Quran with Chichewa translation - Surah Al-hajj ayat 40 - الحج - Page - Juz 17
﴿ٱلَّذِينَ أُخۡرِجُواْ مِن دِيَٰرِهِم بِغَيۡرِ حَقٍّ إِلَّآ أَن يَقُولُواْ رَبُّنَا ٱللَّهُۗ وَلَوۡلَا دَفۡعُ ٱللَّهِ ٱلنَّاسَ بَعۡضَهُم بِبَعۡضٖ لَّهُدِّمَتۡ صَوَٰمِعُ وَبِيَعٞ وَصَلَوَٰتٞ وَمَسَٰجِدُ يُذۡكَرُ فِيهَا ٱسۡمُ ٱللَّهِ كَثِيرٗاۗ وَلَيَنصُرَنَّ ٱللَّهُ مَن يَنصُرُهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَقَوِيٌّ عَزِيزٌ ﴾
[الحج: 40]
﴿الذين أخرجوا من ديارهم بغير حق إلا أن يقولوا ربنا الله ولولا﴾ [الحج: 40]
Khaled Ibrahim Betala “Omwe atulutsidwa m’nyumba zawo popanda chilungamo, koma pachifukwa chakuti akunena: “Mbuye wathu ndi Allah.” Ndipo pakapanda Allah kukankha anthu ena kupyolera mwa ena, (popatsa ena mphamvu kuti agonjetse ena), ndiye kuti Masinagogi, Matchalitchi, nyumba zina zopempheleramo ndi Misikiti momwe dzina la Allah likutchulidwa mochuluka zikadagumulidwa. Ndithu Allah am’thangata amene akuthangata chipembedzo Chake; ndithu Allah Ngwanyonga, Wogonjetsa chilichonse |