Quran with Chichewa translation - Surah Ibrahim ayat 22 - إبراهِيم - Page - Juz 13
﴿وَقَالَ ٱلشَّيۡطَٰنُ لَمَّا قُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ إِنَّ ٱللَّهَ وَعَدَكُمۡ وَعۡدَ ٱلۡحَقِّ وَوَعَدتُّكُمۡ فَأَخۡلَفۡتُكُمۡۖ وَمَا كَانَ لِيَ عَلَيۡكُم مِّن سُلۡطَٰنٍ إِلَّآ أَن دَعَوۡتُكُمۡ فَٱسۡتَجَبۡتُمۡ لِيۖ فَلَا تَلُومُونِي وَلُومُوٓاْ أَنفُسَكُمۖ مَّآ أَنَا۠ بِمُصۡرِخِكُمۡ وَمَآ أَنتُم بِمُصۡرِخِيَّ إِنِّي كَفَرۡتُ بِمَآ أَشۡرَكۡتُمُونِ مِن قَبۡلُۗ إِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ لَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ ﴾
[إبراهِيم: 22]
﴿وقال الشيطان لما قضي الأمر إن الله وعدكم وعد الحق ووعدتكم فأخلفتكم﴾ [إبراهِيم: 22]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo satana adzanena chiweruzo chikadzalamulidwa (oipa kulowa ku Moto, abwino kulowa ku Munda wamtendere): “Ndithu Allah adakulonjezani lonjezo loona (ndipo wakwaniritsa). Nane ndidakulonjezani, koma sindidakukwaniritsireni. Ndidalibe mphamvu pa inu (yokukakamizirani kunditsata) koma ndimangokuitanani basi, ndipo munkandiyankha. Choncho musandidzudzule, koma dzidzudzuleni nokha. Sindingathe kukuthangatani ndiponso inu simungathe kundithangata. Ndithu ine ndidakukana kundiphatikiza kwanu ndi Allah kale. Ndithu ochita zoipa adzapeza chilango chowawa.” |