الر ۚ كِتَابٌ أُحْكِمَتْ آيَاتُهُ ثُمَّ فُصِّلَتْ مِن لَّدُنْ حَكِيمٍ خَبِيرٍ (1) Alif Lam Ra. Ndi Buku limene mavesi ake akonzedwa bwino. Ndipo adafotokozedwa mwatsatane tsatane kuchokera kwa Mwini nzeru ndi wodziwa |
أَلَّا تَعْبُدُوا إِلَّا اللَّهَ ۚ إِنَّنِي لَكُم مِّنْهُ نَذِيرٌ وَبَشِيرٌ (2) Kuti musapembedze wina aliyense koma Mulungu. Ndithudi ine ndine wochokera kwa Iye wochenjeza ndi wobweretsa nkhani zabwino |
وَأَنِ اسْتَغْفِرُوا رَبَّكُمْ ثُمَّ تُوبُوا إِلَيْهِ يُمَتِّعْكُم مَّتَاعًا حَسَنًا إِلَىٰ أَجَلٍ مُّسَمًّى وَيُؤْتِ كُلَّ ذِي فَضْلٍ فَضْلَهُ ۖ وَإِن تَوَلَّوْا فَإِنِّي أَخَافُ عَلَيْكُمْ عَذَابَ يَوْمٍ كَبِيرٍ (3) Ndikuti mupemphe chikhululukiro kwa Ambuye wanu ndipo lapani kwa Iye yekha kuti Iye akupatseni zinthu zabwino mpaka pa nthawi yoikidwa. Ndi kupereka kwa aliyense wochita zabwino chisomo chake chomuyenera. Ndipo ngati inu mukana, ine ndichita mantha ndi chilango chimene chingadze pa inu patsiku lalikulu |
إِلَى اللَّهِ مَرْجِعُكُمْ ۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (4) Ndi kwa Mulungu kumene nonse mudzabwerera ndipo Iye ali ndi mphamvu pa zinthu zonse |
أَلَا إِنَّهُمْ يَثْنُونَ صُدُورَهُمْ لِيَسْتَخْفُوا مِنْهُ ۚ أَلَا حِينَ يَسْتَغْشُونَ ثِيَابَهُمْ يَعْلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعْلِنُونَ ۚ إِنَّهُ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (5) Zoonadi! Iwo amakuta mitima yawo kuti akhoza kubisala kwa Iye. Ndithudi ngakhale pamene iwo avala zovala zawo, Iye amadziwa zonse zimene akubisa ndi zimene akuulula. Iye amadziwa zonse zimene zili m’mitima mwawo |
۞ وَمَا مِن دَابَّةٍ فِي الْأَرْضِ إِلَّا عَلَى اللَّهِ رِزْقُهَا وَيَعْلَمُ مُسْتَقَرَّهَا وَمُسْتَوْدَعَهَا ۚ كُلٌّ فِي كِتَابٍ مُّبِينٍ (6) Ndipo palibe cholengedwa padziko lapansi chimene chakudya chake sichichokera kwa Mulungu. Ndipo Iye amadziwa malo ake okhala ndi malo ake a mpumulo. Zonse zili m’Buku lofotokozera bwino zinthu |
وَهُوَ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ وَكَانَ عَرْشُهُ عَلَى الْمَاءِ لِيَبْلُوَكُمْ أَيُّكُمْ أَحْسَنُ عَمَلًا ۗ وَلَئِن قُلْتَ إِنَّكُم مَّبْعُوثُونَ مِن بَعْدِ الْمَوْتِ لَيَقُولَنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا إِنْ هَٰذَا إِلَّا سِحْرٌ مُّبِينٌ (7) Iye ndi amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi m’masiku asanu ndi limodzi ndipo Mpando wake udali pamwamba pa madzi kuti akuyeseni kuti ndani wa inu amene ali ndi ntchito zabwino. Ndipo iwe ukadanena kuti: “Inu ndithudi mudzaukitsidwa pambuyo pa kufa,” anthu osakhulupirira akadanena kuti: “Ichi si china chilichonse koma matsenga enieni.” |
وَلَئِنْ أَخَّرْنَا عَنْهُمُ الْعَذَابَ إِلَىٰ أُمَّةٍ مَّعْدُودَةٍ لَّيَقُولُنَّ مَا يَحْبِسُهُ ۗ أَلَا يَوْمَ يَأْتِيهِمْ لَيْسَ مَصْرُوفًا عَنْهُمْ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ (8) Ndipo ngati Ife titachedwetsa chilango chawo mpaka pa tsiku lokhazikitsidwa, iwo adzafunsa kuti: “Nanga ndi chifukwa chiyani tsikulo lili kuchedwa?” Ndithudi pa tsiku limene izi zidzachitika, palibe chilichonse chimene chingadzapirikitse chilangocho ndipo zoopsa zimene iwo ali kuseka zidzawazungulira iwo onse |
وَلَئِنْ أَذَقْنَا الْإِنسَانَ مِنَّا رَحْمَةً ثُمَّ نَزَعْنَاهَا مِنْهُ إِنَّهُ لَيَئُوسٌ كَفُورٌ (9) Ndipo ngati Ife timulawitsa munthu chifundo chathu kenaka ndi kumulanda, ndithudi, iye amadandaula ndiponso amakhala osuliza |
وَلَئِنْ أَذَقْنَاهُ نَعْمَاءَ بَعْدَ ضَرَّاءَ مَسَّتْهُ لَيَقُولَنَّ ذَهَبَ السَّيِّئَاتُ عَنِّي ۚ إِنَّهُ لَفَرِحٌ فَخُورٌ (10) Koma ngati Ife titamuonetsa munthu chisoni chathu, pambuyo pa mavuto amene adapeza, iye adzati: “Mavuto atha kwa ine” Ndithudi iye amakhala mosalabadira ndiponso modzikweza kwambiri |
إِلَّا الَّذِينَ صَبَرُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ أُولَٰئِكَ لَهُم مَّغْفِرَةٌ وَأَجْرٌ كَبِيرٌ (11) Kupatula iwo amene amapirira ndi kuchita ntchito zabwino. Iwo adzakhala ndi chikhululukiro ndi malipiro akulu |
فَلَعَلَّكَ تَارِكٌ بَعْضَ مَا يُوحَىٰ إِلَيْكَ وَضَائِقٌ بِهِ صَدْرُكَ أَن يَقُولُوا لَوْلَا أُنزِلَ عَلَيْهِ كَنزٌ أَوْ جَاءَ مَعَهُ مَلَكٌ ۚ إِنَّمَا أَنتَ نَذِيرٌ ۚ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ وَكِيلٌ (12) Mwina iwe ukhoza kusiya kunena zina za zimene zavumbulutsidwa kwa iwe ndi kukhala ovutika mu mtima chifukwa chakuti iwo amanena kuti, “Bwanji chuma sichidatumizidwe kwa iye kapena bwanji Mngelo sadadze pamodzi ndi iye?” Komatu iwe ndiwe wochenjeza. Ndipo Mulungu ndiye Msungi wa zinthu zonse |
أَمْ يَقُولُونَ افْتَرَاهُ ۖ قُلْ فَأْتُوا بِعَشْرِ سُوَرٍ مِّثْلِهِ مُفْتَرَيَاتٍ وَادْعُوا مَنِ اسْتَطَعْتُم مِّن دُونِ اللَّهِ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (13) Kapena iwo akunena kuti: “Iye wapeka yekha!” Nena, “Nanunso bweretsani mitu khumi yofanana ndi yopekedwayi. Ndipo itananiwinaamenemungathekumuitanakupatulaMulungu ngati muli kunena zoona.” |
فَإِلَّمْ يَسْتَجِيبُوا لَكُمْ فَاعْلَمُوا أَنَّمَا أُنزِلَ بِعِلْمِ اللَّهِ وَأَن لَّا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ فَهَلْ أَنتُم مُّسْلِمُونَ (14) Akapanda kukuyankha, dziwa kuti chivumbulutso chatumizidwa ndi nzeru ya Mulungu. Ndipo kuti kulibe wina woti apembedzedwe kupatula Iye yekha. Kodi tsopano mudzakhala ogonjera |
مَن كَانَ يُرِيدُ الْحَيَاةَ الدُّنْيَا وَزِينَتَهَا نُوَفِّ إِلَيْهِمْ أَعْمَالَهُمْ فِيهَا وَهُمْ فِيهَا لَا يُبْخَسُونَ (15) Aliyense amene afuna moyo wa m’dziko lino pamodzi ndi zokondweretsa zake, Ife tidzawalipira molingana ndi ntchito zawo , mopanda kuchotsera chilichonse |
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ لَيْسَ لَهُمْ فِي الْآخِرَةِ إِلَّا النَّارُ ۖ وَحَبِطَ مَا صَنَعُوا فِيهَا وَبَاطِلٌ مَّا كَانُوا يَعْمَلُونَ (16) Awa ndiwo anthu amene sadzapeza chilichonse m’moyo umene uli nkudza kupatula moto ndipo zonse zimene amachita pa dziko lapansi zidzaonongeka ndiponso ntchito zawo zimene ankachita zidzakhala zopanda pake |
أَفَمَن كَانَ عَلَىٰ بَيِّنَةٍ مِّن رَّبِّهِ وَيَتْلُوهُ شَاهِدٌ مِّنْهُ وَمِن قَبْلِهِ كِتَابُ مُوسَىٰ إِمَامًا وَرَحْمَةً ۚ أُولَٰئِكَ يُؤْمِنُونَ بِهِ ۚ وَمَن يَكْفُرْ بِهِ مِنَ الْأَحْزَابِ فَالنَّارُ مَوْعِدُهُ ۚ فَلَا تَكُ فِي مِرْيَةٍ مِّنْهُ ۚ إِنَّهُ الْحَقُّ مِن رَّبِّكَ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يُؤْمِنُونَ (17) Kodi iwo amene amadalira umboni wooneka wochokera kwa Ambuye wawo, umene mboni yochokera kwa Iye amautsatira, ndipo iwo usanadze, linadza Buku la Mose, ulangizi ndi chisomo, iwo amakhulupirira koma a mpatuko amene amalikana, kumoto ndiko kudzakhala malo awo okumana. Motero iwe usakaike za ilo. Ndithudi ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wako koma anthu ambiri sakhulupirira |
وَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّنِ افْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ كَذِبًا ۚ أُولَٰئِكَ يُعْرَضُونَ عَلَىٰ رَبِّهِمْ وَيَقُولُ الْأَشْهَادُ هَٰؤُلَاءِ الَّذِينَ كَذَبُوا عَلَىٰ رَبِّهِمْ ۚ أَلَا لَعْنَةُ اللَّهِ عَلَى الظَّالِمِينَ (18) Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu? Anthu otero adzaonetsedwa pamaso pa Ambuye wawo ndipo mboni zidzati: “Awa ndiwo amene anali kunamizira Ambuye wawo.” Mosakaika! Matemberero a Mulungu ali pa anthu ochita zoipa |
الَّذِينَ يَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ اللَّهِ وَيَبْغُونَهَا عِوَجًا وَهُم بِالْآخِرَةِ هُمْ كَافِرُونَ (19) Iwo amene amaletsa anzawo kuti asatsatire njira ya Mulungu ndipo amafuna kuti njira ya Mulungu ikhale yopindika ndiponso amakana kuti kuli moyo wina umene uli nkudza |
أُولَٰئِكَ لَمْ يَكُونُوا مُعْجِزِينَ فِي الْأَرْضِ وَمَا كَانَ لَهُم مِّن دُونِ اللَّهِ مِنْ أَوْلِيَاءَ ۘ يُضَاعَفُ لَهُمُ الْعَذَابُ ۚ مَا كَانُوا يَسْتَطِيعُونَ السَّمْعَ وَمَا كَانُوا يُبْصِرُونَ (20) Wotere sadzathawa padziko lapansi ndiponso alibe owateteza kupatula Mulungu! Chilango chawo chidzaonjezeredwa chifukwa chakuti iwo samafuna kumva ndiponso samaona |
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ خَسِرُوا أَنفُسَهُمْ وَضَلَّ عَنْهُم مَّا كَانُوا يَفْتَرُونَ (21) Awa ndiwo amene ataya mizimu yawo ndipo zinthu zawo zonse zabodza zidzawathawira |
لَا جَرَمَ أَنَّهُمْ فِي الْآخِرَةِ هُمُ الْأَخْسَرُونَ (22) Ndithudi iwo ndiwo amene sadzapindula zambiri mmoyo umene uli nkudza |
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ وَأَخْبَتُوا إِلَىٰ رَبِّهِمْ أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ الْجَنَّةِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (23) Ndithudi iwo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, ndipo amadzichepetsa kwambiri pamaso pa Ambuye wawo, iwo adzakhala eni ake a Paradiso ndipo kumeneko adzakhalako mpaka kalekale |
۞ مَثَلُ الْفَرِيقَيْنِ كَالْأَعْمَىٰ وَالْأَصَمِّ وَالْبَصِيرِ وَالسَّمِيعِ ۚ هَلْ يَسْتَوِيَانِ مَثَلًا ۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ (24) Fanizo la magulu awiri a anthu lili ngati munthu wakhungu ndi wosamva, wopenya ndi wakumva. Kodi magulu awiriwa ndi ofanana? Kodi simungaganize pamenepa |
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوْمِهِ إِنِّي لَكُمْ نَذِيرٌ مُّبِينٌ (25) Zoonadi tidamutumiza Nowa kwa anthu ake nati: “Ndithudi ine ndine mchenjezi wanu weniweni |
أَن لَّا تَعْبُدُوا إِلَّا اللَّهَ ۖ إِنِّي أَخَافُ عَلَيْكُمْ عَذَابَ يَوْمٍ أَلِيمٍ (26) Kuti musapembedze wina aliyense koma Mulungu, ndithudi, ine ndili kukuderani nkhawa pa chilango cha tsiku lowawa.” |
فَقَالَ الْمَلَأُ الَّذِينَ كَفَرُوا مِن قَوْمِهِ مَا نَرَاكَ إِلَّا بَشَرًا مِّثْلَنَا وَمَا نَرَاكَ اتَّبَعَكَ إِلَّا الَّذِينَ هُمْ أَرَاذِلُنَا بَادِيَ الرَّأْيِ وَمَا نَرَىٰ لَكُمْ عَلَيْنَا مِن فَضْلٍ بَلْ نَظُنُّكُمْ كَاذِبِينَ (27) Akuluakulu osakhulupirira amene adali pakati pa anthu ake adati: “Ife tili kukuona iwe ngati munthu onga ife tomwe ndiponso tili kuona kuti onse amene ali kukutsatira kuti ndi anthu apansi kwambiri pakati pathu ndiponso iwo akutsatira iwe osaganiza. Ndipo ife sitili kuona china chilichonse mwa iwe chopambana ife ndipo, kunena moona, tikuganiza kuti inu ndinu abodza.” |
قَالَ يَا قَوْمِ أَرَأَيْتُمْ إِن كُنتُ عَلَىٰ بَيِّنَةٍ مِّن رَّبِّي وَآتَانِي رَحْمَةً مِّنْ عِندِهِ فَعُمِّيَتْ عَلَيْكُمْ أَنُلْزِمُكُمُوهَا وَأَنتُمْ لَهَا كَارِهُونَ (28) Iye adati: “Oh inu anthu anga! Mukuona bwanji? Ngati ine ndili ndi umboni wochokera kwa Ambuye wanga ndiponso wandipatsa chifundo kuchokera kwa Iye, ndipo umboniwo wabisika kwa inu. Kodi ife tingakuumirizeni kuti mumvomere pamene mukunyansidwa nawo?” |
وَيَا قَوْمِ لَا أَسْأَلُكُمْ عَلَيْهِ مَالًا ۖ إِنْ أَجْرِيَ إِلَّا عَلَى اللَّهِ ۚ وَمَا أَنَا بِطَارِدِ الَّذِينَ آمَنُوا ۚ إِنَّهُم مُّلَاقُو رَبِّهِمْ وَلَٰكِنِّي أَرَاكُمْ قَوْمًا تَجْهَلُونَ (29) “oh inu anthu anga! Ine sindikukupemphani chuma chifukwa cha ichi, malipiro anga sali kwa wina koma Mulungu yekha. Ndipo ine sindiwathamangitsa amene akhulupirira. Ndithudi, iwo adzakumana ndi Ambuye wawo. Koma ine ndikukuonani kuti ndinu anthu osadziwa.” |
وَيَا قَوْمِ مَن يَنصُرُنِي مِنَ اللَّهِ إِن طَرَدتُّهُمْ ۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ (30) “oh inu anthu anga! Ndani anganditeteze ine kwa Mulungu ngati nditawapitikitsa iwo? Kodi inu simungaganizire pamenepa?” |
وَلَا أَقُولُ لَكُمْ عِندِي خَزَائِنُ اللَّهِ وَلَا أَعْلَمُ الْغَيْبَ وَلَا أَقُولُ إِنِّي مَلَكٌ وَلَا أَقُولُ لِلَّذِينَ تَزْدَرِي أَعْيُنُكُمْ لَن يُؤْتِيَهُمُ اللَّهُ خَيْرًا ۖ اللَّهُ أَعْلَمُ بِمَا فِي أَنفُسِهِمْ ۖ إِنِّي إِذًا لَّمِنَ الظَّالِمِينَ (31) “Ine sindili kunena kwa inu kuti ndili ndi Nkhokwe za chuma cha Mulungu kapena kuti ndimadziwa zinthu zobisika. Ine sindili kunena kuti ndine Mngelo ayi ndiponso ine sindinena za iwo amene maso anu akuwanyoza kuti Mulungu sadzawapatsa zokoma zake. Mulungu amadziwa bwinobwino zonse zimene zili m’mitima mwawo, chifukwa nditatero, ndithudi, ine ndidzakhala m’modzi wa anthu olakwa.” |
قَالُوا يَا نُوحُ قَدْ جَادَلْتَنَا فَأَكْثَرْتَ جِدَالَنَا فَأْتِنَا بِمَا تَعِدُنَا إِن كُنتَ مِنَ الصَّادِقِينَ (32) Iwo anati, “Iwe Nowa! Iwe watsutsana nafe kwambiri. Tsopano bweretsa msangamsanga chilango chimene uli nkutiopsyeza nacho ngati uli mmodzi wa anthu onena zoona!” |
قَالَ إِنَّمَا يَأْتِيكُم بِهِ اللَّهُ إِن شَاءَ وَمَا أَنتُم بِمُعْجِزِينَ (33) Iye adati, “Mulungu yekha adzakubweretserani chilango chake pamene Iye afuna. Ndipo inu simudzathawa ai.” |
وَلَا يَنفَعُكُمْ نُصْحِي إِنْ أَرَدتُّ أَنْ أَنصَحَ لَكُمْ إِن كَانَ اللَّهُ يُرِيدُ أَن يُغْوِيَكُمْ ۚ هُوَ رَبُّكُمْ وَإِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (34) “Ndiponso ulangizi wanga siudzakuthandizani ngakhale nditafuna kukulangizani ngati chifuniro cha Mulungu ndi kukusocheretsani. Iye ndi Ambuye wanu ndipo ndi kwa Iye mudzabwerera.” |
أَمْ يَقُولُونَ افْتَرَاهُ ۖ قُلْ إِنِ افْتَرَيْتُهُ فَعَلَيَّ إِجْرَامِي وَأَنَا بَرِيءٌ مِّمَّا تُجْرِمُونَ (35) Kapena iwo akunena kuti, “Iye wapeka.” Nena, “Ngati ine ndapeka, tchimo ndi langa koma ine ndili nazo kutali zoipa zimene mukuchita.” |
وَأُوحِيَ إِلَىٰ نُوحٍ أَنَّهُ لَن يُؤْمِنَ مِن قَوْمِكَ إِلَّا مَن قَدْ آمَنَ فَلَا تَبْتَئِسْ بِمَا كَانُوا يَفْعَلُونَ (36) Ndipo Mau a Mulungu adavumbulutsidwa kwa Nowa ponena kuti: “Palibe mmodzi mwa anthu ako amene adzakhulupirira kupatula okhawo amene akhulupirira kale. Motero usamve chisoni chifukwa cha zimene anali kuchita.” |
وَاصْنَعِ الْفُلْكَ بِأَعْيُنِنَا وَوَحْيِنَا وَلَا تُخَاطِبْنِي فِي الَّذِينَ ظَلَمُوا ۚ إِنَّهُم مُّغْرَقُونَ (37) “Ndipo panga chombo pamaso pathu ndi chilamulo chathu ndipo usalankhule mmalo mwa anthu ochimwa. Ndithudi onse adzamizidwa m’madzi.” |
وَيَصْنَعُ الْفُلْكَ وَكُلَّمَا مَرَّ عَلَيْهِ مَلَأٌ مِّن قَوْمِهِ سَخِرُوا مِنْهُ ۚ قَالَ إِن تَسْخَرُوا مِنَّا فَإِنَّا نَسْخَرُ مِنكُمْ كَمَا تَسْخَرُونَ (38) Pamene iye adayamba kupanga chombo, ndipo nthawi zonse pamene akuluakulu a anthu ake anali kudutsa pafupi ndi iye, iwo amamuchita chipongwe. Iye adati: “Ngati mukutichita chipongwe, nafenso tidzakubwezerani chipongwe monga mmene mukutichitira ife.” |
فَسَوْفَ تَعْلَمُونَ مَن يَأْتِيهِ عَذَابٌ يُخْزِيهِ وَيَحِلُّ عَلَيْهِ عَذَابٌ مُّقِيمٌ (39) “Ndipo inu mudzadziwa posachedwa yemwe chilango chochititsa manyazi chidzamfikira, ndiponso iwo amene adzalandira chilango chosatha.” |
حَتَّىٰ إِذَا جَاءَ أَمْرُنَا وَفَارَ التَّنُّورُ قُلْنَا احْمِلْ فِيهَا مِن كُلٍّ زَوْجَيْنِ اثْنَيْنِ وَأَهْلَكَ إِلَّا مَن سَبَقَ عَلَيْهِ الْقَوْلُ وَمَنْ آمَنَ ۚ وَمَا آمَنَ مَعَهُ إِلَّا قَلِيلٌ (40) Kufikira pamene chilamulo chathu chidadza, ndipo nthaka idayamba kutulutsa madzi. Ife tinati: “Lowetsa m’chombo zinthu ziwiriziwiri, (chachimuna ndi chachikazi), anthu a banja lako kupatula iye amene chiweruzo chaperekedwa kale ndi iwo amene akhulupilira. Koma si ambiri amene adali okhulupirira ndi iye kupatula ochepa okha |
۞ وَقَالَ ارْكَبُوا فِيهَا بِسْمِ اللَّهِ مَجْرَاهَا وَمُرْسَاهَا ۚ إِنَّ رَبِّي لَغَفُورٌ رَّحِيمٌ (41) Iye adati, “Kwerani m’menemo, M’dzina la Mulungu chidzayenda mnjira yake ndipo chidzaima pamalo pofunikira. Ndithudi Ambuye wanga ndi wokhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha.” |
وَهِيَ تَجْرِي بِهِمْ فِي مَوْجٍ كَالْجِبَالِ وَنَادَىٰ نُوحٌ ابْنَهُ وَكَانَ فِي مَعْزِلٍ يَا بُنَيَّ ارْكَب مَّعَنَا وَلَا تَكُن مَّعَ الْكَافِرِينَ (42) Motere icho chinayenda pa mafunde okhala ngati mapiri, ndipo Nowa adamuitana mwana wake amene adaima pambali. “oh mwana wanga! Kwerachombopamodzindiifendipousakhalepamodzindi anthu osakhulupirira.” |
قَالَ سَآوِي إِلَىٰ جَبَلٍ يَعْصِمُنِي مِنَ الْمَاءِ ۚ قَالَ لَا عَاصِمَ الْيَوْمَ مِنْ أَمْرِ اللَّهِ إِلَّا مَن رَّحِمَ ۚ وَحَالَ بَيْنَهُمَا الْمَوْجُ فَكَانَ مِنَ الْمُغْرَقِينَ (43) Iye adati: “Ine ndidzathawira ku phiri limene lidzanditeteza ku chigumula cha madzi.” Nowa adati, “Lero palibe woteteza wina ku lamulo la Mulungu kupatula yekhayo amene Mulungu adzamuonetsera chisomo chake.” Ndipo funde lidatchinga pakati pawo ndipo mwana wa Nowa anali mmodzi wa omizidwa |
وَقِيلَ يَا أَرْضُ ابْلَعِي مَاءَكِ وَيَا سَمَاءُ أَقْلِعِي وَغِيضَ الْمَاءُ وَقُضِيَ الْأَمْرُ وَاسْتَوَتْ عَلَى الْجُودِيِّ ۖ وَقِيلَ بُعْدًا لِّلْقَوْمِ الظَّالِمِينَ (44) Ndipo kudanenedwa: “Nthaka meza madzi ako! Ndi kumwamba siya kugwetsa mvula.” Chigumula chinasiya ndipo chifuniro cha Mulungu chinakwaniritsidwa. Ndipo chombo chinadzaima pa phiri la Al Judi ndipo panamveka mawu onena kuti: “Chionongeko chili kwa anthu ochita zoipa.” |
وَنَادَىٰ نُوحٌ رَّبَّهُ فَقَالَ رَبِّ إِنَّ ابْنِي مِنْ أَهْلِي وَإِنَّ وَعْدَكَ الْحَقُّ وَأَنتَ أَحْكَمُ الْحَاكِمِينَ (45) Ndipo Nowa adaitana kwa Ambuye wake nati: “Ambuye! Ndithudi mwana wanga ndi mmodzi wa anthu a banja langa. Lonjezo lanu, ndithudi, ndi loona. Inu ndinu oweruza bwino kuposa oweruza onse.” |
قَالَ يَا نُوحُ إِنَّهُ لَيْسَ مِنْ أَهْلِكَ ۖ إِنَّهُ عَمَلٌ غَيْرُ صَالِحٍ ۖ فَلَا تَسْأَلْنِ مَا لَيْسَ لَكَ بِهِ عِلْمٌ ۖ إِنِّي أَعِظُكَ أَن تَكُونَ مِنَ الْجَاهِلِينَ (46) Mulungu adati: “Iwe Nowa! Ndithudi iye si wabanja lako ayi. Ndithudi ntchito zake si zabwino motero usandifunse zinthu zimene iwe siudziwa. Ndili kukuchenjeza kuti usakhale mugulu la mbuli ayi.” |
قَالَ رَبِّ إِنِّي أَعُوذُ بِكَ أَنْ أَسْأَلَكَ مَا لَيْسَ لِي بِهِ عِلْمٌ ۖ وَإِلَّا تَغْفِرْ لِي وَتَرْحَمْنِي أَكُن مِّنَ الْخَاسِرِينَ (47) Nowa adati: “Ine ndipempha chitetezo chanu, Ambuye, chifukwa chokupemphani zinthu zimene ine sindili kuzidziwa. Ndipo Inu ngati simundikhululukira ndi kundimvera ine chisoni, ndithudi, ine ndidzakhala mmodzi wa anthu olephera.” |
قِيلَ يَا نُوحُ اهْبِطْ بِسَلَامٍ مِّنَّا وَبَرَكَاتٍ عَلَيْكَ وَعَلَىٰ أُمَمٍ مِّمَّن مَّعَكَ ۚ وَأُمَمٌ سَنُمَتِّعُهُمْ ثُمَّ يَمَسُّهُم مِّنَّا عَذَابٌ أَلِيمٌ (48) Kudanenedwa: “Iwe Nowa! Tsika pa mtunda ndi mtendere wochokera kwa Ife ndi madalitso akhale kwa iwe ndi kugulu la anthu amene ali nawe, koma anthu onse tidzawasangalatsa pa kanthawi ndipo pambuyo pake chidzawapezanso chilango chowawa chochokera kwa Ife.” |
تِلْكَ مِنْ أَنبَاءِ الْغَيْبِ نُوحِيهَا إِلَيْكَ ۖ مَا كُنتَ تَعْلَمُهَا أَنتَ وَلَا قَوْمُكَ مِن قَبْلِ هَٰذَا ۖ فَاصْبِرْ ۖ إِنَّ الْعَاقِبَةَ لِلْمُتَّقِينَ (49) Zimenezi ndi nkhani zobisika zimene tikuvumbulutsa kwa iwe, zimene iwe kapena anthu ako samazidziwa chisanabwere chivumbulutso ichi. Motero pirira. Ndithudi mapeto abwino ndi a iwo amene amuopa Mulungu |
وَإِلَىٰ عَادٍ أَخَاهُمْ هُودًا ۚ قَالَ يَا قَوْمِ اعْبُدُوا اللَّهَ مَا لَكُم مِّنْ إِلَٰهٍ غَيْرُهُ ۖ إِنْ أَنتُمْ إِلَّا مُفْتَرُونَ (50) Ndipo kwa mtundu wa Aad, tidatumiza m’bale wawo Hud. Iye adati: “Oh anthu anga! Pembedzani Mulungu. Inu mulibe mulungu wina kupatula Iye yekha. Ndithudi inu simuchita china chili chonse koma kupeka bodza basi.” |
يَا قَوْمِ لَا أَسْأَلُكُمْ عَلَيْهِ أَجْرًا ۖ إِنْ أَجْرِيَ إِلَّا عَلَى الَّذِي فَطَرَنِي ۚ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (51) “oh anthu anga! Ine sindikukupemphani malipiro pazimenezi. Malipiro anga sali ndi wina koma ali ndi Iye amene adandilenga. Kodi simutha kumva zimenezi?” |
وَيَا قَوْمِ اسْتَغْفِرُوا رَبَّكُمْ ثُمَّ تُوبُوا إِلَيْهِ يُرْسِلِ السَّمَاءَ عَلَيْكُم مِّدْرَارًا وَيَزِدْكُمْ قُوَّةً إِلَىٰ قُوَّتِكُمْ وَلَا تَتَوَلَّوْا مُجْرِمِينَ (52) “oh Anthu anga! Mpempheni Ambuye wanu chikhululukiro ndipo lapani kwa Iye chifukwa Iye adzakutumizirani mvula yambiri ndipo adzakuonjezerani mphamvu pamwamba pa mphamvu zanu. Kotero musatembenuke kukhala anthu oipa.” |
قَالُوا يَا هُودُ مَا جِئْتَنَا بِبَيِّنَةٍ وَمَا نَحْنُ بِتَارِكِي آلِهَتِنَا عَن قَوْلِكَ وَمَا نَحْنُ لَكَ بِمُؤْمِنِينَ (53) Iwo adati, “oh iwe Hud! Iwe siunatibweretsere umboni wokwana. Ndipo ife sitidzasiya kupembedza milungu yathu chifukwa cha mawu ako! Ndipo ife sitikukhulupirira iwe ayi.” |
إِن نَّقُولُ إِلَّا اعْتَرَاكَ بَعْضُ آلِهَتِنَا بِسُوءٍ ۗ قَالَ إِنِّي أُشْهِدُ اللَّهَ وَاشْهَدُوا أَنِّي بَرِيءٌ مِّمَّا تُشْرِكُونَ (54) “Zimene tilikunena ndizakuti ina ya milungu yathu yakupatsa iwe tsoka.” Iye adati: “Ndithudi Mulungu ndiye mboni yanga ndipo nanunso chitirani umboni kuti ine ndatalikirana nazo zimene mukamapembedza mulikuonjezera.” |
مِن دُونِهِ ۖ فَكِيدُونِي جَمِيعًا ثُمَّ لَا تُنظِرُونِ (55) “Motero nonsenu konzani chiwembu chanu pa ine ndipo musandichedwetse.” |
إِنِّي تَوَكَّلْتُ عَلَى اللَّهِ رَبِّي وَرَبِّكُم ۚ مَّا مِن دَابَّةٍ إِلَّا هُوَ آخِذٌ بِنَاصِيَتِهَا ۚ إِنَّ رَبِّي عَلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (56) “Ine ndaika chikhulupiliro changa mwa Mulungu, Ambuye wanga ndiponso Ambuye wanu. Palibe chinthu cha moyo pa dziko lapansi chimene tsogolo lake sililamulidwa ndi Iye. Ndithudi Ambuye wanga ndi amene ali pa njira yoyenera.” |
فَإِن تَوَلَّوْا فَقَدْ أَبْلَغْتُكُم مَّا أُرْسِلْتُ بِهِ إِلَيْكُمْ ۚ وَيَسْتَخْلِفُ رَبِّي قَوْمًا غَيْرَكُمْ وَلَا تَضُرُّونَهُ شَيْئًا ۚ إِنَّ رَبِّي عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ حَفِيظٌ (57) “Ndipo ngati mutembenuka, ine ndakuuzani Uthenga umene ndatumizidwa kwa inu. Ambuye wanga adzaika, m’malo mwanu, anthu ena ndipo inu simungamuchite chinthu choipa chilichonse. Ndithudi Ambuye wanga ndi Msungi wa zinthu zonse.” |
وَلَمَّا جَاءَ أَمْرُنَا نَجَّيْنَا هُودًا وَالَّذِينَ آمَنُوا مَعَهُ بِرَحْمَةٍ مِّنَّا وَنَجَّيْنَاهُم مِّنْ عَذَابٍ غَلِيظٍ (58) Ndipo pamene chiweruzo chathu chidadza, Ife tidamupulumutsa Hud, kudzera mu Chisomo chathu, pamodzi ndi amene adakhulupirira ndi iye. Ife tidawapulumutsa ku chilango chokhwima |
وَتِلْكَ عَادٌ ۖ جَحَدُوا بِآيَاتِ رَبِّهِمْ وَعَصَوْا رُسُلَهُ وَاتَّبَعُوا أَمْرَ كُلِّ جَبَّارٍ عَنِيدٍ (59) Amenewa anali anthu a Aad. Iwo adakana Mawu a Ambuye wawo, ndipo adanyoza Atumwi ake ndipo anatsata malamulo a atsogoleri awo a nkhanza ndi okana chilungamo |
وَأُتْبِعُوا فِي هَٰذِهِ الدُّنْيَا لَعْنَةً وَيَوْمَ الْقِيَامَةِ ۗ أَلَا إِنَّ عَادًا كَفَرُوا رَبَّهُمْ ۗ أَلَا بُعْدًا لِّعَادٍ قَوْمِ هُودٍ (60) Ndipo iwo adatsatiridwa ndi temberero m’dziko lino ndipo adzakhala otembereredwa pa tsiku la chiweruzo. Mosakaika, ndithudi, anthu a Ad adamukana Ambuye wawo. Motero tinathana nawo Ad, anthu a Hud |
۞ وَإِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمْ صَالِحًا ۚ قَالَ يَا قَوْمِ اعْبُدُوا اللَّهَ مَا لَكُم مِّنْ إِلَٰهٍ غَيْرُهُ ۖ هُوَ أَنشَأَكُم مِّنَ الْأَرْضِ وَاسْتَعْمَرَكُمْ فِيهَا فَاسْتَغْفِرُوهُ ثُمَّ تُوبُوا إِلَيْهِ ۚ إِنَّ رَبِّي قَرِيبٌ مُّجِيبٌ (61) Ndipo kwa Thamoud, tidatumiza m’bale wawo Saleh. Iye adati: “Oh anthu anga! Mpembedzeni Mulungu, chifukwa inu mulibe mulungu wina kupatula Iye yekha. Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera ku nthaka, ndipo adakupatsani inu malo okhala pa nthakayo. Motero funani chikhululukiro kwa Iye ndipo idzani kwa Iye ndi kulapa. Ndithudi Ambuye wanga ali pafupi nanu ndipo Iye adzamva mapemphero anu.” |
قَالُوا يَا صَالِحُ قَدْ كُنتَ فِينَا مَرْجُوًّا قَبْلَ هَٰذَا ۖ أَتَنْهَانَا أَن نَّعْبُدَ مَا يَعْبُدُ آبَاؤُنَا وَإِنَّنَا لَفِي شَكٍّ مِّمَّا تَدْعُونَا إِلَيْهِ مُرِيبٍ (62) Iwo adati: “Iwe Saleh! Ndithudi iwe wakhala pakati pathu ndipo udali chiyembekezo chathu. Kodi iwe utiletsa kupembedza zimene amapembedza makolo athu? Ndithudi ife tili ndi chikaiko chambiri ndi chipembedzo chimene uli kutiitanira.” |
قَالَ يَا قَوْمِ أَرَأَيْتُمْ إِن كُنتُ عَلَىٰ بَيِّنَةٍ مِّن رَّبِّي وَآتَانِي مِنْهُ رَحْمَةً فَمَن يَنصُرُنِي مِنَ اللَّهِ إِنْ عَصَيْتُهُ ۖ فَمَا تَزِيدُونَنِي غَيْرَ تَخْسِيرٍ (63) Iye adati: “Oh anthu anga! Ndiuzeni ngati ine ndili ndi umboni wokwanira wochokera kwa Ambuye wanga ndipo Iye wandipatsa chisomo kuchokera kwa Iye, ndani angandipulumutse ine kuchokera ku chilango cha Mulungu ngati nditamunyoza? Inu simungaonjezere china chilichonse kwa ine koma kutayika.” |
وَيَا قَوْمِ هَٰذِهِ نَاقَةُ اللَّهِ لَكُمْ آيَةً فَذَرُوهَا تَأْكُلْ فِي أَرْضِ اللَّهِ وَلَا تَمَسُّوهَا بِسُوءٍ فَيَأْخُذَكُمْ عَذَابٌ قَرِيبٌ (64) “Oh Anthu anga! Iyi ndi Ngamira yaikazi, mwini wake ndi Mulungu, ndipo ndi chizindikiro chooneka kwa inu. Isiyeni kuti izidya mwachifuniro cha Mulungu m’dziko lake ndipo musaizunze chifukwa chilango chingadze pa inu mwamsanga.” |
فَعَقَرُوهَا فَقَالَ تَمَتَّعُوا فِي دَارِكُمْ ثَلَاثَةَ أَيَّامٍ ۖ ذَٰلِكَ وَعْدٌ غَيْرُ مَكْذُوبٍ (65) Koma iwo adaipha ngamirayo ndipo iye adati: “Inu basangalalani m’nyumba zanu masiku atatu. Chimenecho ndi chipangano chimene sichili chabodza.” |
فَلَمَّا جَاءَ أَمْرُنَا نَجَّيْنَا صَالِحًا وَالَّذِينَ آمَنُوا مَعَهُ بِرَحْمَةٍ مِّنَّا وَمِنْ خِزْيِ يَوْمِئِذٍ ۗ إِنَّ رَبَّكَ هُوَ الْقَوِيُّ الْعَزِيزُ (66) Ndipo pamene chiweruzo chathu chimadza, Ife tinamupulumutsa Saleh pamodzi ndi amene adakhulupirira ndi iye kudzera m’Chisomo chathu, kuchokera m’masautso a tsiku limeneli. Ndithudi Ambuye wako ndi wanyonga, ndi wopambana |
وَأَخَذَ الَّذِينَ ظَلَمُوا الصَّيْحَةُ فَأَصْبَحُوا فِي دِيَارِهِمْ جَاثِمِينَ (67) Ndipo mkuwo wowopsa udawaononga anthu ochita zoipa ndipo anthu onse adali lambilambi m’nyumba zawo atafa |
كَأَن لَّمْ يَغْنَوْا فِيهَا ۗ أَلَا إِنَّ ثَمُودَ كَفَرُوا رَبَّهُمْ ۗ أَلَا بُعْدًا لِّثَمُودَ (68) Kukhala ngati sadakhalepo pa malo amenewo. Mosakaika, ndithudi, a Thamoud sadakhulupirire mwa Ambuye wawo. Motero anatha anthu a Thamoud |
وَلَقَدْ جَاءَتْ رُسُلُنَا إِبْرَاهِيمَ بِالْبُشْرَىٰ قَالُوا سَلَامًا ۖ قَالَ سَلَامٌ ۖ فَمَا لَبِثَ أَن جَاءَ بِعِجْلٍ حَنِيذٍ (69) Ndithudi Atumwi athu adadza kwa Abrahamu ndi nkhani yabwino. Iwo adati: “Mtendere!” Iye anayankha: “Mtendere” ndipo posakhalitsa iye adabweretsa nyama ya ng’ombe yowotcha |
فَلَمَّا رَأَىٰ أَيْدِيَهُمْ لَا تَصِلُ إِلَيْهِ نَكِرَهُمْ وَأَوْجَسَ مِنْهُمْ خِيفَةً ۚ قَالُوا لَا تَخَفْ إِنَّا أُرْسِلْنَا إِلَىٰ قَوْمِ لُوطٍ (70) Ndipo pamene iye adaona kuti manja awo sakukhudza nyamayo adawadabwa, nachita mantha. Iwo adati: “Usaope. Ife tatumidwa kwa anthu a Loti.” |
وَامْرَأَتُهُ قَائِمَةٌ فَضَحِكَتْ فَبَشَّرْنَاهَا بِإِسْحَاقَ وَمِن وَرَاءِ إِسْحَاقَ يَعْقُوبَ (71) Ndipo mkazi wake adali chiimire pompo, naseka. Ife tidamuuza kuti adzabereka Isake ndipo kuti Isake adzabala Yakobo |
قَالَتْ يَا وَيْلَتَىٰ أَأَلِدُ وَأَنَا عَجُوزٌ وَهَٰذَا بَعْلِي شَيْخًا ۖ إِنَّ هَٰذَا لَشَيْءٌ عَجِيبٌ (72) Iye adati: “Kalanga ine! Kodi ine ndingabereke pamene ndine wokalamba ndipo mwamuna wanga ndi wokalambanso? Ndithudi ichi ndi chinthu chododometsa.” |
قَالُوا أَتَعْجَبِينَ مِنْ أَمْرِ اللَّهِ ۖ رَحْمَتُ اللَّهِ وَبَرَكَاتُهُ عَلَيْكُمْ أَهْلَ الْبَيْتِ ۚ إِنَّهُ حَمِيدٌ مَّجِيدٌ (73) Iwo adati: “Kodi iwe uli kuwadabwa malamulo a Mulungu? Madalitso ndi chisomo cha Mulungu chikhale pa inu a m’banja la Abrahamu. Ndithudi Iye ndi wotamandidwa ndiponso wolemekezeka.” |
فَلَمَّا ذَهَبَ عَنْ إِبْرَاهِيمَ الرَّوْعُ وَجَاءَتْهُ الْبُشْرَىٰ يُجَادِلُنَا فِي قَوْمِ لُوطٍ (74) Ndipo pamene Abrahamu adamuchoka mantha ndi kumfikirankhaniyabwino, iyeadatifunsa Ifezaanthua Loti |
إِنَّ إِبْرَاهِيمَ لَحَلِيمٌ أَوَّاهٌ مُّنِيبٌ (75) Ndithudi Abrahamu anali woleza mtima, wodzichepetsa ndiponso munthu wodzipereka kwa Mulungu |
يَا إِبْرَاهِيمُ أَعْرِضْ عَنْ هَٰذَا ۖ إِنَّهُ قَدْ جَاءَ أَمْرُ رَبِّكَ ۖ وَإِنَّهُمْ آتِيهِمْ عَذَابٌ غَيْرُ مَرْدُودٍ (76) Angelo adati: “Iwe Abrahamu! Siya zimenezo. Ndithudi lamulo la Ambuye wako ladza. Ndithudi kudzadza chilango kwa iwo chimene sichingaletsedwe.” |
وَلَمَّا جَاءَتْ رُسُلُنَا لُوطًا سِيءَ بِهِمْ وَضَاقَ بِهِمْ ذَرْعًا وَقَالَ هَٰذَا يَوْمٌ عَصِيبٌ (77) Ndipo pamene Atumwi athu adadza kwa Loti, iye adali wodandaula kwambiri ndi kubanika mumtima chifukwa cha iwo. Ndipo adati: “Ndithudi ili ndi tsiku loopsa.” |
وَجَاءَهُ قَوْمُهُ يُهْرَعُونَ إِلَيْهِ وَمِن قَبْلُ كَانُوا يَعْمَلُونَ السَّيِّئَاتِ ۚ قَالَ يَا قَوْمِ هَٰؤُلَاءِ بَنَاتِي هُنَّ أَطْهَرُ لَكُمْ ۖ فَاتَّقُوا اللَّهَ وَلَا تُخْزُونِ فِي ضَيْفِي ۖ أَلَيْسَ مِنكُمْ رَجُلٌ رَّشِيدٌ (78) Anthu ake adadza kwa iye akuthamanga ndipo pambuyo adali kuchita zinthu zoipa. Iye adati: “Oh! Anthu anga, awa ndi ana anga akazi, amene ali oyera kwa inu. Opani Mulungu ndipo musandiyalutse kwa alendo anga. Kodi palibe pakati panu munthu mmodzi wangwiro?” |
قَالُوا لَقَدْ عَلِمْتَ مَا لَنَا فِي بَنَاتِكَ مِنْ حَقٍّ وَإِنَّكَ لَتَعْلَمُ مَا نُرِيدُ (79) Iwo adati: “Iwe ukudziwa kuti tilibe khumbo mu ana ako akazi ayi. Ndiponso iwe ukudziwa zimene tikufuna.” |
قَالَ لَوْ أَنَّ لِي بِكُمْ قُوَّةً أَوْ آوِي إِلَىٰ رُكْنٍ شَدِيدٍ (80) Iye adati: “Ine ndikadakhala ndi mphamvu zoti ndikugonjetseni kapena ndikanapeza munthu wina wamphamvu zambiri ndikadamenyana nanu.” |
قَالُوا يَا لُوطُ إِنَّا رُسُلُ رَبِّكَ لَن يَصِلُوا إِلَيْكَ ۖ فَأَسْرِ بِأَهْلِكَ بِقِطْعٍ مِّنَ اللَّيْلِ وَلَا يَلْتَفِتْ مِنكُمْ أَحَدٌ إِلَّا امْرَأَتَكَ ۖ إِنَّهُ مُصِيبُهَا مَا أَصَابَهُمْ ۚ إِنَّ مَوْعِدَهُمُ الصُّبْحُ ۚ أَلَيْسَ الصُّبْحُ بِقَرِيبٍ (81) Iwo adati: “Iwe Loti! Ndithudi ife ndife Atumwi Ambuye wako, iwo sakukhudza, choka pamodzi ndi anthu ako pakati pa usiku. Ndipo usalole wina wa inu kuti ayang’ane m’mbuyo kupatula mkazi wako, ndithudi, adzaona zonse zimene ena adzaone. Ndithudi lonjezo lawo ndi m’mamawa. Kodi m’mawa si pafupi?” |
فَلَمَّا جَاءَ أَمْرُنَا جَعَلْنَا عَالِيَهَا سَافِلَهَا وَأَمْطَرْنَا عَلَيْهَا حِجَارَةً مِّن سِجِّيلٍ مَّنضُودٍ (82) Ndipo pamene chilamulo chathu chidadza, Ife tidatembenuza pamwamba pa Mzinda kukhala pansi ndipo tidagwetsa pa iwo miyala youmbidwa ndi nthaka ya makande younjikika |
مُّسَوَّمَةً عِندَ رَبِّكَ ۖ وَمَا هِيَ مِنَ الظَّالِمِينَ بِبَعِيدٍ (83) Yokhala ndi zizindikiro, yochokera kwa Ambuye wako ndipo iyo siili kutali ndi anthu wosalungama |
۞ وَإِلَىٰ مَدْيَنَ أَخَاهُمْ شُعَيْبًا ۚ قَالَ يَا قَوْمِ اعْبُدُوا اللَّهَ مَا لَكُم مِّنْ إِلَٰهٍ غَيْرُهُ ۖ وَلَا تَنقُصُوا الْمِكْيَالَ وَالْمِيزَانَ ۚ إِنِّي أَرَاكُم بِخَيْرٍ وَإِنِّي أَخَافُ عَلَيْكُمْ عَذَابَ يَوْمٍ مُّحِيطٍ (84) Ndipo kwa anthu a ku Midiyani tidawatumizira m’bale wawo Shoaib. Iye adati: “oh Anthu anga! Pembedzani Mulungu, chifukwa inu mulibe mulungu wina koma Mulungu mmodzi yekha ndipo musapungule miyeso ya zinthu. Ine ndikuona kuti inu ndinu anthu a chuma. Ine, ndithudi, ndili kuchita mantha ndi chilango cha tsiku limene lidzakuzungulirani inu.” |
وَيَا قَوْمِ أَوْفُوا الْمِكْيَالَ وَالْمِيزَانَ بِالْقِسْطِ ۖ وَلَا تَبْخَسُوا النَّاسَ أَشْيَاءَهُمْ وَلَا تَعْثَوْا فِي الْأَرْضِ مُفْسِدِينَ (85) “Anthu anga! Kwaniritsani muyeso wa zinthu ndipo yesani mwachilungamo ndipo musawapungulire anthu katundu wawo ndipo musachite zoipa padziko ndikuyambitsa chisokonezo.” |
بَقِيَّتُ اللَّهِ خَيْرٌ لَّكُمْ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ ۚ وَمَا أَنَا عَلَيْكُم بِحَفِيظٍ (86) “Zimene Mulungu wakusiyirani inu ndi zimene zili zabwino kwa inu ngati muli okhulupirira. Ndipo ine sindine wokuyang’anirani ayi.” |
قَالُوا يَا شُعَيْبُ أَصَلَاتُكَ تَأْمُرُكَ أَن نَّتْرُكَ مَا يَعْبُدُ آبَاؤُنَا أَوْ أَن نَّفْعَلَ فِي أَمْوَالِنَا مَا نَشَاءُ ۖ إِنَّكَ لَأَنتَ الْحَلِيمُ الرَّشِيدُ (87) Iwo adati: “Iwe Shoaib! Kodi mapemphero ako akulamulira kuti ife tiyenera kuleka kupembedza milungu ya makolo athu kapena kuti sitiyenera kuchita zimene tifuna ndi chuma chathu? Ndithudi iwe ndiwe wopirira ndiponso wa nzeru zokhazikika.” |
قَالَ يَا قَوْمِ أَرَأَيْتُمْ إِن كُنتُ عَلَىٰ بَيِّنَةٍ مِّن رَّبِّي وَرَزَقَنِي مِنْهُ رِزْقًا حَسَنًا ۚ وَمَا أُرِيدُ أَنْ أُخَالِفَكُمْ إِلَىٰ مَا أَنْهَاكُمْ عَنْهُ ۚ إِنْ أُرِيدُ إِلَّا الْإِصْلَاحَ مَا اسْتَطَعْتُ ۚ وَمَا تَوْفِيقِي إِلَّا بِاللَّهِ ۚ عَلَيْهِ تَوَكَّلْتُ وَإِلَيْهِ أُنِيبُ (88) Iye adati: “Ndiuzeni! Ngati ine ndili ndi umboni woonekera wochokera kwa Ambuye wanga ndipo Iye wandipatsa gawo labwino. Ine sindifuna kusemphana nanu pochita chinthu chimene ndili kukuletsani. Palibe chilichonse chimene ndifuna koma kukonza mmene ndingathere. Ndipo ulangizi wanga siubwera kuchokera kwa wina aliyense kupatula Mulungu. Mwa Iye ndaika chikhulupiriro changa ndipo kwa Iye ndiko ndimalapa.” |
وَيَا قَوْمِ لَا يَجْرِمَنَّكُمْ شِقَاقِي أَن يُصِيبَكُم مِّثْلُ مَا أَصَابَ قَوْمَ نُوحٍ أَوْ قَوْمَ هُودٍ أَوْ قَوْمَ صَالِحٍ ۚ وَمَا قَوْمُ لُوطٍ مِّنكُم بِبَعِيدٍ (89) “Oh anthu anga! Musalole kuti kusagwirizana kwanu ndi ine kuti kubweretse pa inu mavuto amene adadza pa anthu a Nowa, kapena pa anthu a Hud ndi Saleh ndiponso sikale pamene anthu a Loti adaonongeka.” |
وَاسْتَغْفِرُوا رَبَّكُمْ ثُمَّ تُوبُوا إِلَيْهِ ۚ إِنَّ رَبِّي رَحِيمٌ وَدُودٌ (90) “Ndipo funani chikhululukiro cha Ambuye wanu, ndiponso lapani kwa Iye. Ndithudi Ambuye wanga ndi wa Chisoni ndiponso wa Chikondi chosatha.” |
قَالُوا يَا شُعَيْبُ مَا نَفْقَهُ كَثِيرًا مِّمَّا تَقُولُ وَإِنَّا لَنَرَاكَ فِينَا ضَعِيفًا ۖ وَلَوْلَا رَهْطُكَ لَرَجَمْنَاكَ ۖ وَمَا أَنتَ عَلَيْنَا بِعَزِيزٍ (91) Iwo adati: “Oh Shoaib! Zambiri zimene unena ife sitili kuzizindikira ndipo ife tili kuona kuti ulibe mphamvu pakati pathu. Pakadapanda mtundu wako, ndithudi, ife tikadakuponya miyala ndiponso iwe ulibe mphamvu zoposa zathu.” |
قَالَ يَا قَوْمِ أَرَهْطِي أَعَزُّ عَلَيْكُم مِّنَ اللَّهِ وَاتَّخَذْتُمُوهُ وَرَاءَكُمْ ظِهْرِيًّا ۖ إِنَّ رَبِّي بِمَا تَعْمَلُونَ مُحِيطٌ (92) Iye adati: “oh anthu anga! Kodi mtundu wanga ndi olemekezeka kwambiri kuposa Mulungu? Ndipo inu mwamuponya Iye kumbuyo kwanu? Ndithudi Ambuye wanga ndi wodziwa zonse zimene muchita.” |
وَيَا قَوْمِ اعْمَلُوا عَلَىٰ مَكَانَتِكُمْ إِنِّي عَامِلٌ ۖ سَوْفَ تَعْلَمُونَ مَن يَأْتِيهِ عَذَابٌ يُخْزِيهِ وَمَنْ هُوَ كَاذِبٌ ۖ وَارْتَقِبُوا إِنِّي مَعَكُمْ رَقِيبٌ (93) “oh anthu anga! Chitani chimene mufuna kuti muchite, nanenso ndidzachita zanga. Inu mudzadziwa kuti ndani adzalangidwa ndi chilango chochititsa manyazi ndiponso kuti kodi ndani amene ali kunama! Ndithudi dikirani nanenso ndili kudikira pamodzi ndi inu.” |
وَلَمَّا جَاءَ أَمْرُنَا نَجَّيْنَا شُعَيْبًا وَالَّذِينَ آمَنُوا مَعَهُ بِرَحْمَةٍ مِّنَّا وَأَخَذَتِ الَّذِينَ ظَلَمُوا الصَّيْحَةُ فَأَصْبَحُوا فِي دِيَارِهِمْ جَاثِمِينَ (94) Ndipo pamene lamulo lathu lidadza tidamupulumutsa Shoaib, pamodzi ndi anzake onse amene anali wokhulupirira mwa chisomo chathu. Ndipo mkuwo waukulu udawaononga anthu onse ochita zoipa ndipo onse adali lambilambi m’nyumba zawo |
كَأَن لَّمْ يَغْنَوْا فِيهَا ۗ أَلَا بُعْدًا لِّمَدْيَنَ كَمَا بَعِدَتْ ثَمُودُ (95) Kukhala ngati iwo sadakhalemo m’menemo! Motero adaonongeka anthu a ku Midiyani monga momwe adaonongekera anthu a ku Thamoud |
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا مُوسَىٰ بِآيَاتِنَا وَسُلْطَانٍ مُّبِينٍ (96) Zoonadi tidamutumiza Mose ndi zizindikiro zathu ndiponso umboni wooneka |
إِلَىٰ فِرْعَوْنَ وَمَلَئِهِ فَاتَّبَعُوا أَمْرَ فِرْعَوْنَ ۖ وَمَا أَمْرُ فِرْعَوْنَ بِرَشِيدٍ (97) Kwa Farao ndi nduna zake, iwo anatsatira malamulo a Farao ndipo malamulo a Farao sanali olungama |
يَقْدُمُ قَوْمَهُ يَوْمَ الْقِيَامَةِ فَأَوْرَدَهُمُ النَّارَ ۖ وَبِئْسَ الْوِرْدُ الْمَوْرُودُ (98) Iye adzawatsogolera anthu ake pa tsiku la chiweruzo ndipo adzawalowetsa ku moto. Aipirenji malo omwe adatengedwerako |
وَأُتْبِعُوا فِي هَٰذِهِ لَعْنَةً وَيَوْمَ الْقِيَامَةِ ۚ بِئْسَ الرِّفْدُ الْمَرْفُودُ (99) Ndipo anatsatiridwa ndi matemberero m’moyo wa m’dziko lino ndi patsiku la chiweruzo. Iyipirenji mphotho yomwe adzapatsidwe |
ذَٰلِكَ مِنْ أَنبَاءِ الْقُرَىٰ نَقُصُّهُ عَلَيْكَ ۖ مِنْهَا قَائِمٌ وَحَصِيدٌ (100) Iyi ndi nkhani, ya m’mizinda imene tinaononga ndipo tili kukufotokozera iwe, ndipo ina mwa Mizindayo ilipo pamene ina idaonongeka |
وَمَا ظَلَمْنَاهُمْ وَلَٰكِن ظَلَمُوا أَنفُسَهُمْ ۖ فَمَا أَغْنَتْ عَنْهُمْ آلِهَتُهُمُ الَّتِي يَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ مِن شَيْءٍ لَّمَّا جَاءَ أَمْرُ رَبِّكَ ۖ وَمَا زَادُوهُمْ غَيْرَ تَتْبِيبٍ (101) Ife sitinawapondereze ayi koma adadzipondereza okha. Motero milungu yawo imene analikuipembedzakuonjezerapa Mulungusiidawathandize chilichonse pamene chiweruzo cha Ambuye wako chidadza ndiponso milungu yawo sidawaonjezere kalikonse koma chionongeko |
وَكَذَٰلِكَ أَخْذُ رَبِّكَ إِذَا أَخَذَ الْقُرَىٰ وَهِيَ ظَالِمَةٌ ۚ إِنَّ أَخْذَهُ أَلِيمٌ شَدِيدٌ (102) Chimenecho ndicho chilango cha Ambuye wako akafuna kulanga mzinda wa anthu ochita zoipa. Ndithudi chilango chake ndi chokhwima ndi chowawa kwambiri |
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَةً لِّمَنْ خَافَ عَذَابَ الْآخِرَةِ ۚ ذَٰلِكَ يَوْمٌ مَّجْمُوعٌ لَّهُ النَّاسُ وَذَٰلِكَ يَوْمٌ مَّشْهُودٌ (103) Ndithudi mu izo muli chizindikiro kwa iye amene aopa chilango cha moyo umene uli nkudza. Ndi tsiku limene anthu onse adzasonkhanitsidwa pamodzi ndiponso ili ndi tsiku lomwe chilichonse chidzakhalapo |
وَمَا نُؤَخِّرُهُ إِلَّا لِأَجَلٍ مَّعْدُودٍ (104) Ife tili kulichedwetsa mpaka pa nthawi yokhazikitsidwa |
يَوْمَ يَأْتِ لَا تَكَلَّمُ نَفْسٌ إِلَّا بِإِذْنِهِ ۚ فَمِنْهُمْ شَقِيٌّ وَسَعِيدٌ (105) Ndipo pamene tsikuli lidza, palibe munthu amene adzalankhula opanda chilolezo cha Mulungu. Ena a iwo adzakhala a tsoka pamene ena adzakhala amwayi |
فَأَمَّا الَّذِينَ شَقُوا فَفِي النَّارِ لَهُمْ فِيهَا زَفِيرٌ وَشَهِيقٌ (106) Akhala iwo amene adzakhala a tsoka, iwo akakhala m’moto ali kubuula mokweza ndiponso motsitsa |
خَالِدِينَ فِيهَا مَا دَامَتِ السَّمَاوَاتُ وَالْأَرْضُ إِلَّا مَا شَاءَ رَبُّكَ ۚ إِنَّ رَبَّكَ فَعَّالٌ لِّمَا يُرِيدُ (107) Iwo adzakhala komweko mpaka pamene kumwamba ndi dziko lapansi zidzakhale zilipobe kupatula ngati Ambuye wako afuna kusintha. Ndithudi Ambuye wako amachita zimene afuna |
۞ وَأَمَّا الَّذِينَ سُعِدُوا فَفِي الْجَنَّةِ خَالِدِينَ فِيهَا مَا دَامَتِ السَّمَاوَاتُ وَالْأَرْضُ إِلَّا مَا شَاءَ رَبُّكَ ۖ عَطَاءً غَيْرَ مَجْذُوذٍ (108) Akakhala anthu odala, iwo adzakhala ku Paradiso mpaka pamene kumwamba ndi dziko lapansi zidzakhale zilipobe kupatula ngati Ambuye wako afuna kusintha, mphatso yosatha mpaka kalekale |
فَلَا تَكُ فِي مِرْيَةٍ مِّمَّا يَعْبُدُ هَٰؤُلَاءِ ۚ مَا يَعْبُدُونَ إِلَّا كَمَا يَعْبُدُ آبَاؤُهُم مِّن قَبْلُ ۚ وَإِنَّا لَمُوَفُّوهُمْ نَصِيبَهُمْ غَيْرَ مَنقُوصٍ (109) Motero usakaike pa zimene anthu awa apembedza. Iwo sali kupembedza koma kungotsatira mmene makolo awo amapembedzera kale. Ndipo ndithudi Ife tidzawalipira malipiro awo mopanda kuchepetsa |
وَلَقَدْ آتَيْنَا مُوسَى الْكِتَابَ فَاخْتُلِفَ فِيهِ ۚ وَلَوْلَا كَلِمَةٌ سَبَقَتْ مِن رَّبِّكَ لَقُضِيَ بَيْنَهُمْ ۚ وَإِنَّهُمْ لَفِي شَكٍّ مِّنْهُ مُرِيبٍ (110) Ndithudi Ife tidamupatsa Mose Buku koma mikangano inabuka pakati pawo ndipo kukadapanda kuti liwu lochokera kwa Ambuye wako lidatsogola kale, lamulo likadadza pa iwo. Ndithudi iwo ndi okaika kwambiri za ili |
وَإِنَّ كُلًّا لَّمَّا لَيُوَفِّيَنَّهُمْ رَبُّكَ أَعْمَالَهُمْ ۚ إِنَّهُ بِمَا يَعْمَلُونَ خَبِيرٌ (111) Ndithudi Ambuye wako adzalipira anthu molingana ndi ntchito zawo. Ndithudi Iye amadziwa zonse zimene akuchita |
فَاسْتَقِمْ كَمَا أُمِرْتَ وَمَن تَابَ مَعَكَ وَلَا تَطْغَوْا ۚ إِنَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (112) Motero pitiriza kukhala m’njira yoyenera monga momwe walamulidwira pamodzi ndi onse amene alapa pamodzi ndi iwe ndipo usapyole malire. Ndithudi Iye amaona zonse zimene mumachita |
وَلَا تَرْكَنُوا إِلَى الَّذِينَ ظَلَمُوا فَتَمَسَّكُمُ النَّارُ وَمَا لَكُم مِّن دُونِ اللَّهِ مِنْ أَوْلِيَاءَ ثُمَّ لَا تُنصَرُونَ (113) Ndipo usatsatire anthu ochita zoipa chifukwa moto ungakupezeni ndiponso palibe wina wokuthandizani kupatula Mulungu ndiponso palibe wokuthandizani |
وَأَقِمِ الصَّلَاةَ طَرَفَيِ النَّهَارِ وَزُلَفًا مِّنَ اللَّيْلِ ۚ إِنَّ الْحَسَنَاتِ يُذْهِبْنَ السَّيِّئَاتِ ۚ ذَٰلِكَ ذِكْرَىٰ لِلذَّاكِرِينَ (114) Ndipo chita mapemphero ako nthawi ziwiri za masana ndi m’maola oyambirira a usiku. Ndithudi ntchito zabwino zimafafaniza machimo. Chimenechi ndi chikumbutso kwa anthu okumbukira |
وَاصْبِرْ فَإِنَّ اللَّهَ لَا يُضِيعُ أَجْرَ الْمُحْسِنِينَ (115) Kotero pirira. Ndithudi Mulungu sasokoneza mphotho ya ochita zabwino |
فَلَوْلَا كَانَ مِنَ الْقُرُونِ مِن قَبْلِكُمْ أُولُو بَقِيَّةٍ يَنْهَوْنَ عَنِ الْفَسَادِ فِي الْأَرْضِ إِلَّا قَلِيلًا مِّمَّنْ أَنجَيْنَا مِنْهُمْ ۗ وَاتَّبَعَ الَّذِينَ ظَلَمُوا مَا أُتْرِفُوا فِيهِ وَكَانُوا مُجْرِمِينَ (116) Kukadakhala kuti pakati pa mibadwo imene inalipo kale, panali anthu a nzeru oletsa anthu kuchita zoipa padziko lapansi kupatula owerengeka amene Ife tidawapulumutsa pakati pawo. Iwo amene amachita zoipa anali kutsatira zokoma za m’moyo uno ndipo adali kupitiliza kuchita zoipa |
وَمَا كَانَ رَبُّكَ لِيُهْلِكَ الْقُرَىٰ بِظُلْمٍ وَأَهْلُهَا مُصْلِحُونَ (117) Ndipo sizinali koyenera kuti Ambuye wako aononge mizinda mwankhanza pamene anthu ake anali kuchita zabwino |
وَلَوْ شَاءَ رَبُّكَ لَجَعَلَ النَّاسَ أُمَّةً وَاحِدَةً ۖ وَلَا يَزَالُونَ مُخْتَلِفِينَ (118) Ndipo Ambuye wako akadafuna, ndithudi, akadawapanga anthu onse kukhala a chipembedzo chimodzi koma akadapitiriza kukhala osiyana |
إِلَّا مَن رَّحِمَ رَبُّكَ ۚ وَلِذَٰلِكَ خَلَقَهُمْ ۗ وَتَمَّتْ كَلِمَةُ رَبِّكَ لَأَمْلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنَ الْجِنَّةِ وَالنَّاسِ أَجْمَعِينَ (119) Kupatula yekhayo amene Ambuye wako wamuonetsera chisomo chake ndipo ndicho chifukwa chake chimene Mulungu adawalengera. Mawu a Ambuye wako adzakwaniritsidwa “Ndithudi Ine ndidzadzadza Gahena ndi Majini ndi anthu onse pamodzi.” |
وَكُلًّا نَّقُصُّ عَلَيْكَ مِنْ أَنبَاءِ الرُّسُلِ مَا نُثَبِّتُ بِهِ فُؤَادَكَ ۚ وَجَاءَكَ فِي هَٰذِهِ الْحَقُّ وَمَوْعِظَةٌ وَذِكْرَىٰ لِلْمُؤْمِنِينَ (120) Ndipo zonse zimene tili kukuuza iwe za nkhani za Atumwi ndi kulimbikitsa mtima wako. Kudzera mu izi choonadi ndi ulangizi wadza kwa iwe ndiponso uthenga wa chikumbutso kwa anthu okhulupirira |
وَقُل لِّلَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ اعْمَلُوا عَلَىٰ مَكَانَتِكُمْ إِنَّا عَامِلُونَ (121) Auze anthu osakhulupirira kuti: “Chitani mmene mungathere, nafenso tidzachita chimodzimodzi.” |
وَانتَظِرُوا إِنَّا مُنتَظِرُونَ (122) dikirani! Ndithudi nafenso tili kudikira |
وَلِلَّهِ غَيْبُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَإِلَيْهِ يُرْجَعُ الْأَمْرُ كُلُّهُ فَاعْبُدْهُ وَتَوَكَّلْ عَلَيْهِ ۚ وَمَا رَبُّكَ بِغَافِلٍ عَمَّا تَعْمَلُونَ (123) Zobisika zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi za Mulungu ndipo zonse zimabwerera kwa Iye. Motero mpembedzeni Iye ndipo ika chikhulupiriro chako mwa Iye. Ambuye wako saiwala zimene mukuchita |