×

سورة يونس باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة يونس

ترجمة معاني سورة يونس باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة يونس مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Yunus in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة يونس باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 109 - رقم السورة 10 - الصفحة 208.

بسم الله الرحمن الرحيم

الر ۚ تِلْكَ آيَاتُ الْكِتَابِ الْحَكِيمِ (1)
Alif Lam Ra. Awa ndi mavesi a Buku la zinthu zanzeru zenizeni
أَكَانَ لِلنَّاسِ عَجَبًا أَنْ أَوْحَيْنَا إِلَىٰ رَجُلٍ مِّنْهُمْ أَنْ أَنذِرِ النَّاسَ وَبَشِّرِ الَّذِينَ آمَنُوا أَنَّ لَهُمْ قَدَمَ صِدْقٍ عِندَ رَبِّهِمْ ۗ قَالَ الْكَافِرُونَ إِنَّ هَٰذَا لَسَاحِرٌ مُّبِينٌ (2)
Kodi n’chodabwitsa kwa anthu kuti Ife tidavumbulutsa chivumbulutso kwa mmodzi wa iwo ponena, “Pereka chenjezo kwa anthu ndipo uwauze nkhani zabwino anthu okhulupirira kuti adzakhala ndi mpando wapamwamba kwa Ambuye wawo?” Anthu osakhulupirira adati: “Ndithudi uyu ndi wamatsenga enieni.”
إِنَّ رَبَّكُمُ اللَّهُ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ ثُمَّ اسْتَوَىٰ عَلَى الْعَرْشِ ۖ يُدَبِّرُ الْأَمْرَ ۖ مَا مِن شَفِيعٍ إِلَّا مِن بَعْدِ إِذْنِهِ ۚ ذَٰلِكُمُ اللَّهُ رَبُّكُمْ فَاعْبُدُوهُ ۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ (3)
Ndithudi Ambuye wanu ndi Mulungu, amene m’masiku asanu ndi limodzi adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo anabuka pamwamba pa Mpando wachifumu, nalamula zinthu zonse. Palibe wina amene adzalandira ulamuliro wopepesa kwa Mulungu pokhapokha atalandira chilolezo cha Mulungu. Ameneyo ndiye Mulungu Ambuye wanu, mpembedzeni Iye. Kodi simudzakumbukira
إِلَيْهِ مَرْجِعُكُمْ جَمِيعًا ۖ وَعْدَ اللَّهِ حَقًّا ۚ إِنَّهُ يَبْدَأُ الْخَلْقَ ثُمَّ يُعِيدُهُ لِيَجْزِيَ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ بِالْقِسْطِ ۚ وَالَّذِينَ كَفَرُوا لَهُمْ شَرَابٌ مِّنْ حَمِيمٍ وَعَذَابٌ أَلِيمٌ بِمَا كَانُوا يَكْفُرُونَ (4)
Kwa Iye nonse mudzabwerera. Lonjezo la Mulungu ndi loona. Iye ndiye adayamba kulenga zolengedwa zonse ndipo pomaliza adzazipatsanso moyo kuti adzawalipire mwa chilungamo onse amene adakhulupirira mwa Iye ndipo ankachita ntchito zabwino. Anthu osakhulupirira adzamwa zakumwa zamadzi ogaduka ndi kulandira chilango chowawa chifukwa chosakhulupirira
هُوَ الَّذِي جَعَلَ الشَّمْسَ ضِيَاءً وَالْقَمَرَ نُورًا وَقَدَّرَهُ مَنَازِلَ لِتَعْلَمُوا عَدَدَ السِّنِينَ وَالْحِسَابَ ۚ مَا خَلَقَ اللَّهُ ذَٰلِكَ إِلَّا بِالْحَقِّ ۚ يُفَصِّلُ الْآيَاتِ لِقَوْمٍ يَعْلَمُونَ (5)
Iye ndiye amene adalipanga dzuwa kukhala muuni ndi mwezi kukhala wowala ndipo adazikonzera modutsa kuti inu muzidziwa kuchuluka kwa zaka ndi chiwerengero. Iye sadazilenge chabe izo koma mu choonadi. Iye amafotokoza mawu ake momveka kwa anthu ake ozindikira
إِنَّ فِي اخْتِلَافِ اللَّيْلِ وَالنَّهَارِ وَمَا خَلَقَ اللَّهُ فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يَتَّقُونَ (6)
Ndithudi mukasinthidwe ka usiku ndi usana ndi zimene Mulungu walenga kumwamba ndi dziko lapansi, muli zizindikiro kwa anthu okana uchimo
إِنَّ الَّذِينَ لَا يَرْجُونَ لِقَاءَنَا وَرَضُوا بِالْحَيَاةِ الدُّنْيَا وَاطْمَأَنُّوا بِهَا وَالَّذِينَ هُمْ عَنْ آيَاتِنَا غَافِلُونَ (7)
Ndithudi iwo ndi anthu amene sayembekeza kuti adzakumana nafe ndipo amasangalala ndi moyo wa m’dziko lapansi ndi kukhutitsidwa nawo ndiponso amene salabadira mawu
أُولَٰئِكَ مَأْوَاهُمُ النَّارُ بِمَا كَانُوا يَكْسِبُونَ (8)
Iwo malo awo okhala ndi kumoto chifukwa cha zoipa zimene anali kuchita
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ يَهْدِيهِمْ رَبُّهُم بِإِيمَانِهِمْ ۖ تَجْرِي مِن تَحْتِهِمُ الْأَنْهَارُ فِي جَنَّاتِ النَّعِيمِ (9)
Ndithudi iwo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, Ambuye wawo adzawatsogolera m’chikhulupiriro chawo. Mitsinje idzakhala ili kuyenda pansi pawo m’minda ya mtendere
دَعْوَاهُمْ فِيهَا سُبْحَانَكَ اللَّهُمَّ وَتَحِيَّتُهُمْ فِيهَا سَلَامٌ ۚ وَآخِرُ دَعْوَاهُمْ أَنِ الْحَمْدُ لِلَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ (10)
Pemphero lawo mmenemo lidzakhala loti; “Ndinu Woyera Ambuye!” Ndipo kulonjerana kwawo kudzakhala koti: “Mtendere” ndipo kumapeto kwa pempho lawo adzati: “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa chilengedwe.”
۞ وَلَوْ يُعَجِّلُ اللَّهُ لِلنَّاسِ الشَّرَّ اسْتِعْجَالَهُم بِالْخَيْرِ لَقُضِيَ إِلَيْهِمْ أَجَلُهُمْ ۖ فَنَذَرُ الَّذِينَ لَا يَرْجُونَ لِقَاءَنَا فِي طُغْيَانِهِمْ يَعْمَهُونَ (11)
Akadakhala kuti Mulungu amabweretsa msanga chilango kwa anthu monga momwe iwo amafunira zabwino kuti zidze mwansanga, nthawi yawo yofera ikadakwaniritsidwa. Kwa iwo amene saopa kukumana ndi Ife tidzawasiya mukusochera kwawo, akusowa chochita
وَإِذَا مَسَّ الْإِنسَانَ الضُّرُّ دَعَانَا لِجَنبِهِ أَوْ قَاعِدًا أَوْ قَائِمًا فَلَمَّا كَشَفْنَا عَنْهُ ضُرَّهُ مَرَّ كَأَن لَّمْ يَدْعُنَا إِلَىٰ ضُرٍّ مَّسَّهُ ۚ كَذَٰلِكَ زُيِّنَ لِلْمُسْرِفِينَ مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (12)
Pamene mavuto amadza pa munthu, iye amapemphera kwa Ifemogonachanthiti, mokhalapansikapenamoimirira. Koma tikangomuchotsera mavuto ake, iye amatsatila njira zake kukhala ngati sadatipemphe kuti timuchotsere mavuto omwe adamupeza. Kotero zidakongoletsedwa kwa anthu oononga zimene anali kuchita
وَلَقَدْ أَهْلَكْنَا الْقُرُونَ مِن قَبْلِكُمْ لَمَّا ظَلَمُوا ۙ وَجَاءَتْهُمْ رُسُلُهُم بِالْبَيِّنَاتِ وَمَا كَانُوا لِيُؤْمِنُوا ۚ كَذَٰلِكَ نَجْزِي الْقَوْمَ الْمُجْرِمِينَ (13)
Zoonadi Ife tidaononga mibadwo imene idalipo inu musanadze, pamene iwo adachita zoipa, anawafikira Atumwi awo ndi umboni weniweni koma iwo sadakhulupilire, motero tidzawalipira anthu ochita zoipa
ثُمَّ جَعَلْنَاكُمْ خَلَائِفَ فِي الْأَرْضِ مِن بَعْدِهِمْ لِنَنظُرَ كَيْفَ تَعْمَلُونَ (14)
Ndipo Ife tidakupangani kukhala alowa mmalo awo m’dziko lawo pambuyo pawo, kuti tione mmene inu mungachitire
وَإِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِمْ آيَاتُنَا بَيِّنَاتٍ ۙ قَالَ الَّذِينَ لَا يَرْجُونَ لِقَاءَنَا ائْتِ بِقُرْآنٍ غَيْرِ هَٰذَا أَوْ بَدِّلْهُ ۚ قُلْ مَا يَكُونُ لِي أَنْ أُبَدِّلَهُ مِن تِلْقَاءِ نَفْسِي ۖ إِنْ أَتَّبِعُ إِلَّا مَا يُوحَىٰ إِلَيَّ ۖ إِنِّي أَخَافُ إِنْ عَصَيْتُ رَبِّي عَذَابَ يَوْمٍ عَظِيمٍ (15)
Ndi pamene Mau athu awerengedwa kwa iwo momveka, anthu amene salabadira zakukumana nafe amanena kuti, “Bweretsa Buku la Korani losiyana ndi ili kapena ulisinthe.” Nena, “Siudindo wanga kusintha Buku ili mwa chifuniro changa. Ndithudi ine ndimangotsatira zokhazo zimene zavumbulutsidwa kwa ine. Ndithudi ine ndimaopa chilango cha tsiku lalikulu ngati nditanyoza Ambuye wanga.”
قُل لَّوْ شَاءَ اللَّهُ مَا تَلَوْتُهُ عَلَيْكُمْ وَلَا أَدْرَاكُم بِهِ ۖ فَقَدْ لَبِثْتُ فِيكُمْ عُمُرًا مِّن قَبْلِهِ ۚ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (16)
Nena, “Mulungu akadafuna, ine sindikadawerengailokwainundiponsoIyesakadakupatsani inu nzeru zoti mulidziwe. Ndithu moyo wanga wonse ndakhala ndili pakati panu, Bukuli lisadavumbulutsidwe. Kodi simungathe kuzindikira?”
فَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّنِ افْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ كَذِبًا أَوْ كَذَّبَ بِآيَاتِهِ ۚ إِنَّهُ لَا يُفْلِحُ الْمُجْرِمُونَ (17)
Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu kapena amene amakana Mau ake? Ndithudi anthu ochita zoipa sadzapambana ayi
وَيَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ مَا لَا يَضُرُّهُمْ وَلَا يَنفَعُهُمْ وَيَقُولُونَ هَٰؤُلَاءِ شُفَعَاؤُنَا عِندَ اللَّهِ ۚ قُلْ أَتُنَبِّئُونَ اللَّهَ بِمَا لَا يَعْلَمُ فِي السَّمَاوَاتِ وَلَا فِي الْأَرْضِ ۚ سُبْحَانَهُ وَتَعَالَىٰ عَمَّا يُشْرِكُونَ (18)
Iwo amapembedza zinthu zina, osati Mulungu, zimene sizingathe kuwapweteka kapena kuwathandiza ndipo amati,“Izi zidzatilankhuliraifekwa Mulungu.” Nena,“Kodi inu mukumuuza Mulungu za zinthu zimene Iye sazidziwa zomwe zili kumwamba kapena pa dziko lapansi? Iye ndi Woyera ndipo akhale wa pamwamba kuposa mafano awo.”
وَمَا كَانَ النَّاسُ إِلَّا أُمَّةً وَاحِدَةً فَاخْتَلَفُوا ۚ وَلَوْلَا كَلِمَةٌ سَبَقَتْ مِن رَّبِّكَ لَقُضِيَ بَيْنَهُمْ فِيمَا فِيهِ يَخْتَلِفُونَ (19)
Mtundu wa anthu unali umodzi koma anasemphana pambuyo pake. Ndipo kukanapanda kuti Mau a Ambuye wako ananenedwa kale, mkangano wawo ukanathetsedwa
وَيَقُولُونَ لَوْلَا أُنزِلَ عَلَيْهِ آيَةٌ مِّن رَّبِّهِ ۖ فَقُلْ إِنَّمَا الْغَيْبُ لِلَّهِ فَانتَظِرُوا إِنِّي مَعَكُم مِّنَ الْمُنتَظِرِينَ (20)
Anthu osakhulupirira amanena kuti: “Kodi chifukwa ninji chizindikiro sichinaperekedwe kwa iye kuchokera kwa Ambuye wake?” Nena, “Mulungu yekha ndiye amene amadziwa chilichonse chobisika. Dikirani, nanenso ndili mmodzi mwa odikira.”
وَإِذَا أَذَقْنَا النَّاسَ رَحْمَةً مِّن بَعْدِ ضَرَّاءَ مَسَّتْهُمْ إِذَا لَهُم مَّكْرٌ فِي آيَاتِنَا ۚ قُلِ اللَّهُ أَسْرَعُ مَكْرًا ۚ إِنَّ رُسُلَنَا يَكْتُبُونَ مَا تَمْكُرُونَ (21)
Ndipo tikawalawitsa anthu mtendere pambuyo pa mavuto amene anawapeza, iwo amayamba kukonza chiwembu chotsutsa chivumbulutso chathu. Nena: “Mulungu ndi wa changu pokonza chiwembu. Ndithudi Angelo athu ali kulemba zonse zimene mumapanga za chiwembu.”
هُوَ الَّذِي يُسَيِّرُكُمْ فِي الْبَرِّ وَالْبَحْرِ ۖ حَتَّىٰ إِذَا كُنتُمْ فِي الْفُلْكِ وَجَرَيْنَ بِهِم بِرِيحٍ طَيِّبَةٍ وَفَرِحُوا بِهَا جَاءَتْهَا رِيحٌ عَاصِفٌ وَجَاءَهُمُ الْمَوْجُ مِن كُلِّ مَكَانٍ وَظَنُّوا أَنَّهُمْ أُحِيطَ بِهِمْ ۙ دَعَوُا اللَّهَ مُخْلِصِينَ لَهُ الدِّينَ لَئِنْ أَنجَيْتَنَا مِنْ هَٰذِهِ لَنَكُونَنَّ مِنَ الشَّاكِرِينَ (22)
Iyendiyeameneamakuyendetsanipamtundandiponso pa nyanja mpaka pamene inu muli m’ngalawa ndipo izo zimayendetsedwa ndi mphepo yabwino imene iwo amasangalala nayo. Koma mphepo ya mkuntho imawafikira ndipo mafunde amadza kwa iwo kuchokera ku mbali zonse ndipo iwo amaganiza kuti yawapeza ndipo amapemphera kwa Mulungu momuyeretsera chipembedzo chake. “Ngati mutipulumutse ku mavuto awa, ife tidzakhala othokoza.”
فَلَمَّا أَنجَاهُمْ إِذَا هُمْ يَبْغُونَ فِي الْأَرْضِ بِغَيْرِ الْحَقِّ ۗ يَا أَيُّهَا النَّاسُ إِنَّمَا بَغْيُكُمْ عَلَىٰ أَنفُسِكُم ۖ مَّتَاعَ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ۖ ثُمَّ إِلَيْنَا مَرْجِعُكُمْ فَنُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (23)
Ndipo pamene Mulungu adawapulumutsa, iwo adayamba kuchita zoipa pa dziko mopanda chilungamo. Oh inu anthu! Zoipa zanu simuchitira wina aliyense koma inu nokha. Chimenecho ndicho chisangalalo cha moyo wa pa dziko lapansi ndipo pambuyo pake inu mudzabwerera kwa Ife ndipo tidzakuuzani zonse zomwe mumachita
إِنَّمَا مَثَلُ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا كَمَاءٍ أَنزَلْنَاهُ مِنَ السَّمَاءِ فَاخْتَلَطَ بِهِ نَبَاتُ الْأَرْضِ مِمَّا يَأْكُلُ النَّاسُ وَالْأَنْعَامُ حَتَّىٰ إِذَا أَخَذَتِ الْأَرْضُ زُخْرُفَهَا وَازَّيَّنَتْ وَظَنَّ أَهْلُهَا أَنَّهُمْ قَادِرُونَ عَلَيْهَا أَتَاهَا أَمْرُنَا لَيْلًا أَوْ نَهَارًا فَجَعَلْنَاهَا حَصِيدًا كَأَن لَّمْ تَغْنَ بِالْأَمْسِ ۚ كَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ الْآيَاتِ لِقَوْمٍ يَتَفَكَّرُونَ (24)
Ndithudi chitsanzo cha moyo wadziko lapansi chili ngati mvula imene timatsitsa kuchokera kumwamba ndipo imameretsa zomera za pa dziko zimene amadya anthu ndi nyama mpaka pamene dziko likongola ndi zomerazo. Ndipo anthu ake amakhulupirira kuti amalipambana ndipo lamulo lathu limadza pa izo nthawi ya usiku kapena ya masana ndipo timaichita kukhala ngati mbewu yokololedwa imene kunalibe dzulo. Mmenemo ndi mmene timaululira chivumbulutso chathu kwa anthu oganiza
وَاللَّهُ يَدْعُو إِلَىٰ دَارِ السَّلَامِ وَيَهْدِي مَن يَشَاءُ إِلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (25)
Mulungu ali kuitanira ku Nyumba ya mtendere, ndi kumutsogolera yemwe wamufuna kunjira yoyenera
۞ لِّلَّذِينَ أَحْسَنُوا الْحُسْنَىٰ وَزِيَادَةٌ ۖ وَلَا يَرْهَقُ وُجُوهَهُمْ قَتَرٌ وَلَا ذِلَّةٌ ۚ أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ الْجَنَّةِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (26)
Kwa iwo onse amene amachita zabwino adzapeza zabwino ndi zoonjezerapo. Ndipo nkhope zawo sizidzakutidwa ndi fumbi kapena kunyozedwa. Iwo ndi anthu a ku Paradiso, komwe adzakhala mpaka kalekale
وَالَّذِينَ كَسَبُوا السَّيِّئَاتِ جَزَاءُ سَيِّئَةٍ بِمِثْلِهَا وَتَرْهَقُهُمْ ذِلَّةٌ ۖ مَّا لَهُم مِّنَ اللَّهِ مِنْ عَاصِمٍ ۖ كَأَنَّمَا أُغْشِيَتْ وُجُوهُهُمْ قِطَعًا مِّنَ اللَّيْلِ مُظْلِمًا ۚ أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (27)
Ndipo iwo amene amachitazoipa, malipiroawondioipamofananandizimene adachita. Mnyozo udzawakuta ndipo iwo sadzakhala ndi wina aliyense wowateteza ku chilango chochokera kwa Mulungu. Ndipo nkhope zawo zidzaoneka ngati kuti zidakutidwa ndi mbali ya mdima wa usiku. Iwo adzakhala anthu a kumoto ndipo adzakhala kumeneko nthawi zonse
وَيَوْمَ نَحْشُرُهُمْ جَمِيعًا ثُمَّ نَقُولُ لِلَّذِينَ أَشْرَكُوا مَكَانَكُمْ أَنتُمْ وَشُرَكَاؤُكُمْ ۚ فَزَيَّلْنَا بَيْنَهُمْ ۖ وَقَالَ شُرَكَاؤُهُم مَّا كُنتُمْ إِيَّانَا تَعْبُدُونَ (28)
Tsiku limene tidzawasonkhanitsa onse, Ife tidzati kwa anthu opembedza mafano: “Khalani m’malo mwanu, inu pamodzi ndi mafano anu.” Ife tidzawasiyanitsa wina ndi mnzake ndipo mafano awo adzati kwa iwo: “Sindife amene inu munali kupembedza ayi.”
فَكَفَىٰ بِاللَّهِ شَهِيدًا بَيْنَنَا وَبَيْنَكُمْ إِن كُنَّا عَنْ عِبَادَتِكُمْ لَغَافِلِينَ (29)
“Akukwanira Mulungu kukhala mboni pakati pa ife ndi inu. Ife sitidziwa kuti munali kutipembedza!”
هُنَالِكَ تَبْلُو كُلُّ نَفْسٍ مَّا أَسْلَفَتْ ۚ وَرُدُّوا إِلَى اللَّهِ مَوْلَاهُمُ الْحَقِّ ۖ وَضَلَّ عَنْهُم مَّا كَانُوا يَفْتَرُونَ (30)
Kumeneko mzimu uliwonse udzadziwa chimene unatsogoza. Iwo adzabwezedwa kwa Mulungu, Ambuye wawo woona ndipo zidzawasokonekera iwo zimene anali kupeka
قُلْ مَن يَرْزُقُكُم مِّنَ السَّمَاءِ وَالْأَرْضِ أَمَّن يَمْلِكُ السَّمْعَ وَالْأَبْصَارَ وَمَن يُخْرِجُ الْحَيَّ مِنَ الْمَيِّتِ وَيُخْرِجُ الْمَيِّتَ مِنَ الْحَيِّ وَمَن يُدَبِّرُ الْأَمْرَ ۚ فَسَيَقُولُونَ اللَّهُ ۚ فَقُلْ أَفَلَا تَتَّقُونَ (31)
Nena, “Kodi ndani amakupatsani zinthu kuchokera kumwamba ndi padziko lapansi? Kodi ndani amene amapereka mphamvu yakumva ndi kuona? Kodi ndani amatulutsa cha moyo kuchokera ku chakufa ndi kutulutsa chakufa kuchokera mu chamoyo? Ndani amene amalamulira zinthu zonse?” Onse adzanena kuti, “Ndi Mulungu.” Nena, “Kodi inu simungaope Mulungu?”
فَذَٰلِكُمُ اللَّهُ رَبُّكُمُ الْحَقُّ ۖ فَمَاذَا بَعْدَ الْحَقِّ إِلَّا الضَّلَالُ ۖ فَأَنَّىٰ تُصْرَفُونَ (32)
Ameneyondiye Mulungu,Ambuyewanuwoona. Kupatula choonadi, kodi ndi chiyani chimene chingakhalepo osati chisokonekero? Nanga ndi chifukwa chiyani inu muli kusocheretsedwa
كَذَٰلِكَ حَقَّتْ كَلِمَتُ رَبِّكَ عَلَى الَّذِينَ فَسَقُوا أَنَّهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (33)
Kotero ndi mmene liwu la Ambuye wako latsimikizidwira kwa anthu ochita zoipa ndipo iwo sadzakhulupirira
قُلْ هَلْ مِن شُرَكَائِكُم مَّن يَبْدَأُ الْخَلْقَ ثُمَّ يُعِيدُهُ ۚ قُلِ اللَّهُ يَبْدَأُ الْخَلْقَ ثُمَّ يُعِيدُهُ ۖ فَأَنَّىٰ تُؤْفَكُونَ (34)
Nena, “Kodi ena a mafano anu angalenge china chake ndi kuchibwezeranso?” Nena, “Mulungu anayambitsa chilengedwendipoadzachibwezeranso.Nangandichifukwa chiyani mukusocheretsedwa?”
قُلْ هَلْ مِن شُرَكَائِكُم مَّن يَهْدِي إِلَى الْحَقِّ ۚ قُلِ اللَّهُ يَهْدِي لِلْحَقِّ ۗ أَفَمَن يَهْدِي إِلَى الْحَقِّ أَحَقُّ أَن يُتَّبَعَ أَمَّن لَّا يَهِدِّي إِلَّا أَن يُهْدَىٰ ۖ فَمَا لَكُمْ كَيْفَ تَحْكُمُونَ (35)
Nena, “Kodi mafano anu angakulondolereni ku choonadi?” Nena, “Mulungu yekha ndiye amene angakulondolereni ku choonadi. Kodi ndani amene ayenera kutsatidwa? Iye amene amakulondolerani ku choonadi kapena iye amene sangathe chifukwa chakuti nayenso afuna kuti atsogozedwe? Kodi mukusiyanitsa bwanji?”
وَمَا يَتَّبِعُ أَكْثَرُهُمْ إِلَّا ظَنًّا ۚ إِنَّ الظَّنَّ لَا يُغْنِي مِنَ الْحَقِّ شَيْئًا ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ بِمَا يَفْعَلُونَ (36)
Ambiri a iwo satsatira china chilichonse koma zongoganiza. Komatu nkhani zongoganiza sizithandiza mu choonadi chilichonse. Ndithu Mulungu amadziwa zonse zimene iwo amachita
وَمَا كَانَ هَٰذَا الْقُرْآنُ أَن يُفْتَرَىٰ مِن دُونِ اللَّهِ وَلَٰكِن تَصْدِيقَ الَّذِي بَيْنَ يَدَيْهِ وَتَفْصِيلَ الْكِتَابِ لَا رَيْبَ فِيهِ مِن رَّبِّ الْعَالَمِينَ (37)
Sizingatheke kuti Korani iyi ikhale yopeka ndiponso kuti siinachokere kwa Mulungu. Koma iyo imatsimikiza zinthu zonse zimene zidavumbulutsidwa kale ndi kufotokoza Mau a m’buku la Mulungu. Ilo ndi losakaikitsa ndipo ndi lochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse
أَمْ يَقُولُونَ افْتَرَاهُ ۖ قُلْ فَأْتُوا بِسُورَةٍ مِّثْلِهِ وَادْعُوا مَنِ اسْتَطَعْتُم مِّن دُونِ اللَّهِ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (38)
Kapena iwo amati “Iye walipeka!” Nena: “Nanunso pekani mutu umodzi wolingana nalo ndipo itanani amene mungathe kuwaitana osakhala Mulungu ngati muli angwiro!”
بَلْ كَذَّبُوا بِمَا لَمْ يُحِيطُوا بِعِلْمِهِ وَلَمَّا يَأْتِهِمْ تَأْوِيلُهُ ۚ كَذَٰلِكَ كَذَّبَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۖ فَانظُرْ كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الظَّالِمِينَ (39)
Iyayi. Iwo ali kutsutsa zinthu zimene sadziwa chilichonse cha izo pamene choona chake chisanafike kwa iwo. Mmenemonso ndi mmene anthu akale adakanira. Taonani zidali bwanji zotsatira za anthu ochita zoipa
وَمِنْهُم مَّن يُؤْمِنُ بِهِ وَمِنْهُم مَّن لَّا يُؤْمِنُ بِهِ ۚ وَرَبُّكَ أَعْلَمُ بِالْمُفْسِدِينَ (40)
Ena a iwo amakhulupirira mu ilo pamene ena sakhulupirira ayi. Ndipo Ambuye wako amawadziwa kwambiri anthu owononga
وَإِن كَذَّبُوكَ فَقُل لِّي عَمَلِي وَلَكُمْ عَمَلُكُمْ ۖ أَنتُم بَرِيئُونَ مِمَّا أَعْمَلُ وَأَنَا بَرِيءٌ مِّمَّا تَعْمَلُونَ (41)
Ngati iwo akukana iwe, nena: “Ine ndili ndi ntchito zanga ndipo nanunso muli ndi ntchito zanu. Inu muli kutali ndi zimene ndikuchita ndipo nanenso ndili kutali ndi zimene mukuchita.”
وَمِنْهُم مَّن يَسْتَمِعُونَ إِلَيْكَ ۚ أَفَأَنتَ تُسْمِعُ الصُّمَّ وَلَوْ كَانُوا لَا يَعْقِلُونَ (42)
Ena a iwo amakumvera iwe. Kodi iwe ungawapangitse agonthi kuti amve ngakhale kuti safuna kuzindikira
وَمِنْهُم مَّن يَنظُرُ إِلَيْكَ ۚ أَفَأَنتَ تَهْدِي الْعُمْيَ وَلَوْ كَانُوا لَا يُبْصِرُونَ (43)
Ena a iwo amakuyang’ana iwe. Kodi iwe ungalangize njira kwa anthu a khungu pamene saona china chilichonse
إِنَّ اللَّهَ لَا يَظْلِمُ النَّاسَ شَيْئًا وَلَٰكِنَّ النَّاسَ أَنفُسَهُمْ يَظْلِمُونَ (44)
Ndithudi Mulungu salakwira anthu koma kuti anthu eni ake amadzipondereza okha
وَيَوْمَ يَحْشُرُهُمْ كَأَن لَّمْ يَلْبَثُوا إِلَّا سَاعَةً مِّنَ النَّهَارِ يَتَعَارَفُونَ بَيْنَهُمْ ۚ قَدْ خَسِرَ الَّذِينَ كَذَّبُوا بِلِقَاءِ اللَّهِ وَمَا كَانُوا مُهْتَدِينَ (45)
Akumbutseni zatsiku limene adzawasonkhanitsa onse. Tsiku limeneli adzaona ngati kuti adangokhala ora limodzi lamasana. Iwo adzazindikirana wina ndi mnzake. Ndithudi olephera adzakhala iwo amene adakana za kukumana ndi Mulungu ndipo sanali otsogozedwa
وَإِمَّا نُرِيَنَّكَ بَعْضَ الَّذِي نَعِدُهُمْ أَوْ نَتَوَفَّيَنَّكَ فَإِلَيْنَا مَرْجِعُهُمْ ثُمَّ اللَّهُ شَهِيدٌ عَلَىٰ مَا يَفْعَلُونَ (46)
Kaya tikuonetsa zina za zimene tawalonjeza kapena kukuchititsa kuti ufe, ndi kwa Ife kumene onse adzabwerera ndipo Mulungu ndi mboni pa zimene akuchita
وَلِكُلِّ أُمَّةٍ رَّسُولٌ ۖ فَإِذَا جَاءَ رَسُولُهُمْ قُضِيَ بَيْنَهُم بِالْقِسْطِ وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ (47)
Ndithudi m’mbadwo uliwonse uli ndi Mtumwi wake ndipo pamene Mtumwi wawo adza, nkhani yawo idzaweruzidwa mwa chilungamo pakati pawo ndipo sadzaponderezedwa
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا الْوَعْدُ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (48)
Iwo amanena: “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati ukunena zoona?”
قُل لَّا أَمْلِكُ لِنَفْسِي ضَرًّا وَلَا نَفْعًا إِلَّا مَا شَاءَ اللَّهُ ۗ لِكُلِّ أُمَّةٍ أَجَلٌ ۚ إِذَا جَاءَ أَجَلُهُمْ فَلَا يَسْتَأْخِرُونَ سَاعَةً ۖ وَلَا يَسْتَقْدِمُونَ (49)
Nena, “Ine ndilibe mphamvu yopeza zabwino kapena kupewa choipa chimene chingadze pa ine kupatula ndi chifuniro cha Mulungu. M’badwo uliwonse uli ndi nthawi imene idakhazikitsidwa kale. Ndipo pamene nthawi yawo idza, iwo sadzatha kuichedwetsa kapena kuifulumizitsa.”
قُلْ أَرَأَيْتُمْ إِنْ أَتَاكُمْ عَذَابُهُ بَيَاتًا أَوْ نَهَارًا مَّاذَا يَسْتَعْجِلُ مِنْهُ الْمُجْرِمُونَ (50)
Nena “Ndiuzeni! Ngati chilango chake chitadza pa inu nthawi ya usiku kapena masana kodi ndi gawo liti limene anthu ochita zoipa angalifulumize?”
أَثُمَّ إِذَا مَا وَقَعَ آمَنتُم بِهِ ۚ آلْآنَ وَقَدْ كُنتُم بِهِ تَسْتَعْجِلُونَ (51)
Kodi inu mudzakhulupirira pamene chidza pa inu? Nanga! Tsopano siuja munali kuchifulumizitsa
ثُمَّ قِيلَ لِلَّذِينَ ظَلَمُوا ذُوقُوا عَذَابَ الْخُلْدِ هَلْ تُجْزَوْنَ إِلَّا بِمَا كُنتُمْ تَكْسِبُونَ (52)
Ndipo kudzanenedwa kwa anthu ochita zoipa! “Lawani chilango chosatha! Inu simudzalipidwa china chilichonse kupatula zimene munali kuchita.”
۞ وَيَسْتَنبِئُونَكَ أَحَقٌّ هُوَ ۖ قُلْ إِي وَرَبِّي إِنَّهُ لَحَقٌّ ۖ وَمَا أَنتُم بِمُعْجِزِينَ (53)
Ndipo amakufunsa kuti uwauze: “Kodi ndizoona?” Nena, “Indedi, pali Ambuye. Zimenezo ndi zoonadi ndipo inu simungazithawe ayi.”
وَلَوْ أَنَّ لِكُلِّ نَفْسٍ ظَلَمَتْ مَا فِي الْأَرْضِ لَافْتَدَتْ بِهِ ۗ وَأَسَرُّوا النَّدَامَةَ لَمَّا رَأَوُا الْعَذَابَ ۖ وَقُضِيَ بَيْنَهُم بِالْقِسْطِ ۚ وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ (54)
Kukadakhala kuti munthu aliyense wochita zoipa anali ndi zinthu zonse zimene zili padziko lapansi ndipo amafuna kuzipereka ngati dipo loti adziombolere, ndipo iwo akanamva chisoni m’mitima yawo pamene akadaona chilango ndipo iwo adzaweruzidwa mwachilungamo ndiponso sadzaponderezedwa ai
أَلَا إِنَّ لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۗ أَلَا إِنَّ وَعْدَ اللَّهِ حَقٌّ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (55)
Ndithudi mosakaika Mulungu ndiye Mwini wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndi padziko lapansi. Ndithudi mosakaika lonjezo la Mulungu ndi loona. Koma ambiri a iwo sadziwa
هُوَ يُحْيِي وَيُمِيتُ وَإِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (56)
Iye ndiye amene amapereka moyo ndipo amaperekanso imfa, ndipo ndi kwa Iye kumene inu nonse mudzabwerera
يَا أَيُّهَا النَّاسُ قَدْ جَاءَتْكُم مَّوْعِظَةٌ مِّن رَّبِّكُمْ وَشِفَاءٌ لِّمَا فِي الصُّدُورِ وَهُدًى وَرَحْمَةٌ لِّلْمُؤْمِنِينَ (57)
Oh inu anthu! Chilangizo chabwino chadza kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu, chochiritsa zimene zili m’mitima mwanu, utsogoleri ndi madalitso kwa anthu okhulupirira m’choonadi
قُلْ بِفَضْلِ اللَّهِ وَبِرَحْمَتِهِ فَبِذَٰلِكَ فَلْيَفْرَحُوا هُوَ خَيْرٌ مِّمَّا يَجْمَعُونَ (58)
Nena, “M’chisomo ndi M’chisoni cha Mulungu asiyeni asangalale. Chifukwa izi ndi zabwino kuposa zimene akusonkhanitsa.”
قُلْ أَرَأَيْتُم مَّا أَنزَلَ اللَّهُ لَكُم مِّن رِّزْقٍ فَجَعَلْتُم مِّنْهُ حَرَامًا وَحَلَالًا قُلْ آللَّهُ أَذِنَ لَكُمْ ۖ أَمْ عَلَى اللَّهِ تَفْتَرُونَ (59)
Ndiuzeni kodi Mulungu wakufulumizirani chiani? Ndipo mwazisandutsa zina kukhala zololedwa ndi zina zoletsedwa. Nena, Kodi Mulungu wakulolani kapena mukumpekera zabodza
وَمَا ظَنُّ الَّذِينَ يَفْتَرُونَ عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۗ إِنَّ اللَّهَ لَذُو فَضْلٍ عَلَى النَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَشْكُرُونَ (60)
Kodi anthu amene amapeka mabodza okhudza Mulungu amaganiza chiyani za tsiku la kuuka kwa akufa? Ndithudi Mulungu ndi wabwino kwa anthu koma ambiri a iwo sathokoza ayi
وَمَا تَكُونُ فِي شَأْنٍ وَمَا تَتْلُو مِنْهُ مِن قُرْآنٍ وَلَا تَعْمَلُونَ مِنْ عَمَلٍ إِلَّا كُنَّا عَلَيْكُمْ شُهُودًا إِذْ تُفِيضُونَ فِيهِ ۚ وَمَا يَعْزُبُ عَن رَّبِّكَ مِن مِّثْقَالِ ذَرَّةٍ فِي الْأَرْضِ وَلَا فِي السَّمَاءِ وَلَا أَصْغَرَ مِن ذَٰلِكَ وَلَا أَكْبَرَ إِلَّا فِي كِتَابٍ مُّبِينٍ (61)
Chilichonse chimene uzichita ndiponso gawo lililonse limene uzilakatula la Korani ndipo chilichonse chimene muzichita, Ife ndife mboni pa icho pamene muli kuchichita. Palibe chobisika kwa Ambuye wanu, ngakhale chochepa ngati nyerere padziko lapansi kapena kumwamba. Palibe chaching’ono choposa ichi kapena chachikulu choposa ichi chimene sichilembedwa mu Buku
أَلَا إِنَّ أَوْلِيَاءَ اللَّهِ لَا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (62)
Mosakaika! Ndithudi abwenzi a Mulungu ndipo amamukonda Iye kwambiri, sadzakhala ndi mantha ndiponso sadzadandaula
الَّذِينَ آمَنُوا وَكَانُوا يَتَّقُونَ (63)
Iwo amene adakhulupirira ndipo anali kuopa Mulungu
لَهُمُ الْبُشْرَىٰ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا وَفِي الْآخِرَةِ ۚ لَا تَبْدِيلَ لِكَلِمَاتِ اللَّهِ ۚ ذَٰلِكَ هُوَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ (64)
Kwa iwo ndi chisangalalo m’dziko lino ndiponso m’dziko limene lili n’kudza. Palibe kusintha kulikonse m’Mau a Mulungu. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu
وَلَا يَحْزُنكَ قَوْلُهُمْ ۘ إِنَّ الْعِزَّةَ لِلَّهِ جَمِيعًا ۚ هُوَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (65)
Ndipo mawu awo asakukhumudwitse iwe. Ndithudi mphamvu zonse Mwini wake ndi Mulungu. Iye ndi wakumva ndi wodziwa
أَلَا إِنَّ لِلَّهِ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَمَن فِي الْأَرْضِ ۗ وَمَا يَتَّبِعُ الَّذِينَ يَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ شُرَكَاءَ ۚ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا الظَّنَّ وَإِنْ هُمْ إِلَّا يَخْرُصُونَ (66)
Mosakaika! Ndithudi Mulungu ndiye mwini wa zimene zili kumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo onse amene amapembedza milungu yabodza satsatira china chilichonse koma zinthu zopanda pake ndipo iwo amangopeka mabodza
هُوَ الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ اللَّيْلَ لِتَسْكُنُوا فِيهِ وَالنَّهَارَ مُبْصِرًا ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يَسْمَعُونَ (67)
Iye ndiye amene adakupangirani usiku kuti muzipumula ndi usana kuti muziona. Ndithudi mu izi muli zizindikiro kwa anthu amene amamva
قَالُوا اتَّخَذَ اللَّهُ وَلَدًا ۗ سُبْحَانَهُ ۖ هُوَ الْغَنِيُّ ۖ لَهُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۚ إِنْ عِندَكُم مِّن سُلْطَانٍ بِهَٰذَا ۚ أَتَقُولُونَ عَلَى اللَّهِ مَا لَا تَعْلَمُونَ (68)
Iwo amanena kuti: “Mulungu wabereka mwana wamwamuna.” Mulungu ayeretsedwe ndi zimenezo. “Iye ndi Wolemera. Zake ndi zonse zimene zili m’lengalenga ndi padzikolapansi. Paichiinumulibeumboni. Kodimukunena zinthu zokhudza Mulungu zimene simuzidziwa?”
قُلْ إِنَّ الَّذِينَ يَفْتَرُونَ عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ لَا يُفْلِحُونَ (69)
Nena, “Ndithudi iwo amene amapeka bodza lokhudza Mulungu sadzapambana ayi.”
مَتَاعٌ فِي الدُّنْيَا ثُمَّ إِلَيْنَا مَرْجِعُهُمْ ثُمَّ نُذِيقُهُمُ الْعَذَابَ الشَّدِيدَ بِمَا كَانُوا يَكْفُرُونَ (70)
Chisangalalo cha kanthawi kochepa ka m’dziko lapansi ndipo ndi kwa Ife kumene adzabwerera ndipo Ife tidzawalawitsa chilango chowawa chifukwa cha kukana kwawo
۞ وَاتْلُ عَلَيْهِمْ نَبَأَ نُوحٍ إِذْ قَالَ لِقَوْمِهِ يَا قَوْمِ إِن كَانَ كَبُرَ عَلَيْكُم مَّقَامِي وَتَذْكِيرِي بِآيَاتِ اللَّهِ فَعَلَى اللَّهِ تَوَكَّلْتُ فَأَجْمِعُوا أَمْرَكُمْ وَشُرَكَاءَكُمْ ثُمَّ لَا يَكُنْ أَمْرُكُمْ عَلَيْكُمْ غُمَّةً ثُمَّ اقْضُوا إِلَيَّ وَلَا تُنظِرُونِ (71)
Ndipo awerengere iwo za nkhani ya Nowa pamene iye adanena kwa anthu ake kuti: “oh! Inu anthu anga! Ngati muli kuipidwa ndi kukhala kwanga pakati panu ndi kukukumbutsani mawu a Mulungu, dziwani kuti ine ndaika chikhulupiliro changa mwa Mulungu motero inu musonkhanitse zopanga zanu ndi mafano anu ndipo inu musapange chiwembu mseri ayi. Gamulani chiweruzo chanu pa ine ndipo musandipatse nthawi ayi.”
فَإِن تَوَلَّيْتُمْ فَمَا سَأَلْتُكُم مِّنْ أَجْرٍ ۖ إِنْ أَجْرِيَ إِلَّا عَلَى اللَّهِ ۖ وَأُمِرْتُ أَنْ أَكُونَ مِنَ الْمُسْلِمِينَ (72)
“Ndipo ngati muyamba kusakhulupirira ine sindidakupempheni mphotho. Mphotho yanga ili ndi Mulungu ndiponso ndalamulidwa kuti ndikhale mmodzi mwa ogonjera malamulo a Mulungu.”
فَكَذَّبُوهُ فَنَجَّيْنَاهُ وَمَن مَّعَهُ فِي الْفُلْكِ وَجَعَلْنَاهُمْ خَلَائِفَ وَأَغْرَقْنَا الَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا ۖ فَانظُرْ كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الْمُنذَرِينَ (73)
Koma iwo adamukana. Ife tidamupulumutsa Nowa pamodzi ndi iwo amene adali naye m’chombo ndipo tinawapanga iwo kukhala olowa m’malo padziko ndipo tidamiza onse amene adakana zonena zathu. Ona, adali bwanji mapeto a anthu ochenjezedwa
ثُمَّ بَعَثْنَا مِن بَعْدِهِ رُسُلًا إِلَىٰ قَوْمِهِمْ فَجَاءُوهُم بِالْبَيِّنَاتِ فَمَا كَانُوا لِيُؤْمِنُوا بِمَا كَذَّبُوا بِهِ مِن قَبْلُ ۚ كَذَٰلِكَ نَطْبَعُ عَلَىٰ قُلُوبِ الْمُعْتَدِينَ (74)
Zitatha izi, tidatumiza Atumwi ena kwa anthu awo. Iwo adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka koma iwo sanali okhulupirira mzimene adazikana kale. Mmenemo ndi mmene timadindira zidindo mitima ya anthu ochita zinthu mopyora muyeso
ثُمَّ بَعَثْنَا مِن بَعْدِهِم مُّوسَىٰ وَهَارُونَ إِلَىٰ فِرْعَوْنَ وَمَلَئِهِ بِآيَاتِنَا فَاسْتَكْبَرُوا وَكَانُوا قَوْمًا مُّجْرِمِينَ (75)
Pambuyo pake tinatumiza Mose ndi Aroni ndi zizindikiro zathu kwa Farawo ndi nduna zake. Koma iwo adadzikweza ndipo anali anthu oipa
فَلَمَّا جَاءَهُمُ الْحَقُّ مِنْ عِندِنَا قَالُوا إِنَّ هَٰذَا لَسِحْرٌ مُّبِينٌ (76)
Pamene chidadza choonadi kwa iwo kuchokera kwa Ife, iwo adati: “Ndithudi awa ndi matsenga woonekereratu.”
قَالَ مُوسَىٰ أَتَقُولُونَ لِلْحَقِّ لَمَّا جَاءَكُمْ ۖ أَسِحْرٌ هَٰذَا وَلَا يُفْلِحُ السَّاحِرُونَ (77)
Mose adati: “Kodi inu mukunena choona pamene chakufikani kuti ndi matsenga? Wamatsenga sapambana ai.”
قَالُوا أَجِئْتَنَا لِتَلْفِتَنَا عَمَّا وَجَدْنَا عَلَيْهِ آبَاءَنَا وَتَكُونَ لَكُمَا الْكِبْرِيَاءُ فِي الْأَرْضِ وَمَا نَحْنُ لَكُمَا بِمُؤْمِنِينَ (78)
Iwo adati: “Kodi iwe wadza kuti utitembenuze m’zimene tidapeza makolo athu akuchita ndi cholinga chakuti inu anthu awiri, mukhale akuluakulu m’dziko? Ife sitikukhulupirirani anthu awirinu.”
وَقَالَ فِرْعَوْنُ ائْتُونِي بِكُلِّ سَاحِرٍ عَلِيمٍ (79)
Ndipo Farawo adati: “Bweretsani wa amatsenga aliyense wodziwa kwa ine.”
فَلَمَّا جَاءَ السَّحَرَةُ قَالَ لَهُم مُّوسَىٰ أَلْقُوا مَا أَنتُم مُّلْقُونَ (80)
Pamene amatsenga adadza, Mose adati kwa izo: “Ponyani zonse zimene mufuna kuponya.”
فَلَمَّا أَلْقَوْا قَالَ مُوسَىٰ مَا جِئْتُم بِهِ السِّحْرُ ۖ إِنَّ اللَّهَ سَيُبْطِلُهُ ۖ إِنَّ اللَّهَ لَا يُصْلِحُ عَمَلَ الْمُفْسِدِينَ (81)
Ndipo pamene adaponya pansi ndodo zawo Mose adati: “Amenewa ndi matsenga ndipo Mulungu, ndithudi, adzagonjetsa matsenga anu. Ndithudi Mulungu savomera ntchito za anthu ochita zoipa kuti zipambane.”
وَيُحِقُّ اللَّهُ الْحَقَّ بِكَلِمَاتِهِ وَلَوْ كَرِهَ الْمُجْرِمُونَ (82)
Mulungu, ndi Mau ake, amakhazikitsa choonadi ngakhale kuti anthu oipa sakondwera
فَمَا آمَنَ لِمُوسَىٰ إِلَّا ذُرِّيَّةٌ مِّن قَوْمِهِ عَلَىٰ خَوْفٍ مِّن فِرْعَوْنَ وَمَلَئِهِمْ أَن يَفْتِنَهُمْ ۚ وَإِنَّ فِرْعَوْنَ لَعَالٍ فِي الْأَرْضِ وَإِنَّهُ لَمِنَ الْمُسْرِفِينَ (83)
Palibe amene adamukhulupirira Mose kupatula ana a anthu ake chifukwa chomuopa Farawo ndi nduna zake kuti angawavutitse. Ndithudi Farawo adali wokakala moyo m’dzikomo ndiponso adali m’modzi wa anthu oononga
وَقَالَ مُوسَىٰ يَا قَوْمِ إِن كُنتُمْ آمَنتُم بِاللَّهِ فَعَلَيْهِ تَوَكَّلُوا إِن كُنتُم مُّسْلِمِينَ (84)
Mose adati: “oh inu anthu anga! Ngati inu mwakhulupirira mwa Mulungu, mudalire mwa Iye yekha, ngatiinumulianthuokhulupirira.”
فَقَالُوا عَلَى اللَّهِ تَوَكَّلْنَا رَبَّنَا لَا تَجْعَلْنَا فِتْنَةً لِّلْقَوْمِ الظَّالِمِينَ (85)
Iwoadati:“Timadalira mwa Mulungu. oh Ambuye wathu! Musalole kuti ife tizunzike m’manja mwa anthu oipa.”
وَنَجِّنَا بِرَحْمَتِكَ مِنَ الْقَوْمِ الْكَافِرِينَ (86)
“Tipulumutseni mwa chisomo chanu kwa anthu osakhulupirira.”
وَأَوْحَيْنَا إِلَىٰ مُوسَىٰ وَأَخِيهِ أَن تَبَوَّآ لِقَوْمِكُمَا بِمِصْرَ بُيُوتًا وَاجْعَلُوا بُيُوتَكُمْ قِبْلَةً وَأَقِيمُوا الصَّلَاةَ ۗ وَبَشِّرِ الْمُؤْمِنِينَ (87)
Tidavumbulutsa Mau athu kwa Mose ndi m’bale wake ponena kuti: “Amangireni nyumba anthu anu m’dziko la Aiguputo ndipo mupange nyumba zanu kukhala malo opemphereramo. Pitirizani mapemphero ndipo muwauze nkhani yabwino anthu okhulupirira.”
وَقَالَ مُوسَىٰ رَبَّنَا إِنَّكَ آتَيْتَ فِرْعَوْنَ وَمَلَأَهُ زِينَةً وَأَمْوَالًا فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا رَبَّنَا لِيُضِلُّوا عَن سَبِيلِكَ ۖ رَبَّنَا اطْمِسْ عَلَىٰ أَمْوَالِهِمْ وَاشْدُدْ عَلَىٰ قُلُوبِهِمْ فَلَا يُؤْمِنُوا حَتَّىٰ يَرَوُا الْعَذَابَ الْأَلِيمَ (88)
Ndipo Mose adati: “Ambuye wathu! Inu mwamupatsa Farao ndi anthu ake zinthu zabwino ndi chuma m’moyo uno, Ambuye wathu, kuti asocheretse anthu ku njira yanu. Ambuye wathu! onongani chuma chawo ndipo limbitsani mitima yawo, kuti iwo asadzakhulupirire mpaka pamene aona chilango chowawa.”
قَالَ قَدْ أُجِيبَت دَّعْوَتُكُمَا فَاسْتَقِيمَا وَلَا تَتَّبِعَانِّ سَبِيلَ الَّذِينَ لَا يَعْلَمُونَ (89)
Mulungu adati: “Pempho lanu layankhidwa. Kotero pitirizani kuyenda m’njira yoyenera nonse awiri ndipo musatsatire njira ya anthu osadziwa.”
۞ وَجَاوَزْنَا بِبَنِي إِسْرَائِيلَ الْبَحْرَ فَأَتْبَعَهُمْ فِرْعَوْنُ وَجُنُودُهُ بَغْيًا وَعَدْوًا ۖ حَتَّىٰ إِذَا أَدْرَكَهُ الْغَرَقُ قَالَ آمَنتُ أَنَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا الَّذِي آمَنَتْ بِهِ بَنُو إِسْرَائِيلَ وَأَنَا مِنَ الْمُسْلِمِينَ (90)
Ife tidatsogolera ana a Israyeli kuoloka nyanja. Farawo, pamodzi ndi magulu ake a nkhondo, adawatsatira ndi chiwembu ndiponso udani. Kufikira pamene anali kumira, Farawo adati: “Ndikhulupirira kuti kulibe mulungu koma Iye amene ana a Israyeli amamukhulupirira. Ndipo ine ndili m’modzi wa odzipereka pogonjera.”
آلْآنَ وَقَدْ عَصَيْتَ قَبْلُ وَكُنتَ مِنَ الْمُفْسِدِينَ (91)
“Chiyani? Tsopano ndiye ukukhulupirira pamene iwe udanyoza kale ndipo udali mmodzi wa anthu oononga?”
فَالْيَوْمَ نُنَجِّيكَ بِبَدَنِكَ لِتَكُونَ لِمَنْ خَلْفَكَ آيَةً ۚ وَإِنَّ كَثِيرًا مِّنَ النَّاسِ عَنْ آيَاتِنَا لَغَافِلُونَ (92)
“Lero, Ife tidzasunga thupi lako, kuti ukhale chizindikiro kwa onse amene adza m’mbuyo mwako. Ndithudi anthu ambiri ndi oiwala zizindikiro zathu.”
وَلَقَدْ بَوَّأْنَا بَنِي إِسْرَائِيلَ مُبَوَّأَ صِدْقٍ وَرَزَقْنَاهُم مِّنَ الطَّيِّبَاتِ فَمَا اخْتَلَفُوا حَتَّىٰ جَاءَهُمُ الْعِلْمُ ۚ إِنَّ رَبَّكَ يَقْضِي بَيْنَهُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ فِيمَا كَانُوا فِيهِ يَخْتَلِفُونَ (93)
Ndithudi Ife tidawakhazika ana a Israyeli malo abwino ndipo tidawapatsa zinthu zabwino. Ndipo iwo sadatsutsane mpaka pamene nzeru zinadza kwa iwo. Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo pa zinthu zimene amasiyana pa tsiku la kuuka kwa akufa
فَإِن كُنتَ فِي شَكٍّ مِّمَّا أَنزَلْنَا إِلَيْكَ فَاسْأَلِ الَّذِينَ يَقْرَءُونَ الْكِتَابَ مِن قَبْلِكَ ۚ لَقَدْ جَاءَكَ الْحَقُّ مِن رَّبِّكَ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ الْمُمْتَرِينَ (94)
Ngati ukaika pa zimene tavumbulutsa kwa iwe, afunse iwo amene adawerenga Buku la kale iwe usanadze. Ndithudi, choonadi chadza kwa iwe kuchokera kwa Ambuyewakokoterousakhalemmodziwaokaika
وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ الَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِ اللَّهِ فَتَكُونَ مِنَ الْخَاسِرِينَ (95)
Ndipo usakhale mmodzi wa anthu amene adakana chivumbulutso cha Mulungu chifukwa ngati utero udzakhala mmodzi olephera
إِنَّ الَّذِينَ حَقَّتْ عَلَيْهِمْ كَلِمَتُ رَبِّكَ لَا يُؤْمِنُونَ (96)
Ndithudi iwo amene Mau a Ambuye wawo akwaniritsidwa, sadzakhulupirira
وَلَوْ جَاءَتْهُمْ كُلُّ آيَةٍ حَتَّىٰ يَرَوُا الْعَذَابَ الْأَلِيمَ (97)
Ngakhale atalandira chizindikiro china chilichonse mpaka pamene adzaone chilango chowawa
فَلَوْلَا كَانَتْ قَرْيَةٌ آمَنَتْ فَنَفَعَهَا إِيمَانُهَا إِلَّا قَوْمَ يُونُسَ لَمَّا آمَنُوا كَشَفْنَا عَنْهُمْ عَذَابَ الْخِزْيِ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا وَمَتَّعْنَاهُمْ إِلَىٰ حِينٍ (98)
Kodi padalinso mzinda wina umene unakhulupirira ndipo kuti chikhulupiriro chake chinaupulumutsa kupatula anthu a Yona, pamene iwo adakhulupirira? Ife tidawachotsera chilango chochititsa manyazi m’moyo uno ndi kuwalola kusangalala pa kanthawi kochepa
وَلَوْ شَاءَ رَبُّكَ لَآمَنَ مَن فِي الْأَرْضِ كُلُّهُمْ جَمِيعًا ۚ أَفَأَنتَ تُكْرِهُ النَّاسَ حَتَّىٰ يَكُونُوا مُؤْمِنِينَ (99)
Ngati Ambuye wako akadafuna, anthu onse a pa dziko lapansi akanakhulupirira mwa Iye yekha. Kodi iwe ungakakamize anthu kuti akhale okhulupirira
وَمَا كَانَ لِنَفْسٍ أَن تُؤْمِنَ إِلَّا بِإِذْنِ اللَّهِ ۚ وَيَجْعَلُ الرِّجْسَ عَلَى الَّذِينَ لَا يَعْقِلُونَ (100)
Palibe munthu angakhulupirire pokhapokha m’chifuniro cha Mulungu. Iye adzagwetsa mkwiyo wake pa anthu opanda nzeru
قُلِ انظُرُوا مَاذَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ وَمَا تُغْنِي الْآيَاتُ وَالنُّذُرُ عَن قَوْمٍ لَّا يُؤْمِنُونَ (101)
Nena, “Taonani zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi!” Koma zizindikiro ndiponso anthu opereka chenjezo, siaphindu kwa anthu osakhulupirira
فَهَلْ يَنتَظِرُونَ إِلَّا مِثْلَ أَيَّامِ الَّذِينَ خَلَوْا مِن قَبْلِهِمْ ۚ قُلْ فَانتَظِرُوا إِنِّي مَعَكُم مِّنَ الْمُنتَظِرِينَ (102)
Kodi pali chimene akudikira kupatula zimene zinaoneka m’masiku a anthu omwe analipo iwo asanadze? Nena, “Dikirani, ine ndili nanu ngati mmodzi mwa odikira.”
ثُمَّ نُنَجِّي رُسُلَنَا وَالَّذِينَ آمَنُوا ۚ كَذَٰلِكَ حَقًّا عَلَيْنَا نُنجِ الْمُؤْمِنِينَ (103)
Pambuyo pake tinawapulumutsa Atumwi athu pamodzi ndi amene amakhulupirira. Kotero ndi koyenera kwa Ife kupulumutsa anthu okhulupirira
قُلْ يَا أَيُّهَا النَّاسُ إِن كُنتُمْ فِي شَكٍّ مِّن دِينِي فَلَا أَعْبُدُ الَّذِينَ تَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ وَلَٰكِنْ أَعْبُدُ اللَّهَ الَّذِي يَتَوَفَّاكُمْ ۖ وَأُمِرْتُ أَنْ أَكُونَ مِنَ الْمُؤْمِنِينَ (104)
Nena, “oh inu anthu! Ngati inu muli ndi chikaiko pa chipembedzo changa, dziwani kuti ine sindidzapembedza zomwe mukuzipembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni. Koma ine ndikupembedza Mulungu amene amakuphani nonse ndipo ndalamulidwa kuti ndikhale mmodzi wa anthu okhulupirira.”
وَأَنْ أَقِمْ وَجْهَكَ لِلدِّينِ حَنِيفًا وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ الْمُشْرِكِينَ (105)
Ine ndidalamulidwa kuti, “Tsatira chipempedzo chopembedza Mulungu mmodzi ndipo usakhale mmodzi mwa anthu opembedza mafano.”
وَلَا تَدْعُ مِن دُونِ اللَّهِ مَا لَا يَنفَعُكَ وَلَا يَضُرُّكَ ۖ فَإِن فَعَلْتَ فَإِنَّكَ إِذًا مِّنَ الظَّالِمِينَ (106)
Ndipo usapembedze wina aliyense yemwe si Mulungu, amene sangathe kukuthandiza kapena kukuononga chifukwa, utatero, udzakhala mmodzi wa wochita zoipa
وَإِن يَمْسَسْكَ اللَّهُ بِضُرٍّ فَلَا كَاشِفَ لَهُ إِلَّا هُوَ ۖ وَإِن يُرِدْكَ بِخَيْرٍ فَلَا رَادَّ لِفَضْلِهِ ۚ يُصِيبُ بِهِ مَن يَشَاءُ مِنْ عِبَادِهِ ۚ وَهُوَ الْغَفُورُ الرَّحِيمُ (107)
Ngati Mulungu akupatsa mavuto palibe wina amene angawachotse kupatula Iye yekha ndipo ngati Iye akufunira zabwino, palibe wina amene angabweze zokoma zake zimene Iye amapereka kwa kapolo wake amene Iye wamufuna. Ndipo Iye ndi wokhululukira ndiponso Mwini chisoni chosatha
قُلْ يَا أَيُّهَا النَّاسُ قَدْ جَاءَكُمُ الْحَقُّ مِن رَّبِّكُمْ ۖ فَمَنِ اهْتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهْتَدِي لِنَفْسِهِ ۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيْهَا ۖ وَمَا أَنَا عَلَيْكُم بِوَكِيلٍ (108)
Nena, “Oh inu anthu! Choonadi chadza kwa inu kuchokerakwaAmbuyewanu.Aliyenseameneatsogozedwa atero podzithandiza iye mwini ndipo aliyense amene asochera adzisocheretsa yekha. Ine sindili wokusamalirani inu.”
وَاتَّبِعْ مَا يُوحَىٰ إِلَيْكَ وَاصْبِرْ حَتَّىٰ يَحْكُمَ اللَّهُ ۚ وَهُوَ خَيْرُ الْحَاكِمِينَ (109)
Tsatira zimene zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndipo pirira mpaka pamene Mulungu aweruza. Iye ndi Muweruzi wodziwa kuposa aweruzi ena onse
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس