الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي أَنزَلَ عَلَىٰ عَبْدِهِ الْكِتَابَ وَلَمْ يَجْعَل لَّهُ عِوَجًا ۜ (1) Kuyamikidwa konse kukhale kwa Mulungu amene wavumbulutsa kwa kapolo wake Buku ndipo sanaike mu ilo zokayikitsa zina zili zonse |
قَيِّمًا لِّيُنذِرَ بَأْسًا شَدِيدًا مِّن لَّدُنْهُ وَيُبَشِّرَ الْمُؤْمِنِينَ الَّذِينَ يَعْمَلُونَ الصَّالِحَاتِ أَنَّ لَهُمْ أَجْرًا حَسَنًا (2) Lolungama kuti lichenjeze za chilango chowawa chochokera kwa Iye ndi kuwauza anthu okhulupirira amene amachita ntchito zabwino kuti adzalandira mphotho yabwino |
مَّاكِثِينَ فِيهِ أَبَدًا (3) M’menemo adzakhalamo mpaka kalekale |
وَيُنذِرَ الَّذِينَ قَالُوا اتَّخَذَ اللَّهُ وَلَدًا (4) Ndi kuchenjeza iwo amene amanena kuti, “Mulungu wabereka mwana wamwamuna.” |
مَّا لَهُم بِهِ مِنْ عِلْمٍ وَلَا لِآبَائِهِمْ ۚ كَبُرَتْ كَلِمَةً تَخْرُجُ مِنْ أَفْوَاهِهِمْ ۚ إِن يَقُولُونَ إِلَّا كَذِبًا (5) Pa izi iwo sadziwa china chilichonse, ngakhale makolo awo. Loopsa ndi liwu lalikulu limene likutuluka m’kamwa mwawo. Iwo sanena china koma bodza |
فَلَعَلَّكَ بَاخِعٌ نَّفْسَكَ عَلَىٰ آثَارِهِمْ إِن لَّمْ يُؤْمِنُوا بِهَٰذَا الْحَدِيثِ أَسَفًا (6) Mwina iwe ukhoza kudzipha ndi chisoni chifukwa chakuti iwo sakhulupirira chivumbulutsochi |
إِنَّا جَعَلْنَا مَا عَلَى الْأَرْضِ زِينَةً لَّهَا لِنَبْلُوَهُمْ أَيُّهُمْ أَحْسَنُ عَمَلًا (7) Ndithudi! Ife tazipanga zimene zili m’dziko lapansi kukhala zokongola ndi cholinga chakuti tiwayese kuti ndani mwa iwo ali wochita zabwino |
وَإِنَّا لَجَاعِلُونَ مَا عَلَيْهَا صَعِيدًا جُرُزًا (8) Ndithudi! Ife tidzapanga zonse zimene zili pa dziko kukhala nthaka youma |
أَمْ حَسِبْتَ أَنَّ أَصْحَابَ الْكَهْفِ وَالرَّقِيمِ كَانُوا مِنْ آيَاتِنَا عَجَبًا (9) Kodi iwe ukuganiza kuti anthu a ku phanga ndi malembo a pa gome ndi zozizwitsa pakati pa zizindikiro zathu |
إِذْ أَوَى الْفِتْيَةُ إِلَى الْكَهْفِ فَقَالُوا رَبَّنَا آتِنَا مِن لَّدُنكَ رَحْمَةً وَهَيِّئْ لَنَا مِنْ أَمْرِنَا رَشَدًا (10) Pamene anyamata adathawa ndipo adalowa ndi cholinga chopeza malo kuphanga ndipo adati, “Ambuye wathu! Tionetseni chisoni chochokera kwa Inu ndipo tikonzereni zinthu zathu munjira zoyenera.” |
فَضَرَبْنَا عَلَىٰ آذَانِهِمْ فِي الْكَهْفِ سِنِينَ عَدَدًا (11) Motero Ife tidawatseka makutu awo pamene anali kuphanga zaka zingapo |
ثُمَّ بَعَثْنَاهُمْ لِنَعْلَمَ أَيُّ الْحِزْبَيْنِ أَحْصَىٰ لِمَا لَبِثُوا أَمَدًا (12) Ndipo Ife tidawadzutsa kuti tidziwe ndani mwa magulu awiriwa amene adasunga bwino nthawi imene iwo adakhala kuphanga |
نَّحْنُ نَقُصُّ عَلَيْكَ نَبَأَهُم بِالْحَقِّ ۚ إِنَّهُمْ فِتْيَةٌ آمَنُوا بِرَبِّهِمْ وَزِدْنَاهُمْ هُدًى (13) Ife tili kukuuza nkhani zawo zonse mwachoonadi. Ndithudi! Iwo anali anyamata amene adakhulupirira mwa Ambuye wawo, ndipo Ife tidawaonjezera malangizo |
وَرَبَطْنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمْ إِذْ قَامُوا فَقَالُوا رَبُّنَا رَبُّ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ لَن نَّدْعُوَ مِن دُونِهِ إِلَٰهًا ۖ لَّقَدْ قُلْنَا إِذًا شَطَطًا (14) Ndipo Ife tidalimbitsa mitima yawo, pamene adaima ndi kunena kuti, “Ambuye wathu ndiye Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi. Ife sitidzapembedza mulungu wina kupatula Iye yekha. Ngati tikatero ndiye kuti tayankhula bodza lopyola muyeso.” |
هَٰؤُلَاءِ قَوْمُنَا اتَّخَذُوا مِن دُونِهِ آلِهَةً ۖ لَّوْلَا يَأْتُونَ عَلَيْهِم بِسُلْطَانٍ بَيِّنٍ ۖ فَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّنِ افْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ كَذِبًا (15) Awa anthu athu amatumikira milungu ina yoonjezera pa Iye. Kodi ndi chifukwa chiyani iwo sawabweretsera umboni woonekera weniweni? Kodi wochimwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu |
وَإِذِ اعْتَزَلْتُمُوهُمْ وَمَا يَعْبُدُونَ إِلَّا اللَّهَ فَأْوُوا إِلَى الْكَهْفِ يَنشُرْ لَكُمْ رَبُّكُم مِّن رَّحْمَتِهِ وَيُهَيِّئْ لَكُم مِّنْ أَمْرِكُم مِّرْفَقًا (16) Pamene inu muwapewa iwo pamodzi ndi zimene iwo akupembedza osati Mulungu, thawirani kuphanga kuti mukapeze mpumulo. Ambuye wanu adzakutambasulirani chisoni chake ndi kukukonzerani njira yoti zinthu zikupepukireni |
۞ وَتَرَى الشَّمْسَ إِذَا طَلَعَت تَّزَاوَرُ عَن كَهْفِهِمْ ذَاتَ الْيَمِينِ وَإِذَا غَرَبَت تَّقْرِضُهُمْ ذَاتَ الشِّمَالِ وَهُمْ فِي فَجْوَةٍ مِّنْهُ ۚ ذَٰلِكَ مِنْ آيَاتِ اللَّهِ ۗ مَن يَهْدِ اللَّهُ فَهُوَ الْمُهْتَدِ ۖ وَمَن يُضْلِلْ فَلَن تَجِدَ لَهُ وَلِيًّا مُّرْشِدًا (17) Mwina iwe udaona dzuwa pamene linali kutuluka kupita ku mbali ya manja kwa phanga lawo ndipo pamene linali kulowa lilikudutsa ku mbali ya manzere, iwo adagona m’kati mwake. Chimenecho ndi chimodzi cha zizindikiro za Mulungu. Yense amene Mulungu amutsogolera ndi wotsogozedwa bwino koma iye amene Iye amusocheza, iwe siungam’pezere bwenzi woti amutsogolere |
وَتَحْسَبُهُمْ أَيْقَاظًا وَهُمْ رُقُودٌ ۚ وَنُقَلِّبُهُمْ ذَاتَ الْيَمِينِ وَذَاتَ الشِّمَالِ ۖ وَكَلْبُهُم بَاسِطٌ ذِرَاعَيْهِ بِالْوَصِيدِ ۚ لَوِ اطَّلَعْتَ عَلَيْهِمْ لَوَلَّيْتَ مِنْهُمْ فِرَارًا وَلَمُلِئْتَ مِنْهُمْ رُعْبًا (18) Ndipo inu mukadaganiza kuti iwo adali maso pamene iwo adali mtulo. Ndipo Ife tinali kuwatembenuza kuchoka ku mbali ya manja kupita ku mbali ya manzere ndipo galu wawo adali chigonere ndi miyendo yake iwiri ya m’tsogolo ili yotambasula pa khomo la phanga. Iwe ukadaona iwo ukadachita mantha ndipo ukadathawa. Ndithudi iwe ukadadzadzidwa ndi mantha chifukwa cha iwo |
وَكَذَٰلِكَ بَعَثْنَاهُمْ لِيَتَسَاءَلُوا بَيْنَهُمْ ۚ قَالَ قَائِلٌ مِّنْهُمْ كَمْ لَبِثْتُمْ ۖ قَالُوا لَبِثْنَا يَوْمًا أَوْ بَعْضَ يَوْمٍ ۚ قَالُوا رَبُّكُمْ أَعْلَمُ بِمَا لَبِثْتُمْ فَابْعَثُوا أَحَدَكُم بِوَرِقِكُمْ هَٰذِهِ إِلَى الْمَدِينَةِ فَلْيَنظُرْ أَيُّهَا أَزْكَىٰ طَعَامًا فَلْيَأْتِكُم بِرِزْقٍ مِّنْهُ وَلْيَتَلَطَّفْ وَلَا يُشْعِرَنَّ بِكُمْ أَحَدًا (19) Chomwecho Ife tidawadzutsa kuti afunsane wina ndi mnzake. Wina wa iwo adafunsa nati, “Kodi inu mwakhala nthawi yotani? Iwo adayankha kuti: ‘Ife takhala tsiku limodzi kapena theka la tsiku.’ Iwo adati: “Ambuye wanu ndiye amene adziwa bwino za nthawi imene mwakhala kuno. Mtumizeni mmodzi wa inu ku mzinda ndi ndalama zanu za siliva kuti akagule chakudya chabwino kuti akubweretsereni. Koma akasamale ndipo asakauze aliyense za inu.” |
إِنَّهُمْ إِن يَظْهَرُوا عَلَيْكُمْ يَرْجُمُوكُمْ أَوْ يُعِيدُوكُمْ فِي مِلَّتِهِمْ وَلَن تُفْلِحُوا إِذًا أَبَدًا (20) “Chifukwa ngati iwo adzadziwa za inu, adzakuponyani miyala kapena adzakubwezerani ku chipembedzo chawo. Ndipo zitatero inu simudzapambana ayi.” |
وَكَذَٰلِكَ أَعْثَرْنَا عَلَيْهِمْ لِيَعْلَمُوا أَنَّ وَعْدَ اللَّهِ حَقٌّ وَأَنَّ السَّاعَةَ لَا رَيْبَ فِيهَا إِذْ يَتَنَازَعُونَ بَيْنَهُمْ أَمْرَهُمْ ۖ فَقَالُوا ابْنُوا عَلَيْهِم بُنْيَانًا ۖ رَّبُّهُمْ أَعْلَمُ بِهِمْ ۚ قَالَ الَّذِينَ غَلَبُوا عَلَىٰ أَمْرِهِمْ لَنَتَّخِذَنَّ عَلَيْهِم مَّسْجِدًا (21) Motero Ifetidawadziwitsaanthuzaiwokutiiwoakhoza kudziwa kuti pangano la Mulungu ndi loona, ndipo kuti ola la chionongeko, ndithudi, lidzadza popanda chikayiko. Nthawi imene amakangana pa nkhani zawo za kuphanga iwo adati; ‘Amangireni nyumba pakhomo la phanga lawo. Ambuye wawo yekha ndiye amene adziwa za iwo.’ Ndipo iwo amene adapambana pa zochita zawo anati: “Ndithudi Ife tidzamanga malo opembedzerapo pamalopo.” |
سَيَقُولُونَ ثَلَاثَةٌ رَّابِعُهُمْ كَلْبُهُمْ وَيَقُولُونَ خَمْسَةٌ سَادِسُهُمْ كَلْبُهُمْ رَجْمًا بِالْغَيْبِ ۖ وَيَقُولُونَ سَبْعَةٌ وَثَامِنُهُمْ كَلْبُهُمْ ۚ قُل رَّبِّي أَعْلَمُ بِعِدَّتِهِم مَّا يَعْلَمُهُمْ إِلَّا قَلِيلٌ ۗ فَلَا تُمَارِ فِيهِمْ إِلَّا مِرَاءً ظَاهِرًا وَلَا تَسْتَفْتِ فِيهِم مِّنْهُمْ أَحَدًا (22) Ena a iwo adati, Adali atatu ndipo galu wawo adali wachinayi, pamene ena akuti adali asanu ndipo galu wawo adali wachisanu ndi chimodzi. Moganizira zinthu zobisika, ena akuti adalipo asanu ndi awiri ndipo galu wawo adali wachisanu ndi chitatu. Nena, “Ambuye wanga ndi wodziwa kwambiri chiwerengero chawo, palibe amene akuwadziwa kupatula ochepa okha.” Usakangane nawo za iwo kupatula mkangano womveka. Ndipo usamufunse wina aliyense wa anthu zokhudza anthu a kuphanga |
وَلَا تَقُولَنَّ لِشَيْءٍ إِنِّي فَاعِلٌ ذَٰلِكَ غَدًا (23) Ndipo usanene za china chilichonse kuti, “Ine ndidzachita ichi mawa.” |
إِلَّا أَن يَشَاءَ اللَّهُ ۚ وَاذْكُر رَّبَّكَ إِذَا نَسِيتَ وَقُلْ عَسَىٰ أَن يَهْدِيَنِ رَبِّي لِأَقْرَبَ مِنْ هَٰذَا رَشَدًا (24) Opanda kuonjezera mawu oti, “Ngati Mulungu afuna.” Ndipo kumbukira Ambuye wako ngati uiwala ndipo unene kuti, “Ngati ndikotheka Mulungu anditsogolere ine ndi kundibweretsa kufupi ndi choonadi m’malo mwa ichi.” |
وَلَبِثُوا فِي كَهْفِهِمْ ثَلَاثَ مِائَةٍ سِنِينَ وَازْدَادُوا تِسْعًا (25) Iwo adakhala m’phanga lawo zaka mazana atatu ndi kuonjeza mphambu zisanu ndi zinayi |
قُلِ اللَّهُ أَعْلَمُ بِمَا لَبِثُوا ۖ لَهُ غَيْبُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ أَبْصِرْ بِهِ وَأَسْمِعْ ۚ مَا لَهُم مِّن دُونِهِ مِن وَلِيٍّ وَلَا يُشْرِكُ فِي حُكْمِهِ أَحَدًا (26) Nena, “Mulungu amadziwa kwambiri mmene adakhalira. Kudziwa zinsinsi zonse za kumwamba ndi za dziko lapansi ndi kwake. Oh! Iye amapenyetsetsa ndipo amamvetsetsa. Iwo alibe wina woti awasamale oposa Mulungu. Ndipo Iye samuphatikiza wina aliyense mu ulamuliro wake.” |
وَاتْلُ مَا أُوحِيَ إِلَيْكَ مِن كِتَابِ رَبِّكَ ۖ لَا مُبَدِّلَ لِكَلِمَاتِهِ وَلَن تَجِدَ مِن دُونِهِ مُلْتَحَدًا (27) Werenga zimene zavumbulitsidwa kwa iwe m’Buku la Ambuye wako. Palibe munthu amene angasinthe mawu ake. Iwe siudzapeza kothawira kupatula kwa Iye |
وَاصْبِرْ نَفْسَكَ مَعَ الَّذِينَ يَدْعُونَ رَبَّهُم بِالْغَدَاةِ وَالْعَشِيِّ يُرِيدُونَ وَجْهَهُ ۖ وَلَا تَعْدُ عَيْنَاكَ عَنْهُمْ تُرِيدُ زِينَةَ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ۖ وَلَا تُطِعْ مَنْ أَغْفَلْنَا قَلْبَهُ عَن ذِكْرِنَا وَاتَّبَعَ هَوَاهُ وَكَانَ أَمْرُهُ فُرُطًا (28) Pirira pamodzi ndi iwo amene akupembedza Ambuye wawo m’mawa ndi madzulo kufuna chisangalalo chake. Maso ako asayang’ane kutali kuwasiya iwo ndi cholinga chakuti upeze zinthu zabwino m’moyo uno ndipo usamumvere iye amene mtima wake tauiwalitsa kuti asamatikumbukire; ndipo watsatira zofuna za mtima wake, ndipo ntchito zake zonse ndi zoonongeka |
وَقُلِ الْحَقُّ مِن رَّبِّكُمْ ۖ فَمَن شَاءَ فَلْيُؤْمِن وَمَن شَاءَ فَلْيَكْفُرْ ۚ إِنَّا أَعْتَدْنَا لِلظَّالِمِينَ نَارًا أَحَاطَ بِهِمْ سُرَادِقُهَا ۚ وَإِن يَسْتَغِيثُوا يُغَاثُوا بِمَاءٍ كَالْمُهْلِ يَشْوِي الْوُجُوهَ ۚ بِئْسَ الشَّرَابُ وَسَاءَتْ مُرْتَفَقًا (29) Nena, “Choonadi chimachokera kwa Ambuye wanu. Amene afuna akhulupirire ndipo amene safuna akane. Ndithudi anthu oipa tawakonzera moto umene mphanda zake zidzawazungulira.” Pamene iwo adzapempha madzi akumwa adzapatsidwa madzi otentha ngati mkuwa wosungunuka amene adzaotcha nkhope zawo. Kuipa kwa chakumwa ndi kuipa kwa malo okhala ndi kumeneku |
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ إِنَّا لَا نُضِيعُ أَجْرَ مَنْ أَحْسَنَ عَمَلًا (30) Kwa iwo amene akhulupirira nachita zabwino, ndithudi, Ife sitidzaononga mphotho ya anthu ochita zabwino |
أُولَٰئِكَ لَهُمْ جَنَّاتُ عَدْنٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهِمُ الْأَنْهَارُ يُحَلَّوْنَ فِيهَا مِنْ أَسَاوِرَ مِن ذَهَبٍ وَيَلْبَسُونَ ثِيَابًا خُضْرًا مِّن سُندُسٍ وَإِسْتَبْرَقٍ مُّتَّكِئِينَ فِيهَا عَلَى الْأَرَائِكِ ۚ نِعْمَ الثَّوَابُ وَحَسُنَتْ مُرْتَفَقًا (31) Iwo adzakhala m’minda yamuyaya ndipo mitsinje izidzayenda pansi pawo. Iwo adzavekedwa zibangiri za golide ndipo adzavala nsalu za sirika wobiriwira, wopepuka ndi wochindikala ndipo adzatsamira pa masofa ndipo malipiro abwino ndi malo abwino ofikira |
۞ وَاضْرِبْ لَهُم مَّثَلًا رَّجُلَيْنِ جَعَلْنَا لِأَحَدِهِمَا جَنَّتَيْنِ مِنْ أَعْنَابٍ وَحَفَفْنَاهُمَا بِنَخْلٍ وَجَعَلْنَا بَيْنَهُمَا زَرْعًا (32) Auze za fanizo la anthu awiri. Mmodzi wa iwo adali ndi minda iwiri ya mphesa imene tidazunguliza m’mbali mwake ndi mitengo ya tende ndipo tidaika pakati pake mbewu zina |
كِلْتَا الْجَنَّتَيْنِ آتَتْ أُكُلَهَا وَلَمْ تَظْلِم مِّنْهُ شَيْئًا ۚ وَفَجَّرْنَا خِلَالَهُمَا نَهَرًا (33) Munda uliwonse umapereka zipatso zake, ndipo siupunguza chilichonse ndipo Ife tidatumphutsa mitsinje m’kati mwa mindayo |
وَكَانَ لَهُ ثَمَرٌ فَقَالَ لِصَاحِبِهِ وَهُوَ يُحَاوِرُهُ أَنَا أَكْثَرُ مِنكَ مَالًا وَأَعَزُّ نَفَرًا (34) Ndipo Iye adali ndi zipatso zambiri ndipo adanena kwa mnzake pamene anali kutsutsana naye nati, “Ine ndili ndi chuma chambiri kuposa iwe ndiponso ndili ndi anthu a ntchito amphamvu kwambiri.” |
وَدَخَلَ جَنَّتَهُ وَهُوَ ظَالِمٌ لِّنَفْسِهِ قَالَ مَا أَظُنُّ أَن تَبِيدَ هَٰذِهِ أَبَدًا (35) Ndipo iye adalowa m’munda mwake modzitukumula yekha nati, “Ine sindiganiza kuti izi zidzatha ayi.” |
وَمَا أَظُنُّ السَّاعَةَ قَائِمَةً وَلَئِن رُّدِدتُّ إِلَىٰ رَبِّي لَأَجِدَنَّ خَيْرًا مِّنْهَا مُنقَلَبًا (36) “Ndipo ine sindikhulupirira kuti ola la chionongeko lidzadza. Ndipo ngakhale nditabwezedwa kwa Ambuye wanga, ine ndikapeza malo abwino oposa awa.” |
قَالَ لَهُ صَاحِبُهُ وَهُوَ يُحَاوِرُهُ أَكَفَرْتَ بِالَّذِي خَلَقَكَ مِن تُرَابٍ ثُمَّ مِن نُّطْفَةٍ ثُمَّ سَوَّاكَ رَجُلًا (37) Mnzake uja adati kwa iye, “Kodi iwe wam’kana Iye amene adakulenga iwe kuchokera ku dothi ndi kuchokera ku dontho la umuna ndipo adakuumba kukhala munthu?” |
لَّٰكِنَّا هُوَ اللَّهُ رَبِّي وَلَا أُشْرِكُ بِرَبِّي أَحَدًا (38) Akakhala ine, Mulungu ndiye Ambuye wanga. Ine sindidzamufanizira Iye ndi china chilichonse |
وَلَوْلَا إِذْ دَخَلْتَ جَنَّتَكَ قُلْتَ مَا شَاءَ اللَّهُ لَا قُوَّةَ إِلَّا بِاللَّهِ ۚ إِن تَرَنِ أَنَا أَقَلَّ مِنكَ مَالًا وَوَلَدًا (39) Bwanji pamene iwe umalowa m’munda mwako, siudanene kuti, “Izi ndi zimene Mulungu wafuna ndipo kulibe mphamvu kwina kulikonse kupatula kwa Mulungu? Ngakhale iwe ukundiona ine kuti ndine wochepekedwa kwambiri m’chuma ndi ana.” |
فَعَسَىٰ رَبِّي أَن يُؤْتِيَنِ خَيْرًا مِّن جَنَّتِكَ وَيُرْسِلَ عَلَيْهَا حُسْبَانًا مِّنَ السَّمَاءِ فَتُصْبِحَ صَعِيدًا زَلَقًا (40) “Mwina Ambuye wanga akhoza kundipatsa munda wabwino oposa wako ndi kutumiza ziphaliwali kuchokera kumwamba ndi kusandutsa nthaka kukhala yosabereka.” |
أَوْ يُصْبِحَ مَاؤُهَا غَوْرًا فَلَن تَسْتَطِيعَ لَهُ طَلَبًا (41) “Kapena kuzamitsa madzi ake kuti iwe usawapeze.” |
وَأُحِيطَ بِثَمَرِهِ فَأَصْبَحَ يُقَلِّبُ كَفَّيْهِ عَلَىٰ مَا أَنفَقَ فِيهَا وَهِيَ خَاوِيَةٌ عَلَىٰ عُرُوشِهَا وَيَقُولُ يَا لَيْتَنِي لَمْ أُشْرِكْ بِرَبِّي أَحَدًا (42) Ndipo zipatso zake zidaonongeka. Ndipo iye adayamba kufikisa zikhato zake mwachisoni chifukwa cha zonse zimene adaononga pa mindayi chifukwa zonse zidaonongeka. Ndipo iye adati: “Kalanga ine! Ndikanadziwa, sindikanaphatikiza milungu ina ndi Ambuye wanga!” |
وَلَمْ تَكُن لَّهُ فِئَةٌ يَنصُرُونَهُ مِن دُونِ اللَّهِ وَمَا كَانَ مُنتَصِرًا (43) Ndipo iye adalibe gulu lomuthandiza polimbana ndi Mulungu ndiponso adalibe mphamvu zoti adzitetezere kapena kudzipulumutsira |
هُنَالِكَ الْوَلَايَةُ لِلَّهِ الْحَقِّ ۚ هُوَ خَيْرٌ ثَوَابًا وَخَيْرٌ عُقْبًا (44) Kumeneko chitetezo chidzakhala chochokera kwa Mulungu, Mwini choonadi. Iye ndiye ali ndi malipiro ndiponso mapeto abwino |
وَاضْرِبْ لَهُم مَّثَلَ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا كَمَاءٍ أَنزَلْنَاهُ مِنَ السَّمَاءِ فَاخْتَلَطَ بِهِ نَبَاتُ الْأَرْضِ فَأَصْبَحَ هَشِيمًا تَذْرُوهُ الرِّيَاحُ ۗ وَكَانَ اللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ مُّقْتَدِرًا (45) Uwapatse chitsanzo cha moyo wa padziko lapansi. Moyowu uli ngati madzi amene timatsitsa kumwamba ndi mbeu za padziko la pansi zimene zimasakanizana ndi iwo ndipo zimakhala zanthete ndi zobiliwira. Koma pambuyo pake zimauma ndi kufumbutuka ndipo mphepo imazimwaza. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu pa chilichonse |
الْمَالُ وَالْبَنُونَ زِينَةُ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ۖ وَالْبَاقِيَاتُ الصَّالِحَاتُ خَيْرٌ عِندَ رَبِّكَ ثَوَابًا وَخَيْرٌ أَمَلًا (46) Chuma ndi ana ndi zinthu zokongola za umoyo wadziko lapansi. Koma ntchito zabwino zokhalitsa ndi zomwe zili ndi malipiro abwino kwa Ambuye wako ndi chiyembekezo chabwino |
وَيَوْمَ نُسَيِّرُ الْجِبَالَ وَتَرَى الْأَرْضَ بَارِزَةً وَحَشَرْنَاهُمْ فَلَمْ نُغَادِرْ مِنْهُمْ أَحَدًا (47) Ndi tsiku limene tidzagudubuza mapiri ndipo mudzaona nthaka ili kukhala poyera popanda chilichonse ndipo Ife tidzasonkhanitsa anthu onse. Palibe aliyense amene tidzamusiye mwa iwo |
وَعُرِضُوا عَلَىٰ رَبِّكَ صَفًّا لَّقَدْ جِئْتُمُونَا كَمَا خَلَقْنَاكُمْ أَوَّلَ مَرَّةٍ ۚ بَلْ زَعَمْتُمْ أَلَّن نَّجْعَلَ لَكُم مَّوْعِدًا (48) Ndipo iwo adzaonetsedwa kwa Ambuye wako ataimikidwa m’mizere ndipo tidzanena kuti, “Ndithudi inu mwabwera kwa Ife monga momwe tidakulengerani poyamba. Koma inu munali kuganiza kuti lonjezo lathu silidzakwaniritsidwa ayi.” |
وَوُضِعَ الْكِتَابُ فَتَرَى الْمُجْرِمِينَ مُشْفِقِينَ مِمَّا فِيهِ وَيَقُولُونَ يَا وَيْلَتَنَا مَالِ هَٰذَا الْكِتَابِ لَا يُغَادِرُ صَغِيرَةً وَلَا كَبِيرَةً إِلَّا أَحْصَاهَا ۚ وَوَجَدُوا مَا عَمِلُوا حَاضِرًا ۗ وَلَا يَظْلِمُ رَبُّكَ أَحَدًا (49) Ndipo Buku lidzaikidwa m’manja mwa aliyense ndipo iwe udzaona anthu ochita zoipa ali ndi mantha poona zonse zimene zidalembedwa mu Bukulo. Iwo adzati, “Tsoka kwa ife! Kodi Buku ili ndi lotani limene silisiya kanthu kakang’ono kapena kakakulu ndipo zonse lidasunga?” Ndipo iwo adzapeza ntchito zawo zonse zitalembedwa momwemo ndipo Ambuye wako sadzapondereza wina aliyense |
وَإِذْ قُلْنَا لِلْمَلَائِكَةِ اسْجُدُوا لِآدَمَ فَسَجَدُوا إِلَّا إِبْلِيسَ كَانَ مِنَ الْجِنِّ فَفَسَقَ عَنْ أَمْرِ رَبِّهِ ۗ أَفَتَتَّخِذُونَهُ وَذُرِّيَّتَهُ أَوْلِيَاءَ مِن دُونِي وَهُمْ لَكُمْ عَدُوٌّ ۚ بِئْسَ لِلظَّالِمِينَ بَدَلًا (50) Pamene Ife tidawauza angelo kuti, “Mugwadireni Adamu.” Motero onse anamugwadira Iye kupatula Satana amene adali mmodzi wa ziwanda ndipo adanyoza lamulo la Ambuye wake. Kodi mudzasankha iyeyo pamodzi ndi ana ake kukhala okutetezani ndi kukuthandizani m’malo mwa Ine, pamene iwo ndi adani? Kodi ndi choipa chotani chimene anthu ochita zoipa asankha |
۞ مَّا أَشْهَدتُّهُمْ خَلْقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَلَا خَلْقَ أَنفُسِهِمْ وَمَا كُنتُ مُتَّخِذَ الْمُضِلِّينَ عَضُدًا (51) Ine sindidawaonetse kalengedwe ka kumwamba ndi dziko lapansi kapena kalengedwe kawo komwe ndiponso Ine sindidawasankhe, osocheretsa anthu, kukhala ondithandiza anga |
وَيَوْمَ يَقُولُ نَادُوا شُرَكَائِيَ الَّذِينَ زَعَمْتُمْ فَدَعَوْهُمْ فَلَمْ يَسْتَجِيبُوا لَهُمْ وَجَعَلْنَا بَيْنَهُم مَّوْبِقًا (52) Ndi tsiku limene Iye adzati kwa iwo, “Itanani onse amene mumandifanizira aja, amene munkadzinamiza aja.” Ndipo iwo adzalira kwa iwo koma sadzawayankha ndipo Ife tidzabzala chidani pakati pawo |
وَرَأَى الْمُجْرِمُونَ النَّارَ فَظَنُّوا أَنَّهُم مُّوَاقِعُوهَا وَلَمْ يَجِدُوا عَنْهَا مَصْرِفًا (53) Ndipo anthu ochimwa adzaona moto wa ku Gahena ndipo adzatsimikiza kuti iwo aulowa. Ndipo iwo sadzapeza njira yothawirako |
وَلَقَدْ صَرَّفْنَا فِي هَٰذَا الْقُرْآنِ لِلنَّاسِ مِن كُلِّ مَثَلٍ ۚ وَكَانَ الْإِنسَانُ أَكْثَرَ شَيْءٍ جَدَلًا (54) Ndithudi Ife tawakhazikitsira anthu chitsanzo chilichonse mu Korani ino. Koma munthu ndi wotsutsa muzinthu zambiri |
وَمَا مَنَعَ النَّاسَ أَن يُؤْمِنُوا إِذْ جَاءَهُمُ الْهُدَىٰ وَيَسْتَغْفِرُوا رَبَّهُمْ إِلَّا أَن تَأْتِيَهُمْ سُنَّةُ الْأَوَّلِينَ أَوْ يَأْتِيَهُمُ الْعَذَابُ قُبُلًا (55) Palibe chimene chimawaletsa anthu kukhulupirira ndi kupempha chikhululukiro kwa Ambuye wawo pamene chilangizo chidza kwa iwo kupatula kuti ali kudikira njira za anthu a zaka zakale kuti ziwapeze iwo kapena kuti akumane ndi mazunzo maso ndi maso |
وَمَا نُرْسِلُ الْمُرْسَلِينَ إِلَّا مُبَشِّرِينَ وَمُنذِرِينَ ۚ وَيُجَادِلُ الَّذِينَ كَفَرُوا بِالْبَاطِلِ لِيُدْحِضُوا بِهِ الْحَقَّ ۖ وَاتَّخَذُوا آيَاتِي وَمَا أُنذِرُوا هُزُوًا (56) Ndipo Ife sitimangotumiza Atumwi kupatula kuti akalalikire nkhani yabwino ndi kupereka chenjezo. Koma anthu osakhulupirira amatsutsa mwabodza kuti agonjetse choonadi ndi bodza lawo. Ndipo iwo amasandutsa mawu anga ndi zonse zomwe achenjezedwa ngati nthabwala kapenachoseketsa |
وَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّن ذُكِّرَ بِآيَاتِ رَبِّهِ فَأَعْرَضَ عَنْهَا وَنَسِيَ مَا قَدَّمَتْ يَدَاهُ ۚ إِنَّا جَعَلْنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمْ أَكِنَّةً أَن يَفْقَهُوهُ وَفِي آذَانِهِمْ وَقْرًا ۖ وَإِن تَدْعُهُمْ إِلَى الْهُدَىٰ فَلَن يَهْتَدُوا إِذًا أَبَدًا (57) Kodiwolakwakwambirindanikuposa munthu amene akakumbutsidwa mavesi a Ambuye wake iye amawakana ndi kuiwala zimene manja ake atsogoza? Ife taika zophimba mitima yawo kuti asazindikire ndipo tatseka m’makutu mwawo. Ndipo ngati iwe utawaitana iwo kuti atsatire njira yoyenera, iwo sadzatsogozedwa |
وَرَبُّكَ الْغَفُورُ ذُو الرَّحْمَةِ ۖ لَوْ يُؤَاخِذُهُم بِمَا كَسَبُوا لَعَجَّلَ لَهُمُ الْعَذَابَ ۚ بَل لَّهُم مَّوْعِدٌ لَّن يَجِدُوا مِن دُونِهِ مَوْئِلًا (58) Ndipo Ambuye wako ndi wokhululukira kwambiri ndi Mwini chisoni. Iye akadafuna kuwalanga chifukwa cha machimo amene achita, ndithudi, Iye akadawafulumizitsira chilango chawo. Koma iwo ali ndi nthawi yawo ndipo sadzapeza kothawirako |
وَتِلْكَ الْقُرَىٰ أَهْلَكْنَاهُمْ لَمَّا ظَلَمُوا وَجَعَلْنَا لِمَهْلِكِهِم مَّوْعِدًا (59) Ndi Mizinda, imene tidaiononga pamene eni ake adachita zoipa tidaika nthawi yachionongeko chawo |
وَإِذْ قَالَ مُوسَىٰ لِفَتَاهُ لَا أَبْرَحُ حَتَّىٰ أَبْلُغَ مَجْمَعَ الْبَحْرَيْنِ أَوْ أَمْضِيَ حُقُبًا (60) Ndipo pamenepo Mose adamuuza mnyamata wake kuti, “Ine ndidzapitirirabe kuyenda mpaka pamene ndidzafika pamalo pamene nyanja ziwiri zikumana kapena ndidzapitirira kuyenda zaka ndi zaka.” |
فَلَمَّا بَلَغَا مَجْمَعَ بَيْنِهِمَا نَسِيَا حُوتَهُمَا فَاتَّخَذَ سَبِيلَهُ فِي الْبَحْرِ سَرَبًا (61) Koma pamene iwo adafika pamalo pamene nyanja ziwiri zidakumana, iwo adaiwala nsomba yawo ndipo iyo idatenga njira yake yodutsa kupita m’madzi |
فَلَمَّا جَاوَزَا قَالَ لِفَتَاهُ آتِنَا غَدَاءَنَا لَقَدْ لَقِينَا مِن سَفَرِنَا هَٰذَا نَصَبًا (62) Ndipo iwo atapitiriza ulendo wawo, Mose adati kwa mnyamata wake, “Bweretsa chakudya chathu. Ndithudi tapeza, mu ulendo wathu, zotopetsa.” |
قَالَ أَرَأَيْتَ إِذْ أَوَيْنَا إِلَى الصَّخْرَةِ فَإِنِّي نَسِيتُ الْحُوتَ وَمَا أَنسَانِيهُ إِلَّا الشَّيْطَانُ أَنْ أَذْكُرَهُ ۚ وَاتَّخَذَ سَبِيلَهُ فِي الْبَحْرِ عَجَبًا (63) Iye adati, “Kodi iwe siudaone pathanthwe pamene tidapuma paja, kuti ine ndidaiwala nsomba ndipo palibe china chimene chidandiiwalitsa kuti ndiikumbukire koma Satana yemwe adandiiwalitsa. Ndipo iyo idalowa m’madzi mozizwitsa.” |
قَالَ ذَٰلِكَ مَا كُنَّا نَبْغِ ۚ فَارْتَدَّا عَلَىٰ آثَارِهِمَا قَصَصًا (64) Mose adati, “Pamenepo ndi pamene timafuna.” Iwo adabwerera kulondola kumene adachokera |
فَوَجَدَا عَبْدًا مِّنْ عِبَادِنَا آتَيْنَاهُ رَحْمَةً مِّنْ عِندِنَا وَعَلَّمْنَاهُ مِن لَّدُنَّا عِلْمًا (65) Ndipo iwo adam’peza mmodzi wa akapolo wathu amene tidamupatsa chifundo chochokera kwa Ife ndiponso tidamuphunzitsa nzeru zochokera kwa Ife |
قَالَ لَهُ مُوسَىٰ هَلْ أَتَّبِعُكَ عَلَىٰ أَن تُعَلِّمَنِ مِمَّا عُلِّمْتَ رُشْدًا (66) Mose adati kwa iye, “Kodi ndingakutsateni kuti mwina mundiphunzitse zabwino zina za zimene mudaphunzitsidwa?” |
قَالَ إِنَّكَ لَن تَسْتَطِيعَ مَعِيَ صَبْرًا (67) Iye adati, “Ndithudi! Iwe siudzatha kupirira ndi ine.” |
وَكَيْفَ تَصْبِرُ عَلَىٰ مَا لَمْ تُحِطْ بِهِ خُبْرًا (68) Kodi iwe ungapirire bwanji pa zinthu zimene suli kuzidziwa |
قَالَ سَتَجِدُنِي إِن شَاءَ اللَّهُ صَابِرًا وَلَا أَعْصِي لَكَ أَمْرًا (69) Mose adati, “Ngati Mulungu afuna, udzandipeza ine ndili wopirira ndipo ine sindidzakunyoza iwe ayi.” |
قَالَ فَإِنِ اتَّبَعْتَنِي فَلَا تَسْأَلْنِي عَن شَيْءٍ حَتَّىٰ أُحْدِثَ لَكَ مِنْهُ ذِكْرًا (70) Iye adati, “Ngati iwe unganditsatire, usandifunse china chilichonse chimene ungawone mpaka pamene ine nditakuuza za chinthucho.” |
فَانطَلَقَا حَتَّىٰ إِذَا رَكِبَا فِي السَّفِينَةِ خَرَقَهَا ۖ قَالَ أَخَرَقْتَهَا لِتُغْرِقَ أَهْلَهَا لَقَدْ جِئْتَ شَيْئًا إِمْرًا (71) Motero iwo adanyamuka ndipo pamene iwo adakwera m’chombo, mnzake wa Mose adaboola chombocho. Mose adati, “Kodi waboola dzenje pa chombochi ndi cholinga chofuna kumiza eni ake? Ndithudi ichi ndi chinthu choipa kwambiri chimene wachita!” |
قَالَ أَلَمْ أَقُلْ إِنَّكَ لَن تَسْتَطِيعَ مَعِيَ صَبْرًا (72) Iye adati, “Kodi sindidakuuze kuti iwe siudzatha kupirira ndi ine?” |
قَالَ لَا تُؤَاخِذْنِي بِمَا نَسِيتُ وَلَا تُرْهِقْنِي مِنْ أَمْرِي عُسْرًا (73) Mose adati, “Musandidzudzule chifukwa cha zimene ndaiwala ndipo musandisenzetse katundu wolemera chifukwa cha zochita zanga.” |
فَانطَلَقَا حَتَّىٰ إِذَا لَقِيَا غُلَامًا فَقَتَلَهُ قَالَ أَقَتَلْتَ نَفْسًا زَكِيَّةً بِغَيْرِ نَفْسٍ لَّقَدْ جِئْتَ شَيْئًا نُّكْرًا (74) Ndipo onse adapitirizabe ulendo wawo mpaka pamene adakumana ndi mnyamata wina amene iye adamupha. Ndipo Mose adati, “Kodi iwe wapha munthu wosalakwa amene sadaphepo wina aliyense? Ndithudi iwe wachita chinthu choipa kwambiri.” |
۞ قَالَ أَلَمْ أَقُل لَّكَ إِنَّكَ لَن تَسْتَطِيعَ مَعِيَ صَبْرًا (75) Iye adati, “Kodi ine sindidakuuze kuti iwe siudzatha kupirira ndi ine?” |
قَالَ إِن سَأَلْتُكَ عَن شَيْءٍ بَعْدَهَا فَلَا تُصَاحِبْنِي ۖ قَدْ بَلَغْتَ مِن لَّدُنِّي عُذْرًا (76) Mose adati, “Ngati ine ndikufunsanso chinthu china pambuyo pa izi, usayende nanenso chifukwa ukhala utachipeza chifukwa kuchokera mwa ine.” |
فَانطَلَقَا حَتَّىٰ إِذَا أَتَيَا أَهْلَ قَرْيَةٍ اسْتَطْعَمَا أَهْلَهَا فَأَبَوْا أَن يُضَيِّفُوهُمَا فَوَجَدَا فِيهَا جِدَارًا يُرِيدُ أَن يَنقَضَّ فَأَقَامَهُ ۖ قَالَ لَوْ شِئْتَ لَتَّخَذْتَ عَلَيْهِ أَجْرًا (77) Ndipo onse adapitirira kuyenda mpaka pamene adapeza anthu a mu mzinda wina wake ndipo iwo adawafunsa anthu aja kuti awapatseko chakudya koma iwo adakana kuwalandira ngati alendo awo. Iwo adapeza mu mzindawo chipupa chikufuna kugwa ndipo Iye adachimanganso. Mose adati, “Iwe ukadafuna, ndithudi, ukadawauza kuti akulipire chifukwa cha ntchito imene wagwira.” |
قَالَ هَٰذَا فِرَاقُ بَيْنِي وَبَيْنِكَ ۚ سَأُنَبِّئُكَ بِتَأْوِيلِ مَا لَمْ تَسْتَطِع عَّلَيْهِ صَبْرًا (78) Iye adati, “Uku ndiye kusiyana kwa pakati pa iwe ndi ine. Ndikuuza tanthauzo la zinthu zimene iwe umakanika kupirira nazo.” |
أَمَّا السَّفِينَةُ فَكَانَتْ لِمَسَاكِينَ يَعْمَلُونَ فِي الْبَحْرِ فَأَرَدتُّ أَنْ أَعِيبَهَا وَكَانَ وَرَاءَهُم مَّلِكٌ يَأْخُذُ كُلَّ سَفِينَةٍ غَصْبًا (79) Chikakhala chombo chija eni ake adali anthu osauka amene amagwira ntchito pa nyanja. Ndipo ine ndinafuna kuti ndichiononge chifukwa kutsogolo kwawo kudali mfumu yomwe imalanda chombo chilichonse mwamphamvu |
وَأَمَّا الْغُلَامُ فَكَانَ أَبَوَاهُ مُؤْمِنَيْنِ فَخَشِينَا أَن يُرْهِقَهُمَا طُغْيَانًا وَكُفْرًا (80) Akakhala mnyamata uja, makolo ake onse adali okhulupirira mu choonadi ndipo timaopa kuti mwina iye akhoza kuwatembenuza ndi kuyamba kuchita zoipa ndi kusiya kukhulupirira |
فَأَرَدْنَا أَن يُبْدِلَهُمَا رَبُّهُمَا خَيْرًا مِّنْهُ زَكَاةً وَأَقْرَبَ رُحْمًا (81) Ndipo tidafuna kuti Ambuye wawo awapatse m’malo mwake, mwana wina wabwino ndi woyera mtima kuposa iye |
وَأَمَّا الْجِدَارُ فَكَانَ لِغُلَامَيْنِ يَتِيمَيْنِ فِي الْمَدِينَةِ وَكَانَ تَحْتَهُ كَنزٌ لَّهُمَا وَكَانَ أَبُوهُمَا صَالِحًا فَأَرَادَ رَبُّكَ أَن يَبْلُغَا أَشُدَّهُمَا وَيَسْتَخْرِجَا كَنزَهُمَا رَحْمَةً مِّن رَّبِّكَ ۚ وَمَا فَعَلْتُهُ عَنْ أَمْرِي ۚ ذَٰلِكَ تَأْوِيلُ مَا لَمْ تَسْطِع عَّلَيْهِ صَبْرًا (82) Chikakhala chipupa chija, eni ake adali ana awiri a masiye amene amakhala mu mzinda uja ndipo pansi pa chipupacho padali chuma chawo. Ndipo bambo wawo adali munthu wabwino motero Ambuye wako adafuna kuti anawo akule kuti adzatulutse okha chuma chawo ngati chifundo chochokera kwa Ambuye wako. Ine sindidachite zimenezi mwachifuniro changa ayi. Limeneli ndilo tanthauzo lake la zinthu zimene umalephera kupirira nazo |
وَيَسْأَلُونَكَ عَن ذِي الْقَرْنَيْنِ ۖ قُلْ سَأَتْلُو عَلَيْكُم مِّنْهُ ذِكْرًا (83) Ndipo iwo akukufunsa za Dhul-Qarnain. Nena, “Ine ndikufotokozerani za mbiri ya iye.” |
إِنَّا مَكَّنَّا لَهُ فِي الْأَرْضِ وَآتَيْنَاهُ مِن كُلِّ شَيْءٍ سَبَبًا (84) Ndithudi Ife tidamukhazika iye padziko ndipo tidamupatsa njira yopezera chilichonse |
فَأَتْبَعَ سَبَبًا (85) Ndipo iye adatsatira njira |
حَتَّىٰ إِذَا بَلَغَ مَغْرِبَ الشَّمْسِ وَجَدَهَا تَغْرُبُ فِي عَيْنٍ حَمِئَةٍ وَوَجَدَ عِندَهَا قَوْمًا ۗ قُلْنَا يَا ذَا الْقَرْنَيْنِ إِمَّا أَن تُعَذِّبَ وَإِمَّا أَن تَتَّخِذَ فِيهِمْ حُسْنًا (86) Mpaka pamene adafika polowera dzuwa ndipo adalipeza dzuwalo lili kulowa m’dziwe la matope akuda. Pafupi pomwepo iye adapeza anthu ena. Ife tidati, “Iwe Dhul-Qarnain! Iwe uli ndi ufulu wowalanga kapena wowachitira chisoni.” |
قَالَ أَمَّا مَن ظَلَمَ فَسَوْفَ نُعَذِّبُهُ ثُمَّ يُرَدُّ إِلَىٰ رَبِّهِ فَيُعَذِّبُهُ عَذَابًا نُّكْرًا (87) Iye adati, “Akakhala iye amene achita zoipa, tidzamulanga ndipo iye adzabwezedwa kwa Ambuye wake yemwe adzamulanga ndi chilango choipa kwambiri.” |
وَأَمَّا مَنْ آمَنَ وَعَمِلَ صَالِحًا فَلَهُ جَزَاءً الْحُسْنَىٰ ۖ وَسَنَقُولُ لَهُ مِنْ أَمْرِنَا يُسْرًا (88) Koma iye amene wakhulupirira ndikumachita ntchito zabwino, adzakhala ndi mphotho yabwino ndipo tidzamuyankhula mawu abwino |
ثُمَّ أَتْبَعَ سَبَبًا (89) Ndipo iye adatsatira njira ina |
حَتَّىٰ إِذَا بَلَغَ مَطْلِعَ الشَّمْسِ وَجَدَهَا تَطْلُعُ عَلَىٰ قَوْمٍ لَّمْ نَجْعَل لَّهُم مِّن دُونِهَا سِتْرًا (90) Mpaka pamene adafika kotulukira dzuwa kumene adalipeza dzuwa lili kutuluka pa anthu amene Ife sitidawaikire chotchinga ku dzuwa |
كَذَٰلِكَ وَقَدْ أَحَطْنَا بِمَا لَدَيْهِ خُبْرًا (91) Kotero Ife tidadziwa zonse zokhudza iye |
ثُمَّ أَتْبَعَ سَبَبًا (92) Ndipo iye adatsatiranso njira ina |
حَتَّىٰ إِذَا بَلَغَ بَيْنَ السَّدَّيْنِ وَجَدَ مِن دُونِهِمَا قَوْمًا لَّا يَكَادُونَ يَفْقَهُونَ قَوْلًا (93) Mpaka pamene iye adafika pakati pa mapiri awiri adapeza pambali pake anthu amene sanali kuzindikira chilichonse |
قَالُوا يَا ذَا الْقَرْنَيْنِ إِنَّ يَأْجُوجَ وَمَأْجُوجَ مُفْسِدُونَ فِي الْأَرْضِ فَهَلْ نَجْعَلُ لَكَ خَرْجًا عَلَىٰ أَن تَجْعَلَ بَيْنَنَا وَبَيْنَهُمْ سَدًّا (94) Iwo adati, “Iwe Dhul-Qarnain! Ndithudi Ya-juj ndi Majuj ali kuchita zoipa m’dziko lino. Kodi tikupatse malipiro kuti utimangire linga lotiteteza nalo pakati pa iwo ndi ife?” |
قَالَ مَا مَكَّنِّي فِيهِ رَبِّي خَيْرٌ فَأَعِينُونِي بِقُوَّةٍ أَجْعَلْ بَيْنَكُمْ وَبَيْنَهُمْ رَدْمًا (95) Iye adati, “Mphamvu zomangira linga zimene Ambuye wanga wandipatsa ndi zabwino. Choncho ndithandizeni ndi anthu amphamvu ogwira ntchito kuti ndimange linga pakati pa inu ndi iwo.” |
آتُونِي زُبَرَ الْحَدِيدِ ۖ حَتَّىٰ إِذَا سَاوَىٰ بَيْنَ الصَّدَفَيْنِ قَالَ انفُخُوا ۖ حَتَّىٰ إِذَا جَعَلَهُ نَارًا قَالَ آتُونِي أُفْرِغْ عَلَيْهِ قِطْرًا (96) Ndipatseni zidutswa zachitsulo; mpaka pamene iye adadzadza gawo limene linali pakati pa mapiriwa. Iye adati, “Uzirani ndi livumbo lanu.” Pamene adazifiwiritsa zidutswazo ngati moto, iye adati, “Ndipatseni mtovu kuti ndiuthire pa zidutswazo.” |
فَمَا اسْطَاعُوا أَن يَظْهَرُوهُ وَمَا اسْتَطَاعُوا لَهُ نَقْبًا (97) Anthu a Ya-juj ndi Majuj sadathe kuchilumpha ndipo sadathe kuchiboola |
قَالَ هَٰذَا رَحْمَةٌ مِّن رَّبِّي ۖ فَإِذَا جَاءَ وَعْدُ رَبِّي جَعَلَهُ دَكَّاءَ ۖ وَكَانَ وَعْدُ رَبِّي حَقًّا (98) Iye adati, “Ichi ndi chifundo chochokera kwa Ambuye wanga. Koma pamene lonjezo la Ambuye wanga lidzadza, Iye adzaliononga. Ndipo lonjezo la Ambuye wanga ndi loona |
۞ وَتَرَكْنَا بَعْضَهُمْ يَوْمَئِذٍ يَمُوجُ فِي بَعْضٍ ۖ وَنُفِخَ فِي الصُّورِ فَجَمَعْنَاهُمْ جَمْعًا (99) Ndipo pa tsikulo tidzawasiya ena mwa iwo akusakanikirana ndi ena. Lipenga lidzaimbidwa ndipo tidzawasonkhanitsa onse pamodzi |
وَعَرَضْنَا جَهَنَّمَ يَوْمَئِذٍ لِّلْكَافِرِينَ عَرْضًا (100) Pa tsiku limeneli tidzaonetsa Gahena kwa anthu osakhulupirira, kuti adzalione lonse moonekera kwambiri |
الَّذِينَ كَانَتْ أَعْيُنُهُمْ فِي غِطَاءٍ عَن ذِكْرِي وَكَانُوا لَا يَسْتَطِيعُونَ سَمْعًا (101) Amene maso awo adali otsekeka kuchikumbutso changa, satha kumva |
أَفَحَسِبَ الَّذِينَ كَفَرُوا أَن يَتَّخِذُوا عِبَادِي مِن دُونِي أَوْلِيَاءَ ۚ إِنَّا أَعْتَدْنَا جَهَنَّمَ لِلْكَافِرِينَ نُزُلًا (102) Kodi anthu osakhulupirira akuganiza kuti akhoza kuwapanga akapolo anga kukhala atetezi awo m’malo mwa Ine? Ndithudi Ife takonza Gahena kukhala malo ofikira anthu onse osakhulupirira |
قُلْ هَلْ نُنَبِّئُكُم بِالْأَخْسَرِينَ أَعْمَالًا (103) Nena, “Kodi tikuuzeni anthu amene ali olephera mu ntchito zawo?” |
الَّذِينَ ضَلَّ سَعْيُهُمْ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا وَهُمْ يَحْسَبُونَ أَنَّهُمْ يُحْسِنُونَ صُنْعًا (104) Iwowo ndi amene ntchito zawo zaonongeka m’moyo uno pamene iwo anali kuganiza kuti ali kulandira zabwino chifukwa cha ntchito zawo |
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ كَفَرُوا بِآيَاتِ رَبِّهِمْ وَلِقَائِهِ فَحَبِطَتْ أَعْمَالُهُمْ فَلَا نُقِيمُ لَهُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ وَزْنًا (105) Iwo ndi amene sadakhulupirire mawu a Ambuye wawo ndi zokumana ndi Iye. Motero ntchito zawo zaonongeka ndipo patsiku lachiweruzo Ife sitidzawakhazikira muyeso |
ذَٰلِكَ جَزَاؤُهُمْ جَهَنَّمُ بِمَا كَفَرُوا وَاتَّخَذُوا آيَاتِي وَرُسُلِي هُزُوًا (106) Gahena idzakhala mphotho yawo chifukwa iwo adalibe chikhulupiriro ndipo achitira chipongwe Atumwi ndiponso mawu anga |
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ كَانَتْ لَهُمْ جَنَّاتُ الْفِرْدَوْسِ نُزُلًا (107) Ndithudi! Iwo amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, minda ya ku Paradiso idzakhala malo awo ofikira |
خَالِدِينَ فِيهَا لَا يَبْغُونَ عَنْهَا حِوَلًا (108) Adzakhala komweko nthawi zonse ndipo sadzafuna kusintha malo |
قُل لَّوْ كَانَ الْبَحْرُ مِدَادًا لِّكَلِمَاتِ رَبِّي لَنَفِدَ الْبَحْرُ قَبْلَ أَن تَنفَدَ كَلِمَاتُ رَبِّي وَلَوْ جِئْنَا بِمِثْلِهِ مَدَدًا (109) Nena, “Ngati Nyanja ikadakhala inki yolembera mawu Ambuye wanga, ndithudi, nyanjayo ikadaphwa koma osati Mawu a Ambuye wanga ngakhale tikadabweretsa nyanja yofanana ndi imeneyo moonjezera.” |
قُلْ إِنَّمَا أَنَا بَشَرٌ مِّثْلُكُمْ يُوحَىٰ إِلَيَّ أَنَّمَا إِلَٰهُكُمْ إِلَٰهٌ وَاحِدٌ ۖ فَمَن كَانَ يَرْجُو لِقَاءَ رَبِّهِ فَلْيَعْمَلْ عَمَلًا صَالِحًا وَلَا يُشْرِكْ بِعِبَادَةِ رَبِّهِ أَحَدًا (110) Nena, “Ine ndine munthu monga inu nomwe, koma zavumbulutsidwa kwa ine kuti Mulungu wanu ndi mmodzi. Kotero aliyense amene afuna kudzakumana ndi Ambuye wake ayenera kuchita zimene zili zabwino ndipo popembedza Ambuye wake, osaphatikizamo wina wake.” |