الرَّحْمَٰنُ (1) Mwini Chifundo Chosatha |
عَلَّمَ الْقُرْآنَ (2) Ndiye amene adamphunzitsa munthu Korani |
خَلَقَ الْإِنسَانَ (3) Ndiye amene adalenga munthu |
عَلَّمَهُ الْبَيَانَ (4) Wamuphunzitsa iye mawu anzeru |
الشَّمْسُ وَالْقَمَرُ بِحُسْبَانٍ (5) Dzuwa ndi mwezi zimayenda m’misewu imene zinalamulidwa |
وَالنَّجْمُ وَالشَّجَرُ يَسْجُدَانِ (6) Zomera (kapena nyenyezi) ndi mitengo zonse zimagwada pomulambira Iye |
وَالسَّمَاءَ رَفَعَهَا وَوَضَعَ الْمِيزَانَ (7) Iye adakweza kumwamba ndi kukhazikitsa muyeso |
أَلَّا تَطْغَوْا فِي الْمِيزَانِ (8) Kuti inu musaphwanye muyeso |
وَأَقِيمُوا الْوَزْنَ بِالْقِسْطِ وَلَا تُخْسِرُوا الْمِيزَانَ (9) Kotero khazikitsani muyeso wachilungamo ndipo musayese monyenga |
وَالْأَرْضَ وَضَعَهَا لِلْأَنَامِ (10) Ndiye amene adalenga dziko lapansi kuti zolengedwa zake zizikhalamo |
فِيهَا فَاكِهَةٌ وَالنَّخْلُ ذَاتُ الْأَكْمَامِ (11) Mu ilo muli zipatso ndi mitengo ya tende yobereka phava la zipatso zambiri |
وَالْحَبُّ ذُو الْعَصْفِ وَالرَّيْحَانُ (12) Ndi chimanga chimene masamba ndi mapesi ake amadyedwa ndi ziweto. Ndi mitengo yonunkhira |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (13) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
خَلَقَ الْإِنسَانَ مِن صَلْصَالٍ كَالْفَخَّارِ (14) Iye adalenga munthu kuchokera ku dothi monga dothi la mbiya |
وَخَلَقَ الْجَانَّ مِن مَّارِجٍ مِّن نَّارٍ (15) Ndipo adalenga majini kuchokera kumoto wopanda utsi |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (16) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
رَبُّ الْمَشْرِقَيْنِ وَرَبُّ الْمَغْرِبَيْنِ (17) Ambuye wa kum’mawa kuwiri ndi Ambuye wa kumadzulo kuwiri |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (18) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
مَرَجَ الْبَحْرَيْنِ يَلْتَقِيَانِ (19) Iye adasiya nyanja ziwiri kuti zikumane |
بَيْنَهُمَا بَرْزَخٌ لَّا يَبْغِيَانِ (20) Pakati pawo pali malire amene madzi a uku sangathe kudutsa kupita uko |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (21) Kodi ndi zokoma ziti za Rahman 573 Ambuye wanu zimene mudzakana |
يَخْرُجُ مِنْهُمَا اللُّؤْلُؤُ وَالْمَرْجَانُ (22) Mu zonse muli nkhombe zazikulu ndi zazing’ono |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (23) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
وَلَهُ الْجَوَارِ الْمُنشَآتُ فِي الْبَحْرِ كَالْأَعْلَامِ (24) Ndipo zake ndi zombo zimene zimayenda pa nyanja, zazikulu ngati mapiri |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (25) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
كُلُّ مَنْ عَلَيْهَا فَانٍ (26) Zonse zimene zili pa dziko zidzatha |
وَيَبْقَىٰ وَجْهُ رَبِّكَ ذُو الْجَلَالِ وَالْإِكْرَامِ (27) Ndipo nkhope ya Ambuye wako mu Ufumu ndi mu Ulemerero idzakhalabe mpaka kalekale |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (28) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
يَسْأَلُهُ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ كُلَّ يَوْمٍ هُوَ فِي شَأْنٍ (29) Zonse zimene zimakhala kumwamba ndi padziko lapansi zimapempha kwa Iye. Tsiku lililonse Iye amakhala ndi chochita |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (30) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
سَنَفْرُغُ لَكُمْ أَيُّهَ الثَّقَلَانِ (31) Ife tidzadza kwa inu, Oh inu magulu awiri |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (32) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
يَا مَعْشَرَ الْجِنِّ وَالْإِنسِ إِنِ اسْتَطَعْتُمْ أَن تَنفُذُوا مِنْ أَقْطَارِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ فَانفُذُوا ۚ لَا تَنفُذُونَ إِلَّا بِسُلْطَانٍ (33) oh inu gulu la Majini ndi Anthu! Ngati muli ndi mphamvu zodutsa malire a kumwamba ndi dziko lapansi, dutsani. Komatu inu simungadutse popanda chilolezo |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (34) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
يُرْسَلُ عَلَيْكُمَا شُوَاظٌ مِّن نَّارٍ وَنُحَاسٌ فَلَا تَنتَصِرَانِ (35) Malawi a moto ndi utsi zidzaponyedwa kwa inu nonse awiri ndipo simudzatha kudziteteza nokha |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (36) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
فَإِذَا انشَقَّتِ السَّمَاءُ فَكَانَتْ وَرْدَةً كَالدِّهَانِ (37) Ndi pamene thambo lidzagawanika pakati ndikukhala lofiira ngati mafuta osungunuka |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (38) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
فَيَوْمَئِذٍ لَّا يُسْأَلُ عَن ذَنبِهِ إِنسٌ وَلَا جَانٌّ (39) Motero patsiku limeneli, sipadzakhala mafunso kuchokera kwa Munthu kapena Majini okhudza machimo awo |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (40) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
يُعْرَفُ الْمُجْرِمُونَ بِسِيمَاهُمْ فَيُؤْخَذُ بِالنَّوَاصِي وَالْأَقْدَامِ (41) ochimwa adzadziwika ndi zizindikiro ndipo adzawagwira tsumba ndi pamapazi pawo |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (42) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye |
هَٰذِهِ جَهَنَّمُ الَّتِي يُكَذِّبُ بِهَا الْمُجْرِمُونَ (43) Iyi ndi Gahena imene anthu ochimwa amati ndi bodza |
يَطُوفُونَ بَيْنَهَا وَبَيْنَ حَمِيمٍ آنٍ (44) Iwo adzalowa m’kati mwake ndi m’kati mwa madzi ogaduka |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (45) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
وَلِمَنْ خَافَ مَقَامَ رَبِّهِ جَنَّتَانِ (46) Ndipo kwa iye amene aopa kuima pamaso pa Ambuye wawo, kudzakhala minda iwiri |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (47) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
ذَوَاتَا أَفْنَانٍ (48) Zokhala ndi mphanda zotambasuka |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (49) Kodi ndi zokoma ziti zaAmbuye wanu zimene mudzakana |
فِيهِمَا عَيْنَانِ تَجْرِيَانِ (50) Monse mudzakhala a kasupe awiri otumphuka |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (51) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
فِيهِمَا مِن كُلِّ فَاكِهَةٍ زَوْجَانِ (52) M’menemu mudzakhala zipatso ziwiriziwiri za mitundumitundu |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (53) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
مُتَّكِئِينَ عَلَىٰ فُرُشٍ بَطَائِنُهَا مِنْ إِسْتَبْرَقٍ ۚ وَجَنَى الْجَنَّتَيْنِ دَانٍ (54) Iwo adzagona pa makama amene nsalu yake ya m’kati idzakhala yasilika ndipo zipatso za m’minda iwiriyi zidzakhala pafupi pawo |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (55) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
فِيهِنَّ قَاصِرَاتُ الطَّرْفِ لَمْ يَطْمِثْهُنَّ إِنسٌ قَبْلَهُمْ وَلَا جَانٌّ (56) M’menemo mudzakhala wodzisunga ndi ogwetsa nkhope zawo pansi amene Munthu kapena Majini sadawakhudze |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (57) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
كَأَنَّهُنَّ الْيَاقُوتُ وَالْمَرْجَانُ (58) olingana ndi miyala ya rubiya ndi ndolo |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (59) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
هَلْ جَزَاءُ الْإِحْسَانِ إِلَّا الْإِحْسَانُ (60) Kodi dipo la ntchito yabwino lingakhale lina loposa ubwino |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (61) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
وَمِن دُونِهِمَا جَنَّتَانِ (62) Ndipo poonjezera pa minda iwiri pali minda ina iwiri |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (63) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
مُدْهَامَّتَانِ (64) Yooneka mobiriwira |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (65) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
فِيهِمَا عَيْنَانِ نَضَّاخَتَانِ (66) Monse mudzakhala a kasupe awiri otulutsa madzi ochuluka |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (67) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
فِيهِمَا فَاكِهَةٌ وَنَخْلٌ وَرُمَّانٌ (68) Monse mudzakhala zipatso, tende ndi chimanga chachizungu |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (69) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
فِيهِنَّ خَيْرَاتٌ حِسَانٌ (70) Mmenemo mudzakhala zinthu zokongola |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (71) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
حُورٌ مَّقْصُورَاتٌ فِي الْخِيَامِ (72) Angwiro ndi okhala m’mahema |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (73) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
لَمْ يَطْمِثْهُنَّ إِنسٌ قَبْلَهُمْ وَلَا جَانٌّ (74) Amene Munthu kapena Majini sadawakhudze |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (75) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
مُتَّكِئِينَ عَلَىٰ رَفْرَفٍ خُضْرٍ وَعَبْقَرِيٍّ حِسَانٍ (76) Atakhala pa mipando yawofowofo, yobiriwira ndi mabedi okongola |
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (77) Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana |
تَبَارَكَ اسْمُ رَبِّكَ ذِي الْجَلَالِ وَالْإِكْرَامِ (78) Lidalitsike dzina la Ambuye wako, Mwini ulemerero, chuma ndi ulemu |