Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 233 - البَقَرَة - Page - Juz 2
﴿۞ وَٱلۡوَٰلِدَٰتُ يُرۡضِعۡنَ أَوۡلَٰدَهُنَّ حَوۡلَيۡنِ كَامِلَيۡنِۖ لِمَنۡ أَرَادَ أَن يُتِمَّ ٱلرَّضَاعَةَۚ وَعَلَى ٱلۡمَوۡلُودِ لَهُۥ رِزۡقُهُنَّ وَكِسۡوَتُهُنَّ بِٱلۡمَعۡرُوفِۚ لَا تُكَلَّفُ نَفۡسٌ إِلَّا وُسۡعَهَاۚ لَا تُضَآرَّ وَٰلِدَةُۢ بِوَلَدِهَا وَلَا مَوۡلُودٞ لَّهُۥ بِوَلَدِهِۦۚ وَعَلَى ٱلۡوَارِثِ مِثۡلُ ذَٰلِكَۗ فَإِنۡ أَرَادَا فِصَالًا عَن تَرَاضٖ مِّنۡهُمَا وَتَشَاوُرٖ فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡهِمَاۗ وَإِنۡ أَرَدتُّمۡ أَن تَسۡتَرۡضِعُوٓاْ أَوۡلَٰدَكُمۡ فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ إِذَا سَلَّمۡتُم مَّآ ءَاتَيۡتُم بِٱلۡمَعۡرُوفِۗ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٞ ﴾
[البَقَرَة: 233]
﴿والوالدات يرضعن أولادهن حولين كاملين لمن أراد أن يتم الرضاعة وعلى المولود﴾ [البَقَرَة: 233]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo akazi omwe angobereka kumene ayamwitse ana awo zaka ziwiri zathunthu kwa yemwe akufuna kukwaniritsa kuyamwitsa. Ndiudindo wa abambo kuwapezera chakudya chawo ndi chovala chawo (ana awo ndi ) amayiwo, motsatira malamulo a Shariya. Ndipo mzimu wa munthu aliyense sukakamizidwa, koma m’mene ungathere. Ndipo mayi wa mwanayo asazunzidwe chifukwa cha mwana wakeyo. Nayenso bambo wa mwanayo asazunzike chifukwa cha mwana wakeyo. Ndipo lamuloli lilinso chimodzimodzi pa mlowam’malo (ngati bambo atamwalira). Ndipo onse awiri ngati atafuna kumletsa kuyamwa, mogwirizana pakati pa awiriwo, ndi mokambirana palibe kulakwa pa iwo awiriwo. Ndipo ngati mutafuna kuwapezera ana anu akazi ena owayamwitsa (omwe si amayi awo), palibe uchimo mwa inu ngati mwapereka chimene udalonjeza kuwapatsa (oyamwitsawo) mwa ubwino. Ndipo opani Allah; dziwaninso kuti Allah akuona zonse zimene mukuchita |