اقْتَرَبَتِ السَّاعَةُ وَانشَقَّ الْقَمَرُ (1) Ola lachiweruzo lili pafupi ndipo mwezi wagawanika pakati |
وَإِن يَرَوْا آيَةً يُعْرِضُوا وَيَقُولُوا سِحْرٌ مُّسْتَمِرٌّ (2) Koma iwo akaona chozizwitsa, sakhulupirira ndipo amati, “Ichi sichina ayi koma matsenga ozama.” |
وَكَذَّبُوا وَاتَّبَعُوا أَهْوَاءَهُمْ ۚ وَكُلُّ أَمْرٍ مُّسْتَقِرٌّ (3) Iwo amakana choonadi koma amatsatira zilakolako zawo. Koma chinthu chilichonse chili ndi kumaliza kwake |
وَلَقَدْ جَاءَهُم مِّنَ الْأَنبَاءِ مَا فِيهِ مُزْدَجَرٌ (4) Ndithudi uthenga waperekedwa kale kwa iwo umene uli ndi chenjezo |
حِكْمَةٌ بَالِغَةٌ ۖ فَمَا تُغْنِ النُّذُرُ (5) Wodzadzidwa ndi nzeru koma machenjezo ake sawathandiza iwo china chilichonse |
فَتَوَلَّ عَنْهُمْ ۘ يَوْمَ يَدْعُ الدَّاعِ إِلَىٰ شَيْءٍ نُّكُرٍ (6) Kotero iwe, asiye okha. Patsiku limene woitana adzawaitana kudza ku chinthu choopsa |
خُشَّعًا أَبْصَارُهُمْ يَخْرُجُونَ مِنَ الْأَجْدَاثِ كَأَنَّهُمْ جَرَادٌ مُّنتَشِرٌ (7) Iwo adzadza kumeneko ndi nkhope zogwa pansi, kuchokera kumanda awo monga dzombe louluka ponseponse |
مُّهْطِعِينَ إِلَى الدَّاعِ ۖ يَقُولُ الْكَافِرُونَ هَٰذَا يَوْمٌ عَسِرٌ (8) Adzadza mofulumira kwa oitana anthu osakhulupirira adzati, “Ili ndi tsiku lovuta kwambiri.” |
۞ كَذَّبَتْ قَبْلَهُمْ قَوْمُ نُوحٍ فَكَذَّبُوا عَبْدَنَا وَقَالُوا مَجْنُونٌ وَازْدُجِرَ (9) Asanadze iwo, anthu a Nowa adakana kapolo wathu ndipo adati, “Uyu ndi munthu wamisala.” Ndipo iwo adamuthamangitsa iye ndi kumunyoza kwambiri |
فَدَعَا رَبَّهُ أَنِّي مَغْلُوبٌ فَانتَصِرْ (10) Ndipo iye adadandaula kwa Ambuye wake nati, “Ndagonjetsedwa kotero idzani kuti mundithandize.” |
فَفَتَحْنَا أَبْوَابَ السَّمَاءِ بِمَاءٍ مُّنْهَمِرٍ (11) Motero Ife tidatsekula makomo a kumwamba, ndipo mvula idagwa nthawi yomweyo |
وَفَجَّرْنَا الْأَرْضَ عُيُونًا فَالْتَقَى الْمَاءُ عَلَىٰ أَمْرٍ قَدْ قُدِرَ (12) Ndipo tidatumphutsa a kasupe padziko lapansi kotero madzi onse adakumana monga mwa lamulo lathu |
وَحَمَلْنَاهُ عَلَىٰ ذَاتِ أَلْوَاحٍ وَدُسُرٍ (13) Ndipo tidamunyamula iye m’chombo chopangidwandimatabwandichokhomedwandimisomali |
تَجْرِي بِأَعْيُنِنَا جَزَاءً لِّمَن كَانَ كُفِرَ (14) Chidanyamuka potsogozedwa ndi Ife. Mphotho kwa iye amene adakanidwa |
وَلَقَد تَّرَكْنَاهَا آيَةً فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (15) Ndithudi tidachisiya icho ngati chizindikiro koma kodi alipo ena amene adzachenjezedwa |
فَكَيْفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ (16) Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zalikulu bwanji |
وَلَقَدْ يَسَّرْنَا الْقُرْآنَ لِلذِّكْرِ فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (17) Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulidziwa ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa |
كَذَّبَتْ عَادٌ فَكَيْفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ (18) Anthu a Aad adakana. Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zoopsa bwanji |
إِنَّا أَرْسَلْنَا عَلَيْهِمْ رِيحًا صَرْصَرًا فِي يَوْمِ نَحْسٍ مُّسْتَمِرٍّ (19) Ndithudi Ife tidatumiza mphepo yamkhuntho pa tsiku latsoka losasimbika |
تَنزِعُ النَّاسَ كَأَنَّهُمْ أَعْجَازُ نَخْلٍ مُّنقَعِرٍ (20) Kugwetsa anthu ngati kuti adali mathunthu a mitengo ya mgwalangwa yozulidwa |
فَكَيْفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ (21) Kodi chilango changa ndipo chenjezo langa zidali zoopsa bwanji |
وَلَقَدْ يَسَّرْنَا الْقُرْآنَ لِلذِّكْرِ فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (22) Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa |
كَذَّبَتْ ثَمُودُ بِالنُّذُرِ (23) Anthu a Thamoud adakana machenjezo |
فَقَالُوا أَبَشَرًا مِّنَّا وَاحِدًا نَّتَّبِعُهُ إِنَّا إِذًا لَّفِي ضَلَالٍ وَسُعُرٍ (24) Iwo adati, “Munthu! Mmodzi yekha wochokera ku mtundu wathu kuti timutsatire? Ndithudi ife tikhala olakwa kwambiri ndiponso a misala.” |
أَأُلْقِيَ الذِّكْرُ عَلَيْهِ مِن بَيْنِنَا بَلْ هُوَ كَذَّابٌ أَشِرٌ (25) “Kodi ndiye kuti uthenga waperekedwa kwa iye yekha pakati pa ife tonse? Iyayi! Iye ndi wabodza ndi wodzikweza.” |
سَيَعْلَمُونَ غَدًا مَّنِ الْكَذَّابُ الْأَشِرُ (26) Mawa iwo adzadziwa kuti wabodza ndi wodzikweza ndani |
إِنَّا مُرْسِلُو النَّاقَةِ فِتْنَةً لَّهُمْ فَارْتَقِبْهُمْ وَاصْطَبِرْ (27) Ndithudi Ife titumiza ngamira yaikazi ngati mayesero kwa iwo. Motero iwe uwapenyetsetse ndipo ukhale wopirira |
وَنَبِّئْهُمْ أَنَّ الْمَاءَ قِسْمَةٌ بَيْنَهُمْ ۖ كُلُّ شِرْبٍ مُّحْتَضَرٌ (28) Ndipo uwauze kuti azigawana madzi. Ndipo nthawi yomwera madzi idzakhazikitsidwa |
فَنَادَوْا صَاحِبَهُمْ فَتَعَاطَىٰ فَعَقَرَ (29) Ndipo iwo adaitana m’bale wawo ndipo iye adatulutsa lupanga ndi kuipha |
فَكَيْفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ (30) Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zoopsa bwanji |
إِنَّا أَرْسَلْنَا عَلَيْهِمْ صَيْحَةً وَاحِدَةً فَكَانُوا كَهَشِيمِ الْمُحْتَظِرِ (31) Ndithudi tidawatumizira mfuwu umodzi ndipo onse adali ngati nkhuni zodula zimene munthu womanga mpanda amatola |
وَلَقَدْ يَسَّرْنَا الْقُرْآنَ لِلذِّكْرِ فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (32) Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Koma kodi alipo ena amene adzachenjezedwa |
كَذَّبَتْ قَوْمُ لُوطٍ بِالنُّذُرِ (33) Anthu a Loti adati chenjezo lathu ndi labodza |
إِنَّا أَرْسَلْنَا عَلَيْهِمْ حَاصِبًا إِلَّا آلَ لُوطٍ ۖ نَّجَّيْنَاهُم بِسَحَرٍ (34) Ndithudi Ife tidawatumizira mphepo yonyamula miyala kupatula a pa banja la Loti amene tidawapulumutsa mu ola lomaliza la usiku |
نِّعْمَةً مِّنْ عِندِنَا ۚ كَذَٰلِكَ نَجْزِي مَن شَكَرَ (35) Monga chisomo chochokera kwa Ife, motero ndi mmene timalipirira anthu oyamika |
وَلَقَدْ أَنذَرَهُم بَطْشَتَنَا فَتَمَارَوْا بِالنُّذُرِ (36) Ndithudi iye adawachenjeza za chilango chathu choopsa koma iwo adakana chenjezo lathu |
وَلَقَدْ رَاوَدُوهُ عَن ضَيْفِهِ فَطَمَسْنَا أَعْيُنَهُمْ فَذُوقُوا عَذَابِي وَنُذُرِ (37) Ndipo, ndithudi, iwo adafuna kuchititsa manyazi alendo ake. Motero Ife tidawachititsa khungu. Kotero inu lawani chilango changa ndi machenjezo anga |
وَلَقَدْ صَبَّحَهُم بُكْرَةً عَذَابٌ مُّسْتَقِرٌّ (38) Ndithudi chilango chowawa chidadza pa iwo nthawi yam’mawa |
فَذُوقُوا عَذَابِي وَنُذُرِ (39) Kotero inu lawani chilango changa ndi machenjezo anga |
وَلَقَدْ يَسَّرْنَا الْقُرْآنَ لِلذِّكْرِ فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (40) Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa |
وَلَقَدْ جَاءَ آلَ فِرْعَوْنَ النُّذُرُ (41) Ndipo, ndithudi, machenjezo adadza kwa anthu a Farawo |
كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا كُلِّهَا فَأَخَذْنَاهُمْ أَخْذَ عَزِيزٍ مُّقْتَدِرٍ (42) Iwo adati machenjezo athu onse ndi abodza motero tidawaononga ndi chilango champhamvu yochuluka |
أَكُفَّارُكُمْ خَيْرٌ مِّنْ أُولَٰئِكُمْ أَمْ لَكُم بَرَاءَةٌ فِي الزُّبُرِ (43) Kodi anthu anu osakhulupirira ndi abwino kuposa awa? Kapena inu muli ndi chitetezo mu m’mawu a Mulungu |
أَمْ يَقُولُونَ نَحْنُ جَمِيعٌ مُّنتَصِرٌ (44) Kodi kapena iwo amati, “Ife ndife ambiri ndipo tidzapambana?” |
سَيُهْزَمُ الْجَمْعُ وَيُوَلُّونَ الدُّبُرَ (45) Tsopano magulu awo ali kupirikitsidwa ndipo iwo ali kuthawa |
بَلِ السَّاعَةُ مَوْعِدُهُمْ وَالسَّاعَةُ أَدْهَىٰ وَأَمَرُّ (46) Iyayi, koma ola lachiweruzo ndi nthawi imene iwo adalonjezedwa ndipo ola limeneli lidzakhala loopsa kwambiri |
إِنَّ الْمُجْرِمِينَ فِي ضَلَالٍ وَسُعُرٍ (47) Ndithudi anthu osakhulupirira ndi olakwa adzapsya |
يَوْمَ يُسْحَبُونَ فِي النَّارِ عَلَىٰ وُجُوهِهِمْ ذُوقُوا مَسَّ سَقَرَ (48) Tsiku limene iwo adzaduduluzidwa pa nkhope zawo kunka ku moto, (zidzanenedwa) “Lawani ululu wa ku Moto.” |
إِنَّا كُلَّ شَيْءٍ خَلَقْنَاهُ بِقَدَرٍ (49) Ndithudi tidalenga chilichonse molingana ndi muyeso wake |
وَمَا أَمْرُنَا إِلَّا وَاحِدَةٌ كَلَمْحٍ بِالْبَصَرِ (50) Ndipo ulamuliro wathu ndi umodzi monga kuphenira kwa diso |
وَلَقَدْ أَهْلَكْنَا أَشْيَاعَكُمْ فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (51) Ndithudi Ife tidaononga kale anthu onga inu koma kodi alipo amene anga chenjezedwe |
وَكُلُّ شَيْءٍ فَعَلُوهُ فِي الزُّبُرِ (52) Ndipo zonse zimene adachita zidalembedwa |
وَكُلُّ صَغِيرٍ وَكَبِيرٍ مُّسْتَطَرٌ (53) Ndipo chilichonse chaching’ono ndi chachikulu chidalembedwa kale |
إِنَّ الْمُتَّقِينَ فِي جَنَّاتٍ وَنَهَرٍ (54) Ndithudi onse amene amalewa zoipa adzakhala m’kati mwa minda ndi mitsinje |
فِي مَقْعَدِ صِدْقٍ عِندَ مَلِيكٍ مُّقْتَدِرٍ (55) Ku Paradiso kufupi ndi Mfumu yamphamvu zonse |