Quran with Chichewa translation - Surah Al-Kahf ayat 19 - الكَهف - Page - Juz 15
﴿وَكَذَٰلِكَ بَعَثۡنَٰهُمۡ لِيَتَسَآءَلُواْ بَيۡنَهُمۡۚ قَالَ قَآئِلٞ مِّنۡهُمۡ كَمۡ لَبِثۡتُمۡۖ قَالُواْ لَبِثۡنَا يَوۡمًا أَوۡ بَعۡضَ يَوۡمٖۚ قَالُواْ رَبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِمَا لَبِثۡتُمۡ فَٱبۡعَثُوٓاْ أَحَدَكُم بِوَرِقِكُمۡ هَٰذِهِۦٓ إِلَى ٱلۡمَدِينَةِ فَلۡيَنظُرۡ أَيُّهَآ أَزۡكَىٰ طَعَامٗا فَلۡيَأۡتِكُم بِرِزۡقٖ مِّنۡهُ وَلۡيَتَلَطَّفۡ وَلَا يُشۡعِرَنَّ بِكُمۡ أَحَدًا ﴾
[الكَهف: 19]
﴿وكذلك بعثناهم ليتساءلوا بينهم قال قائل منهم كم لبثتم قالوا لبثنا يوما﴾ [الكَهف: 19]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo momwemonso tidawautsa kuti afunsane pakati pawo (zanthawi imene akhala ali chigonere). Adanena wonena mwa iwo: “Kodi mwakhala nthawi yotani muli mtulo?” Adati: “Takhala tsiku limodzi kapena gawo la tsiku.” (Ena) adati: “Mbuye wanu akudziwa kwambiri za nyengo imene mwakhala. Choncho mtumeni mmodzi wa inu ndindalama zanuzi za siliva kumudzi ndipo akayang’ane chakudya chake nchotani chomwe chili choyera bwino, ndikubwerera nacho chakudyacho; koma izi akachite mochenjera ndipo asamzindikiritse aliyense za inu.” |