×

Auze akazi okhulupirira kuti azitsitsa maso awo ndipo asachite chiwerewere ndiponso azibisa 24:31 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah An-Nur ⮕ (24:31) ayat 31 in Chichewa

24:31 Surah An-Nur ayat 31 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah An-Nur ayat 31 - النور - Page - Juz 18

﴿وَقُل لِّلۡمُؤۡمِنَٰتِ يَغۡضُضۡنَ مِنۡ أَبۡصَٰرِهِنَّ وَيَحۡفَظۡنَ فُرُوجَهُنَّ وَلَا يُبۡدِينَ زِينَتَهُنَّ إِلَّا مَا ظَهَرَ مِنۡهَاۖ وَلۡيَضۡرِبۡنَ بِخُمُرِهِنَّ عَلَىٰ جُيُوبِهِنَّۖ وَلَا يُبۡدِينَ زِينَتَهُنَّ إِلَّا لِبُعُولَتِهِنَّ أَوۡ ءَابَآئِهِنَّ أَوۡ ءَابَآءِ بُعُولَتِهِنَّ أَوۡ أَبۡنَآئِهِنَّ أَوۡ أَبۡنَآءِ بُعُولَتِهِنَّ أَوۡ إِخۡوَٰنِهِنَّ أَوۡ بَنِيٓ إِخۡوَٰنِهِنَّ أَوۡ بَنِيٓ أَخَوَٰتِهِنَّ أَوۡ نِسَآئِهِنَّ أَوۡ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُنَّ أَوِ ٱلتَّٰبِعِينَ غَيۡرِ أُوْلِي ٱلۡإِرۡبَةِ مِنَ ٱلرِّجَالِ أَوِ ٱلطِّفۡلِ ٱلَّذِينَ لَمۡ يَظۡهَرُواْ عَلَىٰ عَوۡرَٰتِ ٱلنِّسَآءِۖ وَلَا يَضۡرِبۡنَ بِأَرۡجُلِهِنَّ لِيُعۡلَمَ مَا يُخۡفِينَ مِن زِينَتِهِنَّۚ وَتُوبُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ جَمِيعًا أَيُّهَ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ لَعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ ﴾
[النور: 31]

Auze akazi okhulupirira kuti azitsitsa maso awo ndipo asachite chiwerewere ndiponso azibisa zinthu zimene zimawakongoletsa kupatula zokhazo zimene sizingabisike. Ndipo azifunda nsalu kumutu ndi pa chifuwa chawo ndiponso asaonetse kukongola kwawo kupatula kwa amuna awo, abambo awo, abambo a amuna awo, ana awo aamuna, ana a amuna awo, ana a chemwali awo kapena ana a achimwene awo kapena ana a alongo awo kapena akazi anzawo owakhulupirira; ndiponso antchito awo aakazi, a ntchito awo a amuna ndi ana amene alibe chilakolako cha akazi. Ndipo iwo asamamenyetse mapazi awo pansi akamayenda ndi cholinga choonetsa zina zokongola zawo zobisika. Oh inu okhulupirira! Lapani kwa Mulungu mogonja kuti mupambane

❮ Previous Next ❯

ترجمة: وقل للمؤمنات يغضضن من أبصارهن ويحفظن فروجهن ولا يبدين زينتهن إلا ما, باللغة نيانجا

﴿وقل للمؤمنات يغضضن من أبصارهن ويحفظن فروجهن ولا يبدين زينتهن إلا ما﴾ [النور: 31]

Khaled Ibrahim Betala
“Ndipo auze okhulupirira achikazi kuti adzolitse maso awo, ndikusunga umaliseche wawo, ndipo asaonetse (poyera) zomwe amadzikongoletsa nazo kupatula zimene zaonekera poyera (popanda cholinga chotero). Ndipo afunde kumutu mipango yawo mpaka m’zifuwa zawo; ndipo asaonetse poyera zodzikongoletsa nazo koma kwa amuna awo, kapena atate awo, kapena apongozi awo, kapena ana awo, kapena ana a amuna awo, kapena abale awo, kapena ana a abale awo, kapena ana a alongo awo, kapena akazi anzawo (achisilamu). Kapena yemwe wapatidwa ndi dzanja lamanja (monga kapolo), kapena otsatira (antchito) omwe ndi amuna opanda zilakolako za akazi ndi ana omwe sadziwa za akazi. Ndipo asamenyetse miyendo yawo (pansi) kuti zidziwike zimene akubisa mwa zomwe amadzikongoletsa nazo. Ndipo tembenukirani kwa Allah, nonse inu okhulupirira kuti mupambane
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek