×

Kwaniritsani miyambo ya Hajji ndi Umra chifukwa cha Mulungu. Ndipo ngati mwatsekerezedwa, 2:196 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Al-Baqarah ⮕ (2:196) ayat 196 in Chichewa

2:196 Surah Al-Baqarah ayat 196 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 196 - البَقَرَة - Page - Juz 2

﴿وَأَتِمُّواْ ٱلۡحَجَّ وَٱلۡعُمۡرَةَ لِلَّهِۚ فَإِنۡ أُحۡصِرۡتُمۡ فَمَا ٱسۡتَيۡسَرَ مِنَ ٱلۡهَدۡيِۖ وَلَا تَحۡلِقُواْ رُءُوسَكُمۡ حَتَّىٰ يَبۡلُغَ ٱلۡهَدۡيُ مَحِلَّهُۥۚ فَمَن كَانَ مِنكُم مَّرِيضًا أَوۡ بِهِۦٓ أَذٗى مِّن رَّأۡسِهِۦ فَفِدۡيَةٞ مِّن صِيَامٍ أَوۡ صَدَقَةٍ أَوۡ نُسُكٖۚ فَإِذَآ أَمِنتُمۡ فَمَن تَمَتَّعَ بِٱلۡعُمۡرَةِ إِلَى ٱلۡحَجِّ فَمَا ٱسۡتَيۡسَرَ مِنَ ٱلۡهَدۡيِۚ فَمَن لَّمۡ يَجِدۡ فَصِيَامُ ثَلَٰثَةِ أَيَّامٖ فِي ٱلۡحَجِّ وَسَبۡعَةٍ إِذَا رَجَعۡتُمۡۗ تِلۡكَ عَشَرَةٞ كَامِلَةٞۗ ذَٰلِكَ لِمَن لَّمۡ يَكُنۡ أَهۡلُهُۥ حَاضِرِي ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ شَدِيدُ ٱلۡعِقَابِ ﴾
[البَقَرَة: 196]

Kwaniritsani miyambo ya Hajji ndi Umra chifukwa cha Mulungu. Ndipo ngati mwatsekerezedwa, iphani, ngati nsembe, nyama zimene sizili zovuta kuzipeza ndipo musamete mitu yanu mpaka nyama zitafika pa malo ake ophera. Koma aliyense wa inu amene ndi wodwala kapena ali ndi vuto m’mutu mwake ayenera kudziombola posala kapena kupereka nsembe kapena kupha nyama. Ngati muli pa mtendere ndiponso wina wa inu aphatikiza Umra ndi Hajji, ayenera kupha nyama imene angaipeze mosavutikira kwambiri. Koma ngati sangathe kuipeza ayenera kusala masiku atatu pa nthawi ya Hajji ndi masiku asanu ndi awiri akabwerera kwawo; amenewo ndi masiku khumi okwana. Zimenezi ndi za iye amene banja lake silili pafupi ndi Mzikiti Woyera. Muopeni Mulungu. Ndipo dziwani kuti Mulungu amakhwimitsa chilango

❮ Previous Next ❯

ترجمة: وأتموا الحج والعمرة لله فإن أحصرتم فما استيسر من الهدي ولا تحلقوا, باللغة نيانجا

﴿وأتموا الحج والعمرة لله فإن أحصرتم فما استيسر من الهدي ولا تحلقوا﴾ [البَقَرَة: 196]

Khaled Ibrahim Betala
“Ndipo kwaniritsani Hajj ndi Umrah chifukwa chofuna kukondweretsa Allah. (Izi zili mkutsimikiza kulowa m’mapemphero a Hajj). Ndipo ngati mutatsekerezedwa (kukwaniritsa mapempherowo), choncho zingani nyama zimene zili zosavuta kuzipeza (monga mbuzi), ndipo musamete mitu yanu kufikira nsembeyo ifike pamalo pake pozingirapo (pomwe ndi pamalo pamene mwatsekerezedwapo). Ndipo amene mwa inu ali odwala kapena ali ndi zovutitsa ku mutu kwake, (nachita zomwe zidali zoletsedwa monga kumeta) apereke dipo la kusala kapena kupereka sadaka (chopereka chaulere), kapena kuzinga chinyama. Ndipo ngati muli pa mtendere, choncho amene angadzisangalatse pochita Umrah kenako nkuchita Hajj, azinge nyama imene ili yosavuta kupezeka (monga mbuzi). Ndipo Amene sadapeze, asale masiku atatu konko ku hajjiko ndipo asalenso masiku asanu ndi awiri mutabwerera (kwanu). Amenewo ndi masiku khumi okwanira. Lamuloli ndi la yemwe banja lake silili pafupi ndi Msikiti Wopatulika. Ndipo opani Allah, dziwani kuti Allah Ngwaukali polanga
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek