Quran with Chichewa translation - Surah Yunus ayat 22 - يُونس - Page - Juz 11
﴿هُوَ ٱلَّذِي يُسَيِّرُكُمۡ فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِۖ حَتَّىٰٓ إِذَا كُنتُمۡ فِي ٱلۡفُلۡكِ وَجَرَيۡنَ بِهِم بِرِيحٖ طَيِّبَةٖ وَفَرِحُواْ بِهَا جَآءَتۡهَا رِيحٌ عَاصِفٞ وَجَآءَهُمُ ٱلۡمَوۡجُ مِن كُلِّ مَكَانٖ وَظَنُّوٓاْ أَنَّهُمۡ أُحِيطَ بِهِمۡ دَعَوُاْ ٱللَّهَ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ لَئِنۡ أَنجَيۡتَنَا مِنۡ هَٰذِهِۦ لَنَكُونَنَّ مِنَ ٱلشَّٰكِرِينَ ﴾
[يُونس: 22]
﴿هو الذي يسيركم في البر والبحر حتى إذا كنتم في الفلك وجرين﴾ [يُونس: 22]
Khaled Ibrahim Betala “Iye ndi Yemwe amakuyendetsani pa ntunda ndi pa nyanja; kufikira pomwe mumakhala m’zombo; ndipo zimayenda nawo (zombozo) ndi mphepo yabwino, naisangalalira. (Mwadzidzidzi) namondwe nkuzidzera (zombozo) ndipo mafunde nkuwadzera mbali zonse natsimikiza kuti azingidwa (ndi chionongeko); amampempha Allah modzipereka kwa Iye mukupempha kwawo (uku akunena): “Ngati mutipulumutsa pa ichi, tidzakhala m’gulu la oyamika (nthawi zonse)!” |