الر ۚ تِلْكَ آيَاتُ الْكِتَابِ الْمُبِينِ (1) Alif Lam Ra. Awa ndi mawu a Buku lofotokoza bwino |
إِنَّا أَنزَلْنَاهُ قُرْآنًا عَرَبِيًّا لَّعَلَّكُمْ تَعْقِلُونَ (2) Ndithudi Ife talivumbulutsa ilo ngati Korani ya Chiarabu kuti mukhale ozindikira |
نَحْنُ نَقُصُّ عَلَيْكَ أَحْسَنَ الْقَصَصِ بِمَا أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ هَٰذَا الْقُرْآنَ وَإِن كُنتَ مِن قَبْلِهِ لَمِنَ الْغَافِلِينَ (3) Ife tili kukuuza iwe nkhani zabwino kudzera m’Korani ino. Ndipo isanafike iwe udali m’gulu la anthu amene samadziwa za ilo |
إِذْ قَالَ يُوسُفُ لِأَبِيهِ يَا أَبَتِ إِنِّي رَأَيْتُ أَحَدَ عَشَرَ كَوْكَبًا وَالشَّمْسَ وَالْقَمَرَ رَأَيْتُهُمْ لِي سَاجِدِينَ (4) PameneYosefe adawauzaabamboakekuti,“Ohabambo anga! Ndithudi ine ndaona nyenyezi khumi ndi imodzi ndiponso dzuwa ndi mwezi zonsezi zili kundigwadira ine.” |
قَالَ يَا بُنَيَّ لَا تَقْصُصْ رُؤْيَاكَ عَلَىٰ إِخْوَتِكَ فَيَكِيدُوا لَكَ كَيْدًا ۖ إِنَّ الشَّيْطَانَ لِلْإِنسَانِ عَدُوٌّ مُّبِينٌ (5) Iye adati, “Oh Mwana wanga! Usauze wina aliyense wa abale ako za maloto ako, chifukwa mwina akhoza kukonza chiwembu choti akuononge iwe. Ndithudi! Satana, kwa munthu, ndi mdani woonekeratu.” |
وَكَذَٰلِكَ يَجْتَبِيكَ رَبُّكَ وَيُعَلِّمُكَ مِن تَأْوِيلِ الْأَحَادِيثِ وَيُتِمُّ نِعْمَتَهُ عَلَيْكَ وَعَلَىٰ آلِ يَعْقُوبَ كَمَا أَتَمَّهَا عَلَىٰ أَبَوَيْكَ مِن قَبْلُ إِبْرَاهِيمَ وَإِسْحَاقَ ۚ إِنَّ رَبَّكَ عَلِيمٌ حَكِيمٌ (6) “Kotero Ambuye wako adzakusankha iwe ndikukuphunzitsa kutathauzira maloto ndi kukwaniritsa chisomo chake pa iwe ndiponso kwa ana a Yakobo, monga momwe adakwaniritsira kwa makolo ako Abrahamu ndi Isake kale! Ndithudi Ambuye wako ndi wodziwa zilizonse ndi Wanzeru.” |
۞ لَّقَدْ كَانَ فِي يُوسُفَ وَإِخْوَتِهِ آيَاتٌ لِّلسَّائِلِينَ (7) Ndithudi m’mbiri ya Yosefe ndi abale ake muli zizindikiro ndiponso phunziro kwa anthu ofuna kudziwa |
إِذْ قَالُوا لَيُوسُفُ وَأَخُوهُ أَحَبُّ إِلَىٰ أَبِينَا مِنَّا وَنَحْنُ عُصْبَةٌ إِنَّ أَبَانَا لَفِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (8) Pamene iwo adati, “Yosefe pamodzi ndi m’bale wake amakondedwa kwambiri ndi abambo athu kuposa ife tonse pamene ife tili gulu lamphamvu. Ndithudi, abambo athu ali kulakwa koonekeratu.” |
اقْتُلُوا يُوسُفَ أَوِ اطْرَحُوهُ أَرْضًا يَخْلُ لَكُمْ وَجْهُ أَبِيكُمْ وَتَكُونُوا مِن بَعْدِهِ قَوْمًا صَالِحِينَ (9) “Mumuphe Yosefe kapena mukamutaye ku dziko lakutali kuti chikondi cha bambo anu chikhale pa inu nokha ndipo pambuyo pa izi inu mudzakhale anthu abwino.” |
قَالَ قَائِلٌ مِّنْهُمْ لَا تَقْتُلُوا يُوسُفَ وَأَلْقُوهُ فِي غَيَابَتِ الْجُبِّ يَلْتَقِطْهُ بَعْضُ السَّيَّارَةِ إِن كُنتُمْ فَاعِلِينَ (10) Mmodzi mwa iwo adati, “Musamuphe Yosefe ayi koma ngati mufuna kuchita china chake kamuponyeni m’chitsime chakuya chamdima kapena anthu apaulendo adzamutola iye ngati mungathe kutero.” |
قَالُوا يَا أَبَانَا مَا لَكَ لَا تَأْمَنَّا عَلَىٰ يُوسُفَ وَإِنَّا لَهُ لَنَاصِحُونَ (11) Iwo adati, “Abambo athu! Kodi chifukwa chiyani inu simutikhulupirira ndi Yosefe pamene ife timamufunira iye zabwino?” |
أَرْسِلْهُ مَعَنَا غَدًا يَرْتَعْ وَيَلْعَبْ وَإِنَّا لَهُ لَحَافِظُونَ (12) “Mtumizeni iye pamodzi ndi ife mawa kuti akasangalale ndi kusewera ndipo, ndithudi, Ife tidzamusamalira iye.” |
قَالَ إِنِّي لَيَحْزُنُنِي أَن تَذْهَبُوا بِهِ وَأَخَافُ أَن يَأْكُلَهُ الذِّئْبُ وَأَنتُمْ عَنْهُ غَافِلُونَ (13) Iye adati, “Ndithudi zikundidandaulitsa ine kuti mupite naye. Ine ndikuopa kuti mmbulu ukhoza kukamudya iye inu mutamuiwala iye.” |
قَالُوا لَئِنْ أَكَلَهُ الذِّئْبُ وَنَحْنُ عُصْبَةٌ إِنَّا إِذًا لَّخَاسِرُونَ (14) Iwo adati, “Ngati mmbulu ungamudye pamene ife tili gulu lamphamvu, ndiye kuti tidzakhala olephera.” |
فَلَمَّا ذَهَبُوا بِهِ وَأَجْمَعُوا أَن يَجْعَلُوهُ فِي غَيَابَتِ الْجُبِّ ۚ وَأَوْحَيْنَا إِلَيْهِ لَتُنَبِّئَنَّهُم بِأَمْرِهِمْ هَٰذَا وَهُمْ لَا يَشْعُرُونَ (15) Ndipo pamene iwo adapita naye, iwo adagwirizana zomuponya m’chitsime chamdima ndipo Ife tidamuuza iye kuti, “Iwe udzawauza zonsezi nthawi ina pamene iwo sakudziwa.” |
وَجَاءُوا أَبَاهُمْ عِشَاءً يَبْكُونَ (16) Ndipo iwo adabwera kwa abambo awo ali kulira nthawi ya madzulo |
قَالُوا يَا أَبَانَا إِنَّا ذَهَبْنَا نَسْتَبِقُ وَتَرَكْنَا يُوسُفَ عِندَ مَتَاعِنَا فَأَكَلَهُ الذِّئْبُ ۖ وَمَا أَنتَ بِمُؤْمِنٍ لَّنَا وَلَوْ كُنَّا صَادِقِينَ (17) Iwo adati, “oh bambo wathu! Ife tinapita kukathamangitsana ndipo tinamusiya Yosefe pa katundu wathu ndipo mmbulu wamudya iye, koma inu simutikhulupirira ayi ngakhale kuti ife tili kunena choonadi.” |
وَجَاءُوا عَلَىٰ قَمِيصِهِ بِدَمٍ كَذِبٍ ۚ قَالَ بَلْ سَوَّلَتْ لَكُمْ أَنفُسُكُمْ أَمْرًا ۖ فَصَبْرٌ جَمِيلٌ ۖ وَاللَّهُ الْمُسْتَعَانُ عَلَىٰ مَا تَصِفُونَ (18) Ndipo iwo adabweretsa malaya ake ali ndi magazi omwe sanali a Yosefe. Iye adati, “Iyayi! Inu mwapeka nokha nkhani koma kupirira ndi kwabwino. Ndi Mulungu yekha amene ayenera kupemphedwa chithandizo choteteza zimene mukunena.” |
وَجَاءَتْ سَيَّارَةٌ فَأَرْسَلُوا وَارِدَهُمْ فَأَدْلَىٰ دَلْوَهُ ۖ قَالَ يَا بُشْرَىٰ هَٰذَا غُلَامٌ ۚ وَأَسَرُّوهُ بِضَاعَةً ۚ وَاللَّهُ عَلِيمٌ بِمَا يَعْمَلُونَ (19) Ndipo gulu la anthu a paulendo lidabwera ndipo lidatumiza mmodzi wa anthu otunga madzi, ndipo adaponya ndowa yake, Iye adafuula nati, “Imvani nkhani yabwino! Uyu mnyamata.” Ndipo iwo adamutenga iye namubisa iye ngati katundu wawo wa malonda. Koma Mulungu anali kudziwa zonse zimene iwo anali kuchita |
وَشَرَوْهُ بِثَمَنٍ بَخْسٍ دَرَاهِمَ مَعْدُودَةٍ وَكَانُوا فِيهِ مِنَ الزَّاهِدِينَ (20) Ndipo iwo adamugulitsa pa mtengo wotsika wa ndalama zowerengeka za siliva. Iwo sanalabadire china chilichonse cha iye |
وَقَالَ الَّذِي اشْتَرَاهُ مِن مِّصْرَ لِامْرَأَتِهِ أَكْرِمِي مَثْوَاهُ عَسَىٰ أَن يَنفَعَنَا أَوْ نَتَّخِذَهُ وَلَدًا ۚ وَكَذَٰلِكَ مَكَّنَّا لِيُوسُفَ فِي الْأَرْضِ وَلِنُعَلِّمَهُ مِن تَأْوِيلِ الْأَحَادِيثِ ۚ وَاللَّهُ غَالِبٌ عَلَىٰ أَمْرِهِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَعْلَمُونَ (21) Ndipo munthu wa mtundu wa Aiguputo, amene adamugula iye, adati kwa mkazi wake, “Mupatseni malo aulemu mwina angatithandize kapena tikhoza kumutenga kuti akhale mwana wathu.” Chomwecho Ife tidamukhazikitsira malo okhalaYosefe, kuti timuphunzitse kutanthauzira maloto. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu ndi ulamuliro pa zinthu zake, koma anthu ambiri sadziwa |
وَلَمَّا بَلَغَ أَشُدَّهُ آتَيْنَاهُ حُكْمًا وَعِلْمًا ۚ وَكَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ (22) Ndipo pamene iye adakula, tidamupatsa luntha ndi nzeru. Chomwecho timalipira anthu ochita zabwino |
وَرَاوَدَتْهُ الَّتِي هُوَ فِي بَيْتِهَا عَن نَّفْسِهِ وَغَلَّقَتِ الْأَبْوَابَ وَقَالَتْ هَيْتَ لَكَ ۚ قَالَ مَعَاذَ اللَّهِ ۖ إِنَّهُ رَبِّي أَحْسَنَ مَثْوَايَ ۖ إِنَّهُ لَا يُفْلِحُ الظَّالِمُونَ (23) Ndipo mkazi wam’nyumba imene Yosefe anali kukhala adamunyengerera kuti agone naye, ndipo adatseka zitseko ndipo adati kwa iye, “Bwera kuno iwe.” Iye adati, “Ndilikupempha chitetezo kwa Mulungu! Ndithudi iye ndi bwana wanga amene amandisamalira bwino. Ndithudi ochita zoipa sapambana ayi.” |
وَلَقَدْ هَمَّتْ بِهِ ۖ وَهَمَّ بِهَا لَوْلَا أَن رَّأَىٰ بُرْهَانَ رَبِّهِ ۚ كَذَٰلِكَ لِنَصْرِفَ عَنْهُ السُّوءَ وَالْفَحْشَاءَ ۚ إِنَّهُ مِنْ عِبَادِنَا الْمُخْلَصِينَ (24) Ndithudi mkazi adamufunitsitsa Yosefe ndipo nayenso akadamufuna iye pakadapanda kuti adaona umboni wochokera kwa Ambuye ake. Ife tidatero ndi cholinga chomuteteza ku chinthu chochititsa manyazi ndiponso choipa. Ndithudi iye adali mmodzi wa akapolo athu otsogozedwa |
وَاسْتَبَقَا الْبَابَ وَقَدَّتْ قَمِيصَهُ مِن دُبُرٍ وَأَلْفَيَا سَيِّدَهَا لَدَى الْبَابِ ۚ قَالَتْ مَا جَزَاءُ مَنْ أَرَادَ بِأَهْلِكَ سُوءًا إِلَّا أَن يُسْجَنَ أَوْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (25) Ndipo onse adathamangitsana mpaka ku khomo ndipo mkazi uja adamung’ambira Yosefe malaya ake kumbuyo. Ndipo onse atafika pa khomo, adakumana ndi mwamuna wake wa mkaziyo. Mkazi adati, “Kodi ndi malipilo otani amene angaperekedwe kwa iye amene amafuna kuchita zoipa mkazi wako kupatula kumangidwa kapena chilango chowawakwambiri |
قَالَ هِيَ رَاوَدَتْنِي عَن نَّفْسِي ۚ وَشَهِدَ شَاهِدٌ مِّنْ أَهْلِهَا إِن كَانَ قَمِيصُهُ قُدَّ مِن قُبُلٍ فَصَدَقَتْ وَهُوَ مِنَ الْكَاذِبِينَ (26) Yosefe adati,“Sindinekomamkaziyu ndiye amene amandifuna ine.” Ndipo munthu wina, wachibalendimkaziyo, adaikiraumboninati,“Ngatimalaya ake ang’ambika kumimba ndiye kuti mkaziyu ali kunena zoona, ndipo kuti iye ndi wabodza.” |
وَإِن كَانَ قَمِيصُهُ قُدَّ مِن دُبُرٍ فَكَذَبَتْ وَهُوَ مِنَ الصَّادِقِينَ (27) “Koma ngati malaya ake ang’ambika kumbuyo, ndiye kuti mkaziyu wanama ndi kuti iye ali kunena zoona.” |
فَلَمَّا رَأَىٰ قَمِيصَهُ قُدَّ مِن دُبُرٍ قَالَ إِنَّهُ مِن كَيْدِكُنَّ ۖ إِنَّ كَيْدَكُنَّ عَظِيمٌ (28) Ndipo pamene mwamuna wake adaona kuti malaya ake adang’ambika kumbuyo, iye adati, “Ichi ndi chimodzi cha ukamberembere wanu wa amayi. Ndithudi ukamberembere wanu ndi waukulu.” |
يُوسُفُ أَعْرِضْ عَنْ هَٰذَا ۚ وَاسْتَغْفِرِي لِذَنبِكِ ۖ إِنَّكِ كُنتِ مِنَ الْخَاطِئِينَ (29) “oh Yosefe! Usayankhulenso china chilichonse pankhani izi. Iwe mkazi pempha chikhululukiro cha machimo ako. Ndithudi iwe ndiwe mmodzi wa olakwa zedi.” |
۞ وَقَالَ نِسْوَةٌ فِي الْمَدِينَةِ امْرَأَتُ الْعَزِيزِ تُرَاوِدُ فَتَاهَا عَن نَّفْسِهِ ۖ قَدْ شَغَفَهَا حُبًّا ۖ إِنَّا لَنَرَاهَا فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (30) Ndipo amai a mumzinda muja adati: “Mkazi wa Mfumu alikunyenga mnyamata wake. Ndithudi iye anali kumulakalaka zedi. Ndithudi ife tili kuona kuti mkaziyu wasochera kwambiri.” |
فَلَمَّا سَمِعَتْ بِمَكْرِهِنَّ أَرْسَلَتْ إِلَيْهِنَّ وَأَعْتَدَتْ لَهُنَّ مُتَّكَأً وَآتَتْ كُلَّ وَاحِدَةٍ مِّنْهُنَّ سِكِّينًا وَقَالَتِ اخْرُجْ عَلَيْهِنَّ ۖ فَلَمَّا رَأَيْنَهُ أَكْبَرْنَهُ وَقَطَّعْنَ أَيْدِيَهُنَّ وَقُلْنَ حَاشَ لِلَّهِ مَا هَٰذَا بَشَرًا إِنْ هَٰذَا إِلَّا مَلَكٌ كَرِيمٌ (31) Ndipo pamene iye adamva zokamba zawo, adawatumizira uthenga owaitana ndi kuwakonzera chakudya ndipo kwa aliyense, adamupatsa mpeni wodyera. Ndipo adati kwa Yosefe, “Tulukira kumene kuli iwo.” Ndipo pamene iwo adamuona iye, onse adamulemekeza ndipo adadzicheka manja awo. Ndipo iwo adati, “Mulungu ayeretsedwe! Uyu si munthu ayi koma mngelo wolemekezeka.” |
قَالَتْ فَذَٰلِكُنَّ الَّذِي لُمْتُنَّنِي فِيهِ ۖ وَلَقَدْ رَاوَدتُّهُ عَن نَّفْسِهِ فَاسْتَعْصَمَ ۖ وَلَئِن لَّمْ يَفْعَلْ مَا آمُرُهُ لَيُسْجَنَنَّ وَلَيَكُونًا مِّنَ الصَّاغِرِينَ (32) Mkazi uja adati, “Uyu ndiye mnyamata uja amene nonsenu munali kundidzudzula naye. Ndithudi ine ndidamunyenga koma iye adakanitsitsa. Tsopano ngati iye sachita zimene ndikumulamulira, ndithudi, adzaponyedwa ku ndende ndipo adzakhala mmodziwaanthuonyozedwa.” |
قَالَ رَبِّ السِّجْنُ أَحَبُّ إِلَيَّ مِمَّا يَدْعُونَنِي إِلَيْهِ ۖ وَإِلَّا تَصْرِفْ عَنِّي كَيْدَهُنَّ أَصْبُ إِلَيْهِنَّ وَأَكُن مِّنَ الْجَاهِلِينَ (33) Yosefe adati,“ohAmbuye wanga! Ndende ndi yabwino kwa ine kuposa zimene akundiitanira. Ngati inu simunditchinjiriza kuchiwembu chawo ine ndidzapendekera kwa iwo ndikukhala mmodzi wa anthu osadziwa.” |
فَاسْتَجَابَ لَهُ رَبُّهُ فَصَرَفَ عَنْهُ كَيْدَهُنَّ ۚ إِنَّهُ هُوَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (34) Motero Ambuye wake adamva pempho lake ndipo adam’phwetsera chiwembu chawo pa iye. Ndithudi Iye amamva zonse ndipo amadziwa chilichonse |
ثُمَّ بَدَا لَهُم مِّن بَعْدِ مَا رَأَوُا الْآيَاتِ لَيَسْجُنُنَّهُ حَتَّىٰ حِينٍ (35) Ndipo zidaonekera kwa iwo, atatha kuona zizindikiro, kuti iye am’mange mwakanthawi kochepa |
وَدَخَلَ مَعَهُ السِّجْنَ فَتَيَانِ ۖ قَالَ أَحَدُهُمَا إِنِّي أَرَانِي أَعْصِرُ خَمْرًا ۖ وَقَالَ الْآخَرُ إِنِّي أَرَانِي أَحْمِلُ فَوْقَ رَأْسِي خُبْزًا تَأْكُلُ الطَّيْرُ مِنْهُ ۖ نَبِّئْنَا بِتَأْوِيلِهِ ۖ إِنَّا نَرَاكَ مِنَ الْمُحْسِنِينَ (36) Ndipo anyamata awiri adalowa m’ndende pamodzi ndi iye. Mmodzi wa iwo adati, “Ndithudi ine ndalota ndili kutcheza vinyo” Ndipo wina adanena kuti, “Ine ndinalota nditanyamula pamutu panga mkate umene mbalame zimadya. Tiuze matanthauzo ake. Ndithudi ife tikukuona iwe kuti uli mmodzi wa anthu wochita zabwino.” |
قَالَ لَا يَأْتِيكُمَا طَعَامٌ تُرْزَقَانِهِ إِلَّا نَبَّأْتُكُمَا بِتَأْوِيلِهِ قَبْلَ أَن يَأْتِيَكُمَا ۚ ذَٰلِكُمَا مِمَّا عَلَّمَنِي رَبِّي ۚ إِنِّي تَرَكْتُ مِلَّةَ قَوْمٍ لَّا يُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَهُم بِالْآخِرَةِ هُمْ كَافِرُونَ (37) Yosefe adati, “Palibe chakudya chimene mumalandira, ngati chakudya chanu, chimene chidze kwa inu ine ndisanamasulire tanthauzo lake. Ichi ndicho chimene Ambuye wanga adandiphunzitsa. Ndithudi ine ndasiya chipembedzo cha anthu osakhulupirira mwa Mulungu ndiponso m’moyo umene uli nkudza.” |
وَاتَّبَعْتُ مِلَّةَ آبَائِي إِبْرَاهِيمَ وَإِسْحَاقَ وَيَعْقُوبَ ۚ مَا كَانَ لَنَا أَن نُّشْرِكَ بِاللَّهِ مِن شَيْءٍ ۚ ذَٰلِكَ مِن فَضْلِ اللَّهِ عَلَيْنَا وَعَلَى النَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَشْكُرُونَ (38) “Ine ndidatsatira chipembedzo cha makolo anga, Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Sikuli koyenera kwa ife kum’phatikiza Mulungu ndi chilichonse. Ichi ndi chisomo cha Mulungu kwa ife ndi kwa anthu a mitundu yonse, koma anthu ambiri sayamika ayi.” |
يَا صَاحِبَيِ السِّجْنِ أَأَرْبَابٌ مُّتَفَرِّقُونَ خَيْرٌ أَمِ اللَّهُ الْوَاحِدُ الْقَهَّارُ (39) “Oh inu anzanga awiri a m’mndende! Kodi milungu yosiyanasiyana ndi yabwino kapena wabwino ndi Mulungu mmodziyekhamwinimphamvuzonse?” |
مَا تَعْبُدُونَ مِن دُونِهِ إِلَّا أَسْمَاءً سَمَّيْتُمُوهَا أَنتُمْ وَآبَاؤُكُم مَّا أَنزَلَ اللَّهُ بِهَا مِن سُلْطَانٍ ۚ إِنِ الْحُكْمُ إِلَّا لِلَّهِ ۚ أَمَرَ أَلَّا تَعْبُدُوا إِلَّا إِيَّاهُ ۚ ذَٰلِكَ الدِّينُ الْقَيِّمُ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَعْلَمُونَ (40) “Palibechimene mumapembedza kuonjezera pa Iye, koma mayina chabe amene inu ndi makolo anu mudapeka, amene Mulungu sadatumize umboni wa mayinawo. Chiweruzo chili m’manja mwa Mulungu yekha. Iye adakulamulirani kuti inu musamapembedze wina koma Iye yekha. Chimenecho ndicho chipembedzo changwiro, koma anthu ambiri sazindikira.” |
يَا صَاحِبَيِ السِّجْنِ أَمَّا أَحَدُكُمَا فَيَسْقِي رَبَّهُ خَمْرًا ۖ وَأَمَّا الْآخَرُ فَيُصْلَبُ فَتَأْكُلُ الطَّيْرُ مِن رَّأْسِهِ ۚ قُضِيَ الْأَمْرُ الَّذِي فِيهِ تَسْتَفْتِيَانِ (41) “Oh inu akaidi anzanga awiri! Mmodzi wa inu adzaperekera kwa Ambuye wake vinyo kuti amwe ndipo wina adzapachikidwa pa mtanda ndipo mbalame zizidzadya kuchokera pamutu pake. Motero lamulo laperekedwa pa zinthu zimene munali kufunsa.” |
وَقَالَ لِلَّذِي ظَنَّ أَنَّهُ نَاجٍ مِّنْهُمَا اذْكُرْنِي عِندَ رَبِّكَ فَأَنسَاهُ الشَّيْطَانُ ذِكْرَ رَبِّهِ فَلَبِثَ فِي السِّجْنِ بِضْعَ سِنِينَ (42) Ndipo iye adati kwa mmodzi amene iye adamuganizira kuti adzapulumuka, “Ukandikumbukire ine kwa Ambuye wako.” Koma Satana adamuiwalitsa kuti anene za Yosefe kwa Mfumu. Kotero iye adakhala kundende zaka zingapo |
وَقَالَ الْمَلِكُ إِنِّي أَرَىٰ سَبْعَ بَقَرَاتٍ سِمَانٍ يَأْكُلُهُنَّ سَبْعٌ عِجَافٌ وَسَبْعَ سُنبُلَاتٍ خُضْرٍ وَأُخَرَ يَابِسَاتٍ ۖ يَا أَيُّهَا الْمَلَأُ أَفْتُونِي فِي رُؤْيَايَ إِن كُنتُمْ لِلرُّؤْيَا تَعْبُرُونَ (43) Ndipo Mfumu idati, “Ndithudi ine ndalota ndili kuona ng’ombe zisanu ndi ziwiri zonenepa, zimene zinali kudyedwa ndi ng’ombe zisanu ndi ziwiri zoonda ndiponso ngala zina zisanu ndi ziwiri zaziwisi ndi ngala zisanu ndi ziwiri zouma. Oh inu nduna zanga! Ndiuzeni tanthauzo la maloto anga, ngati inu mungathe kutanthauzira maloto.” |
قَالُوا أَضْغَاثُ أَحْلَامٍ ۖ وَمَا نَحْنُ بِتَأْوِيلِ الْأَحْلَامِ بِعَالِمِينَ (44) Iwo adati, “Awa ndi maloto opanda ntchito ndipo ife sititha kutanthauzira maloto.” |
وَقَالَ الَّذِي نَجَا مِنْهُمَا وَادَّكَرَ بَعْدَ أُمَّةٍ أَنَا أُنَبِّئُكُم بِتَأْوِيلِهِ فَأَرْسِلُونِ (45) Ndipo munthu amene adatulutsidwa m’ndende, adakumbukira patapita nthawi yaitali ndipo adati, “Ine ndikuuzani kutanthauzira kwake koma nditumizeni kuti ndipite.” |
يُوسُفُ أَيُّهَا الصِّدِّيقُ أَفْتِنَا فِي سَبْعِ بَقَرَاتٍ سِمَانٍ يَأْكُلُهُنَّ سَبْعٌ عِجَافٌ وَسَبْعِ سُنبُلَاتٍ خُضْرٍ وَأُخَرَ يَابِسَاتٍ لَّعَلِّي أَرْجِعُ إِلَى النَّاسِ لَعَلَّهُمْ يَعْلَمُونَ (46) “Oh Yosefe munthu wa choonadi! Tiuzeni za ng’ombe zisanu ndi ziwiri zonenepa zimene zinali kudyedwa ndi ng’ombe zisanu ndi ziwiri zoonda ndiponso za ngala zisanu ndi ziwiri zaziwisi ndi ngala zisanu ndi ziwiri zouma, kuti ndibwerere ndikawauze anthu kuti akadziwe tanthauzo lake?” |
قَالَ تَزْرَعُونَ سَبْعَ سِنِينَ دَأَبًا فَمَا حَصَدتُّمْ فَذَرُوهُ فِي سُنبُلِهِ إِلَّا قَلِيلًا مِّمَّا تَأْكُلُونَ (47) Yosefe adati, “Inu mudzabzala zaka zisanu ndi ziwiri monga momwe mumachitira ndipo zimene muzikolola muzizisiya mumakoko ake kupatula pang’ono zomwe muzidya.” |
ثُمَّ يَأْتِي مِن بَعْدِ ذَٰلِكَ سَبْعٌ شِدَادٌ يَأْكُلْنَ مَا قَدَّمْتُمْ لَهُنَّ إِلَّا قَلِيلًا مِّمَّا تُحْصِنُونَ (48) “Ndipo potha izi kudzadza zaka zisanu ndi ziwiri za chilala pamene mudzadya zimene mudasunga kupatula pang’ono zimene mudzasunge.” |
ثُمَّ يَأْتِي مِن بَعْدِ ذَٰلِكَ عَامٌ فِيهِ يُغَاثُ النَّاسُ وَفِيهِ يَعْصِرُونَ (49) “Ndipo pambuyo pa izi kudzabwera chaka chimene anthu adzalandira mvula yambiri, ndipo m’chaka chimenecho azidzafinya zipatso.” |
وَقَالَ الْمَلِكُ ائْتُونِي بِهِ ۖ فَلَمَّا جَاءَهُ الرَّسُولُ قَالَ ارْجِعْ إِلَىٰ رَبِّكَ فَاسْأَلْهُ مَا بَالُ النِّسْوَةِ اللَّاتِي قَطَّعْنَ أَيْدِيَهُنَّ ۚ إِنَّ رَبِّي بِكَيْدِهِنَّ عَلِيمٌ (50) Ndipo Mfumu idati, “Mubweretseni pamaso panga.” Koma pamene Kazembe wa Mfumu anadza kwa iye, Yosefe adati, “Bwerera kwa Ambuye wako ndipo ukamufunse za amayi amene adacheka manja awo. Ndithudi Ambuye wanga adziwa za ukachenjede wawo.” |
قَالَ مَا خَطْبُكُنَّ إِذْ رَاوَدتُّنَّ يُوسُفَ عَن نَّفْسِهِ ۚ قُلْنَ حَاشَ لِلَّهِ مَا عَلِمْنَا عَلَيْهِ مِن سُوءٍ ۚ قَالَتِ امْرَأَتُ الْعَزِيزِ الْآنَ حَصْحَصَ الْحَقُّ أَنَا رَاوَدتُّهُ عَن نَّفْسِهِ وَإِنَّهُ لَمِنَ الصَّادِقِينَ (51) Iyo inati, “Kodi cholinga chanu chinali chotani pamene inu munali kufuna kumunyenga Yosefe?” Amai anati, “Mulungu atiletse! Ife sitidziwa choipa chilichonse chimene iye anachita.” Mkazi wa mfumu adati, “Tsopano choonadi chadziwika. Ndine amene ndimamufuna ndipo iye, ndithudi, ndi wachilungamo.” |
ذَٰلِكَ لِيَعْلَمَ أَنِّي لَمْ أَخُنْهُ بِالْغَيْبِ وَأَنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي كَيْدَ الْخَائِنِينَ (52) “Kuchokera mu izi bwana wanga adzadziwa kuti sindidachite chinyengo pamene iye kunalibe ndiponso kuti Mulungu satsogolera ntchito za anthu a chinyengo.” |
۞ وَمَا أُبَرِّئُ نَفْسِي ۚ إِنَّ النَّفْسَ لَأَمَّارَةٌ بِالسُّوءِ إِلَّا مَا رَحِمَ رَبِّي ۚ إِنَّ رَبِّي غَفُورٌ رَّحِيمٌ (53) “Ine sindili kudziyeretsa, ndithudi, mtima wa munthu umakonda zoipa kupatula pamene Ambuye wanga aonetsa chisomo chake. Ndithudi Ambuye wanga amakhululukira ndiponso ndi Wachisoni chosatha.” |
وَقَالَ الْمَلِكُ ائْتُونِي بِهِ أَسْتَخْلِصْهُ لِنَفْسِي ۖ فَلَمَّا كَلَّمَهُ قَالَ إِنَّكَ الْيَوْمَ لَدَيْنَا مَكِينٌ أَمِينٌ (54) Mfumu idati, “Mubweretseni iye kwa ine kuti ndimusankhe iye kukhala munthu wanga.” Ndipo atayankhula naye, Mfumu idati, “Ndithudi iwe udzakhala ndi ife kuyambira lero ndipo udzakhala wolemekezeka ndiponso wokhulupirika.” |
قَالَ اجْعَلْنِي عَلَىٰ خَزَائِنِ الْأَرْضِ ۖ إِنِّي حَفِيظٌ عَلِيمٌ (55) Yosefe adati, “Ndiikeni pa udindo woyang’anira nkhokwe za m’dziko. Ine, ndithudi, ndidzazisunga bwino.” |
وَكَذَٰلِكَ مَكَّنَّا لِيُوسُفَ فِي الْأَرْضِ يَتَبَوَّأُ مِنْهَا حَيْثُ يَشَاءُ ۚ نُصِيبُ بِرَحْمَتِنَا مَن نَّشَاءُ ۖ وَلَا نُضِيعُ أَجْرَ الْمُحْسِنِينَ (56) Mmenemo ndi mmene tidamupatsira Yosefe udindo mdziko ndipo adakhala paliponse pamene amafuna. Ife timampatsa chisomo amene tamufuna ndipo sitisokoneza mphotho za anthu ochita zabwino |
وَلَأَجْرُ الْآخِرَةِ خَيْرٌ لِّلَّذِينَ آمَنُوا وَكَانُوا يَتَّقُونَ (57) Ndipo, ndithudi, mphotho ya m’moyo umene uli nkudza ndi yabwino kwa anthu okhulupirira ndi amene anali kuopa Mulungu |
وَجَاءَ إِخْوَةُ يُوسُفَ فَدَخَلُوا عَلَيْهِ فَعَرَفَهُمْ وَهُمْ لَهُ مُنكِرُونَ (58) Ndipo abale ake a Yosefe adadza, nalowa kwa iye. Iye adawazindikira koma iwo sadamuzindikire iye |
وَلَمَّا جَهَّزَهُم بِجَهَازِهِمْ قَالَ ائْتُونِي بِأَخٍ لَّكُم مِّنْ أَبِيكُمْ ۚ أَلَا تَرَوْنَ أَنِّي أُوفِي الْكَيْلَ وَأَنَا خَيْرُ الْمُنزِلِينَ (59) Ndipo pamene iye adawakonzera chakudya chawo, iye adati, “Ndibweretsereni m’bale wanu mwa abambo anu. Kodi inu simukuona kuti ine ndikukwaniritsa muyeso ndiponso ndimalandira bwino alendo?” |
فَإِن لَّمْ تَأْتُونِي بِهِ فَلَا كَيْلَ لَكُمْ عِندِي وَلَا تَقْرَبُونِ (60) “Koma ngati inu simudzabwera naye kwa ine inu simudzalandira muyeso wa chakudya kuchokera kwa ine ndiponso simudzandiyandikira.” |
قَالُوا سَنُرَاوِدُ عَنْهُ أَبَاهُ وَإِنَّا لَفَاعِلُونَ (61) Iwo adati, “Ife tikawanyengerera abambo ake kuti akamulole kuti adzabwere nafe. Ichi, ndithudi, tikachita.” |
وَقَالَ لِفِتْيَانِهِ اجْعَلُوا بِضَاعَتَهُمْ فِي رِحَالِهِمْ لَعَلَّهُمْ يَعْرِفُونَهَا إِذَا انقَلَبُوا إِلَىٰ أَهْلِهِمْ لَعَلَّهُمْ يَرْجِعُونَ (62) Yosefe adawauza anyamata a ntchito ake kuti aike ndalama zawo m’matumba mwawo kuti akazindikire akakafika kwa abale awo kuti mwina akabwerenso |
فَلَمَّا رَجَعُوا إِلَىٰ أَبِيهِمْ قَالُوا يَا أَبَانَا مُنِعَ مِنَّا الْكَيْلُ فَأَرْسِلْ مَعَنَا أَخَانَا نَكْتَلْ وَإِنَّا لَهُ لَحَافِظُونَ (63) Pamene iwo adabwerera kwa abambo awo iwo adati, “oh inu abambo athu! Kwaletsedwa kwa ife kugula muyeso wachakudya. Motero mtumizeni m’bale wathu pamodzi ndi ife kuti ife tikapeze muyeso wa chakudya. Ndipo ife tikamusamala.” |
قَالَ هَلْ آمَنُكُمْ عَلَيْهِ إِلَّا كَمَا أَمِنتُكُمْ عَلَىٰ أَخِيهِ مِن قَبْلُ ۖ فَاللَّهُ خَيْرٌ حَافِظًا ۖ وَهُوَ أَرْحَمُ الرَّاحِمِينَ (64) Yakobo adati, “Kodi ine ndikukhulupirireni pokupatsani uyu monga momwe ndidakukhulupirirani kale ndi m’bale wake uja? Komatu Mulungu ndiye Msungi wabwino ndipo Iye ndiye wachifundo mwa achifundo onse.” |
وَلَمَّا فَتَحُوا مَتَاعَهُمْ وَجَدُوا بِضَاعَتَهُمْ رُدَّتْ إِلَيْهِمْ ۖ قَالُوا يَا أَبَانَا مَا نَبْغِي ۖ هَٰذِهِ بِضَاعَتُنَا رُدَّتْ إِلَيْنَا ۖ وَنَمِيرُ أَهْلَنَا وَنَحْفَظُ أَخَانَا وَنَزْدَادُ كَيْلَ بَعِيرٍ ۖ ذَٰلِكَ كَيْلٌ يَسِيرٌ (65) Ndipo pamene iwo adatsekula katundu wawo, adapeza kuti ndalama zawo zabwezedwa kwa iwo. Iwo adati, “oh Atate athu! Kodi ndi chiyani chimene tingafunenso? Nazi ndalama zathu zabwezedwa kwa ife motero tidzapeza chakudya chambiri cha mabanja athu. Ndiponso tidzamusamala m’bale wathu ndi kuonjezera muyeso wokwana kunyamulidwa ndi ngamira imodzi. Umenewu ndiwo muyeso wochepa.” |
قَالَ لَنْ أُرْسِلَهُ مَعَكُمْ حَتَّىٰ تُؤْتُونِ مَوْثِقًا مِّنَ اللَّهِ لَتَأْتُنَّنِي بِهِ إِلَّا أَن يُحَاطَ بِكُمْ ۖ فَلَمَّا آتَوْهُ مَوْثِقَهُمْ قَالَ اللَّهُ عَلَىٰ مَا نَقُولُ وَكِيلٌ (66) Iye adati, “Ine sindidzamutumiza iye pamodzi ndi inu pokhapokha ngati mutandipatsalonjezoM’dzinalaMulungu,kutimudzabwera naye kwa ine kupatula ngati mutagonjetsedwa.” Ndipo pamene iwo adapereka lonjezo lawo, iye adanena kuti, “Pa zonse zimene tikunena, Mulungu akhale mboni.” |
وَقَالَ يَا بَنِيَّ لَا تَدْخُلُوا مِن بَابٍ وَاحِدٍ وَادْخُلُوا مِنْ أَبْوَابٍ مُّتَفَرِّقَةٍ ۖ وَمَا أُغْنِي عَنكُم مِّنَ اللَّهِ مِن شَيْءٍ ۖ إِنِ الْحُكْمُ إِلَّا لِلَّهِ ۖ عَلَيْهِ تَوَكَّلْتُ ۖ وَعَلَيْهِ فَلْيَتَوَكَّلِ الْمُتَوَكِّلُونَ (67) Ndipo iye adati, “E inu ana anga! Musakalowere khomo limodzi koma kaloweni m’makomo osiyanasiyana ndipo ine sindingakuthandizeni chilichonse polimbana ndi Mulungu. Zoonadi chiweruzo ndi cha Mulungu yekha. Mwa Iye yekha ine ndimaika chikhulupiriro changa ndipo onse amene amakhulupirira aike chikhulupiriro chawo mwa Iye.” |
وَلَمَّا دَخَلُوا مِنْ حَيْثُ أَمَرَهُمْ أَبُوهُم مَّا كَانَ يُغْنِي عَنْهُم مِّنَ اللَّهِ مِن شَيْءٍ إِلَّا حَاجَةً فِي نَفْسِ يَعْقُوبَ قَضَاهَا ۚ وَإِنَّهُ لَذُو عِلْمٍ لِّمَا عَلَّمْنَاهُ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَعْلَمُونَ (68) Pamene iwo adalowa, monga momwe atate awo adawalangizira, sizidawathandize chilichonse kwa Mulungu. Ichi sichinali china chilichonse koma kungokwaniritsa chifuniro chimene Yakobo adali nacho. Ndithudi iye adali ndi nzeru chifukwa Ife tidamuphunzitsa, koma anthu ambiri sadziwa |
وَلَمَّا دَخَلُوا عَلَىٰ يُوسُفَ آوَىٰ إِلَيْهِ أَخَاهُ ۖ قَالَ إِنِّي أَنَا أَخُوكَ فَلَا تَبْتَئِسْ بِمَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (69) NdipopameneiwoadalowakwaYosefe,iyeadamutenga m’bale wake pambali nati, “Ndithudi ine ndine m’bale wako ndipo usadandaule ndi zimene iwo adali kuchita.” |
فَلَمَّا جَهَّزَهُم بِجَهَازِهِمْ جَعَلَ السِّقَايَةَ فِي رَحْلِ أَخِيهِ ثُمَّ أَذَّنَ مُؤَذِّنٌ أَيَّتُهَا الْعِيرُ إِنَّكُمْ لَسَارِقُونَ (70) Ndipo pamene iye adawakonzera chakudya chawo,iye adaika mbale m’nthumba, la m’bale wake. Ndipo woitana adafuula kwa iwo nati, “oh inu apaulendo! Ndithudi inu ndinu akuba!” |
قَالُوا وَأَقْبَلُوا عَلَيْهِم مَّاذَا تَفْقِدُونَ (71) Iwo adatembenuka nati, “Kodi mwasowa chiyani?” |
قَالُوا نَفْقِدُ صُوَاعَ الْمَلِكِ وَلِمَن جَاءَ بِهِ حِمْلُ بَعِيرٍ وَأَنَا بِهِ زَعِيمٌ (72) Iwo adati, “Tikusowa mbale ya Mfumu ndipo aliyense amene abweretse mbale adzalandira katundu wokwana kunyamula ndi ngamira imodzi. Ndipo ine ndine mboni.” |
قَالُوا تَاللَّهِ لَقَدْ عَلِمْتُم مَّا جِئْنَا لِنُفْسِدَ فِي الْأَرْضِ وَمَا كُنَّا سَارِقِينَ (73) Iwo adanena kuti, “Pali Mulungu! Ndithudi inu muli kudziwa kuti ife sitinadze kudzaononga m’dziko lanu ndipo sindife mbala ayi!” |
قَالُوا فَمَا جَزَاؤُهُ إِن كُنتُمْ كَاذِبِينَ (74) Iwo adati, “Kodi chilango chake ndi chotani, ngati inu mukunena zabodza?” |
قَالُوا جَزَاؤُهُ مَن وُجِدَ فِي رَحْلِهِ فَهُوَ جَزَاؤُهُ ۚ كَذَٰلِكَ نَجْزِي الظَّالِمِينَ (75) Iwo adati: “Aliyense amene m’thumba mwake mupezeke mbale, iyeyo ndiye adzalandira chilango cha mbaleyo. Kotero ndimo mmene ife timalangira athu ochita zoipa.” |
فَبَدَأَ بِأَوْعِيَتِهِمْ قَبْلَ وِعَاءِ أَخِيهِ ثُمَّ اسْتَخْرَجَهَا مِن وِعَاءِ أَخِيهِ ۚ كَذَٰلِكَ كِدْنَا لِيُوسُفَ ۖ مَا كَانَ لِيَأْخُذَ أَخَاهُ فِي دِينِ الْمَلِكِ إِلَّا أَن يَشَاءَ اللَّهُ ۚ نَرْفَعُ دَرَجَاتٍ مَّن نَّشَاءُ ۗ وَفَوْقَ كُلِّ ذِي عِلْمٍ عَلِيمٌ (76) Ndipo iye adayamba kusanthula matumba awo asadasanthule thumba la mng’ono wake. Ndipo pomaliza iye adaitulutsa mbale ija m’thumba la mng’ono wakeyo. Mmenemo ndimo tidamphunzitsira nzeru Yosefe chifukwa ndi ulamulo wa m’dziko limenelo sakadatha kusunga m’bale wake pokhapokha ngati Mulungu akadafuna kuti zichitike motero. Ife timakweza paudindo amene tamufuna; koma pamwamba pa iwo amene ali ndi nzeru, alipo ena amene ndi odziwa kwambiri |
۞ قَالُوا إِن يَسْرِقْ فَقَدْ سَرَقَ أَخٌ لَّهُ مِن قَبْلُ ۚ فَأَسَرَّهَا يُوسُفُ فِي نَفْسِهِ وَلَمْ يُبْدِهَا لَهُمْ ۚ قَالَ أَنتُمْ شَرٌّ مَّكَانًا ۖ وَاللَّهُ أَعْلَمُ بِمَا تَصِفُونَ (77) Iwo adati, “Ngati iye waba, ndiye kuti panali m’bale wake wina amene adabanso kale.” Koma Yosefe adasunga chinsinsi ndipo sadawauze iwo ayi. Iye adaganiza kuti “Inu muli pa mlandu. Mulungu ali kudziwa bwino zonse zimene mukunena.” |
قَالُوا يَا أَيُّهَا الْعَزِيزُ إِنَّ لَهُ أَبًا شَيْخًا كَبِيرًا فَخُذْ أَحَدَنَا مَكَانَهُ ۖ إِنَّا نَرَاكَ مِنَ الْمُحْسِنِينَ (78) Iwo adati, “oh inu Mfumu! Ndithudi iye ali ndi abambo ake wokalamba kwambiri. Motero tengani mmodzi wa ife m’malo mwake. Ndithudi ife tili kukuonani kuti inu ndinu mmodzi wa anthu ochita zabwino.” |
قَالَ مَعَاذَ اللَّهِ أَن نَّأْخُذَ إِلَّا مَن وَجَدْنَا مَتَاعَنَا عِندَهُ إِنَّا إِذًا لَّظَالِمُونَ (79) Iye adati, “Mulungu ateteze kuti ife titenge wina wake m’malo mwa munthu amene tam’peza ndi katundu wathu. Ndithudi titatero tikhala opanda chilungamo.” |
فَلَمَّا اسْتَيْأَسُوا مِنْهُ خَلَصُوا نَجِيًّا ۖ قَالَ كَبِيرُهُمْ أَلَمْ تَعْلَمُوا أَنَّ أَبَاكُمْ قَدْ أَخَذَ عَلَيْكُم مَّوْثِقًا مِّنَ اللَّهِ وَمِن قَبْلُ مَا فَرَّطتُمْ فِي يُوسُفَ ۖ فَلَنْ أَبْرَحَ الْأَرْضَ حَتَّىٰ يَأْذَنَ لِي أَبِي أَوْ يَحْكُمَ اللَّهُ لِي ۖ وَهُوَ خَيْرُ الْحَاكِمِينَ (80) Motero pamene iwo anada nkhawa ndi iye, iwo adakhala paokha ndikunong’onezana. Ndipo wamkulu wawo adati, “Kodi inu simudziwa kuti abambo anu adatenga lonjezo kwa inu, M’dzina la Mulungu ndiponso kuti mudaphwanya chikhulupiriro chanu kale ndi nkhani ya Yosefe? Motero ine sindidzachoka m’dziko muno mpaka pamene abambo anga andilola kapena kufikira pamene Mulungu atapereka chiweruzo chake pa nkhani iyi. Iye ndiye Muweruzi wabwino pa aweruzi onse.” |
ارْجِعُوا إِلَىٰ أَبِيكُمْ فَقُولُوا يَا أَبَانَا إِنَّ ابْنَكَ سَرَقَ وَمَا شَهِدْنَا إِلَّا بِمَا عَلِمْنَا وَمَا كُنَّا لِلْغَيْبِ حَافِظِينَ (81) “Bwererani kwa atate wanu ndipo mukawauze kuti, “Oh Bambo wathu! Ndithudi mwana wanu waba ndipo ife sitiikira umboni kupatula pa zimene tikudziwa. Ndipo ife sitikadadziwa zinthu zobisika!” |
وَاسْأَلِ الْقَرْيَةَ الَّتِي كُنَّا فِيهَا وَالْعِيرَ الَّتِي أَقْبَلْنَا فِيهَا ۖ وَإِنَّا لَصَادِقُونَ (82) “Ndipo funsani anthu a mumzinda umene tidali ndiponso apaulendo amene tafika nawo, ndipo ndithudi ife tili kunena zoonadi.” |
قَالَ بَلْ سَوَّلَتْ لَكُمْ أَنفُسُكُمْ أَمْرًا ۖ فَصَبْرٌ جَمِيلٌ ۖ عَسَى اللَّهُ أَن يَأْتِيَنِي بِهِمْ جَمِيعًا ۚ إِنَّهُ هُوَ الْعَلِيمُ الْحَكِيمُ (83) Yakobo adati, “Iyayi! Mizimu yanu yakunyengani kuchita zoipa. Koma kupirira ndi kwabwino. Mwina Mulungu adzawabweretsa onse awiri kwa ine. Ndithudi Iye yekha amadziwa zinthu zonse ndiponso ndi waluntha.” |
وَتَوَلَّىٰ عَنْهُمْ وَقَالَ يَا أَسَفَىٰ عَلَىٰ يُوسُفَ وَابْيَضَّتْ عَيْنَاهُ مِنَ الْحُزْنِ فَهُوَ كَظِيمٌ (84) Ndipo iye adayang’ana kumbali nati, “Kalanga! Ine ndili ndi chisoni ndi Yosefe!” Maso ake adachita khungu chifukwachachisonichachikuluchimenechinalimumtima mwake |
قَالُوا تَاللَّهِ تَفْتَأُ تَذْكُرُ يُوسُفَ حَتَّىٰ تَكُونَ حَرَضًا أَوْ تَكُونَ مِنَ الْهَالِكِينَ (85) Ana ake adati, “Pali Mulungu! Inu simudzasiya kumukumbukira Yosefe mpaka mufoka ndi ukalamba kapena mufa.” |
قَالَ إِنَّمَا أَشْكُو بَثِّي وَحُزْنِي إِلَى اللَّهِ وَأَعْلَمُ مِنَ اللَّهِ مَا لَا تَعْلَمُونَ (86) Iye adati, “Ine ndili kudandaula kwa Mulungu za chisoni changa ndipo ndilikudziwa kuchokera kwa Mulungu zimene inu simukuzidziwa.” |
يَا بَنِيَّ اذْهَبُوا فَتَحَسَّسُوا مِن يُوسُفَ وَأَخِيهِ وَلَا تَيْأَسُوا مِن رَّوْحِ اللَّهِ ۖ إِنَّهُ لَا يَيْأَسُ مِن رَّوْحِ اللَّهِ إِلَّا الْقَوْمُ الْكَافِرُونَ (87) “oh ana anga!, Pitani mukafufuze za Yosefe pamodzi ndi m’bale wake, ndipo musataye mtima ndi chisomo cha Mulungu. Ndithudi palibe amene amataya mtima ndi chisomo cha Mulungu kupatula anthu osakhulupirira.” |
فَلَمَّا دَخَلُوا عَلَيْهِ قَالُوا يَا أَيُّهَا الْعَزِيزُ مَسَّنَا وَأَهْلَنَا الضُّرُّ وَجِئْنَا بِبِضَاعَةٍ مُّزْجَاةٍ فَأَوْفِ لَنَا الْكَيْلَ وَتَصَدَّقْ عَلَيْنَا ۖ إِنَّ اللَّهَ يَجْزِي الْمُتَصَدِّقِينَ (88) Ndipo pamene iwo adalowa kwa Yosefe, iwo adati, “Oh inu Mfumu yolemekezeka! Ife pamodzi ndi anthu athu tapeza mavuto, ndipo ife tabweretsa ndalama zochepa motero tiyesereni chakudya chokwanira ndipo tipatseni china chaulere. Ndithudi Mulungu amalipira anthu ochita zabwino.” |
قَالَ هَلْ عَلِمْتُم مَّا فَعَلْتُم بِيُوسُفَ وَأَخِيهِ إِذْ أَنتُمْ جَاهِلُونَ (89) Iye adati, “Kodi inu muli kudziwa zimene mudamuchitira Yosefe ndi m’bale wake pamene inu simumadziwa?” |
قَالُوا أَإِنَّكَ لَأَنتَ يُوسُفُ ۖ قَالَ أَنَا يُوسُفُ وَهَٰذَا أَخِي ۖ قَدْ مَنَّ اللَّهُ عَلَيْنَا ۖ إِنَّهُ مَن يَتَّقِ وَيَصْبِرْ فَإِنَّ اللَّهَ لَا يُضِيعُ أَجْرَ الْمُحْسِنِينَ (90) Iwo adati, “Kodi iwe ndiwedi Yosefe?” Iye adati, “Ine ndine Yosefe ndipo uyu ndi m’bale wanga. Mulungu, ndithudi, watikomera mtima ife. Ndithudi iye amene amaopa Mulungu ndi kupirira molimba ndithudi Mulungu sasokoneza malipiro a anthu ochita zabwino.” |
قَالُوا تَاللَّهِ لَقَدْ آثَرَكَ اللَّهُ عَلَيْنَا وَإِن كُنَّا لَخَاطِئِينَ (91) Iwo adati, “Pali Mulungu, ndithudi, Mulungu wakulemekezani inu kuposa ife ndipo, ndithudi, ife tidali olakwa.” |
قَالَ لَا تَثْرِيبَ عَلَيْكُمُ الْيَوْمَ ۖ يَغْفِرُ اللَّهُ لَكُمْ ۖ وَهُوَ أَرْحَمُ الرَّاحِمِينَ (92) Iye adati, “Palibe chidzudzulo kwa inu tsiku lalero ndipo Mulungu akukhululukireni inu. Iye ndiye wokhululukira mwa okhululukira onse.” |
اذْهَبُوا بِقَمِيصِي هَٰذَا فَأَلْقُوهُ عَلَىٰ وَجْهِ أَبِي يَأْتِ بَصِيرًا وَأْتُونِي بِأَهْلِكُمْ أَجْمَعِينَ (93) “Pitani ndi malaya angawa ndipo mukawaponye pamaso pa abambo anga ndipo maso awo adzayambanso kuona. Ndipo mukabwere, ndi abale anu onse kwa ine.” |
وَلَمَّا فَصَلَتِ الْعِيرُ قَالَ أَبُوهُمْ إِنِّي لَأَجِدُ رِيحَ يُوسُفَ ۖ لَوْلَا أَن تُفَنِّدُونِ (94) Ndipo pamene gulu la a paulendo lidanyamuka, atate awo adati, “Ndikumva fungo la Yosefe ngati inu muganiza kuti nzeru zanga zatha.” |
قَالُوا تَاللَّهِ إِنَّكَ لَفِي ضَلَالِكَ الْقَدِيمِ (95) Iwo adati, “Pali Mulungu! Iwe ndiwe wosokonekera kuyambira kale.” |
فَلَمَّا أَن جَاءَ الْبَشِيرُ أَلْقَاهُ عَلَىٰ وَجْهِهِ فَارْتَدَّ بَصِيرًا ۖ قَالَ أَلَمْ أَقُل لَّكُمْ إِنِّي أَعْلَمُ مِنَ اللَّهِ مَا لَا تَعْلَمُونَ (96) Ndipo pamene mthenga wa nkhani zabwino adadza iye adaponya malaya a Yosefe pamaso pake, ndipo nthawi yomweyo adayambanso kupenya. Iye adati, “Kodi ine sindidakuuzeni kuti ine ndinali kudziwa, kuchokera kwa Mulungu, zinthu zimene inu simuzidziwa?” |
قَالُوا يَا أَبَانَا اسْتَغْفِرْ لَنَا ذُنُوبَنَا إِنَّا كُنَّا خَاطِئِينَ (97) Iwo adati, “oh abambo athu! Tipempherenichikhululukirochamachimoathu, ndithudi, ife tidali ochimwa.” |
قَالَ سَوْفَ أَسْتَغْفِرُ لَكُمْ رَبِّي ۖ إِنَّهُ هُوَ الْغَفُورُ الرَّحِيمُ (98) Iye adati, “Ine ndidzakupempherani chikhululukiro kwa Ambuye wanga. Ndithudi Iye ndi wokhululukira ndiponso ndi Wachisoni chosatha.” |
فَلَمَّا دَخَلُوا عَلَىٰ يُوسُفَ آوَىٰ إِلَيْهِ أَبَوَيْهِ وَقَالَ ادْخُلُوا مِصْرَ إِن شَاءَ اللَّهُ آمِنِينَ (99) Ndipo pamene iwo adalowa kwa Yosefe iye adatenga makolo ake pa yekha nati, “Lowani mu dziko la Aiguputo, ngati Mulungu afuna, mwamtendere.” |
وَرَفَعَ أَبَوَيْهِ عَلَى الْعَرْشِ وَخَرُّوا لَهُ سُجَّدًا ۖ وَقَالَ يَا أَبَتِ هَٰذَا تَأْوِيلُ رُؤْيَايَ مِن قَبْلُ قَدْ جَعَلَهَا رَبِّي حَقًّا ۖ وَقَدْ أَحْسَنَ بِي إِذْ أَخْرَجَنِي مِنَ السِّجْنِ وَجَاءَ بِكُم مِّنَ الْبَدْوِ مِن بَعْدِ أَن نَّزَغَ الشَّيْطَانُ بَيْنِي وَبَيْنَ إِخْوَتِي ۚ إِنَّ رَبِّي لَطِيفٌ لِّمَا يَشَاءُ ۚ إِنَّهُ هُوَ الْعَلِيمُ الْحَكِيمُ (100) Ndipo iye adanyamula makolo ake ndikuwakhazika pa mpando wolemekezeka ndipo onse adagwa pansi kulemekeza iye. Ndipo iye adati, “Oh bambo wanga! Ili ndi tanthauzo la maloto anga aja akale. Ndithudi Ambuye wanga adawapanga kukhala oona. Iye adandichitira ine ubwino pamene adanditulutsa kundende ndipo adakubweretsani inu kuchokera ku midzi pambuyo pakuti satana adakhazikitsa udani pakati pa ine ndi abale anga. Ndithudi Ambuye wanga ndi waulemu ndi wachisoni kwa amene Iye wamufuna. Ndithudi! Iye yekha ndi wodziwa zonse ndi wanzeru.” |
۞ رَبِّ قَدْ آتَيْتَنِي مِنَ الْمُلْكِ وَعَلَّمْتَنِي مِن تَأْوِيلِ الْأَحَادِيثِ ۚ فَاطِرَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ أَنتَ وَلِيِّي فِي الدُّنْيَا وَالْآخِرَةِ ۖ تَوَفَّنِي مُسْلِمًا وَأَلْحِقْنِي بِالصَّالِحِينَ (101) “Ambuye, Inu ndithudi, mwandipatsa ine ulemerero ndi kundiphunzitsa kutanthauzira maloto. Inu ndinu Namalenga wakumwamba ndi dziko lapansi. Inu ndinu Msungi wanga m’dziko lino ndiponso m’dziko limene lili nkudza. Ndilekeni kuti ndife ndili kukulambirani inu ndipo ndiikeni m’gulu la anthu abwino.” |
ذَٰلِكَ مِنْ أَنبَاءِ الْغَيْبِ نُوحِيهِ إِلَيْكَ ۖ وَمَا كُنتَ لَدَيْهِمْ إِذْ أَجْمَعُوا أَمْرَهُمْ وَهُمْ يَمْكُرُونَ (102) Chimene tavumbulutsa kwa iwe ndi mbiri yakale yachinsinsi. Iwe kudalibe pamene abale ake a Yosefe onse adakonza chiwembu |
وَمَا أَكْثَرُ النَّاسِ وَلَوْ حَرَصْتَ بِمُؤْمِنِينَ (103) Ndipo anthu ambiri sadzakhulupirira ngakhale ungalimbikire motani |
وَمَا تَسْأَلُهُمْ عَلَيْهِ مِنْ أَجْرٍ ۚ إِنْ هُوَ إِلَّا ذِكْرٌ لِّلْعَالَمِينَ (104) Iwe siuwafunsamalipirochifukwachaichi. Ichindichizindikiro ndi chikumbutso kwa anthu a mitundu yonse |
وَكَأَيِّن مِّنْ آيَةٍ فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ يَمُرُّونَ عَلَيْهَا وَهُمْ عَنْهَا مُعْرِضُونَ (105) Kodi ndi zizindikiro zingati za mu mlengalenga ndi za m’dziko lapansi zimene iwo amangozipyola osalabadira china chilichonse |
وَمَا يُؤْمِنُ أَكْثَرُهُم بِاللَّهِ إِلَّا وَهُم مُّشْرِكُونَ (106) Ndipo ambiri a iwo sakhulupirira mwa Mulungu kupatula kupembedza milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni |
أَفَأَمِنُوا أَن تَأْتِيَهُمْ غَاشِيَةٌ مِّنْ عَذَابِ اللَّهِ أَوْ تَأْتِيَهُمُ السَّاعَةُ بَغْتَةً وَهُمْ لَا يَشْعُرُونَ (107) Kodi iwo amaganiza kuti ndi otetezedwa ku chilango cha Mulungu kuti chilango chake sichidzadza pa iwo mwadzidzidzi opanda kuzindikira |
قُلْ هَٰذِهِ سَبِيلِي أَدْعُو إِلَى اللَّهِ ۚ عَلَىٰ بَصِيرَةٍ أَنَا وَمَنِ اتَّبَعَنِي ۖ وَسُبْحَانَ اللَّهِ وَمَا أَنَا مِنَ الْمُشْرِكِينَ (108) Nena, “Iyi ndi njira yanga. Ine mosakayika, ndili kukuitanani ndi nzeru kuti mukhale ndi chikhulupiriro mwa Mulungu, ine pamodzi ndi onditsatira anga. Ulemerero ukhale kwa Mulungu ndipo ine sindine wopembedza mafano ayi.” |
وَمَا أَرْسَلْنَا مِن قَبْلِكَ إِلَّا رِجَالًا نُّوحِي إِلَيْهِم مِّنْ أَهْلِ الْقُرَىٰ ۗ أَفَلَمْ يَسِيرُوا فِي الْأَرْضِ فَيَنظُرُوا كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۗ وَلَدَارُ الْآخِرَةِ خَيْرٌ لِّلَّذِينَ اتَّقَوْا ۗ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (109) Ndipo Ife sitinatumizepo iwe usanadze, wina kupatula anthu amene tinawatsogolera kuchokera pakati pa anthu a m’mizinda. Kodi iwo sanayende padziko ndi kuona zimene zidawachitikira amene adalipo kale? Ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza ndi wabwino kwa anthu amene amaopa Mulungu ndipo amamumvera Iye. Kodi mulibe nzeru |
حَتَّىٰ إِذَا اسْتَيْأَسَ الرُّسُلُ وَظَنُّوا أَنَّهُمْ قَدْ كُذِبُوا جَاءَهُمْ نَصْرُنَا فَنُجِّيَ مَن نَّشَاءُ ۖ وَلَا يُرَدُّ بَأْسُنَا عَنِ الْقَوْمِ الْمُجْرِمِينَ (110) Mpaka pamene Atumwi athu adataya mtima ndipo anali kuganiza kuti kulibe wina aliyense amene akadawakhulupirira iwo, thandizo lathu lidadza pa iwo ndi kupulumutsa aliyense amene Ife tidamufuna. Ndipo chilango chathu sichingabweretsedwe m’mbuyo kwa anthu ochita zoipa |
لَقَدْ كَانَ فِي قَصَصِهِمْ عِبْرَةٌ لِّأُولِي الْأَلْبَابِ ۗ مَا كَانَ حَدِيثًا يُفْتَرَىٰ وَلَٰكِن تَصْدِيقَ الَّذِي بَيْنَ يَدَيْهِ وَتَفْصِيلَ كُلِّ شَيْءٍ وَهُدًى وَرَحْمَةً لِّقَوْمٍ يُؤْمِنُونَ (111) Ndithudi m’mbiri yawo muli phunziro kwa anthu ozindikira. Iyi si nkhani yopeka ayi koma ndi chitsimikiziro cha ma buku a Mulungu amene adaperekedwa kale, ndipo ndi mfotokozi wa zinthu zonse ndi chilangizo ndiponso madalitso kwa anthu okhulupirira |