Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 143 - البَقَرَة - Page - Juz 2
﴿وَكَذَٰلِكَ جَعَلۡنَٰكُمۡ أُمَّةٗ وَسَطٗا لِّتَكُونُواْ شُهَدَآءَ عَلَى ٱلنَّاسِ وَيَكُونَ ٱلرَّسُولُ عَلَيۡكُمۡ شَهِيدٗاۗ وَمَا جَعَلۡنَا ٱلۡقِبۡلَةَ ٱلَّتِي كُنتَ عَلَيۡهَآ إِلَّا لِنَعۡلَمَ مَن يَتَّبِعُ ٱلرَّسُولَ مِمَّن يَنقَلِبُ عَلَىٰ عَقِبَيۡهِۚ وَإِن كَانَتۡ لَكَبِيرَةً إِلَّا عَلَى ٱلَّذِينَ هَدَى ٱللَّهُۗ وَمَا كَانَ ٱللَّهُ لِيُضِيعَ إِيمَٰنَكُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ بِٱلنَّاسِ لَرَءُوفٞ رَّحِيمٞ ﴾
[البَقَرَة: 143]
﴿وكذلك جعلناكم أمة وسطا لتكونوا شهداء على الناس ويكون الرسول عليكم شهيدا﴾ [البَقَرَة: 143]
Khaled Ibrahim Betala “Choncho takusankhani (inu Asilamu) kukhala mpingo wabwino (wapakatikati) kuti mukhale mboni pa anthu ndi kuti Mtumiki (s.a.w) akhale mboni pa inu. Ndipo chibula (choyang’ana mbali ya ku Yerusalemu) chomwe udali nacho sitidachichite koma kuti timdziwitse (adziwike kwa anthu) amene akutsata Mtumiki (s.a.w), ndi yemwe akutembenukira m’mbuyo. Ndipo ndithudi, chidali chinthu chovuta kupatula kwa omwe Allah wawaongola. Ndipo nkosayenera kwa Allah kusokoneza Swala zanu, pakuti Allah Ngoleza kwabasi kwa anthu, Ngwachifundo chambiri |