Quran with Chichewa translation - Surah Al-Kahf ayat 17 - الكَهف - Page - Juz 15
﴿۞ وَتَرَى ٱلشَّمۡسَ إِذَا طَلَعَت تَّزَٰوَرُ عَن كَهۡفِهِمۡ ذَاتَ ٱلۡيَمِينِ وَإِذَا غَرَبَت تَّقۡرِضُهُمۡ ذَاتَ ٱلشِّمَالِ وَهُمۡ فِي فَجۡوَةٖ مِّنۡهُۚ ذَٰلِكَ مِنۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِۗ مَن يَهۡدِ ٱللَّهُ فَهُوَ ٱلۡمُهۡتَدِۖ وَمَن يُضۡلِلۡ فَلَن تَجِدَ لَهُۥ وَلِيّٗا مُّرۡشِدٗا ﴾
[الكَهف: 17]
﴿وترى الشمس إذا طلعت تزاور عن كهفهم ذات اليمين وإذا غربت تقرضهم﴾ [الكَهف: 17]
Khaled Ibrahim Betala “(Zidali tere) ukadakhala ukuliona dzuwa pamene linkatuluka (ndikuyamba kukwera), ukadaliona likulambalala kumbali kwa phanga lawo mbali yakudzanjadzanja, ndipo pamene linkalowa limawadutsa mbali yakumanzere (popanda kuwalunjika) pomwe iwo adali pamtetete mmenemo. Zimenezo ndi zina mwa zisonyezo za Allah (zosonyeza kukhoza Kwake). Amene Allah wamuongola iyeyo ndiye woongoka; ndipo amene wamulekelera kuti asokere, simungampezere mtetezi kapena muongoli |