Quran with Chichewa translation - Surah Hud ayat 61 - هُود - Page - Juz 12
﴿۞ وَإِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمۡ صَٰلِحٗاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥۖ هُوَ أَنشَأَكُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ وَٱسۡتَعۡمَرَكُمۡ فِيهَا فَٱسۡتَغۡفِرُوهُ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِۚ إِنَّ رَبِّي قَرِيبٞ مُّجِيبٞ ﴾
[هُود: 61]
﴿وإلى ثمود أخاهم صالحا قال ياقوم اعبدوا الله ما لكم من إله﴾ [هُود: 61]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo kwa anthu (a mtundu) wa Samud, (tidatuma) m’bale wawo Swaleh. Adati: “E inu anthu anga! Lambirani Allah. Mulibe mulungu wina koma Iye Yekha. Iye adakuumbani ndi nthaka ndi kukukhazikani m’menemo. Ndipo mpempheni chikhululuko (pa zolakwa zanu), kenako tembenukirani kwa Iye. Ndithu Mbuye wanga ali pafupi (ndi akapolo Ake). Ndipo Ngovomera mapempho (aopempha).” |