×

Surah Ar-Rad in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Raad

Translation of the Meanings of Surah Raad in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Raad translated into Chichewa, Surah Ar-Rad in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Raad in Chichewa - نيانجا, Verses 43 - Surah Number 13 - Page 249.

بسم الله الرحمن الرحيم

المر ۚ تِلْكَ آيَاتُ الْكِتَابِ ۗ وَالَّذِي أُنزِلَ إِلَيْكَ مِن رَّبِّكَ الْحَقُّ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يُؤْمِنُونَ (1)
Alif Lam Mim Raa. Awa ndi mavesi a Buku. Chimene chavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako ndi choonadi. Koma anthu ambiri sakhulupirira
اللَّهُ الَّذِي رَفَعَ السَّمَاوَاتِ بِغَيْرِ عَمَدٍ تَرَوْنَهَا ۖ ثُمَّ اسْتَوَىٰ عَلَى الْعَرْشِ ۖ وَسَخَّرَ الشَّمْسَ وَالْقَمَرَ ۖ كُلٌّ يَجْرِي لِأَجَلٍ مُّسَمًّى ۚ يُدَبِّرُ الْأَمْرَ يُفَصِّلُ الْآيَاتِ لَعَلَّكُم بِلِقَاءِ رَبِّكُمْ تُوقِنُونَ (2)
Mulungu ndi amene adakweza mlengalenga popanda nsanamira yomwe mungaione. Ndipo Iye adabuka pamwamba pa Mpando wa Chifumu ndipo adalamulira dzuwa ndi mwezi, ndipo chilichonse chimayenda monga momwe chidalamulidwira kufikira munthawi yake. Iye amalamulira zinthu zonse ndipo amafotokoza chivumbulutso chake momveka kuti inu mukhulupirire zoti mudzakumana ndi Ambuye wanu
وَهُوَ الَّذِي مَدَّ الْأَرْضَ وَجَعَلَ فِيهَا رَوَاسِيَ وَأَنْهَارًا ۖ وَمِن كُلِّ الثَّمَرَاتِ جَعَلَ فِيهَا زَوْجَيْنِ اثْنَيْنِ ۖ يُغْشِي اللَّيْلَ النَّهَارَ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يَتَفَكَّرُونَ (3)
Iye ndiye amene adatambasula dziko lapansi ndi kuika mu ilo mapiri ndi mitsinje. Ndipo pa mtundu uliwonse wa zipatso, adazilenga ziwiriziwiri. Iye amapanga usiku kuti uzivundikira usana. Ndithudi mu izi muli zizindikiro kwa anthu oganiza
وَفِي الْأَرْضِ قِطَعٌ مُّتَجَاوِرَاتٌ وَجَنَّاتٌ مِّنْ أَعْنَابٍ وَزَرْعٌ وَنَخِيلٌ صِنْوَانٌ وَغَيْرُ صِنْوَانٍ يُسْقَىٰ بِمَاءٍ وَاحِدٍ وَنُفَضِّلُ بَعْضَهَا عَلَىٰ بَعْضٍ فِي الْأُكُلِ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يَعْقِلُونَ (4)
Ndipo m’dziko muli njira zoyandikirana ndi minda ya mitengo ya mphesa ndi minda yobzalidwa ndi chimanga, nkhalango za mitengo ya tende, zofanana ndi zina zosafanana. Zipatso zake zimathiriridwa ndi madzi a mtundu umodzi: Ife timazipanga zina kukhala zabwino kupitirira zinzake pakudya. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu oganiza
۞ وَإِن تَعْجَبْ فَعَجَبٌ قَوْلُهُمْ أَإِذَا كُنَّا تُرَابًا أَإِنَّا لَفِي خَلْقٍ جَدِيدٍ ۗ أُولَٰئِكَ الَّذِينَ كَفَرُوا بِرَبِّهِمْ ۖ وَأُولَٰئِكَ الْأَغْلَالُ فِي أَعْنَاقِهِمْ ۖ وَأُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (5)
Ngati iwe ukudabwa, zodabwitsa kwambiri ndi mawu awo oti, “Ife tikadzakhala dothi, kodi tidzalengedwanso kwatsopano?” Amenewa ndiwo sadakhulupirire Ambuye wawo. Iwo ndiwo amene adzakhala ndi unyolo wa zitsulo umene udzamangiriridwa manja ku makosi awo. Amenewo ndi anthu akumoto ndipo iwo adzakhalako mpaka kalekale
وَيَسْتَعْجِلُونَكَ بِالسَّيِّئَةِ قَبْلَ الْحَسَنَةِ وَقَدْ خَلَتْ مِن قَبْلِهِمُ الْمَثُلَاتُ ۗ وَإِنَّ رَبَّكَ لَذُو مَغْفِرَةٍ لِّلنَّاسِ عَلَىٰ ظُلْمِهِمْ ۖ وَإِنَّ رَبَّكَ لَشَدِيدُ الْعِقَابِ (6)
Iwo ali kukuchititsa iwe kuti uchite choipa m’malo mwa chinthu chabwino. Komatu ndi anthu ambiri amene adalangidwa iwo asanadze. Ndithudi Ambuye wako amaonetsa chifundo kwa anthu ngakhale kuti iwo ndi ochimwa. Ndithudi Ambuye wako amalangiratu
وَيَقُولُ الَّذِينَ كَفَرُوا لَوْلَا أُنزِلَ عَلَيْهِ آيَةٌ مِّن رَّبِّهِ ۗ إِنَّمَا أَنتَ مُنذِرٌ ۖ وَلِكُلِّ قَوْمٍ هَادٍ (7)
Anthu osakhulupirira amanena kuti, “Bwanji sichinatumizidwe chizindikiro chochokera kwa Ambuye wake?” Iwe ndiwe mchenjezi basi ndipo mtundu uliwonse uli ndi mlangizi wawo
اللَّهُ يَعْلَمُ مَا تَحْمِلُ كُلُّ أُنثَىٰ وَمَا تَغِيضُ الْأَرْحَامُ وَمَا تَزْدَادُ ۖ وَكُلُّ شَيْءٍ عِندَهُ بِمِقْدَارٍ (8)
Mulungu amadziwa chinthu chilichonse chimene chili m’mimba mwa chachikazi ndi chimene chili choperewera ndiponso chimene chimabadwa nthawi yake isanakwane kapena itapitirira. Ndipo chithu chilichonse kwa Iye, chili ndi muyeso wake
عَالِمُ الْغَيْبِ وَالشَّهَادَةِ الْكَبِيرُ الْمُتَعَالِ (9)
Iye amadziwa zinthu zonse zooneka ndi zosaoneka. Iye ndi Wamkulu ndi wapamwamba kwambiri
سَوَاءٌ مِّنكُم مَّنْ أَسَرَّ الْقَوْلَ وَمَن جَهَرَ بِهِ وَمَنْ هُوَ مُسْتَخْفٍ بِاللَّيْلِ وَسَارِبٌ بِالنَّهَارِ (10)
Ndi chimodzimodzi kaya wina wa inu ayankhula monong’ona kapena mokweza kaya adzibisa mu mdima kapena ayenda usana
لَهُ مُعَقِّبَاتٌ مِّن بَيْنِ يَدَيْهِ وَمِنْ خَلْفِهِ يَحْفَظُونَهُ مِنْ أَمْرِ اللَّهِ ۗ إِنَّ اللَّهَ لَا يُغَيِّرُ مَا بِقَوْمٍ حَتَّىٰ يُغَيِّرُوا مَا بِأَنفُسِهِمْ ۗ وَإِذَا أَرَادَ اللَّهُ بِقَوْمٍ سُوءًا فَلَا مَرَدَّ لَهُ ۚ وَمَا لَهُم مِّن دُونِهِ مِن وَالٍ (11)
Aliyense ali ndi angelo amene amakhala patsogolo ndi pambuyo pake. Iwo amamuyang’anira iye potsatira malamulo a Mulungu. Ndithudi! Mulungu sadzasintha chikhalidwe cha anthu pokhapokha iwo eni ake asintha makhalidwe awo. Koma ngati Mulungu afuna kulanga anthu, palibe amene angathawe ndipo iwo sadzapeza wina kupatula Iye amene angawateteze
هُوَ الَّذِي يُرِيكُمُ الْبَرْقَ خَوْفًا وَطَمَعًا وَيُنشِئُ السَّحَابَ الثِّقَالَ (12)
Iye ndiye amene amakuonetsani mphenzi ngati choopsa ndi chobweretsa chiyembekezo. Ndipo Iye amasonkhanitsa mitambo yolemera
وَيُسَبِّحُ الرَّعْدُ بِحَمْدِهِ وَالْمَلَائِكَةُ مِنْ خِيفَتِهِ وَيُرْسِلُ الصَّوَاعِقَ فَيُصِيبُ بِهَا مَن يَشَاءُ وَهُمْ يُجَادِلُونَ فِي اللَّهِ وَهُوَ شَدِيدُ الْمِحَالِ (13)
Mabingu amamuyamika Iye ndipo angelo nawo amamuyamika ndipo amamuopa Iye kwambiri. Iye amaponya ziphaliwali ndipo ndi ziphaliwalizo amaononga aliyense amene wamufuna ngakhale kuti anthu osakhulupirira amatsutsa za Mulungu. Iye ndi wamphamvu zonse ndipo amalanga kwambiri
لَهُ دَعْوَةُ الْحَقِّ ۖ وَالَّذِينَ يَدْعُونَ مِن دُونِهِ لَا يَسْتَجِيبُونَ لَهُم بِشَيْءٍ إِلَّا كَبَاسِطِ كَفَّيْهِ إِلَى الْمَاءِ لِيَبْلُغَ فَاهُ وَمَا هُوَ بِبَالِغِهِ ۚ وَمَا دُعَاءُ الْكَافِرِينَ إِلَّا فِي ضَلَالٍ (14)
Kwa Iye kuli mawu a choonadi. Ndipo zimene iwo amazipembedza siziwayankha china chilichonse monga momwe munthu amene amatambasula manja ake ku madzi ndi kumawaitana kuti alowe m’kamwa mwake. Koma madzi sangathe kulowa m’kamwa! Ndipo mapemphero a anthu osakhulupirira ndi opanda phindu
وَلِلَّهِ يَسْجُدُ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ طَوْعًا وَكَرْهًا وَظِلَالُهُم بِالْغُدُوِّ وَالْآصَالِ ۩ (15)
Onse amene amakhala kumwamba ndi pa dziko lapansi amagwa pansi kugwadira Mulungu, mwachifuniro chawo kapena mokakamizidwa. Ndipo zithunzi zawo zimamugwadira Iye m’mawa ndi madzulo aliwonse
قُلْ مَن رَّبُّ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ قُلِ اللَّهُ ۚ قُلْ أَفَاتَّخَذْتُم مِّن دُونِهِ أَوْلِيَاءَ لَا يَمْلِكُونَ لِأَنفُسِهِمْ نَفْعًا وَلَا ضَرًّا ۚ قُلْ هَلْ يَسْتَوِي الْأَعْمَىٰ وَالْبَصِيرُ أَمْ هَلْ تَسْتَوِي الظُّلُمَاتُ وَالنُّورُ ۗ أَمْ جَعَلُوا لِلَّهِ شُرَكَاءَ خَلَقُوا كَخَلْقِهِ فَتَشَابَهَ الْخَلْقُ عَلَيْهِمْ ۚ قُلِ اللَّهُ خَالِقُ كُلِّ شَيْءٍ وَهُوَ الْوَاحِدُ الْقَهَّارُ (16)
Nena, “Kodi Ambuye wakumwamba ndi pa dziko lapansi ndani?” Nena, “Mulungu.” Nena, “Kodi inu mwasankha milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni imene, ngakhale kwa iyo yokha, singathe kuchita zinthu zoipa kapena zabwino?” Nena, “Kodi anthu a khungu ndi anthu oona ndi ofanana? Kapena mdima umafanana ndi kuwala? Kodi iwo akuphatikiza Mulungu ndi mafano awo? Kodi mafano awo adalenga zinthu zofanana ndi zimene Iye adalenga; kotero kuti zolengedwa zonse zimaoneka kwa iwo ngati zofanana?” Nena, “Mulungu ndi Namalenga wa zinthu zonse. Iye ndi Mmodzi yekha ndipo ndi Mwini Mphamvu zonse.”
أَنزَلَ مِنَ السَّمَاءِ مَاءً فَسَالَتْ أَوْدِيَةٌ بِقَدَرِهَا فَاحْتَمَلَ السَّيْلُ زَبَدًا رَّابِيًا ۚ وَمِمَّا يُوقِدُونَ عَلَيْهِ فِي النَّارِ ابْتِغَاءَ حِلْيَةٍ أَوْ مَتَاعٍ زَبَدٌ مِّثْلُهُ ۚ كَذَٰلِكَ يَضْرِبُ اللَّهُ الْحَقَّ وَالْبَاطِلَ ۚ فَأَمَّا الزَّبَدُ فَيَذْهَبُ جُفَاءً ۖ وَأَمَّا مَا يَنفَعُ النَّاسَ فَيَمْكُثُ فِي الْأَرْضِ ۚ كَذَٰلِكَ يَضْرِبُ اللَّهُ الْأَمْثَالَ (17)
Iye amagwetsa mvula kuchokera kumwamba ndipo madzi amayenda m’madambo molingana ndi muyeso wake. Ndipo madzi oyenda amapanga thovu lokwera. Ndipo kuchokera ku zitsulo zimene anthu amatenthetsa pa moto pofuna zinthu zodzikongoletsera ndi zodzisangalatsira, mumatuluka thovu chimodzimodzi. Mmenemo ndi mmene Mulungu amaonetsera poyera choona ndi chabodza. Likakhala thovu limatayidwa, pamene chimene chili chabwino kwa anthu chimatsala pa dziko. Kotero ndi mmene Mulungu amaperekera zitsanzo
لِلَّذِينَ اسْتَجَابُوا لِرَبِّهِمُ الْحُسْنَىٰ ۚ وَالَّذِينَ لَمْ يَسْتَجِيبُوا لَهُ لَوْ أَنَّ لَهُم مَّا فِي الْأَرْضِ جَمِيعًا وَمِثْلَهُ مَعَهُ لَافْتَدَوْا بِهِ ۚ أُولَٰئِكَ لَهُمْ سُوءُ الْحِسَابِ وَمَأْوَاهُمْ جَهَنَّمُ ۖ وَبِئْسَ الْمِهَادُ (18)
Iwo amene adayankha kuitana kwa Ambuye wawo ali ndi mphotho yamtengo wapatali. Koma iwo amene adakana kuitana kwake, ngakhale kuti akadakhala ndi chuma chonse chimene chili pa dziko lapansi ndi china choonjezera kuti chikakhale ngati dipo lawo; chawo chidzakhala chiweruzo choipa. Gahena ndiyo idzakhala mudzi wawo womwe ndi malo onyansa okhalamo
۞ أَفَمَن يَعْلَمُ أَنَّمَا أُنزِلَ إِلَيْكَ مِن رَّبِّكَ الْحَقُّ كَمَنْ هُوَ أَعْمَىٰ ۚ إِنَّمَا يَتَذَكَّرُ أُولُو الْأَلْبَابِ (19)
Kodi iye amene adziwa chimene chavumbulutsidwa kwaiwekuchokerakwaAmbuyewakokutindichoonadindi olingana ndi iye amene ali wakhungu? Ndi okhawo amene ali ndinzeruameneazindikira
الَّذِينَ يُوفُونَ بِعَهْدِ اللَّهِ وَلَا يَنقُضُونَ الْمِيثَاقَ (20)
Iwoameneamakwaniritsa lonjezo la Mulungu ndipo saphwanya lonjezolo
وَالَّذِينَ يَصِلُونَ مَا أَمَرَ اللَّهُ بِهِ أَن يُوصَلَ وَيَخْشَوْنَ رَبَّهُمْ وَيَخَافُونَ سُوءَ الْحِسَابِ (21)
Iwo amene amalumikiza chimene Iye wawalamula kuti chikhale chimodzi, amaopa Ambuye wawo ndipo amaopa zoopsa zimene zidzaoneka patsiku lachiweruzo
وَالَّذِينَ صَبَرُوا ابْتِغَاءَ وَجْهِ رَبِّهِمْ وَأَقَامُوا الصَّلَاةَ وَأَنفَقُوا مِمَّا رَزَقْنَاهُمْ سِرًّا وَعَلَانِيَةً وَيَدْرَءُونَ بِالْحَسَنَةِ السَّيِّئَةَ أُولَٰئِكَ لَهُمْ عُقْبَى الدَّارِ (22)
Ndi iwo amene amapirira chifukwa chofuna mtendere wa Mulungu modzipereka, amapitiriza mapemphero awo ndi kupereka zimene tawapatsa mseri kapena moonekera, ndipo amaletsa choipa pochita chinthu chabwino. Awa ndiwo amene adzaone zinthu zokoma
جَنَّاتُ عَدْنٍ يَدْخُلُونَهَا وَمَن صَلَحَ مِنْ آبَائِهِمْ وَأَزْوَاجِهِمْ وَذُرِّيَّاتِهِمْ ۖ وَالْمَلَائِكَةُ يَدْخُلُونَ عَلَيْهِم مِّن كُلِّ بَابٍ (23)
Iwo adzalowa ku Paradiso kwa muyaya pamodzi ndi ena a makolo awo angwiro, ndi akazi awo ndi ana awo. Kuchokera ku khomo lililonse angelo adzadza nati kwa iwo
سَلَامٌ عَلَيْكُم بِمَا صَبَرْتُمْ ۚ فَنِعْمَ عُقْبَى الدَّارِ (24)
“Mtendere ukhale pa inu chifukwa cha kupirira kwanu pa mavuto ochuluka. Yodalitsika ndi mphotho ya ku Paradiso!”
وَالَّذِينَ يَنقُضُونَ عَهْدَ اللَّهِ مِن بَعْدِ مِيثَاقِهِ وَيَقْطَعُونَ مَا أَمَرَ اللَّهُ بِهِ أَن يُوصَلَ وَيُفْسِدُونَ فِي الْأَرْضِ ۙ أُولَٰئِكَ لَهُمُ اللَّعْنَةُ وَلَهُمْ سُوءُ الدَّارِ (25)
Iwoameneamaphwanyalonjezola Mulunguatalilandira ndipo amalekanitsa zinthu zimene Iye adawalamulira kuti azilumikize, ndipo amachita zinthu zoipa pa dziko lapansi, temberero lidzaikidwa pa iwo ndipo malo awo okhala adzakhala osasangalatsa
اللَّهُ يَبْسُطُ الرِّزْقَ لِمَن يَشَاءُ وَيَقْدِرُ ۚ وَفَرِحُوا بِالْحَيَاةِ الدُّنْيَا وَمَا الْحَيَاةُ الدُّنْيَا فِي الْآخِرَةِ إِلَّا مَتَاعٌ (26)
Mulungu amapereka mowolowa manja kwa aliyense amene Iye wamufuna ndi monyalapsa ndipo iwo amasangalala m’moyo uno pamene chisangalalo cha m’moyo uno ndi cha kanthawi kochepa kwambiri pofanizira ndi cha moyo umene uli nkudza
وَيَقُولُ الَّذِينَ كَفَرُوا لَوْلَا أُنزِلَ عَلَيْهِ آيَةٌ مِّن رَّبِّهِ ۗ قُلْ إِنَّ اللَّهَ يُضِلُّ مَن يَشَاءُ وَيَهْدِي إِلَيْهِ مَنْ أَنَابَ (27)
Ndipo iwo amene sakhulupirira amati, “Kodi ndi chifukwa chiyani chizindikiro sichidaperekedwe kuchokera kwa Ambuye wake?” Nena, “Ndithudi Mulungu amasocheretsa aliyense amene wamufuna ndipo amatsogolera onse amene amalapa kwa Iye.”
الَّذِينَ آمَنُوا وَتَطْمَئِنُّ قُلُوبُهُم بِذِكْرِ اللَّهِ ۗ أَلَا بِذِكْرِ اللَّهِ تَطْمَئِنُّ الْقُلُوبُ (28)
Iwo ndi amene amakhulupirira ndipo mitima yawo imapeza mpumulo akamakumbukira Mulungu. Ndithudi m’chikumbukiro cha Mulungu mitima imapeza mpumulo
الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ طُوبَىٰ لَهُمْ وَحُسْنُ مَآبٍ (29)
Iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino adzasangalala ndipo mapeto awo adzakhala okoma
كَذَٰلِكَ أَرْسَلْنَاكَ فِي أُمَّةٍ قَدْ خَلَتْ مِن قَبْلِهَا أُمَمٌ لِّتَتْلُوَ عَلَيْهِمُ الَّذِي أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ وَهُمْ يَكْفُرُونَ بِالرَّحْمَٰنِ ۚ قُلْ هُوَ رَبِّي لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ عَلَيْهِ تَوَكَّلْتُ وَإِلَيْهِ مَتَابِ (30)
Kotero Ife takutumiza iwe ku mtundu wa anthu umene anthu ake ena adafa kale kuti ulakatule kwa iwo chivumbulutso chathu chimene tidavumbulutsa kwa iwe. Pamene iwo sakhulupirira mwa mwini chifundo. Nena “Iye ndiye Ambuye wanga. Kulibe Mulungu wina kupatula Iye yekha. Mwa Iye ine ndimadalira ndipo ndi kwa Iye kumene ine ndidzabwerera.”
وَلَوْ أَنَّ قُرْآنًا سُيِّرَتْ بِهِ الْجِبَالُ أَوْ قُطِّعَتْ بِهِ الْأَرْضُ أَوْ كُلِّمَ بِهِ الْمَوْتَىٰ ۗ بَل لِّلَّهِ الْأَمْرُ جَمِيعًا ۗ أَفَلَمْ يَيْأَسِ الَّذِينَ آمَنُوا أَن لَّوْ يَشَاءُ اللَّهُ لَهَدَى النَّاسَ جَمِيعًا ۗ وَلَا يَزَالُ الَّذِينَ كَفَرُوا تُصِيبُهُم بِمَا صَنَعُوا قَارِعَةٌ أَوْ تَحُلُّ قَرِيبًا مِّن دَارِهِمْ حَتَّىٰ يَأْتِيَ وَعْدُ اللَّهِ ۚ إِنَّ اللَّهَ لَا يُخْلِفُ الْمِيعَادَ (31)
Ndipo ngati pakadakhala Korani imene ikadayendetsa mapiri, kapena ikadaphwanya nthaka kapena kuwapanga anthu akufa kuti ayankhule ikanakhala Korani inoyi. Zinthu zonse zimayendera chifuniro cha Mulungu. Kodi anthu okhulupirira sadziwa kuti Mulungu, akadafuna akadatsogolera anthu a mitundu yonse? Ndipo tsoka silidzaleka kugwa pa iwo amene sakhulupirira chifukwa cha ntchito zawo zoipa kapena ilo lidzakhala pafupi ndi midzi yawo mpaka pamene lonjezo la Mulungu likwaniritsidwa
وَلَقَدِ اسْتُهْزِئَ بِرُسُلٍ مِّن قَبْلِكَ فَأَمْلَيْتُ لِلَّذِينَ كَفَرُوا ثُمَّ أَخَذْتُهُمْ ۖ فَكَيْفَ كَانَ عِقَابِ (32)
Ndipo ndithudi Atumwi ambiri adanyozedwa iwe usanadze ndipo Ine ndidawalekerera anthu osakhulupirira, ndipo pomaliza ndidawalanga. Kodi chilango changa chidali chowawa bwanji
أَفَمَنْ هُوَ قَائِمٌ عَلَىٰ كُلِّ نَفْسٍ بِمَا كَسَبَتْ ۗ وَجَعَلُوا لِلَّهِ شُرَكَاءَ قُلْ سَمُّوهُمْ ۚ أَمْ تُنَبِّئُونَهُ بِمَا لَا يَعْلَمُ فِي الْأَرْضِ أَم بِظَاهِرٍ مِّنَ الْقَوْلِ ۗ بَلْ زُيِّنَ لِلَّذِينَ كَفَرُوا مَكْرُهُمْ وَصُدُّوا عَنِ السَّبِيلِ ۗ وَمَن يُضْلِلِ اللَّهُ فَمَا لَهُ مِنْ هَادٍ (33)
Kodi Iye amene amayang’anira mizimu yonse ndi ntchito zonse zimene imachita angafanane ndi wina wosadziwa? Komabe iwo amakhazikitsa milungu ina m’malo mwa Mulungu weniweni. Nena, “Itchuleni! Kodi inu mungamuuze Mulungu zinthu zimene Iye sadziwa pa dziko kapena iwo ndi mawu abodza chabe?” Iyayi. Kwa iwo amene sakhulupirira, chiwembu chawo chimaoneka chabwino ndipo iwo atsekerezedwa kutsatira njira yoyenera ndipo aliyense amene Mulungu amamusocheza, kwa iye kulibe amene angamutsogolere
لَّهُمْ عَذَابٌ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ۖ وَلَعَذَابُ الْآخِرَةِ أَشَقُّ ۖ وَمَا لَهُم مِّنَ اللَّهِ مِن وَاقٍ (34)
Iwo ali ndi chilango mmoyo uno, ndipo, ndithudi, chilango chowawa kwambiri ndi chimene chili m’moyo umene uli nkudza. Ndipo iwo alibe amene adzawateteza kwa Mulungu
۞ مَّثَلُ الْجَنَّةِ الَّتِي وُعِدَ الْمُتَّقُونَ ۖ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ ۖ أُكُلُهَا دَائِمٌ وَظِلُّهَا ۚ تِلْكَ عُقْبَى الَّذِينَ اتَّقَوا ۖ وَّعُقْبَى الْكَافِرِينَ النَّارُ (35)
Chitsanzo cha Paradiso imene anthu oopa Mulungu adalonjezedwa, pansi pake pamadutsa mitsinje; zipatso zake ndi zosatha ndi mithunzi yake ndi yosathanso. Imeneyi ndiyo mphotho ya anthu oopa Mulungu. Koma mphotho ya anthu osakhulupirira ndi moto
وَالَّذِينَ آتَيْنَاهُمُ الْكِتَابَ يَفْرَحُونَ بِمَا أُنزِلَ إِلَيْكَ ۖ وَمِنَ الْأَحْزَابِ مَن يُنكِرُ بَعْضَهُ ۚ قُلْ إِنَّمَا أُمِرْتُ أَنْ أَعْبُدَ اللَّهَ وَلَا أُشْرِكَ بِهِ ۚ إِلَيْهِ أَدْعُو وَإِلَيْهِ مَآبِ (36)
Iwo amene tidawapatsa Buku, amasangalala ndi zimene zavumbulutsidwa kwa iwe koma pali kagulu kena kamene kamakana zina mwa izo. Nena, “Ine ndalamulidwa kupembedza Mulungu mmodzi ndipo kuti ndisamuphatikize Iye ndi chinthu china chilichonse. Ndi kwa Iye kumene ndimapempha ndipo kwa Iye ndidzabwerera.”
وَكَذَٰلِكَ أَنزَلْنَاهُ حُكْمًا عَرَبِيًّا ۚ وَلَئِنِ اتَّبَعْتَ أَهْوَاءَهُم بَعْدَمَا جَاءَكَ مِنَ الْعِلْمِ مَا لَكَ مِنَ اللَّهِ مِن وَلِيٍّ وَلَا وَاقٍ (37)
Kotero Ife talitumiza pansi kukhala chiweruzo champhamvu m’chiyankhulo cha Chiarabu. Ngati iwe utsatira zofuna zawo pamene utapatsidwa nzeru, palibe amene adzakupulumutsa kapena kukuteteza kwa Mulungu
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا رُسُلًا مِّن قَبْلِكَ وَجَعَلْنَا لَهُمْ أَزْوَاجًا وَذُرِّيَّةً ۚ وَمَا كَانَ لِرَسُولٍ أَن يَأْتِيَ بِآيَةٍ إِلَّا بِإِذْنِ اللَّهِ ۗ لِكُلِّ أَجَلٍ كِتَابٌ (38)
Ndithudi Ife tidatumiza Atumwi iwe usanadze ndipo tidawapatsa akazi ndi ana. Koma padalibe Mtumwi amene amabweretsa zizindikiro zozizwitsa popanda chilolezo cha Mulungu. Chilichonse chili ndi nthawi yake
يَمْحُو اللَّهُ مَا يَشَاءُ وَيُثْبِتُ ۖ وَعِندَهُ أُمُّ الْكِتَابِ (39)
Mulungu amafafaniza chimene Iye afuna kapena amakhazikitsa. Ndipo kwa Iye ndi kumene kuli Manthu wa Buku
وَإِن مَّا نُرِيَنَّكَ بَعْضَ الَّذِي نَعِدُهُمْ أَوْ نَتَوَفَّيَنَّكَ فَإِنَّمَا عَلَيْكَ الْبَلَاغُ وَعَلَيْنَا الْحِسَابُ (40)
Kaya tikuonetsa zina mwa zimene tikuwalonjeza kapena tikupha chilangocho chisanadze, udindo wako ndi kufalitsa uthenga, ndipo kwa Ife ndiko kuli chiwerengero
أَوَلَمْ يَرَوْا أَنَّا نَأْتِي الْأَرْضَ نَنقُصُهَا مِنْ أَطْرَافِهَا ۚ وَاللَّهُ يَحْكُمُ لَا مُعَقِّبَ لِحُكْمِهِ ۚ وَهُوَ سَرِيعُ الْحِسَابِ (41)
Kodi iwo saona mmene Ife timachepetsera malire a dziko pang’onopang’ono? Ndipo Mulungu akalamulira chinthu, palibe amene angatsutse. Iye ndi wachangu powerengera
وَقَدْ مَكَرَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ فَلِلَّهِ الْمَكْرُ جَمِيعًا ۖ يَعْلَمُ مَا تَكْسِبُ كُلُّ نَفْسٍ ۗ وَسَيَعْلَمُ الْكُفَّارُ لِمَنْ عُقْبَى الدَّارِ (42)
Ndithudi iwo amene adalipo awa asanadze nawonso adali kuchita ziwembu koma chikonzero chonse ndi cha Mulungu. Iye amadziwa chimene aliyense amalandira ndipo anthu osakhulupirira adzadziwa kuti kodi ndani amene adzalandira ubwino pomaliza
وَيَقُولُ الَّذِينَ كَفَرُوا لَسْتَ مُرْسَلًا ۚ قُلْ كَفَىٰ بِاللَّهِ شَهِيدًا بَيْنِي وَبَيْنَكُمْ وَمَنْ عِندَهُ عِلْمُ الْكِتَابِ (43)
Ndipo iwo amene sakhulupirira amati, “Iwe sindiwe Mtumwi.” Nena, “Mulungu akukwanira kukhala mboni pakati pa ine ndi inu ndi iwo amene amadziwa za m’Buku.”
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas