×

Ndipo pamene musudzula akazi ndipo iwo akwanitsa nthawi yawo yodikira, asungeni mwaubwino 2:231 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Al-Baqarah ⮕ (2:231) ayat 231 in Chichewa

2:231 Surah Al-Baqarah ayat 231 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 231 - البَقَرَة - Page - Juz 2

﴿وَإِذَا طَلَّقۡتُمُ ٱلنِّسَآءَ فَبَلَغۡنَ أَجَلَهُنَّ فَأَمۡسِكُوهُنَّ بِمَعۡرُوفٍ أَوۡ سَرِّحُوهُنَّ بِمَعۡرُوفٖۚ وَلَا تُمۡسِكُوهُنَّ ضِرَارٗا لِّتَعۡتَدُواْۚ وَمَن يَفۡعَلۡ ذَٰلِكَ فَقَدۡ ظَلَمَ نَفۡسَهُۥۚ وَلَا تَتَّخِذُوٓاْ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ هُزُوٗاۚ وَٱذۡكُرُواْ نِعۡمَتَ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ وَمَآ أَنزَلَ عَلَيۡكُم مِّنَ ٱلۡكِتَٰبِ وَٱلۡحِكۡمَةِ يَعِظُكُم بِهِۦۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ ﴾
[البَقَرَة: 231]

Ndipo pamene musudzula akazi ndipo iwo akwanitsa nthawi yawo yodikira, asungeni mwaubwino kapena alekeni mwa mtendere. Koma musawasunge ndi cholinga chowazunza. Ndipo aliyense amene achita ichi, ndithudi adzilakwira yekha. Ndipo musachite chipongwe Mau a Mulungu koma kumbukirani madalitso a Mulungu kwa inu ndi zimene Iye watumiza m’Buku ndi luntha limene Iye akulangizani inu. Muopeni Mulungu ndipo dziwani kuti Mulungu amadziwa chilichonse

❮ Previous Next ❯

ترجمة: وإذا طلقتم النساء فبلغن أجلهن فأمسكوهن بمعروف أو سرحوهن بمعروف ولا تمسكوهن, باللغة نيانجا

﴿وإذا طلقتم النساء فبلغن أجلهن فأمسكوهن بمعروف أو سرحوهن بمعروف ولا تمسكوهن﴾ [البَقَرَة: 231]

Khaled Ibrahim Betala
“Ndipo pamene musiya akazi powanenera mawu achilekaniro, niiyandikira kukwana nyengo ya edda yawo (chiyembekezero chawo), abwelereni mwa ubwino; kapena lekananaoni mwa ubwino, ndipo musawabwelere mowavutitsa kuti mupyole malire a Allah (poswa malamulo ake). Ndipo amene achite zimenezo ndiye kuti wadzichitira yekha zoipa. Ndipo ndime za mawu a Allah musazichitire chibwana. Ndipo kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu; makamaka chisomo chokuvumbulutsirani buku (la Qur’an) ndi kudziwitsidwa nzeru zomwe akukulangizani nazo. Ndipo opani Allah, ndithudi dziwani kuti Allah Ngodziwa chirichonse
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek