السَّلَمَ فَمَا جَعَلَ اللَّهُ لَكُمْ عَلَيْهِمْ سَبِيلًا (90) Kupatula okhawo amene gulu lina limene liri pakati panu ndipo inu mwachita nawo pangano lokhazikitsa mtendere kapena adza kwa inu chifukwa mitima yawo yawaletsa kuti amenyane nanu kapena kumenyana ndi anthu a mtundu wawo. Mulungu akadafuna akadawapatsa iwo mphamvu zoti akugonjetseni inu, kotero akadamenyana nanu. Choncho ngati atalikirana nanu ndipo asiya kumenyana nanu ndi kukuonetsani mtendere, Mulungu wakulamulirani kuti musawaononge |
سَتَجِدُونَ آخَرِينَ يُرِيدُونَ أَن يَأْمَنُوكُمْ وَيَأْمَنُوا قَوْمَهُمْ كُلَّ مَا رُدُّوا إِلَى الْفِتْنَةِ أُرْكِسُوا فِيهَا ۚ فَإِن لَّمْ يَعْتَزِلُوكُمْ وَيُلْقُوا إِلَيْكُمُ السَّلَمَ وَيَكُفُّوا أَيْدِيَهُمْ فَخُذُوهُمْ وَاقْتُلُوهُمْ حَيْثُ ثَقِفْتُمُوهُمْ ۚ وَأُولَٰئِكُمْ جَعَلْنَا لَكُمْ عَلَيْهِمْ سُلْطَانًا مُّبِينًا (91) Mudzawapeza ena ali kufuna chitetezo chanu ndiponso chitetezo chochokera kwa anthu awo. Nthawi iliyonse akayesedwa iwo amapita mwamsangamsanga. Ngati iwo sachoka kwa inu ndiponso ngati iwo sakhazikitsa mtendere ndi inu kapena kusiya nkhondo ndi inu, agwireni ndi kuwapha pali ponse pamene muwapeza. Pa anthu otere, Ife takupatsani chilolezo chomenyana nawo |
وَمَا كَانَ لِمُؤْمِنٍ أَن يَقْتُلَ مُؤْمِنًا إِلَّا خَطَأً ۚ وَمَن قَتَلَ مُؤْمِنًا خَطَأً فَتَحْرِيرُ رَقَبَةٍ مُّؤْمِنَةٍ وَدِيَةٌ مُّسَلَّمَةٌ إِلَىٰ أَهْلِهِ إِلَّا أَن يَصَّدَّقُوا ۚ فَإِن كَانَ مِن قَوْمٍ عَدُوٍّ لَّكُمْ وَهُوَ مُؤْمِنٌ فَتَحْرِيرُ رَقَبَةٍ مُّؤْمِنَةٍ ۖ وَإِن كَانَ مِن قَوْمٍ بَيْنَكُمْ وَبَيْنَهُم مِّيثَاقٌ فَدِيَةٌ مُّسَلَّمَةٌ إِلَىٰ أَهْلِهِ وَتَحْرِيرُ رَقَبَةٍ مُّؤْمِنَةٍ ۖ فَمَن لَّمْ يَجِدْ فَصِيَامُ شَهْرَيْنِ مُتَتَابِعَيْنِ تَوْبَةً مِّنَ اللَّهِ ۗ وَكَانَ اللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمًا (92) Ndi chinthu choletsedwa kuti munthu wokhulupirira aphe mzake wokhulupirira kupatula mwangozi. Ndipo aliyense amene, mwangozi, akupha munthu wokhulupirira ayenera kumasula kapolo wokhulupirira m’modzi ndi kulipira ndalama zopepesera ku banja la ophedwayo, kupatula ngati iwo asankha kuti amukhululukira munthu wakuphayo. Ngati malemuyo anali wochokera kwa adani anu ndipo anali wokhulupirira, chilango chake ndi kumasula kapolo m’modzi wa wokhulupirira. Koma ngati malemuyo anali ochokera ku mtundu wa athu ogwirizana nawo, ndalama za chipepeso ziyenera kuperekedwa kubanja la munthu wakufayo ndi kumasula kapolo mmodzi wa wokhulupirira. Ngati munthu sangathe kupeza izi, ayenera kusala miyezi iwiri motsatizana ndi cholinga chopeza chikhululukiro kwa Mulungu. Ndipo Mulungu ndi Wodziwa ndi Waluntha |
وَمَن يَقْتُلْ مُؤْمِنًا مُّتَعَمِّدًا فَجَزَاؤُهُ جَهَنَّمُ خَالِدًا فِيهَا وَغَضِبَ اللَّهُ عَلَيْهِ وَلَعَنَهُ وَأَعَدَّ لَهُ عَذَابًا عَظِيمًا (93) Ndipo aliyense amene apha munthu wokhulupirira mwadala, mphotho yake ndi kupsya ku moto wa ku Gahena ndipo adzakhala komweko ndipo mkwiyo ndi temberero la Mulungu zili pa iye ndipo chilango chowawa chili kukonzedwa chifukwa cha iye |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِذَا ضَرَبْتُمْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ فَتَبَيَّنُوا وَلَا تَقُولُوا لِمَنْ أَلْقَىٰ إِلَيْكُمُ السَّلَامَ لَسْتَ مُؤْمِنًا تَبْتَغُونَ عَرَضَ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا فَعِندَ اللَّهِ مَغَانِمُ كَثِيرَةٌ ۚ كَذَٰلِكَ كُنتُم مِّن قَبْلُ فَمَنَّ اللَّهُ عَلَيْكُمْ فَتَبَيَّنُوا ۚ إِنَّ اللَّهَ كَانَ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرًا (94) oh inu anthu okhulupirira! onetsetsani kuti pamene mupita kukamenya nkhondo m’njira ya Mulungu, kuti musanene kwa iwo amene akhulupirira kuti ndi osakhulupirira pofuna kuti mupeze katundu wosakhalitsa wa mdziko lino. Kwa Mulungu kuli zinthu zambiri zabwino. Monga mmene iye ali, nanunso mudali wosakhulupirira m’masiku adzana koma tsopano Mulungu wakupatsani chisomo chake pokutsogolerani ku njira yoyenera. Kotero musachite tsankho! Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita |
لَّا يَسْتَوِي الْقَاعِدُونَ مِنَ الْمُؤْمِنِينَ غَيْرُ أُولِي الضَّرَرِ وَالْمُجَاهِدُونَ فِي سَبِيلِ اللَّهِ بِأَمْوَالِهِمْ وَأَنفُسِهِمْ ۚ فَضَّلَ اللَّهُ الْمُجَاهِدِينَ بِأَمْوَالِهِمْ وَأَنفُسِهِمْ عَلَى الْقَاعِدِينَ دَرَجَةً ۚ وَكُلًّا وَعَدَ اللَّهُ الْحُسْنَىٰ ۚ وَفَضَّلَ اللَّهُ الْمُجَاهِدِينَ عَلَى الْقَاعِدِينَ أَجْرًا عَظِيمًا (95) Anthu okhulupirira amene akhala, safanana kupatula iwo amene ali ndi bvuto ndi amene amenyana nkhondo m’njira ya Mulungu ndi chuma chawo ndi iwo eni. Mulungu adawakweza pamwamba iwo amene amamenya nkhondo ndi chuma chawo pamodzi ndi iwo eni kuposa iwo amene akhala kunyumba. Kwa aliyense, Iye walonjeza malipiro abwino koma Mulungu wawapatsa mphotho yaikulu amene amalimbikira ndipo amamenya nkhondo m’njira ya Mulungu kuposa amene amakhala kunyumba |
دَرَجَاتٍ مِّنْهُ وَمَغْفِرَةً وَرَحْمَةً ۚ وَكَانَ اللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا (96) Adzapeza maudindo kuchokera kwa Iye, chikhululukiro ndi chisoni. Mulungu amakhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha |
إِنَّ الَّذِينَ تَوَفَّاهُمُ الْمَلَائِكَةُ ظَالِمِي أَنفُسِهِمْ قَالُوا فِيمَ كُنتُمْ ۖ قَالُوا كُنَّا مُسْتَضْعَفِينَ فِي الْأَرْضِ ۚ قَالُوا أَلَمْ تَكُنْ أَرْضُ اللَّهِ وَاسِعَةً فَتُهَاجِرُوا فِيهَا ۚ فَأُولَٰئِكَ مَأْوَاهُمْ جَهَنَّمُ ۖ وَسَاءَتْ مَصِيرًا (97) Ndithudi! Iwo amene angelo amachotsa moyo wawo pamene ali ochimwa, adzafunsidwa kuti: “Mudali kuchita chiyani?” Iwo adzanena: “Tinali opanda mphamvu ndi oponderezedwa padziko lapansi.” Angelo adzati kwa iwo: “Kodi dziko la Mulungu silinali lotambasuka kuti inu mukadasamuka?” Iwo mudzi wawo ndi Gahena. Malo oipa kwambiri ofikirako |
إِلَّا الْمُسْتَضْعَفِينَ مِنَ الرِّجَالِ وَالنِّسَاءِ وَالْوِلْدَانِ لَا يَسْتَطِيعُونَ حِيلَةً وَلَا يَهْتَدُونَ سَبِيلًا (98) Kupatula anthu ofoka pakati pa amuna, akazi ndi ana amene alibe mphamvu kapena njira zothawira |
فَأُولَٰئِكَ عَسَى اللَّهُ أَن يَعْفُوَ عَنْهُمْ ۚ وَكَانَ اللَّهُ عَفُوًّا غَفُورًا (99) Kwa otere pali chikhulupiriro choti Mulungu adzawakhululukira ndipo Mulungu ndi wachisoni ndi wokhululuka nthawi zonse |
۞ وَمَن يُهَاجِرْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ يَجِدْ فِي الْأَرْضِ مُرَاغَمًا كَثِيرًا وَسَعَةً ۚ وَمَن يَخْرُجْ مِن بَيْتِهِ مُهَاجِرًا إِلَى اللَّهِ وَرَسُولِهِ ثُمَّ يُدْرِكْهُ الْمَوْتُ فَقَدْ وَقَعَ أَجْرُهُ عَلَى اللَّهِ ۗ وَكَانَ اللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا (100) Iye amene asamuka kwawo mu njira ya Mulungu adzapeza padziko lapansi malo ochuluka othawirako ndi katundu wochuluka. Ndipo iye amene asamuka chifukwa cha Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo imfa impeza, ndithu malipiro ake ali ndi Mulungu. Ndipo Mulungu ndi wokhululuka ndi wachisoni chosatha |
وَإِذَا ضَرَبْتُمْ فِي الْأَرْضِ فَلَيْسَ عَلَيْكُمْ جُنَاحٌ أَن تَقْصُرُوا مِنَ الصَّلَاةِ إِنْ خِفْتُمْ أَن يَفْتِنَكُمُ الَّذِينَ كَفَرُوا ۚ إِنَّ الْكَافِرِينَ كَانُوا لَكُمْ عَدُوًّا مُّبِينًا (101) Ndipo pamene inu muyenda padziko lapansi sikulakwa kwa inu kupungula mapemphero ngati muopa kuti anthu osakhulupirira akuvutitsani. Ndithudi anthu osakhulupirira ndi adani anu enieni |
وَإِذَا كُنتَ فِيهِمْ فَأَقَمْتَ لَهُمُ الصَّلَاةَ فَلْتَقُمْ طَائِفَةٌ مِّنْهُم مَّعَكَ وَلْيَأْخُذُوا أَسْلِحَتَهُمْ فَإِذَا سَجَدُوا فَلْيَكُونُوا مِن وَرَائِكُمْ وَلْتَأْتِ طَائِفَةٌ أُخْرَىٰ لَمْ يُصَلُّوا فَلْيُصَلُّوا مَعَكَ وَلْيَأْخُذُوا حِذْرَهُمْ وَأَسْلِحَتَهُمْ ۗ وَدَّ الَّذِينَ كَفَرُوا لَوْ تَغْفُلُونَ عَنْ أَسْلِحَتِكُمْ وَأَمْتِعَتِكُمْ فَيَمِيلُونَ عَلَيْكُم مَّيْلَةً وَاحِدَةً ۚ وَلَا جُنَاحَ عَلَيْكُمْ إِن كَانَ بِكُمْ أَذًى مِّن مَّطَرٍ أَوْ كُنتُم مَّرْضَىٰ أَن تَضَعُوا أَسْلِحَتَكُمْ ۖ وَخُذُوا حِذْرَكُمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ أَعَدَّ لِلْكَافِرِينَ عَذَابًا مُّهِينًا (102) Pamene iwe uli pakati pawo ndipo uli kuwatsogolera pa mapemphero, lola gulu lina la iwo kuti liime pamodzi ndi iwe, atanyamula zida zawo za nkhondo. Akatha kugwetsa nkhope zawo pansi apite kumbuyo kwanu ndipo libwere gulu lina limene silinapemphere kuti lipemphere nawe, ayenera kukhala tcheru ndi kutenga zida zawo za nkhondo. Anthu osakhulupirira amafuna inu mutaiwala zida zanu ndi katundu wanu kuti akukantheni nthawi imodzi, koma palibe cholakwa ngati musiya zida zanu chifukwa cha mavuto ena monga mvula kapena matenda koma khala tcheru. Ndithudi Mulungu wawakonzera anthu wosakhulupirira chilango chochititsa manyazi |
فَإِذَا قَضَيْتُمُ الصَّلَاةَ فَاذْكُرُوا اللَّهَ قِيَامًا وَقُعُودًا وَعَلَىٰ جُنُوبِكُمْ ۚ فَإِذَا اطْمَأْنَنتُمْ فَأَقِيمُوا الصَّلَاةَ ۚ إِنَّ الصَّلَاةَ كَانَتْ عَلَى الْمُؤْمِنِينَ كِتَابًا مَّوْقُوتًا (103) Pamene mumaliza mapemphero, kumbukirani Mulungu pamene muli choimirira, chokhala pansi kapena chogona. Koma pamene muli pabwino, pempherani nthawi zonse. Ndithudi mapemphero ndi udindo umene udaperekedwa kwa anthu okhulupirira kuti azichita pa nthawi zimene zidakhazikitsidwa |
وَلَا تَهِنُوا فِي ابْتِغَاءِ الْقَوْمِ ۖ إِن تَكُونُوا تَأْلَمُونَ فَإِنَّهُمْ يَأْلَمُونَ كَمَا تَأْلَمُونَ ۖ وَتَرْجُونَ مِنَ اللَّهِ مَا لَا يَرْجُونَ ۗ وَكَانَ اللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمًا (104) Ndipo musafoke pofunafuna mdani. Ngati inu mumva kuwawa nawonso, ndithudi, akumva kuwawa monga mmene mukuonera kuwawa inu. Koma inu muli ndi chiyembekezo chochokera kwa Mulungu chimene iwo alibe. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi wanzeru |
إِنَّا أَنزَلْنَا إِلَيْكَ الْكِتَابَ بِالْحَقِّ لِتَحْكُمَ بَيْنَ النَّاسِ بِمَا أَرَاكَ اللَّهُ ۚ وَلَا تَكُن لِّلْخَائِنِينَ خَصِيمًا (105) Ndithudi Ife tavumbulutsa Buku kwa iwe mwachoonadi kuti uweruze pakati pa anthu pogwiritsa ntchito chimene Mulungu wakulangiza iwe. Motero iwe usawapemphere anthu oipa |
وَاسْتَغْفِرِ اللَّهَ ۖ إِنَّ اللَّهَ كَانَ غَفُورًا رَّحِيمًا (106) Ndipo pempha chikhululukiro cha Mulungu, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni |
وَلَا تُجَادِلْ عَنِ الَّذِينَ يَخْتَانُونَ أَنفُسَهُمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ لَا يُحِبُّ مَن كَانَ خَوَّانًا أَثِيمًا (107) Ndipo iwe usawaimire iwo amene amasokeretsa miyoyo yawo. Ndithudi Mulungu sakonda munthu wodzipondereza yekha amene amachita zoipa |
يَسْتَخْفُونَ مِنَ النَّاسِ وَلَا يَسْتَخْفُونَ مِنَ اللَّهِ وَهُوَ مَعَهُمْ إِذْ يُبَيِّتُونَ مَا لَا يَرْضَىٰ مِنَ الْقَوْلِ ۚ وَكَانَ اللَّهُ بِمَا يَعْمَلُونَ مُحِيطًا (108) Iwo akhoza kudzibisa kwa anthu koma sangathe kudzibisa kwa Mulungu chifukwa Iye ali pamodzi ndi iwo pamene akonza chiwembu nthawi ya usiku ndi mawu amene samukondweretsa. Ndipo Mulungu amadziwa zimene iwo amachita |
هَا أَنتُمْ هَٰؤُلَاءِ جَادَلْتُمْ عَنْهُمْ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا فَمَن يُجَادِلُ اللَّهَ عَنْهُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ أَم مَّن يَكُونُ عَلَيْهِمْ وَكِيلًا (109) Lo! Inu ndi amene mudawaimirira mu umoyo wa padzikolapansi.Nangakodindaniameneadzawadandaulire, kwa Mulungu pa tsiku la kuuka kwa akufa kapena ndani amene adzakhala mtetezi wawo |
وَمَن يَعْمَلْ سُوءًا أَوْ يَظْلِمْ نَفْسَهُ ثُمَّ يَسْتَغْفِرِ اللَّهَ يَجِدِ اللَّهَ غَفُورًا رَّحِيمًا (110) Ndipo iye amene achita choipa kapena achimwira mzimu wake koma pambuyo pake apempha chikhululukiro cha Mulungu, adzamupeza Mulungu ali Wokhululuka ndi Wachisoni |
وَمَن يَكْسِبْ إِثْمًا فَإِنَّمَا يَكْسِبُهُ عَلَىٰ نَفْسِهِ ۚ وَكَانَ اللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمًا (111) Ndipo aliyense amene achita zoipa akudzilakwira yekha. Ndipo Mulungu ndi Waluntha ndi Wanzeru |
وَمَن يَكْسِبْ خَطِيئَةً أَوْ إِثْمًا ثُمَّ يَرْمِ بِهِ بَرِيئًا فَقَدِ احْتَمَلَ بُهْتَانًا وَإِثْمًا مُّبِينًا (112) Ndipo aliyense amene achita zoipa kapena tchimo koma anamizira munthu wina wopanda chifukwa, ndithudi, iye wadzisenzetsa bodza ndi tchimo limene lili loonekera |
وَلَوْلَا فَضْلُ اللَّهِ عَلَيْكَ وَرَحْمَتُهُ لَهَمَّت طَّائِفَةٌ مِّنْهُمْ أَن يُضِلُّوكَ وَمَا يُضِلُّونَ إِلَّا أَنفُسَهُمْ ۖ وَمَا يَضُرُّونَكَ مِن شَيْءٍ ۚ وَأَنزَلَ اللَّهُ عَلَيْكَ الْكِتَابَ وَالْحِكْمَةَ وَعَلَّمَكَ مَا لَمْ تَكُن تَعْلَمُ ۚ وَكَانَ فَضْلُ اللَّهِ عَلَيْكَ عَظِيمًا (113) Koma pakadapanda Chisomo ndi Chisoni cha Mulungu pa iwe gulu lina la iwo likadafuna kuti likusokeretse koma iwo sangasokeretse wina aliyense koma iwo okha, ndipo iwo sangakupweteke iwe ayi. Mulungu wavumbulutsa kwa iwe Buku la luntha ndi kukuphunzitsa iwe zinthu zimene siunali kuzidziwa. Ndipo ubwino wa Mulungu pa iwe ndi waukulu zedi |
۞ لَّا خَيْرَ فِي كَثِيرٍ مِّن نَّجْوَاهُمْ إِلَّا مَنْ أَمَرَ بِصَدَقَةٍ أَوْ مَعْرُوفٍ أَوْ إِصْلَاحٍ بَيْنَ النَّاسِ ۚ وَمَن يَفْعَلْ ذَٰلِكَ ابْتِغَاءَ مَرْضَاتِ اللَّهِ فَسَوْفَ نُؤْتِيهِ أَجْرًا عَظِيمًا (114) Mulibe zabwino zambiri muzokambirana zawo za mseri kupatula mwa iye amene amalangiza za kupereka chaulere, kuonetsa chifundo ndi chiyanjanitso pakati pa anthu, ndipo iye amene amachita izi ndi cholinga chokondweretsa Mulungu, Ife tidzampatsa mphotho yaikulu |
وَمَن يُشَاقِقِ الرَّسُولَ مِن بَعْدِ مَا تَبَيَّنَ لَهُ الْهُدَىٰ وَيَتَّبِعْ غَيْرَ سَبِيلِ الْمُؤْمِنِينَ نُوَلِّهِ مَا تَوَلَّىٰ وَنُصْلِهِ جَهَنَّمَ ۖ وَسَاءَتْ مَصِيرًا (115) Ndipo aliyense amene amatsutsa ndi kutsutsana ndi Mtumwi, langizo lathu litaonetsedwa kwa iye ndipo atsatira njira imene siili ya anthu okhulupirira, Ife tidzamusunga mnjira imene wasankha ndipo tidzamuotcha iye ku Moto, malo onyansa kwambiri |
إِنَّ اللَّهَ لَا يَغْفِرُ أَن يُشْرَكَ بِهِ وَيَغْفِرُ مَا دُونَ ذَٰلِكَ لِمَن يَشَاءُ ۚ وَمَن يُشْرِكْ بِاللَّهِ فَقَدْ ضَلَّ ضَلَالًا بَعِيدًا (116) Ndithudi! Mulungu sadzakhululukira munthu wopembedza mafano. Iye adzakhululukira wina aliyense amene wamufuna pa machimo ena onse ndipo aliyense amene amalambira milungu ina osati Mulungu, iye wasochera kwambiri kuchokera ku choonadi |
إِن يَدْعُونَ مِن دُونِهِ إِلَّا إِنَاثًا وَإِن يَدْعُونَ إِلَّا شَيْطَانًا مَّرِيدًا (117) Iwo sapembedza china koma milungu ya ikazi m’malo mwa Iye ndipo iwo sapembedza wina koma Satana wogalukira |
لَّعَنَهُ اللَّهُ ۘ وَقَالَ لَأَتَّخِذَنَّ مِنْ عِبَادِكَ نَصِيبًا مَّفْرُوضًا (118) Mulungu anamutemberera iye ndipo iye adati: “Ine ndidzalanda gawo lina lokhazikika la akapolo ako.” |
وَلَأُضِلَّنَّهُمْ وَلَأُمَنِّيَنَّهُمْ وَلَآمُرَنَّهُمْ فَلَيُبَتِّكُنَّ آذَانَ الْأَنْعَامِ وَلَآمُرَنَّهُمْ فَلَيُغَيِّرُنَّ خَلْقَ اللَّهِ ۚ وَمَن يَتَّخِذِ الشَّيْطَانَ وَلِيًّا مِّن دُونِ اللَّهِ فَقَدْ خَسِرَ خُسْرَانًا مُّبِينًا (119) “Ndithudi ine ndidzawasocheretsa ndipo, ndithudi, ndidzaukitsa zilakolako zawo zopanda pake ndipo, ndithudi, ndidzawalamula kuboola makutu a ng’ombe ndipo, ndithudi, ndidzawalamula kusintha zinthu zimene zinalengedwa ndi Mulungu.” Ndithudi aliyense amene asankha Satana m’malo mwa Mulungu ngati mtetezi wake, iye ndi wotayika kodziwikiratu |
يَعِدُهُمْ وَيُمَنِّيهِمْ ۖ وَمَا يَعِدُهُمُ الشَّيْطَانُ إِلَّا غُرُورًا (120) Iye akuwalonjeza ndi kuwakhulupiritsa zinthu zopanda pake ndipo malonjezo a Satana si ena koma chinyengo |
أُولَٰئِكَ مَأْوَاهُمْ جَهَنَّمُ وَلَا يَجِدُونَ عَنْهَا مَحِيصًا (121) Malo a anthu otere ndi Gahena ndipo sadzapeza njira yothawira kumeneko |
وَالَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ سَنُدْخِلُهُمْ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا أَبَدًا ۖ وَعْدَ اللَّهِ حَقًّا ۚ وَمَنْ أَصْدَقُ مِنَ اللَّهِ قِيلًا (122) Koma iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, tidzawalowetsa ku Minda yothiriridwa ndi mitsinje ya madzi yoyenda pansi pake ndipo kumeneko adzakhalako mpaka kalekale. Lonjezo la Mulungu ndi loona. Kodi ndani amene anganene zoona kuposa Mulungu |
لَّيْسَ بِأَمَانِيِّكُمْ وَلَا أَمَانِيِّ أَهْلِ الْكِتَابِ ۗ مَن يَعْمَلْ سُوءًا يُجْزَ بِهِ وَلَا يَجِدْ لَهُ مِن دُونِ اللَّهِ وَلِيًّا وَلَا نَصِيرًا (123) Sikudzakhala molingana ndi zilakolako zanu kapena za anthu a m’Buku. Iye amene achita zoipa adzalandira zoipa, ndipo sadzapeza wina kukhala omuteteza kapena kumuthandiza iye pambali pa Mulungu |
وَمَن يَعْمَلْ مِنَ الصَّالِحَاتِ مِن ذَكَرٍ أَوْ أُنثَىٰ وَهُوَ مُؤْمِنٌ فَأُولَٰئِكَ يَدْخُلُونَ الْجَنَّةَ وَلَا يُظْلَمُونَ نَقِيرًا (124) Ndipo aliyense amene amachita ntchito zabwino, mwamuna kapena mkazi, ndipo ndi wokhulupirira, ameneyo ndiye adzalowa ku Paradiso ndipo sadzaponderezedwa ngakhale pang’ono |
وَمَنْ أَحْسَنُ دِينًا مِّمَّنْ أَسْلَمَ وَجْهَهُ لِلَّهِ وَهُوَ مُحْسِنٌ وَاتَّبَعَ مِلَّةَ إِبْرَاهِيمَ حَنِيفًا ۗ وَاتَّخَذَ اللَّهُ إِبْرَاهِيمَ خَلِيلًا (125) Kodi ndani ali ndi chipembedzo chabwino kuposa munthu amene amadzipereka kwathunthu kwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino ndipo amatsatira chikhulupiriro cha Abrahamu wangwiro? Ndipo Mulungu anamusankha Abrahamu kukhala bwenzi lake la pamtima |
وَلِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۚ وَكَانَ اللَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ مُّحِيطًا (126) Mwini wa chilichonse chimene chili mu mlengalenga ndi padziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse |
وَيَسْتَفْتُونَكَ فِي النِّسَاءِ ۖ قُلِ اللَّهُ يُفْتِيكُمْ فِيهِنَّ وَمَا يُتْلَىٰ عَلَيْكُمْ فِي الْكِتَابِ فِي يَتَامَى النِّسَاءِ اللَّاتِي لَا تُؤْتُونَهُنَّ مَا كُتِبَ لَهُنَّ وَتَرْغَبُونَ أَن تَنكِحُوهُنَّ وَالْمُسْتَضْعَفِينَ مِنَ الْوِلْدَانِ وَأَن تَقُومُوا لِلْيَتَامَىٰ بِالْقِسْطِ ۚ وَمَا تَفْعَلُوا مِنْ خَيْرٍ فَإِنَّ اللَّهَ كَانَ بِهِ عَلِيمًا (127) Iwo amakufunsa malamulo okhudza akazi. Nena: “Mulungu ali kukuuzani za iwo ndi zomwe zikuwerengedwa m’buku zokhudza ana akazi a masiye amene simukuwapatsa zimene zidalamulidwa kwa iwo komabe inu mufuna kuwakwatira ndi ana opanda mphamvu ndi oponderezedwa ndipo kuti muonetse chilungamo kwa ana a masiye. Ndipo zilizonse zabwino zimene muchita, Mulungu amazidziwa.” |
وَإِنِ امْرَأَةٌ خَافَتْ مِن بَعْلِهَا نُشُوزًا أَوْ إِعْرَاضًا فَلَا جُنَاحَ عَلَيْهِمَا أَن يُصْلِحَا بَيْنَهُمَا صُلْحًا ۚ وَالصُّلْحُ خَيْرٌ ۗ وَأُحْضِرَتِ الْأَنفُسُ الشُّحَّ ۚ وَإِن تُحْسِنُوا وَتَتَّقُوا فَإِنَّ اللَّهَ كَانَ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرًا (128) Ndipo ngati mkazi aopa kuzunzidwa kapena kusiyidwa ndi mwamuna wake, sichidzakhala chinthu cholakwa kwa iwo awiriwo ngati onse afuna kugwirizana pakati pawo chifukwa mgwirizano ndi wabwino. Ndipo umunthu umalamulidwa ndi umbombo. Koma ngati inu muchita chinthu chabwino ndi kulewa zoipa, ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene mukuchita |
وَلَن تَسْتَطِيعُوا أَن تَعْدِلُوا بَيْنَ النِّسَاءِ وَلَوْ حَرَصْتُمْ ۖ فَلَا تَمِيلُوا كُلَّ الْمَيْلِ فَتَذَرُوهَا كَالْمُعَلَّقَةِ ۚ وَإِن تُصْلِحُوا وَتَتَّقُوا فَإِنَّ اللَّهَ كَانَ غَفُورًا رَّحِيمًا (129) Inu simudzatha kuchita chilungamo pakati pa akazi anu ngakhale mutafuna kutero. Motero musakondere mbali imodzi ndikumusiya winayo osadziwa chimene chili kuchitika. Ndipo ngati inu muchita chilungamo ndi kuchita chili chonse chabwino ndi kuopa Mulungu, ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha |
وَإِن يَتَفَرَّقَا يُغْنِ اللَّهُ كُلًّا مِّن سَعَتِهِ ۚ وَكَانَ اللَّهُ وَاسِعًا حَكِيمًا (130) Koma ngati iwo asiyana, Mulungu adzapereka zochuluka kwa aliyense wa iwo kuchokera ku zinthu zake zambiri. Ndipo Mulungu ndi wopereka mowolowa manja kwa zolengedwa zake ndipo ndi Wanzeru |
وَلِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۗ وَلَقَدْ وَصَّيْنَا الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ مِن قَبْلِكُمْ وَإِيَّاكُمْ أَنِ اتَّقُوا اللَّهَ ۚ وَإِن تَكْفُرُوا فَإِنَّ لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۚ وَكَانَ اللَّهُ غَنِيًّا حَمِيدًا (131) Ndipo mwini wake wa zonse za m’mlengalenga ndi za pa dziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo, Ife tidawalangiza iwo amene analandira Buku inu musadadze ndiponso ndi inu nomwe kuti muziopa Mulungu. Koma ngati mukana, ndithudi, Mulungu ndiye mwini wa zonse zimene zili m’mlengalenga ndi padziko lapansi. Mulungu sasowa chilichonse ndipo ndi otamandidwa |
وَلِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۚ وَكَفَىٰ بِاللَّهِ وَكِيلًا (132) Ndipo mwini wake wa zonse zimene zili mlengalenga ndi padziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo Mulungu ndi wokwanira kukhala Mtetezi wanu |
إِن يَشَأْ يُذْهِبْكُمْ أَيُّهَا النَّاسُ وَيَأْتِ بِآخَرِينَ ۚ وَكَانَ اللَّهُ عَلَىٰ ذَٰلِكَ قَدِيرًا (133) Ngati Iye atafuna, akhoza kukuchotsani inu ndi kubweretsa ena. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu yotero |
مَّن كَانَ يُرِيدُ ثَوَابَ الدُّنْيَا فَعِندَ اللَّهِ ثَوَابُ الدُّنْيَا وَالْآخِرَةِ ۚ وَكَانَ اللَّهُ سَمِيعًا بَصِيرًا (134) Aliyense amene afuna dipo la moyo uno ndi Mulungu yekha amene amasunga dipo la m’moyo uno ndi umoyo umene uli nkudza. Ndipo Mulungu amamva zonse ndipo amaona zonse |
۞ يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا كُونُوا قَوَّامِينَ بِالْقِسْطِ شُهَدَاءَ لِلَّهِ وَلَوْ عَلَىٰ أَنفُسِكُمْ أَوِ الْوَالِدَيْنِ وَالْأَقْرَبِينَ ۚ إِن يَكُنْ غَنِيًّا أَوْ فَقِيرًا فَاللَّهُ أَوْلَىٰ بِهِمَا ۖ فَلَا تَتَّبِعُوا الْهَوَىٰ أَن تَعْدِلُوا ۚ وَإِن تَلْوُوا أَوْ تُعْرِضُوا فَإِنَّ اللَّهَ كَانَ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرًا (135) oh inu anthu okhulupirira! Khalani anthu ochita chilungamo ngati mboni za Mulungu ngakhale kuti umboniwo ndi wosakomera inu kapena makolo anu kapena abale anu, kaya iwo ndi wolemera kapena wosauka. Mulungu ndiye Mtetezi wa iwo onse. Motero musatsatire zilakolako zanu ndi kusiya kuchita chilungamo. Ndipo ngati mukapereka umboni wosayenera kapena kukana kupereka, ndithudi Mulungu ali kudziwa ntchito zanu zimene muchita |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا آمِنُوا بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ وَالْكِتَابِ الَّذِي نَزَّلَ عَلَىٰ رَسُولِهِ وَالْكِتَابِ الَّذِي أَنزَلَ مِن قَبْلُ ۚ وَمَن يَكْفُرْ بِاللَّهِ وَمَلَائِكَتِهِ وَكُتُبِهِ وَرُسُلِهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ فَقَدْ ضَلَّ ضَلَالًا بَعِيدًا (136) oh inu anthu okhulupirira! Khulupirirani mwa Mulungundi Mtumwiwakendi Bukulimenewavumbulutsa kwa Mtumwi wake ndi Buku limene Iye adavumbulutsa kale ndipo aliyense amene sakhulupirira Mulungu, Angelo ake, Mabuku ake, Atumwi ake ndi tsiku lomaliza ndithudi wasokera |
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا ثُمَّ كَفَرُوا ثُمَّ آمَنُوا ثُمَّ كَفَرُوا ثُمَّ ازْدَادُوا كُفْرًا لَّمْ يَكُنِ اللَّهُ لِيَغْفِرَ لَهُمْ وَلَا لِيَهْدِيَهُمْ سَبِيلًا (137) Ndithudi iwo amene akhulupirira ndipo kenaka akana ndipo akhulupirira ndipo akananso ndipo aonjezera kusakhulupirira, Mulungu sadzawakhululukira kapena kuwatsogolera kunjira ya choonadi |
بَشِّرِ الْمُنَافِقِينَ بِأَنَّ لَهُمْ عَذَابًا أَلِيمًا (138) Achenjezeni anthu achinyengo kuti chilango chowawa chili kuwadikira |
الَّذِينَ يَتَّخِذُونَ الْكَافِرِينَ أَوْلِيَاءَ مِن دُونِ الْمُؤْمِنِينَ ۚ أَيَبْتَغُونَ عِندَهُمُ الْعِزَّةَ فَإِنَّ الْعِزَّةَ لِلَّهِ جَمِيعًا (139) Iwo amene amasankha anthu osakhulupirira kukhala atetezi awo m’malo mwa anthu okhulupirira, kodi iwo ali kufuna ulemerero kuchokera kwa iwo? Ndithudi ulemerero, mphamvu ndi kuyamikidwa, Mwini wake ndi Mulungu |
وَقَدْ نَزَّلَ عَلَيْكُمْ فِي الْكِتَابِ أَنْ إِذَا سَمِعْتُمْ آيَاتِ اللَّهِ يُكْفَرُ بِهَا وَيُسْتَهْزَأُ بِهَا فَلَا تَقْعُدُوا مَعَهُمْ حَتَّىٰ يَخُوضُوا فِي حَدِيثٍ غَيْرِهِ ۚ إِنَّكُمْ إِذًا مِّثْلُهُمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ جَامِعُ الْمُنَافِقِينَ وَالْكَافِرِينَ فِي جَهَنَّمَ جَمِيعًا (140) Ndipo zavumbulutsidwa kale kwa inu m’Buku kuti pamene inu mukumva chivumbulutso cha Mulungu chili kukanidwa kapena kunyozedwa, inu musakhale pa malo amenewo mpaka pamene ayamba kukamba nkhani zina chifukwa mukakhala nawo, mudzakhala ngati iwo. Ndithudi Mulungu adzasonkhanitsa anthu a chinyengo ndi anthu osakhulupirira ku Gahena |
الَّذِينَ يَتَرَبَّصُونَ بِكُمْ فَإِن كَانَ لَكُمْ فَتْحٌ مِّنَ اللَّهِ قَالُوا أَلَمْ نَكُن مَّعَكُمْ وَإِن كَانَ لِلْكَافِرِينَ نَصِيبٌ قَالُوا أَلَمْ نَسْتَحْوِذْ عَلَيْكُمْ وَنَمْنَعْكُم مِّنَ الْمُؤْمِنِينَ ۚ فَاللَّهُ يَحْكُمُ بَيْنَكُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۗ وَلَن يَجْعَلَ اللَّهُ لِلْكَافِرِينَ عَلَى الْمُؤْمِنِينَ سَبِيلًا (141) Iwo amene amayembekezera ndi kuyang’ana; ndipo ngati Mulungu akupambanitsani, iwo amati: “Kodi ife sitinali kumbali yanu?” Ndipo ngati anthu osakhulupirira apambana, iwo amati kwa iwo: “Kodi ife sitidali ndi mphamvu zoposa inu ndiponso kodi ife sitidakutetezeni kwa anthu okhulupirira?” Mulungu adzaweruza, pakati panu, pa tsiku lakuuka kwa akufa. Ndipo Mulungu sadzawapatsa anthu osakhulupirira njira yoti apambane anthu okhulupirira |
إِنَّ الْمُنَافِقِينَ يُخَادِعُونَ اللَّهَ وَهُوَ خَادِعُهُمْ وَإِذَا قَامُوا إِلَى الصَّلَاةِ قَامُوا كُسَالَىٰ يُرَاءُونَ النَّاسَ وَلَا يَذْكُرُونَ اللَّهَ إِلَّا قَلِيلًا (142) Ndithudi anthu a chinyengo afuna kunyenga Mulungu koma ndi Mulungu amene amawanyenga iwo ndipo pamene iwo amaima pamapemphero, amaimirira mwaulesi kuti anthu awaone ndipo sakumbukira Mulungu ngakhale mwapang’ono |
مُّذَبْذَبِينَ بَيْنَ ذَٰلِكَ لَا إِلَىٰ هَٰؤُلَاءِ وَلَا إِلَىٰ هَٰؤُلَاءِ ۚ وَمَن يُضْلِلِ اللَّهُ فَلَن تَجِدَ لَهُ سَبِيلًا (143) Iwo ali kupita uku ndi uko, ndipo sali m’gulu ili ndipo aliyense amene Mulungu wamusocheretsa simungampezere iye njira |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَتَّخِذُوا الْكَافِرِينَ أَوْلِيَاءَ مِن دُونِ الْمُؤْمِنِينَ ۚ أَتُرِيدُونَ أَن تَجْعَلُوا لِلَّهِ عَلَيْكُمْ سُلْطَانًا مُّبِينًا (144) oh inu anthu okhulupirira! Musasankhe anthu osakhulupirira kuti akhale abwenzi anu mmalo mwa anthu okhulupirira. Kodi mukufuna kuika umboni woonekera kwa Mulungu wokutsutsani inu |
إِنَّ الْمُنَافِقِينَ فِي الدَّرْكِ الْأَسْفَلِ مِنَ النَّارِ وَلَن تَجِدَ لَهُمْ نَصِيرًا (145) Ndithudi anthu achinyengo adzaponyedwa ku malo apansipansi a ku Moto. Inu simudzawapezera wowathandiza |
إِلَّا الَّذِينَ تَابُوا وَأَصْلَحُوا وَاعْتَصَمُوا بِاللَّهِ وَأَخْلَصُوا دِينَهُمْ لِلَّهِ فَأُولَٰئِكَ مَعَ الْمُؤْمِنِينَ ۖ وَسَوْفَ يُؤْتِ اللَّهُ الْمُؤْمِنِينَ أَجْرًا عَظِيمًا (146) Kupatula iwo amene alapa zoipa zawo ndi kuchita ntchito zabwino ndipo ayeretsa chipembedzo chawo. Iwo adzakhala pamodzi ndi anthu okhulupirira. Ndipo Mulungu adzawapatsa anthu okhulupirira mphotho yaikulu |
مَّا يَفْعَلُ اللَّهُ بِعَذَابِكُمْ إِن شَكَرْتُمْ وَآمَنتُمْ ۚ وَكَانَ اللَّهُ شَاكِرًا عَلِيمًا (147) Kodi Mulungu angakulangeni bwanji inu ngati muthokoza ndi kukhulupirira mwa Iye? Ndithudi Mulungu amayamika, ndipo ndi Wodziwa zonse |
۞ لَّا يُحِبُّ اللَّهُ الْجَهْرَ بِالسُّوءِ مِنَ الْقَوْلِ إِلَّا مَن ظُلِمَ ۚ وَكَانَ اللَّهُ سَمِيعًا عَلِيمًا (148) Mulungu sakondwera ndi kuyankhula mawu oipa pagulu kupatula kuchokera kwa amene waponderezedwa. Ndipo Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa zonse |
إِن تُبْدُوا خَيْرًا أَوْ تُخْفُوهُ أَوْ تَعْفُوا عَن سُوءٍ فَإِنَّ اللَّهَ كَانَ عَفُوًّا قَدِيرًا (149) Kaya inu muonetsera pochita zabwino kapena mubisa, kapena mukhululukira zoipa, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira ndi wamphamvu zonse |
إِنَّ الَّذِينَ يَكْفُرُونَ بِاللَّهِ وَرُسُلِهِ وَيُرِيدُونَ أَن يُفَرِّقُوا بَيْنَ اللَّهِ وَرُسُلِهِ وَيَقُولُونَ نُؤْمِنُ بِبَعْضٍ وَنَكْفُرُ بِبَعْضٍ وَيُرِيدُونَ أَن يَتَّخِذُوا بَيْنَ ذَٰلِكَ سَبِيلًا (150) Ndithudi iwo amene sakhulupirira Mulungu ndi Atumwi ake ndipo afuna kusiyanitsa pakati pa Mulungu ndi Atumwi ake ponena kuti: “Ife timakhulupirira mwa ena ndipo sitikhulupirira ena.” Ndipo amafuna kusankha njira yapakati ndi pakati |
أُولَٰئِكَ هُمُ الْكَافِرُونَ حَقًّا ۚ وَأَعْتَدْنَا لِلْكَافِرِينَ عَذَابًا مُّهِينًا (151) Amenewa ndithudi ndi osakhulupirira enieni. Ndipo Ife tawakonzera anthu osakhulupirira chilango chochititsa manyazi |
وَالَّذِينَ آمَنُوا بِاللَّهِ وَرُسُلِهِ وَلَمْ يُفَرِّقُوا بَيْنَ أَحَدٍ مِّنْهُمْ أُولَٰئِكَ سَوْفَ يُؤْتِيهِمْ أُجُورَهُمْ ۗ وَكَانَ اللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا (152) Ndipo iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Atumwi ake ndipo sasiyanitsa pakati pa aliyense wa iwo, Ife tidzawapatsa mphotho zawo ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi wa chisoni chosatha |
يَسْأَلُكَ أَهْلُ الْكِتَابِ أَن تُنَزِّلَ عَلَيْهِمْ كِتَابًا مِّنَ السَّمَاءِ ۚ فَقَدْ سَأَلُوا مُوسَىٰ أَكْبَرَ مِن ذَٰلِكَ فَقَالُوا أَرِنَا اللَّهَ جَهْرَةً فَأَخَذَتْهُمُ الصَّاعِقَةُ بِظُلْمِهِمْ ۚ ثُمَّ اتَّخَذُوا الْعِجْلَ مِن بَعْدِ مَا جَاءَتْهُمُ الْبَيِّنَاتُ فَعَفَوْنَا عَن ذَٰلِكَ ۚ وَآتَيْنَا مُوسَىٰ سُلْطَانًا مُّبِينًا (153) Anthu otsatira a m’Buku akukufunsa iwe kuti uwatsitsire buku kuchokera kumwamba. Ndithudi iwo adafunsa Mose zazikulu kuposa zimenezi pamene iwo adati: “Tionetse Mulungu poyera.” Koma iwo anakanthidwa ndi mphenzi chifukwa cha uchimo wawo. Ndipo iwo adapembedza mwana wa ng’ombe ngakhale analandira zizindikiro zathu. Komabe Ife tidawakhululukira zimenezo. Ndipo tidampatsa Mose mphamvu zooneka |
وَرَفَعْنَا فَوْقَهُمُ الطُّورَ بِمِيثَاقِهِمْ وَقُلْنَا لَهُمُ ادْخُلُوا الْبَابَ سُجَّدًا وَقُلْنَا لَهُمْ لَا تَعْدُوا فِي السَّبْتِ وَأَخَذْنَا مِنْهُم مِّيثَاقًا غَلِيظًا (154) Pokwaniritsa lonjezo, Ife tidakweza pamwamba pawo phiri, ndipo tidati kwa iwo: “Lowani pa chipata mogwetsa nkhope ndi modzichepetsa.” Ndipo Ife tidawalamula kuti: “Musaswe malamulo a tsiku la Sabata.” Ndipo Ife tidatenga lonjezo lokhazikika kuchokera kwa iwo |
فَبِمَا نَقْضِهِم مِّيثَاقَهُمْ وَكُفْرِهِم بِآيَاتِ اللَّهِ وَقَتْلِهِمُ الْأَنبِيَاءَ بِغَيْرِ حَقٍّ وَقَوْلِهِمْ قُلُوبُنَا غُلْفٌ ۚ بَلْ طَبَعَ اللَّهُ عَلَيْهَا بِكُفْرِهِمْ فَلَا يُؤْمِنُونَ إِلَّا قَلِيلًا (155) Chifukwa chakuphwanya pangano lawo ndi kukana zizindikiro za Mulungu ndi kupha Atumwi popanda chilungamo ndi kulankhula kwawo koti: Mitima yathu ndi yokutidwa. Iyayi, Mulungu wamata mitima yawo chifukwa chakusakhulupirira kwawo. Ndipo iwo sakhulupirira kwenikweni koma pang’ono |
وَبِكُفْرِهِمْ وَقَوْلِهِمْ عَلَىٰ مَرْيَمَ بُهْتَانًا عَظِيمًا (156) Ndi chifukwa cha kusakhulupirira kwawo ndi kulankhula zoipa za Maria, tchimo lalikulu |
وَقَوْلِهِمْ إِنَّا قَتَلْنَا الْمَسِيحَ عِيسَى ابْنَ مَرْيَمَ رَسُولَ اللَّهِ وَمَا قَتَلُوهُ وَمَا صَلَبُوهُ وَلَٰكِن شُبِّهَ لَهُمْ ۚ وَإِنَّ الَّذِينَ اخْتَلَفُوا فِيهِ لَفِي شَكٍّ مِّنْهُ ۚ مَا لَهُم بِهِ مِنْ عِلْمٍ إِلَّا اتِّبَاعَ الظَّنِّ ۚ وَمَا قَتَلُوهُ يَقِينًا (157) Ndikulankhula kwawo koti: “Ife tidamupha Messiya, Yesu mwana wamwamuna wa Maria, Mthenga wa Mulungu,” koma iwo sadamuphe ayi ndipo sadampachike koma maonekedwe a Yesu anaikidwa pa munthu wina ndipo iwo amene amatsutsa za izo ndi okaika. Iwo sadziwa chili chonse, koma akutsatira nkhani za m’maluwa. Ndithudi iwo sadamuphe ayi |
بَل رَّفَعَهُ اللَّهُ إِلَيْهِ ۚ وَكَانَ اللَّهُ عَزِيزًا حَكِيمًا (158) Koma Mulungu adamukweza kudza kwa Iye. Ndipo Mulungu ndi wa mphamvu ndi Wanzeru |
وَإِن مِّنْ أَهْلِ الْكِتَابِ إِلَّا لَيُؤْمِنَنَّ بِهِ قَبْلَ مَوْتِهِ ۖ وَيَوْمَ الْقِيَامَةِ يَكُونُ عَلَيْهِمْ شَهِيدًا (159) Ndipo palibe mmodzi wa anthu a m’Buku amene angakhulupirire mwa iye, asadafe. Ndipo patsiku louka kwa akufa, iye adzakhala mboni yowatsutsa iwo |
فَبِظُلْمٍ مِّنَ الَّذِينَ هَادُوا حَرَّمْنَا عَلَيْهِمْ طَيِّبَاتٍ أُحِلَّتْ لَهُمْ وَبِصَدِّهِمْ عَن سَبِيلِ اللَّهِ كَثِيرًا (160) Chifukwa chakulakwa kwa Ayuda, Ife tidawaletsa chakudya china chabwino chimene chidali chololedwa kwa iwo ndi chifukwa chotsekereza anthu ambiri mnjira ya Mulungu |
وَأَخْذِهِمُ الرِّبَا وَقَدْ نُهُوا عَنْهُ وَأَكْلِهِمْ أَمْوَالَ النَّاسِ بِالْبَاطِلِ ۚ وَأَعْتَدْنَا لِلْكَافِرِينَ مِنْهُمْ عَذَابًا أَلِيمًا (161) Ndi kulandira kwawo kwa katapira pamene iwo ataletsedwa kutero, ndi kudya kwawo kwa chuma cha anthu mwachinyengo. Ndipo Ife takonza chilango chowawa cha anthu osakhulupirira amene ali pakati pawo |
لَّٰكِنِ الرَّاسِخُونَ فِي الْعِلْمِ مِنْهُمْ وَالْمُؤْمِنُونَ يُؤْمِنُونَ بِمَا أُنزِلَ إِلَيْكَ وَمَا أُنزِلَ مِن قَبْلِكَ ۚ وَالْمُقِيمِينَ الصَّلَاةَ ۚ وَالْمُؤْتُونَ الزَّكَاةَ وَالْمُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ أُولَٰئِكَ سَنُؤْتِيهِمْ أَجْرًا عَظِيمًا (162) Koma iwo ozindikira kwambiri amene ali pakati pawo ndi okhulupirira amene amakhulupirira mu zimene zavumbulutsidwa kwa iwe ndi zimene zidavumbulitsidwa iwe usanadze, ndipo amapemphera nthawi zonse ndikupereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo ali ndi chikhulupiriro mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza, awa ndiwo amene Ife tidzawapatsa mphotho yaikulu |
۞ إِنَّا أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ كَمَا أَوْحَيْنَا إِلَىٰ نُوحٍ وَالنَّبِيِّينَ مِن بَعْدِهِ ۚ وَأَوْحَيْنَا إِلَىٰ إِبْرَاهِيمَ وَإِسْمَاعِيلَ وَإِسْحَاقَ وَيَعْقُوبَ وَالْأَسْبَاطِ وَعِيسَىٰ وَأَيُّوبَ وَيُونُسَ وَهَارُونَ وَسُلَيْمَانَ ۚ وَآتَيْنَا دَاوُودَ زَبُورًا (163) Ife tavumbulutsa kwa iwe monga momwe tidavumbulutsira kwa Nowa ndi kwa Atumwi ena amene anadza pambuyo pa iye. Ndipo tidavumbulutsa kwa Abrahamu, Ishimayeli, Isake, Yakobo ndi a mitundu, Yesu, Yobu, Yona, Aroni ndi Solomoni ndipo Davide tidamupatsa Buku la Masalimo |
وَرُسُلًا قَدْ قَصَصْنَاهُمْ عَلَيْكَ مِن قَبْلُ وَرُسُلًا لَّمْ نَقْصُصْهُمْ عَلَيْكَ ۚ وَكَلَّمَ اللَّهُ مُوسَىٰ تَكْلِيمًا (164) Ndi Atumwi amene Ife takuuza kale mbiri yawo ndi Atumwi amene sitidakuuze ayi, ndipo ndi Mose Mulungu adalankhula naye mwachindunji |
رُّسُلًا مُّبَشِّرِينَ وَمُنذِرِينَ لِئَلَّا يَكُونَ لِلنَّاسِ عَلَى اللَّهِ حُجَّةٌ بَعْدَ الرُّسُلِ ۚ وَكَانَ اللَّهُ عَزِيزًا حَكِيمًا (165) Atumwi ngati obweretsa nkhani zabwino kwa mitundu ya anthu ndipo chenjezo kuti iwo asadzakhale ndi chodandaula kwa Mulungu pambuyo pa Atumwi. Ndipo Mulungu ndi Wamphamvu nd Wanzeru |
لَّٰكِنِ اللَّهُ يَشْهَدُ بِمَا أَنزَلَ إِلَيْكَ ۖ أَنزَلَهُ بِعِلْمِهِ ۖ وَالْمَلَائِكَةُ يَشْهَدُونَ ۚ وَكَفَىٰ بِاللَّهِ شَهِيدًا (166) Koma Mulungu achitira umboni pa zimene wavumbulutsakwaiwe, Iyewalitumizandinzeruzakendipo angelo achitira umboni. Ndipo Mulungu ndi wokwana kukhalamboni |
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا وَصَدُّوا عَن سَبِيلِ اللَّهِ قَدْ ضَلُّوا ضَلَالًا بَعِيدًا (167) Ndithudiiwoamenesakhulupirirandipo amaletsa ena kutsatira njira ya Mulungu, ndithudi, asochera kwenikweni |
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا وَظَلَمُوا لَمْ يَكُنِ اللَّهُ لِيَغْفِرَ لَهُمْ وَلَا لِيَهْدِيَهُمْ طَرِيقًا (168) Ndithudi iwo amene sakhulupirira ndipo adachita zosalungama, Mulungu sazawakhululukira ndipo sadzawatsogolera kunjira ina |
إِلَّا طَرِيقَ جَهَنَّمَ خَالِدِينَ فِيهَا أَبَدًا ۚ وَكَانَ ذَٰلِكَ عَلَى اللَّهِ يَسِيرًا (169) Kupatula njira ya ku Gahena, kuti adzakhaleko mpaka kalekale. Ndipo imeneyi ndi ntchito yopepuka kwa Mulungu |
يَا أَيُّهَا النَّاسُ قَدْ جَاءَكُمُ الرَّسُولُ بِالْحَقِّ مِن رَّبِّكُمْ فَآمِنُوا خَيْرًا لَّكُمْ ۚ وَإِن تَكْفُرُوا فَإِنَّ لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ وَكَانَ اللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمًا (170) oh inu anthu! Ndithudi wadza kwa inu Mtumwi ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wanu, motero khulupirirani mwa iye ndipo zonse zidzakhala bwino kwa inu. Ngati inu simukhulupirira ndithudi mwini wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndi padziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo Mulungu ndi wodziwa chilichonse ndi Wanzeru |
يَا أَهْلَ الْكِتَابِ لَا تَغْلُوا فِي دِينِكُمْ وَلَا تَقُولُوا عَلَى اللَّهِ إِلَّا الْحَقَّ ۚ إِنَّمَا الْمَسِيحُ عِيسَى ابْنُ مَرْيَمَ رَسُولُ اللَّهِ وَكَلِمَتُهُ أَلْقَاهَا إِلَىٰ مَرْيَمَ وَرُوحٌ مِّنْهُ ۖ فَآمِنُوا بِاللَّهِ وَرُسُلِهِ ۖ وَلَا تَقُولُوا ثَلَاثَةٌ ۚ انتَهُوا خَيْرًا لَّكُمْ ۚ إِنَّمَا اللَّهُ إِلَٰهٌ وَاحِدٌ ۖ سُبْحَانَهُ أَن يَكُونَ لَهُ وَلَدٌ ۘ لَّهُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۗ وَكَفَىٰ بِاللَّهِ وَكِيلًا (171) oh inu anthu a m’Buku! Musadutse malire a chipembedzo chanu kapena kunena zokhudza Mulungu kupatula choonadi. Messiya Yesu, mwana wa Maria, sadali wina aliyense koma Mtumwi wa Mulungu ndi Mawu ake amene adanena kwa Maria, ndi Mzimu wolengedwa ndi Iye. Kotero khulupirirani mwa Mulungu ndi Atumwi ake. Ndipo musanene kuti: “Atatu.” Siyani! Zidzakhala bwino kwa inu. Chifukwa Mulungu ndi mmodzi yekha. Ulemerero ukhale kwa Iye. Iye sangakhale ndi mwana. Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndipo Mulungu ndi okwana kukhala Mtetezi wodalirika |
لَّن يَسْتَنكِفَ الْمَسِيحُ أَن يَكُونَ عَبْدًا لِّلَّهِ وَلَا الْمَلَائِكَةُ الْمُقَرَّبُونَ ۚ وَمَن يَسْتَنكِفْ عَنْ عِبَادَتِهِ وَيَسْتَكْبِرْ فَسَيَحْشُرُهُمْ إِلَيْهِ جَمِيعًا (172) Messiya sangakane kukhala kapolo wa Mulungu ndiponso angelo amene ali kufupi ndi Mulungu. Ndipo aliyense amene amakana kumutumikira Mulungu chifukwa cha kudzikweza, Iye adzawasonkhanitsa onse kudza pamaso pake |
فَأَمَّا الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ فَيُوَفِّيهِمْ أُجُورَهُمْ وَيَزِيدُهُم مِّن فَضْلِهِ ۖ وَأَمَّا الَّذِينَ اسْتَنكَفُوا وَاسْتَكْبَرُوا فَيُعَذِّبُهُمْ عَذَابًا أَلِيمًا وَلَا يَجِدُونَ لَهُم مِّن دُونِ اللَّهِ وَلِيًّا وَلَا نَصِيرًا (173) Motero iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndipo amachita ntchito zabwino, Iye adzawapatsa mphotho zawo mokwanira ndipo adzawalemeretsa iwo mwachisomo chake chochuluka. Koma iwo amene akana kupembedza kapena oyerekedwa, Iye adzawalanga ndi chilango chowawa. Ndipo iwo sadzapeza wina woposa Mulungu kuti awateteze kapena kuwathandiza |
يَا أَيُّهَا النَّاسُ قَدْ جَاءَكُم بُرْهَانٌ مِّن رَّبِّكُمْ وَأَنزَلْنَا إِلَيْكُمْ نُورًا مُّبِينًا (174) oh inu anthu! Ndithudi wadza kwa inu umboni wooneka kuchokera kwa Ambuye wanu ndipo Ife takutumizirani Muuni woonekera |
فَأَمَّا الَّذِينَ آمَنُوا بِاللَّهِ وَاعْتَصَمُوا بِهِ فَسَيُدْخِلُهُمْ فِي رَحْمَةٍ مِّنْهُ وَفَضْلٍ وَيَهْدِيهِمْ إِلَيْهِ صِرَاطًا مُّسْتَقِيمًا (175) Motero iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndipo amadzipereka kwathunthu kwa Iye, adzawalowetsa ku chifundo ndi chisomo chake ndi kuwatsogolera kunjira yoyenera |
يَسْتَفْتُونَكَ قُلِ اللَّهُ يُفْتِيكُمْ فِي الْكَلَالَةِ ۚ إِنِ امْرُؤٌ هَلَكَ لَيْسَ لَهُ وَلَدٌ وَلَهُ أُخْتٌ فَلَهَا نِصْفُ مَا تَرَكَ ۚ وَهُوَ يَرِثُهَا إِن لَّمْ يَكُن لَّهَا وَلَدٌ ۚ فَإِن كَانَتَا اثْنَتَيْنِ فَلَهُمَا الثُّلُثَانِ مِمَّا تَرَكَ ۚ وَإِن كَانُوا إِخْوَةً رِّجَالًا وَنِسَاءً فَلِلذَّكَرِ مِثْلُ حَظِّ الْأُنثَيَيْنِ ۗ يُبَيِّنُ اللَّهُ لَكُمْ أَن تَضِلُّوا ۗ وَاللَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (176) Iwo amakufunsa za malamulo; Nena: “Mulungu akukuuzani za munthu amene alibe makolo kapena mwana. Ngati munthu wa mwamuna akufa, ndipo alibe mwana koma ali ndi mlongo wake, mlongo wake adzalandire theka la katundu amene asiya. Ndipo ngati mkazi sasiya mwana, mlongo wake adzatenga chuma chake. Koma ngati akhala ndi alongo ake awiri, iwo adzalandire magawo awiri a magawo atatu a katundu amene asiya. Ndipo ngati pali abale amuna ndi akazi, mwamuna adzalandira magawo amene angalandire akazi awiri. Mulungu akukulongosolerani kuti musasochere. Ndipo Mulungu ndi wodziwa chilichonse.” |