Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 213 - البَقَرَة - Page - Juz 2
﴿كَانَ ٱلنَّاسُ أُمَّةٗ وَٰحِدَةٗ فَبَعَثَ ٱللَّهُ ٱلنَّبِيِّـۧنَ مُبَشِّرِينَ وَمُنذِرِينَ وَأَنزَلَ مَعَهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ بِٱلۡحَقِّ لِيَحۡكُمَ بَيۡنَ ٱلنَّاسِ فِيمَا ٱخۡتَلَفُواْ فِيهِۚ وَمَا ٱخۡتَلَفَ فِيهِ إِلَّا ٱلَّذِينَ أُوتُوهُ مِنۢ بَعۡدِ مَا جَآءَتۡهُمُ ٱلۡبَيِّنَٰتُ بَغۡيَۢا بَيۡنَهُمۡۖ فَهَدَى ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لِمَا ٱخۡتَلَفُواْ فِيهِ مِنَ ٱلۡحَقِّ بِإِذۡنِهِۦۗ وَٱللَّهُ يَهۡدِي مَن يَشَآءُ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٍ ﴾
[البَقَرَة: 213]
﴿كان الناس أمة واحدة فبعث الله النبيين مبشرين ومنذرين وأنـزل معهم الكتاب﴾ [البَقَرَة: 213]
Khaled Ibrahim Betala “Anthu onse adali a chipembedzo chimodzi (cha Chisilamu panthawi ya Adam kufikira Nuh kenako adayamba kupatukana), ndipo Allah adatumiza aneneri onena nkhani zabwino ndi ochenjeza; ndipo pamodzi nawo adavumbulutsa mabuku achoonadi kuti aweruzire pakati pa anthu pa zimene adasemphana. Ndipo sadasemphane pa zimenezo koma aja amene adapatsidwa mabukuwo pambuyo powadzera zizindikiro zoonekera poyera, chifukwa chakuchitirana dumbo pakati pawo. Koma Allah adawaongolera amene adakhulupirira kuchoonadi cha zomwe adasempaniranazo, mwachifuniro chake. Ndipo Allah amamutsogolera ku njira yolunjika amene wamfuna |