Quran with Chichewa translation - Surah An-Nisa’ ayat 6 - النِّسَاء - Page - Juz 4
﴿وَٱبۡتَلُواْ ٱلۡيَتَٰمَىٰ حَتَّىٰٓ إِذَا بَلَغُواْ ٱلنِّكَاحَ فَإِنۡ ءَانَسۡتُم مِّنۡهُمۡ رُشۡدٗا فَٱدۡفَعُوٓاْ إِلَيۡهِمۡ أَمۡوَٰلَهُمۡۖ وَلَا تَأۡكُلُوهَآ إِسۡرَافٗا وَبِدَارًا أَن يَكۡبَرُواْۚ وَمَن كَانَ غَنِيّٗا فَلۡيَسۡتَعۡفِفۡۖ وَمَن كَانَ فَقِيرٗا فَلۡيَأۡكُلۡ بِٱلۡمَعۡرُوفِۚ فَإِذَا دَفَعۡتُمۡ إِلَيۡهِمۡ أَمۡوَٰلَهُمۡ فَأَشۡهِدُواْ عَلَيۡهِمۡۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ حَسِيبٗا ﴾
[النِّسَاء: 6]
﴿وابتلوا اليتامى حتى إذا بلغوا النكاح فإن آنستم منهم رشدا فادفعوا إليهم﴾ [النِّسَاء: 6]
Khaled Ibrahim Betala “Ayeseni amasiye (akayandikira kukula nsinkhu kuti muone kuti atha kuchita ntchito yabwino ndi chuma chawo mukawapatsa), kufikira atafika nthawi yokwatira/kukwatiwa. Ndipo ngati mutawaona kuti ali ndi nzeru zabwino, apatseni chuma chawo. Musachidye mosasamala ndi mwachangu poopa kuti angakule. Ndipo amene ali opeza bwino adziletse (kulandira mphoto yolelera ana amasiyewo). Koma amene ali wosauka adye mwa ubwino (osati moononga). Ndipo pamene mukuwapatsa chuma chawo, funani mboni (zoonelera kuperekedwa kwa chumacho). Ndipo Allah ali Wokwana kukhala Muwelengeri (ndi Woyang’anira) |