Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ahqaf ayat 15 - الأحقَاف - Page - Juz 26
﴿وَوَصَّيۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ بِوَٰلِدَيۡهِ إِحۡسَٰنًاۖ حَمَلَتۡهُ أُمُّهُۥ كُرۡهٗا وَوَضَعَتۡهُ كُرۡهٗاۖ وَحَمۡلُهُۥ وَفِصَٰلُهُۥ ثَلَٰثُونَ شَهۡرًاۚ حَتَّىٰٓ إِذَا بَلَغَ أَشُدَّهُۥ وَبَلَغَ أَرۡبَعِينَ سَنَةٗ قَالَ رَبِّ أَوۡزِعۡنِيٓ أَنۡ أَشۡكُرَ نِعۡمَتَكَ ٱلَّتِيٓ أَنۡعَمۡتَ عَلَيَّ وَعَلَىٰ وَٰلِدَيَّ وَأَنۡ أَعۡمَلَ صَٰلِحٗا تَرۡضَىٰهُ وَأَصۡلِحۡ لِي فِي ذُرِّيَّتِيٓۖ إِنِّي تُبۡتُ إِلَيۡكَ وَإِنِّي مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ ﴾
[الأحقَاف: 15]
﴿ووصينا الإنسان بوالديه إحسانا حملته أمه كرها ووضعته كرها وحمله وفصاله ثلاثون﴾ [الأحقَاف: 15]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo tamulangiza munthu kuchitira zabwino makolo ake. Mayi wake adatenga pathupi pake mwamasautso; ndipo adam’bala mwamasautso. Kutenga pakati pake ndi kumsiitsa kuyamwa ndi miyezi makumi atatu. Kufikira atakula nsinkhu nkukwana zaka makumi anayi, (akakhala mwana wabwino) amanena: “E Mbuye wanga! Ndilimbikitseni kuthokoza mtendere Wanu umene mwandipatsa pamodzi ndi makolo anga, ndipo ndilimbitseni kuti ndizichita zabwino zimene (Inu) muziyanja ndipo ndikonzereni ndi kundilungamitsira ana anga. Ine ndatembenukira kwa Inu; ndiponso ine ndine m’modzi mwa ogonjera (Inu).” |