إِنَّا أَرْسَلْنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوْمِهِ أَنْ أَنذِرْ قَوْمَكَ مِن قَبْلِ أَن يَأْتِيَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (1) Ndithudi tidatumiza Nowa kwa anthu ake: “Chenjeza anthu ako chilango chowawa chisadafike pa iwo.” |
قَالَ يَا قَوْمِ إِنِّي لَكُمْ نَذِيرٌ مُّبِينٌ (2) Iye adati: “oh inu anthu anga! Ndithudi ine, ndine Mchenjezi wooneka kwa inu.” |
أَنِ اعْبُدُوا اللَّهَ وَاتَّقُوهُ وَأَطِيعُونِ (3) “Kuti muzipembedza Mulungu ndi kumuopa Iye ndipo mundimvere ine.” |
يَغْفِرْ لَكُم مِّن ذُنُوبِكُمْ وَيُؤَخِّرْكُمْ إِلَىٰ أَجَلٍ مُّسَمًّى ۚ إِنَّ أَجَلَ اللَّهِ إِذَا جَاءَ لَا يُؤَخَّرُ ۖ لَوْ كُنتُمْ تَعْلَمُونَ (4) “Iye adzakukhululukirani machimo anu ndi kukusungani bwino mpaka nthawi ya imfa yanu. Ndithudi nthawi ya Mulungu ikakwana, palibe wina aliyense amene angaibwezere m’mbuyo inu mukadadziwa.” |
قَالَ رَبِّ إِنِّي دَعَوْتُ قَوْمِي لَيْلًا وَنَهَارًا (5) Iye adati: “oh Ambuye! Ndithudi usana ndi usiku ndakhala ndiri kuwaitana anthu anga.” |
فَلَمْ يَزِدْهُمْ دُعَائِي إِلَّا فِرَارًا (6) “Koma kuitana kwanga kwangoonjezera kusamvera kwawo.” |
وَإِنِّي كُلَّمَا دَعَوْتُهُمْ لِتَغْفِرَ لَهُمْ جَعَلُوا أَصَابِعَهُمْ فِي آذَانِهِمْ وَاسْتَغْشَوْا ثِيَابَهُمْ وَأَصَرُّوا وَاسْتَكْبَرُوا اسْتِكْبَارًا (7) “Ndipo, ndithudi, nthawi yonse imene ndiitana kuti Inu muwakhululukire, iwo amatenga zala zawo ndi kutseka m’makutu mwawo ndipo amatenga mikhanjo yawo ndi kufunditsa kumutu kwawo ndipo amapitirirabe kuchita zoipa monyada.” |
ثُمَّ إِنِّي دَعَوْتُهُمْ جِهَارًا (8) “Ndipo, ndithudi, ine ndidalalikira mokweza kwa iwo.” |
ثُمَّ إِنِّي أَعْلَنتُ لَهُمْ وَأَسْرَرْتُ لَهُمْ إِسْرَارًا (9) “Ndipo, ndithudi, ndidawalankhula pagulu ndi mwamseri.” |
فَقُلْتُ اسْتَغْفِرُوا رَبَّكُمْ إِنَّهُ كَانَ غَفَّارًا (10) Ndidawauza: “Funsani chikhululukiro cha Ambuye wanu. Ndithudi Iye amakhululukira nthawi zonse.” |
يُرْسِلِ السَّمَاءَ عَلَيْكُم مِّدْرَارًا (11) “Iye adzakutumizirani Nuh 621 mvula yochuluka.” |
وَيُمْدِدْكُم بِأَمْوَالٍ وَبَنِينَ وَيَجْعَل لَّكُمْ جَنَّاتٍ وَيَجْعَل لَّكُمْ أَنْهَارًا (12) “Ndikukupatsani inu chuma, ana, minda ndi mitsinje.” |
مَّا لَكُمْ لَا تَرْجُونَ لِلَّهِ وَقَارًا (13) Kodi mwatani, inu simuyembekeza mphotho |
وَقَدْ خَلَقَكُمْ أَطْوَارًا (14) Pamene Iye adakulengani inu m’nthawi zosiyana siyana |
أَلَمْ تَرَوْا كَيْفَ خَلَقَ اللَّهُ سَبْعَ سَمَاوَاتٍ طِبَاقًا (15) Kodi inu simuona mmene Mulungu adalengera miyamba isanu ndi iwiri, wina pamwamba pa unzake |
وَجَعَلَ الْقَمَرَ فِيهِنَّ نُورًا وَجَعَلَ الشَّمْسَ سِرَاجًا (16) Ndipo anapanga mwezi ngati muuni ndi dzuwa ngati nyali |
وَاللَّهُ أَنبَتَكُم مِّنَ الْأَرْضِ نَبَاتًا (17) Mulungu adakulengani inu kuchokera ku nthaka |
ثُمَّ يُعِيدُكُمْ فِيهَا وَيُخْرِجُكُمْ إِخْرَاجًا (18) Ndipo ku nthaka komweko adzakubwezerani inu ndi kukudzutsaninso |
وَاللَّهُ جَعَلَ لَكُمُ الْأَرْضَ بِسَاطًا (19) Ndipo Mulungu adalenga dziko kukhala lalikulu kwa inu |
لِّتَسْلُكُوا مِنْهَا سُبُلًا فِجَاجًا (20) Kuti muziyenda m’njira zambiri za zikuluzikulu |
قَالَ نُوحٌ رَّبِّ إِنَّهُمْ عَصَوْنِي وَاتَّبَعُوا مَن لَّمْ يَزِدْهُ مَالُهُ وَوَلَدُهُ إِلَّا خَسَارًا (21) Nowa adati: “oh Ambuye! Anthu anga sali kundimvera ine koma mmalo mwake ali kutsatira amene sangawaonjezere chuma ndi ana koma mavuto.” |
وَمَكَرُوا مَكْرًا كُبَّارًا (22) Ndipo iwo akonza chiwembu champhamvu |
وَقَالُوا لَا تَذَرُنَّ آلِهَتَكُمْ وَلَا تَذَرُنَّ وَدًّا وَلَا سُوَاعًا وَلَا يَغُوثَ وَيَعُوقَ وَنَسْرًا (23) Ndipo ati: “Mwanjira ina iliyonse inu musaleke kupembedza milungu yanu. Musaleke kupembedza Wadd, Suwa, Yaghuth, Yauq kapena Nasr.” |
وَقَدْ أَضَلُّوا كَثِيرًا ۖ وَلَا تَزِدِ الظَّالِمِينَ إِلَّا ضَلَالًا (24) “Ndipo, ndithudi, iwo asocheza anthu ambiri. Ndipo Inu musaonjeze china chili chonse kwa anthu ochita zoipa chifukwa apitirizabe kuchita zoipa.” |
مِّمَّا خَطِيئَاتِهِمْ أُغْرِقُوا فَأُدْخِلُوا نَارًا فَلَمْ يَجِدُوا لَهُم مِّن دُونِ اللَّهِ أَنصَارًا (25) Chifukwa cha machimo awo iwo anamizidwa ndipo adaponyedwa ku moto ndipo iwo sanapeze wina aliyense kuti awathandize, m’malo mwa Mulungu |
وَقَالَ نُوحٌ رَّبِّ لَا تَذَرْ عَلَى الْأَرْضِ مِنَ الْكَافِرِينَ دَيَّارًا (26) Ndipo Nowa adati: Ambuye wanga! Musasiye munthu aliyense padziko lapansi mwa anthu osakhulupirira |
إِنَّكَ إِن تَذَرْهُمْ يُضِلُّوا عِبَادَكَ وَلَا يَلِدُوا إِلَّا فَاجِرًا كَفَّارًا (27) “Ngati Inu muwasiya iwo adzasocheretsa akapolo anu okhulupirira ndipo iwo adzabereka anthu ochita zoipa ndi osakhulupirira.” |
رَّبِّ اغْفِرْ لِي وَلِوَالِدَيَّ وَلِمَن دَخَلَ بَيْتِيَ مُؤْمِنًا وَلِلْمُؤْمِنِينَ وَالْمُؤْمِنَاتِ وَلَا تَزِدِ الظَّالِمِينَ إِلَّا تَبَارًا (28) “Ambuye wanga! Ndikhululukireni ine ndi makolo anga ndi iye amene alowa mnyumba yanga ngati wokhulupirira ndiponso okhulupirira onse amuna ndi akazi. Ndipo kwa anthu osakhulupilira, Inu musawaonjezere china koma chionongeko |