Quran with Chichewa translation - Surah Al-Kahf ayat 22 - الكَهف - Page - Juz 15
﴿سَيَقُولُونَ ثَلَٰثَةٞ رَّابِعُهُمۡ كَلۡبُهُمۡ وَيَقُولُونَ خَمۡسَةٞ سَادِسُهُمۡ كَلۡبُهُمۡ رَجۡمَۢا بِٱلۡغَيۡبِۖ وَيَقُولُونَ سَبۡعَةٞ وَثَامِنُهُمۡ كَلۡبُهُمۡۚ قُل رَّبِّيٓ أَعۡلَمُ بِعِدَّتِهِم مَّا يَعۡلَمُهُمۡ إِلَّا قَلِيلٞۗ فَلَا تُمَارِ فِيهِمۡ إِلَّا مِرَآءٗ ظَٰهِرٗا وَلَا تَسۡتَفۡتِ فِيهِم مِّنۡهُمۡ أَحَدٗا ﴾
[الكَهف: 22]
﴿سيقولون ثلاثة رابعهم كلبهم ويقولون خمسة سادسهم كلبهم رجما بالغيب ويقولون سبعة﴾ [الكَهف: 22]
Khaled Ibrahim Betala “(Ena) akhala akunena (kuti) adali anthu atatu, wachinayi ndi galu wawo; ndipo (ena) akuti adali asanu, wachisanu ndichimodzi ndigalu wawo. (Akunena) mwakungoganizira chabe zomwe sakuzidziwa; ndipo (ena) akuti adali asanu ndi awiri, ndipo wachisanu ndi chitatu ndi galu wawo. Nena: “Mbuye wanga ndiye akudziwa bwinobwino za chiwerengero chawo. Palibe amene akudziwa (za iwo) koma ndi ochepa chabe.” Choncho usatsutsane nawo za iwo, kupatula kutsutsana kwa pa zinthu zodziwika, ndipo usamfunse aliyense mwa iwo za iwo |