Quran with Chichewa translation - Surah Yusuf ayat 80 - يُوسُف - Page - Juz 13
﴿فَلَمَّا ٱسۡتَيۡـَٔسُواْ مِنۡهُ خَلَصُواْ نَجِيّٗاۖ قَالَ كَبِيرُهُمۡ أَلَمۡ تَعۡلَمُوٓاْ أَنَّ أَبَاكُمۡ قَدۡ أَخَذَ عَلَيۡكُم مَّوۡثِقٗا مِّنَ ٱللَّهِ وَمِن قَبۡلُ مَا فَرَّطتُمۡ فِي يُوسُفَۖ فَلَنۡ أَبۡرَحَ ٱلۡأَرۡضَ حَتَّىٰ يَأۡذَنَ لِيٓ أَبِيٓ أَوۡ يَحۡكُمَ ٱللَّهُ لِيۖ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلۡحَٰكِمِينَ ﴾
[يُوسُف: 80]
﴿فلما استيأسوا منه خلصوا نجيا قال كبيرهم ألم تعلموا أن أباكم قد﴾ [يُوسُف: 80]
Khaled Ibrahim Betala “Choncho, pamene adataya mtima za iye, adapita pambali kukanong’onezana. Wamkulu wawo adati: “Kodi simudziwa kuti bambo wanu adatenga lonjezo kuchokera kwa inu m’dzina la Allah (kuti mudzam’bweza iyeyo?) ndiponso kale mudalakwa (pa mapangano anu) pa za Yûsuf. Choncho sindichoka dziko lino kufikira atandilola bambo (kutero) kapena Allah andilamule (zondichotsa kuno pomasulidwa m’bale wangayu); Iye Ngwabwino polamula kuposa olamula.” |