×

Surah Nuh in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Nuh

Translation of the Meanings of Surah Nuh in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Nuh translated into Chichewa, Surah Nuh in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Nuh in Chichewa - نيانجا, Verses 28 - Surah Number 71 - Page 570.

بسم الله الرحمن الرحيم

إِنَّا أَرْسَلْنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوْمِهِ أَنْ أَنذِرْ قَوْمَكَ مِن قَبْلِ أَن يَأْتِيَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (1)
Ndithudi tidatumiza Nowa kwa anthu ake: “Chenjeza anthu ako chilango chowawa chisadafike pa iwo.”
قَالَ يَا قَوْمِ إِنِّي لَكُمْ نَذِيرٌ مُّبِينٌ (2)
Iye adati: “oh inu anthu anga! Ndithudi ine, ndine Mchenjezi wooneka kwa inu.”
أَنِ اعْبُدُوا اللَّهَ وَاتَّقُوهُ وَأَطِيعُونِ (3)
“Kuti muzipembedza Mulungu ndi kumuopa Iye ndipo mundimvere ine.”
يَغْفِرْ لَكُم مِّن ذُنُوبِكُمْ وَيُؤَخِّرْكُمْ إِلَىٰ أَجَلٍ مُّسَمًّى ۚ إِنَّ أَجَلَ اللَّهِ إِذَا جَاءَ لَا يُؤَخَّرُ ۖ لَوْ كُنتُمْ تَعْلَمُونَ (4)
“Iye adzakukhululukirani machimo anu ndi kukusungani bwino mpaka nthawi ya imfa yanu. Ndithudi nthawi ya Mulungu ikakwana, palibe wina aliyense amene angaibwezere m’mbuyo inu mukadadziwa.”
قَالَ رَبِّ إِنِّي دَعَوْتُ قَوْمِي لَيْلًا وَنَهَارًا (5)
Iye adati: “oh Ambuye! Ndithudi usana ndi usiku ndakhala ndiri kuwaitana anthu anga.”
فَلَمْ يَزِدْهُمْ دُعَائِي إِلَّا فِرَارًا (6)
“Koma kuitana kwanga kwangoonjezera kusamvera kwawo.”
وَإِنِّي كُلَّمَا دَعَوْتُهُمْ لِتَغْفِرَ لَهُمْ جَعَلُوا أَصَابِعَهُمْ فِي آذَانِهِمْ وَاسْتَغْشَوْا ثِيَابَهُمْ وَأَصَرُّوا وَاسْتَكْبَرُوا اسْتِكْبَارًا (7)
“Ndipo, ndithudi, nthawi yonse imene ndiitana kuti Inu muwakhululukire, iwo amatenga zala zawo ndi kutseka m’makutu mwawo ndipo amatenga mikhanjo yawo ndi kufunditsa kumutu kwawo ndipo amapitirirabe kuchita zoipa monyada.”
ثُمَّ إِنِّي دَعَوْتُهُمْ جِهَارًا (8)
“Ndipo, ndithudi, ine ndidalalikira mokweza kwa iwo.”
ثُمَّ إِنِّي أَعْلَنتُ لَهُمْ وَأَسْرَرْتُ لَهُمْ إِسْرَارًا (9)
“Ndipo, ndithudi, ndidawalankhula pagulu ndi mwamseri.”
فَقُلْتُ اسْتَغْفِرُوا رَبَّكُمْ إِنَّهُ كَانَ غَفَّارًا (10)
Ndidawauza: “Funsani chikhululukiro cha Ambuye wanu. Ndithudi Iye amakhululukira nthawi zonse.”
يُرْسِلِ السَّمَاءَ عَلَيْكُم مِّدْرَارًا (11)
“Iye adzakutumizirani Nuh 621 mvula yochuluka.”
وَيُمْدِدْكُم بِأَمْوَالٍ وَبَنِينَ وَيَجْعَل لَّكُمْ جَنَّاتٍ وَيَجْعَل لَّكُمْ أَنْهَارًا (12)
“Ndikukupatsani inu chuma, ana, minda ndi mitsinje.”
مَّا لَكُمْ لَا تَرْجُونَ لِلَّهِ وَقَارًا (13)
Kodi mwatani, inu simuyembekeza mphotho
وَقَدْ خَلَقَكُمْ أَطْوَارًا (14)
Pamene Iye adakulengani inu m’nthawi zosiyana siyana
أَلَمْ تَرَوْا كَيْفَ خَلَقَ اللَّهُ سَبْعَ سَمَاوَاتٍ طِبَاقًا (15)
Kodi inu simuona mmene Mulungu adalengera miyamba isanu ndi iwiri, wina pamwamba pa unzake
وَجَعَلَ الْقَمَرَ فِيهِنَّ نُورًا وَجَعَلَ الشَّمْسَ سِرَاجًا (16)
Ndipo anapanga mwezi ngati muuni ndi dzuwa ngati nyali
وَاللَّهُ أَنبَتَكُم مِّنَ الْأَرْضِ نَبَاتًا (17)
Mulungu adakulengani inu kuchokera ku nthaka
ثُمَّ يُعِيدُكُمْ فِيهَا وَيُخْرِجُكُمْ إِخْرَاجًا (18)
Ndipo ku nthaka komweko adzakubwezerani inu ndi kukudzutsaninso
وَاللَّهُ جَعَلَ لَكُمُ الْأَرْضَ بِسَاطًا (19)
Ndipo Mulungu adalenga dziko kukhala lalikulu kwa inu
لِّتَسْلُكُوا مِنْهَا سُبُلًا فِجَاجًا (20)
Kuti muziyenda m’njira zambiri za zikuluzikulu
قَالَ نُوحٌ رَّبِّ إِنَّهُمْ عَصَوْنِي وَاتَّبَعُوا مَن لَّمْ يَزِدْهُ مَالُهُ وَوَلَدُهُ إِلَّا خَسَارًا (21)
Nowa adati: “oh Ambuye! Anthu anga sali kundimvera ine koma mmalo mwake ali kutsatira amene sangawaonjezere chuma ndi ana koma mavuto.”
وَمَكَرُوا مَكْرًا كُبَّارًا (22)
Ndipo iwo akonza chiwembu champhamvu
وَقَالُوا لَا تَذَرُنَّ آلِهَتَكُمْ وَلَا تَذَرُنَّ وَدًّا وَلَا سُوَاعًا وَلَا يَغُوثَ وَيَعُوقَ وَنَسْرًا (23)
Ndipo ati: “Mwanjira ina iliyonse inu musaleke kupembedza milungu yanu. Musaleke kupembedza Wadd, Suwa, Yaghuth, Yauq kapena Nasr.”
وَقَدْ أَضَلُّوا كَثِيرًا ۖ وَلَا تَزِدِ الظَّالِمِينَ إِلَّا ضَلَالًا (24)
“Ndipo, ndithudi, iwo asocheza anthu ambiri. Ndipo Inu musaonjeze china chili chonse kwa anthu ochita zoipa chifukwa apitirizabe kuchita zoipa.”
مِّمَّا خَطِيئَاتِهِمْ أُغْرِقُوا فَأُدْخِلُوا نَارًا فَلَمْ يَجِدُوا لَهُم مِّن دُونِ اللَّهِ أَنصَارًا (25)
Chifukwa cha machimo awo iwo anamizidwa ndipo adaponyedwa ku moto ndipo iwo sanapeze wina aliyense kuti awathandize, m’malo mwa Mulungu
وَقَالَ نُوحٌ رَّبِّ لَا تَذَرْ عَلَى الْأَرْضِ مِنَ الْكَافِرِينَ دَيَّارًا (26)
Ndipo Nowa adati: Ambuye wanga! Musasiye munthu aliyense padziko lapansi mwa anthu osakhulupirira
إِنَّكَ إِن تَذَرْهُمْ يُضِلُّوا عِبَادَكَ وَلَا يَلِدُوا إِلَّا فَاجِرًا كَفَّارًا (27)
“Ngati Inu muwasiya iwo adzasocheretsa akapolo anu okhulupirira ndipo iwo adzabereka anthu ochita zoipa ndi osakhulupirira.”
رَّبِّ اغْفِرْ لِي وَلِوَالِدَيَّ وَلِمَن دَخَلَ بَيْتِيَ مُؤْمِنًا وَلِلْمُؤْمِنِينَ وَالْمُؤْمِنَاتِ وَلَا تَزِدِ الظَّالِمِينَ إِلَّا تَبَارًا (28)
“Ambuye wanga! Ndikhululukireni ine ndi makolo anga ndi iye amene alowa mnyumba yanga ngati wokhulupirira ndiponso okhulupirira onse amuna ndi akazi. Ndipo kwa anthu osakhulupilira, Inu musawaonjezere china koma chionongeko
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas