Quran with Chichewa translation - Surah An-Nisa’ ayat 78 - النِّسَاء - Page - Juz 5
﴿أَيۡنَمَا تَكُونُواْ يُدۡرِككُّمُ ٱلۡمَوۡتُ وَلَوۡ كُنتُمۡ فِي بُرُوجٖ مُّشَيَّدَةٖۗ وَإِن تُصِبۡهُمۡ حَسَنَةٞ يَقُولُواْ هَٰذِهِۦ مِنۡ عِندِ ٱللَّهِۖ وَإِن تُصِبۡهُمۡ سَيِّئَةٞ يَقُولُواْ هَٰذِهِۦ مِنۡ عِندِكَۚ قُلۡ كُلّٞ مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِۖ فَمَالِ هَٰٓؤُلَآءِ ٱلۡقَوۡمِ لَا يَكَادُونَ يَفۡقَهُونَ حَدِيثٗا ﴾
[النِّسَاء: 78]
﴿أينما تكونوا يدرككم الموت ولو كنتم في بروج مشيدة وإن تصبهم حسنة﴾ [النِّسَاء: 78]
Khaled Ibrahim Betala “Paliponse pamene mungakhale imfa ikupezani ngakhale mutakhala m’malinga olimba, ndipo ngati ubwino utawafika (opembedza mafano ndi achiphamaso) amati: “Ubwinowu, ukuchokera kwa Allah.” Koma choipa chikawafikira, amati: “Ichi chachitika chifukwa cha iwe (Muhammad).” Nena: “Zonse zachokera kwa Allah.” Kodi ngotani anthu awa, sangathe kuzindikira nkhani |