Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 253 - البَقَرَة - Page - Juz 3
﴿۞ تِلۡكَ ٱلرُّسُلُ فَضَّلۡنَا بَعۡضَهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖۘ مِّنۡهُم مَّن كَلَّمَ ٱللَّهُۖ وَرَفَعَ بَعۡضَهُمۡ دَرَجَٰتٖۚ وَءَاتَيۡنَا عِيسَى ٱبۡنَ مَرۡيَمَ ٱلۡبَيِّنَٰتِ وَأَيَّدۡنَٰهُ بِرُوحِ ٱلۡقُدُسِۗ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَا ٱقۡتَتَلَ ٱلَّذِينَ مِنۢ بَعۡدِهِم مِّنۢ بَعۡدِ مَا جَآءَتۡهُمُ ٱلۡبَيِّنَٰتُ وَلَٰكِنِ ٱخۡتَلَفُواْ فَمِنۡهُم مَّنۡ ءَامَنَ وَمِنۡهُم مَّن كَفَرَۚ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَا ٱقۡتَتَلُواْ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ يَفۡعَلُ مَا يُرِيدُ ﴾
[البَقَرَة: 253]
﴿تلك الرسل فضلنا بعضهم على بعض منهم من كلم الله ورفع بعضهم﴾ [البَقَرَة: 253]
Khaled Ibrahim Betala “۞ Amenewo ndi aneneri tidawapatsa ulemelero mosiyanitsa pakati pawo, ena kuposa ena. Mwa iwo alipo amene Allah adawalankhula; ndipo ena adawakwezera kwambiri maulemelero awo. Naye Isa (Yesu) mwana wa Mariya tidampatsa zisonyezo zooneka, ndi kumlimbikitsa ndi Mzimu Woyera (rnngelo Gabriel). Allah akadafuna skadamenyana amene adalipo pambuyo pawo, (pa atumikiwo) pambuyo powadzera zizindikiro zooneka, koma adasiyana. Choncho mwa iwo alipo amene adakhulupirira, ndipo ena mwa iwo sadakhulupirire. Ndipo Allah akadafuna, sakadamenyana; koma Allah amachita zimene akufuna |