Quran with Chichewa translation - Surah An-Naml ayat 19 - النَّمل - Page - Juz 19
﴿فَتَبَسَّمَ ضَاحِكٗا مِّن قَوۡلِهَا وَقَالَ رَبِّ أَوۡزِعۡنِيٓ أَنۡ أَشۡكُرَ نِعۡمَتَكَ ٱلَّتِيٓ أَنۡعَمۡتَ عَلَيَّ وَعَلَىٰ وَٰلِدَيَّ وَأَنۡ أَعۡمَلَ صَٰلِحٗا تَرۡضَىٰهُ وَأَدۡخِلۡنِي بِرَحۡمَتِكَ فِي عِبَادِكَ ٱلصَّٰلِحِينَ ﴾
[النَّمل: 19]
﴿فتبسم ضاحكا من قولها وقال رب أوزعني أن أشكر نعمتك التي أنعمت﴾ [النَّمل: 19]
Khaled Ibrahim Betala “Choncho adamwetulira, mosekelera chifukwa cha mawu ake aja (mawu a nyelere); ndipo (Sulaiman) adati: “E Mbuye wanga! Ndipatseni nyonga zakuti ndizithokozera mtendere wanu umene mwandidalitsa nawo pamodzi ndi makolo anga, ndi kuti ndizichita zabwino (zomwe) mukuziyanja; Kupyolera m’chifundo chanu, ndiponso ndilowetseni m’gulu la akapolo anu abwino.” |