×

Ndipo ngati pakadakhala Korani imene ikadayendetsa mapiri, kapena ikadaphwanya nthaka kapena kuwapanga 13:31 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Ar-Ra‘d ⮕ (13:31) ayat 31 in Chichewa

13:31 Surah Ar-Ra‘d ayat 31 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Ar-Ra‘d ayat 31 - الرَّعد - Page - Juz 13

﴿وَلَوۡ أَنَّ قُرۡءَانٗا سُيِّرَتۡ بِهِ ٱلۡجِبَالُ أَوۡ قُطِّعَتۡ بِهِ ٱلۡأَرۡضُ أَوۡ كُلِّمَ بِهِ ٱلۡمَوۡتَىٰۗ بَل لِّلَّهِ ٱلۡأَمۡرُ جَمِيعًاۗ أَفَلَمۡ يَاْيۡـَٔسِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَن لَّوۡ يَشَآءُ ٱللَّهُ لَهَدَى ٱلنَّاسَ جَمِيعٗاۗ وَلَا يَزَالُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ تُصِيبُهُم بِمَا صَنَعُواْ قَارِعَةٌ أَوۡ تَحُلُّ قَرِيبٗا مِّن دَارِهِمۡ حَتَّىٰ يَأۡتِيَ وَعۡدُ ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُخۡلِفُ ٱلۡمِيعَادَ ﴾
[الرَّعد: 31]

Ndipo ngati pakadakhala Korani imene ikadayendetsa mapiri, kapena ikadaphwanya nthaka kapena kuwapanga anthu akufa kuti ayankhule ikanakhala Korani inoyi. Zinthu zonse zimayendera chifuniro cha Mulungu. Kodi anthu okhulupirira sadziwa kuti Mulungu, akadafuna akadatsogolera anthu a mitundu yonse? Ndipo tsoka silidzaleka kugwa pa iwo amene sakhulupirira chifukwa cha ntchito zawo zoipa kapena ilo lidzakhala pafupi ndi midzi yawo mpaka pamene lonjezo la Mulungu likwaniritsidwa

❮ Previous Next ❯

ترجمة: ولو أن قرآنا سيرت به الجبال أو قطعت به الأرض أو كلم, باللغة نيانجا

﴿ولو أن قرآنا سيرت به الجبال أو قطعت به الأرض أو كلم﴾ [الرَّعد: 31]

Khaled Ibrahim Betala
“Ndipo ikadakhalapo Qur’an yomwe chifukwa cha iyo mapiri akadayendetsedwa (panthawi yoiwerenga), kapena chifukwa cha iyo, nthaka ikadang’ambidwa, kapena chifukwa cha iyo, akufa akadayankhulitsidwa, (yochititsa zimenezi ikadakhala Qur’an iyi. Koma ntchito ya Qur’an siimeneyo)! Zinthu zonse nza Allah. Kodi sadadziwebe amene akhulupirira, kuti Allah akadafuna akadawaongolera anthu onse (ku Chisilamu; akadawalenga monga angelo opanda zilakolako, koma wawapatsa nzeru ndi zilakolako kuti alimbane ndi ziwirizi; ena apambane ndi kulowa ku Munda wamtendere). Ndipo tsoka silisiya kuwapeza amene sadakhulupirire chifukwa cha zomwe achita, kapena litsika pafupi ndi dziko lawo kufikira lonjezo la Allah lifike (lowachotsa moyo), ndithudi, Allah saswa malonjezo (Ake)
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek