×

Surah An-Naml in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Naml

Translation of the Meanings of Surah Naml in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Naml translated into Chichewa, Surah An-Naml in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Naml in Chichewa - نيانجا, Verses 93 - Surah Number 27 - Page 377.

بسم الله الرحمن الرحيم

طس ۚ تِلْكَ آيَاتُ الْقُرْآنِ وَكِتَابٍ مُّبِينٍ (1)
Ichi ndi chivumbulutso cha Korani, Buku lofotokoza bwino
هُدًى وَبُشْرَىٰ لِلْمُؤْمِنِينَ (2)
Malangizo ndi nkhani yosangalatsa kwa anthu okhulupirira
الَّذِينَ يُقِيمُونَ الصَّلَاةَ وَيُؤْتُونَ الزَّكَاةَ وَهُم بِالْآخِرَةِ هُمْ يُوقِنُونَ (3)
Amene amapitiriza kupemphera ndipo amapereka msonkho wothandiza anthu osauka ndiponso amakhulupirira kwambiri m’moyo umene uli nkudza
إِنَّ الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ زَيَّنَّا لَهُمْ أَعْمَالَهُمْ فَهُمْ يَعْمَهُونَ (4)
Ndithudi iwo ndi amene amakana za moyo umene uli nkudza. Ife tazipanga ntchito zawo kuti zioneke ngati zabwino motero iwo amayenda mwakhungu
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ لَهُمْ سُوءُ الْعَذَابِ وَهُمْ فِي الْآخِرَةِ هُمُ الْأَخْسَرُونَ (5)
Iwo adzalangidwa koposa. Ndipo m’moyo umene uli nkudza, iwo sadzapindula china chilichonse
وَإِنَّكَ لَتُلَقَّى الْقُرْآنَ مِن لَّدُنْ حَكِيمٍ عَلِيمٍ (6)
Ndithudi iwe walandira Korani kuchokera kwa Iye amene ali ndi nzeru ndipo amadziwa chilichonse
إِذْ قَالَ مُوسَىٰ لِأَهْلِهِ إِنِّي آنَسْتُ نَارًا سَآتِيكُم مِّنْهَا بِخَبَرٍ أَوْ آتِيكُم بِشِهَابٍ قَبَسٍ لَّعَلَّكُمْ تَصْطَلُونَ (7)
Pamenepo Mose adauza banja lake kuti, “Ine ndili kuona moto. Ine posachedwapa ndikubweretserani nkhani kapena khala la moto kuti mukhoza kuotha.”
فَلَمَّا جَاءَهَا نُودِيَ أَن بُورِكَ مَن فِي النَّارِ وَمَنْ حَوْلَهَا وَسُبْحَانَ اللَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ (8)
Ndipo pamene iye adafika pamoto paja, mawu adamveka akunena naye kuti, “odalitsidwa ndiye amene ali mu moto uwu ndiponso alionse a pamalo pozungulira. Ulemerero ukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwe zonse.”
يَا مُوسَىٰ إِنَّهُ أَنَا اللَّهُ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (9)
“Mose! Ine ndine Mulungu, Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse.”
وَأَلْقِ عَصَاكَ ۚ فَلَمَّا رَآهَا تَهْتَزُّ كَأَنَّهَا جَانٌّ وَلَّىٰ مُدْبِرًا وَلَمْ يُعَقِّبْ ۚ يَا مُوسَىٰ لَا تَخَفْ إِنِّي لَا يَخَافُ لَدَيَّ الْمُرْسَلُونَ (10)
“Ponya ndodo yako pansi.” Ndipo pamene iye adaona kuti ilikuyenda ngati njoka, adatembenuka ndi kuthawa ndipo sadayang’ane m’mbuyo. “Iwe Mose!” Atumwi anga sachita mantha pamene ali ndi Ine
إِلَّا مَن ظَلَمَ ثُمَّ بَدَّلَ حُسْنًا بَعْدَ سُوءٍ فَإِنِّي غَفُورٌ رَّحِيمٌ (11)
Akakhala iwo amene amalakwa ndipo amachita zabwino pambuyo pochita zoipa Ine ndine wokhululukira ndiponso wachisoni chosatha
وَأَدْخِلْ يَدَكَ فِي جَيْبِكَ تَخْرُجْ بَيْضَاءَ مِنْ غَيْرِ سُوءٍ ۖ فِي تِسْعِ آيَاتٍ إِلَىٰ فِرْعَوْنَ وَقَوْمِهِ ۚ إِنَّهُمْ كَانُوا قَوْمًا فَاسِقِينَ (12)
“Pisa dzanja m’thumba mwako. Litulutse lili loyera ngakhale kuti siudapweteke. Ichi ndi chimodzi cha zizindikiro zisanu ndi zinayi zimene zidzaonetsedwa kwa Farawo ndi anthu ake. Ndithudi iwo ndi anthu ochimwa kwambiri.”
فَلَمَّا جَاءَتْهُمْ آيَاتُنَا مُبْصِرَةً قَالُوا هَٰذَا سِحْرٌ مُّبِينٌ (13)
Pamene zizindikiro zathu zooneka bwino zinaonetsedwa kwa iwo, iwo adati, “Uwu ndiwo ufiti weniweni.”
وَجَحَدُوا بِهَا وَاسْتَيْقَنَتْهَا أَنفُسُهُمْ ظُلْمًا وَعُلُوًّا ۚ فَانظُرْ كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الْمُفْسِدِينَ (14)
Mitima yawo idadziwa kuti zizindikiro zidali zoona koma adazikana izo chifukwa chakulakwa ndiponso kunyada kwawo. Taona zimene zidawaonekera anthu olakwa
وَلَقَدْ آتَيْنَا دَاوُودَ وَسُلَيْمَانَ عِلْمًا ۖ وَقَالَا الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي فَضَّلَنَا عَلَىٰ كَثِيرٍ مِّنْ عِبَادِهِ الْمُؤْمِنِينَ (15)
Ndithudi Ife tidapereka nzeru kwa Davide ndi Solomoni. Iwo adati, “Kuyamikidwa ndi kwa Iye amene watikweza ife kukhala pamwamba pa akapolo ake ambiri okhulupirira.”
وَوَرِثَ سُلَيْمَانُ دَاوُودَ ۖ وَقَالَ يَا أَيُّهَا النَّاسُ عُلِّمْنَا مَنطِقَ الطَّيْرِ وَأُوتِينَا مِن كُلِّ شَيْءٍ ۖ إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ الْفَضْلُ الْمُبِينُ (16)
Solomoniadalowam’malomwaDavide.Iye adati, “Oh inu anthu anga! Ife taphunzitsidwa chiyankhulo cha mbalame ndipo tapatsidwa zinthu zabwino zambiri. Ndithudi ichi ndi chifundo choonekeratu.”
وَحُشِرَ لِسُلَيْمَانَ جُنُودُهُ مِنَ الْجِنِّ وَالْإِنسِ وَالطَّيْرِ فَهُمْ يُوزَعُونَ (17)
Asirikali a nkhondo a mtundu wa majini, anthu ena ndi mbalame anasonkhanitsidwa pamaso pa Solomoni ndipo adaimitsidwa pa mizere m’magulu osiyanasiyana mogwirizana ndi maudindo
حَتَّىٰ إِذَا أَتَوْا عَلَىٰ وَادِ النَّمْلِ قَالَتْ نَمْلَةٌ يَا أَيُّهَا النَّمْلُ ادْخُلُوا مَسَاكِنَكُمْ لَا يَحْطِمَنَّكُمْ سُلَيْمَانُ وَجُنُودُهُ وَهُمْ لَا يَشْعُرُونَ (18)
Mpaka pamene iwo anafika pa chigwa cha nyerere, nyerere ina idati, “Oh inu nyerere! Lowani ku maenje anu chifukwa mwina Solomoni pamodzi ndi Asirikali ake, akhoza kukuonongani mosadziwa.”
فَتَبَسَّمَ ضَاحِكًا مِّن قَوْلِهَا وَقَالَ رَبِّ أَوْزِعْنِي أَنْ أَشْكُرَ نِعْمَتَكَ الَّتِي أَنْعَمْتَ عَلَيَّ وَعَلَىٰ وَالِدَيَّ وَأَنْ أَعْمَلَ صَالِحًا تَرْضَاهُ وَأَدْخِلْنِي بِرَحْمَتِكَ فِي عِبَادِكَ الصَّالِحِينَ (19)
Solomoni adamwetulira posangalatsidwa ndi mawu ake ndipo iye adati, “Ndilangizeni Ambuye kuti ndizikuthokozani pa zabwino zonse zimene mwandipatsa ine ndi makolo anga ndiponso kuti ndizichita ntchito zabwino zimene zimakukondweretsani inu. Ndilowetseni ine ku Paradiso kudzera m’chisomo chanu, kuti ndikhale pakati pa akapolo anu angwiro.”
وَتَفَقَّدَ الطَّيْرَ فَقَالَ مَا لِيَ لَا أَرَى الْهُدْهُدَ أَمْ كَانَ مِنَ الْغَائِبِينَ (20)
Iye adayendera mbalame nati, “Kodi mbalame yotchedwa mnthengu ili kuti? Kodi kapena iyo ili pamodzi ndi amene sadabwere?”
لَأُعَذِّبَنَّهُ عَذَابًا شَدِيدًا أَوْ لَأَذْبَحَنَّهُ أَوْ لَيَأْتِيَنِّي بِسُلْطَانٍ مُّبِينٍ (21)
“Ndithudi ndidzailanga iyo ndi chilango chowawa kapena ndidzaipha kupatula ngati ibweretsa kwa ine chifukwa chomveka.”
فَمَكَثَ غَيْرَ بَعِيدٍ فَقَالَ أَحَطتُ بِمَا لَمْ تُحِطْ بِهِ وَجِئْتُكَ مِن سَبَإٍ بِنَبَإٍ يَقِينٍ (22)
Ndipo mbalame ya mnthengu siidachedwe ndipo idati, “Ndadziwa zimene iwe siudziwa ndipo ndikubweretsera nkhani yoona kuchokera ku Saba.”
إِنِّي وَجَدتُّ امْرَأَةً تَمْلِكُهُمْ وَأُوتِيَتْ مِن كُلِّ شَيْءٍ وَلَهَا عَرْشٌ عَظِيمٌ (23)
“Ine ndapeza munthu wamkazi akulamulira iwo ndipo iye wapatsidwa zinthu zonse zomuyenereza ndipo ali ndi Mpando waukulu wachifumu
وَجَدتُّهَا وَقَوْمَهَا يَسْجُدُونَ لِلشَّمْسِ مِن دُونِ اللَّهِ وَزَيَّنَ لَهُمُ الشَّيْطَانُ أَعْمَالَهُمْ فَصَدَّهُمْ عَنِ السَّبِيلِ فَهُمْ لَا يَهْتَدُونَ (24)
Ndidamupeza iye pamodzi ndi anthu ake ali kupembedza dzuwa moonjezera pa Mulungu ndipo Satana wawakongoletsera ntchito zawo zoipa ndipo wawasocheretsakunjirayoyenerandipoiwosiotsogozedwa bwino.”
أَلَّا يَسْجُدُوا لِلَّهِ الَّذِي يُخْرِجُ الْخَبْءَ فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَيَعْلَمُ مَا تُخْفُونَ وَمَا تُعْلِنُونَ (25)
Ndi kuti sapembedza Mulungu amene amaulula zobisika za kumwamba ndi pa dziko lapansi ndipo Iye amadziwa zimene inu mumabisa ndi zimene mumaulula
اللَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ رَبُّ الْعَرْشِ الْعَظِيمِ ۩ (26)
Mulungu! Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Ambuye wa mpando wa Chifumu
۞ قَالَ سَنَنظُرُ أَصَدَقْتَ أَمْ كُنتَ مِنَ الْكَاذِبِينَ (27)
Solomoni adati, “Tidzaona posachedwapa ngati zimene ukunena ndi zoona kapena zabodza.”
اذْهَب بِّكِتَابِي هَٰذَا فَأَلْقِهْ إِلَيْهِمْ ثُمَّ تَوَلَّ عَنْهُمْ فَانظُرْ مَاذَا يَرْجِعُونَ (28)
“Pita ukapereke kalata yangayi kwa iwo ndipo ukachoke pang’ono poyembekezera yankho lawo.”
قَالَتْ يَا أَيُّهَا الْمَلَأُ إِنِّي أُلْقِيَ إِلَيَّ كِتَابٌ كَرِيمٌ (29)
Mfumukazi ya ku Saba adati, “Oh inu nduna zanga! Ine ndalandira kalata yolemekezeka.”
إِنَّهُ مِن سُلَيْمَانَ وَإِنَّهُ بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ (30)
Kalatayi ndi yochokera kwa Solomoni ndipo ikuti, “M’dzina la Mulungu, Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha.”
أَلَّا تَعْلُوا عَلَيَّ وَأْتُونِي مُسْلِمِينَ (31)
“Usadzikweze kwa ine koma bwerani nonse kwa ine modzipereka.”
قَالَتْ يَا أَيُّهَا الْمَلَأُ أَفْتُونِي فِي أَمْرِي مَا كُنتُ قَاطِعَةً أَمْرًا حَتَّىٰ تَشْهَدُونِ (32)
Iye adati, “oh inu mafumu! Ndipatseni chilangizo chokhudza nkhani iyi ndipo sindilamula china chilichonse pokhapokha inu mutakhalapo.”
قَالُوا نَحْنُ أُولُو قُوَّةٍ وَأُولُو بَأْسٍ شَدِيدٍ وَالْأَمْرُ إِلَيْكِ فَانظُرِي مَاذَا تَأْمُرِينَ (33)
Iwo adati, “Ife ndife olimba mtima ndiponso odziwa kumenya nkhondo molimba, ndipo nkhani ili kwa iwe. Ndipo udziwe mmene ungalamulire.”
قَالَتْ إِنَّ الْمُلُوكَ إِذَا دَخَلُوا قَرْيَةً أَفْسَدُوهَا وَجَعَلُوا أَعِزَّةَ أَهْلِهَا أَذِلَّةً ۖ وَكَذَٰلِكَ يَفْعَلُونَ (34)
Iye adati, “Ndithudi mafumu akalowa mu mzinda amaononga mwaupandu ndi kuwasandutsa anthu olemekezeka kukhala onyozeka. Umo ndi mmene iwo amachitira.”
وَإِنِّي مُرْسِلَةٌ إِلَيْهِم بِهَدِيَّةٍ فَنَاظِرَةٌ بِمَ يَرْجِعُ الْمُرْسَلُونَ (35)
“Koma ine ndiwatumizira mphatso ndipo ndidzaona yankho limene a Kazembe anga adzabwere nalo.”
فَلَمَّا جَاءَ سُلَيْمَانَ قَالَ أَتُمِدُّونَنِ بِمَالٍ فَمَا آتَانِيَ اللَّهُ خَيْرٌ مِّمَّا آتَاكُم بَلْ أَنتُم بِهَدِيَّتِكُمْ تَفْرَحُونَ (36)
Ndipo pamene akazembe adadza kwa Solomoni, iye adati, “Kodi muli kundipatsa chuma chambiri? Icho chimene Mulungu wandipatsa ine ndi chabwino kuposa chuma chonse chimene wakupatsani inu. Koma inu mumasangalala ndi mphatso zanu.”
ارْجِعْ إِلَيْهِمْ فَلَنَأْتِيَنَّهُم بِجُنُودٍ لَّا قِبَلَ لَهُم بِهَا وَلَنُخْرِجَنَّهُم مِّنْهَا أَذِلَّةً وَهُمْ صَاغِرُونَ (37)
“Bwererani kwa iwo. Ife tidzapita kwa iwo ndi magulu ankhondo amene iwo sangathe kuwagonjetsa ndipo tidzawathamangitsa m’dziko lawo mochititsa manyazi ndipo iwo adzanyozeka.”
قَالَ يَا أَيُّهَا الْمَلَأُ أَيُّكُمْ يَأْتِينِي بِعَرْشِهَا قَبْلَ أَن يَأْتُونِي مُسْلِمِينَ (38)
Iye adati, “oh inu mafumu! Kodi ndani amene angandibweretsere mpando wake wachifumu iwo asanabwerekwainemogonja?”
قَالَ عِفْرِيتٌ مِّنَ الْجِنِّ أَنَا آتِيكَ بِهِ قَبْلَ أَن تَقُومَ مِن مَّقَامِكَ ۖ وَإِنِّي عَلَيْهِ لَقَوِيٌّ أَمِينٌ (39)
Winawamphamvu, amene adalimmodziwamajiniadati,“Inendidzakubweretseraniinu musadanyamuke pa mpando wanu. Ine ndili ndi mphamvu zonyamulira mpando ndiponso ndine wokhulupirika.”
قَالَ الَّذِي عِندَهُ عِلْمٌ مِّنَ الْكِتَابِ أَنَا آتِيكَ بِهِ قَبْلَ أَن يَرْتَدَّ إِلَيْكَ طَرْفُكَ ۚ فَلَمَّا رَآهُ مُسْتَقِرًّا عِندَهُ قَالَ هَٰذَا مِن فَضْلِ رَبِّي لِيَبْلُوَنِي أَأَشْكُرُ أَمْ أَكْفُرُ ۖ وَمَن شَكَرَ فَإِنَّمَا يَشْكُرُ لِنَفْسِهِ ۖ وَمَن كَفَرَ فَإِنَّ رَبِّي غَنِيٌّ كَرِيمٌ (40)
Koma wina amene anali kudziwa Mawu a Mulungu adati “Ine ndidzakubweretserani msanga musadaphenire maso anu.” Ndipo pamene iye adaona kuti mpando wabwera kwa iye adati, “Ichi ndi chisomo cha Ambuye wanga kuti andiyese ngati ndikuthokoza kapena sindikuthokoza. Ndipo aliyense amene athokoza atero podzipezera yekha zabwino. Ndipo amene sathokoza ndithu, Ambuye wanga ali ndi zonse ndipo ndi Wolemekezeka.”
قَالَ نَكِّرُوا لَهَا عَرْشَهَا نَنظُرْ أَتَهْتَدِي أَمْ تَكُونُ مِنَ الَّذِينَ لَا يَهْتَدُونَ (41)
Ndipo iye adati, “Sinthani mpando wake wachifumu kuti tione ngati iye akhoza kuuzindikira kapena ayi.”
فَلَمَّا جَاءَتْ قِيلَ أَهَٰكَذَا عَرْشُكِ ۖ قَالَتْ كَأَنَّهُ هُوَ ۚ وَأُوتِينَا الْعِلْمَ مِن قَبْلِهَا وَكُنَّا مُسْلِمِينَ (42)
Ndipo pamene mfumukazi inadza kwa Solomoni idafunsidwa kuti, “Kodi mpando wako wachifumu ndi otere?” Iye adati, “Ukukhala ngati umenewu” ndipo ife tinadziwa kale ndipo tagonja kwa Mulungu mwamtendere.”
وَصَدَّهَا مَا كَانَت تَّعْبُدُ مِن دُونِ اللَّهِ ۖ إِنَّهَا كَانَتْ مِن قَوْمٍ كَافِرِينَ (43)
Zinthu zimene amapembedza zoonjezera pa Mulungu ndi zimene zamusokoneza. Iye adali mmodzi wa anthu osakhulupirira
قِيلَ لَهَا ادْخُلِي الصَّرْحَ ۖ فَلَمَّا رَأَتْهُ حَسِبَتْهُ لُجَّةً وَكَشَفَتْ عَن سَاقَيْهَا ۚ قَالَ إِنَّهُ صَرْحٌ مُّمَرَّدٌ مِّن قَوَارِيرَ ۗ قَالَتْ رَبِّ إِنِّي ظَلَمْتُ نَفْسِي وَأَسْلَمْتُ مَعَ سُلَيْمَانَ لِلَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ (44)
Iye adauzidwa kuti, “Lowa mnyumba yachifumu.” Ndipo pamene iye anaiona iyo, adaganiza kuti ndi dziwe la madzi ndipo miyendo yake adaionetsa poyera. Solomoni adati, “Iyi ndi nyumba yachifumu yomatidwa ndi magalasi.” Iye adati, “Ambuye, ine ndalakwira mzimu wanga. Tsopano ndili kudzipereka pamodzi ndi Solomoni kwa Mulungu, Ambuye wazolengedwa zonse.”
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا إِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمْ صَالِحًا أَنِ اعْبُدُوا اللَّهَ فَإِذَا هُمْ فَرِيقَانِ يَخْتَصِمُونَ (45)
A Thamoud, ndithudi, tidawatumizira m’bale wawo Saleh, amene adati, “Muzipembedza Mulungu basi.” Koma iwo adagawikana m’magulu awiri okangana
قَالَ يَا قَوْمِ لِمَ تَسْتَعْجِلُونَ بِالسَّيِّئَةِ قَبْلَ الْحَسَنَةِ ۖ لَوْلَا تَسْتَغْفِرُونَ اللَّهَ لَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ (46)
Iye adati, “Anthu anga! Kodi bwanji mufuna kubweretsa choipa msanga musanabweretse chabwino? Nanga ndi chifukwa chiyani simupempha chikhululukiro kwa Mulungu kuti mukhoza kupeza chisomo chake?”
قَالُوا اطَّيَّرْنَا بِكَ وَبِمَن مَّعَكَ ۚ قَالَ طَائِرُكُمْ عِندَ اللَّهِ ۖ بَلْ أَنتُمْ قَوْمٌ تُفْتَنُونَ (47)
Iwo adati, “Ife tili kuona choipa chochokera kwa iwe ndiponso kwa anthu amene amakutsatira iwe.” Iye adati, “Choipa chimene muli kuchiona chili kuchokera kwa Mulungu. Inu ndinu anthu amene muli kuyesedwa.”
وَكَانَ فِي الْمَدِينَةِ تِسْعَةُ رَهْطٍ يُفْسِدُونَ فِي الْأَرْضِ وَلَا يُصْلِحُونَ (48)
M’mizinda mwawo mudali anthu asanu ndi anayi amene anali kuchita zoipa mdziko ndipo samachita zabwino ayi
قَالُوا تَقَاسَمُوا بِاللَّهِ لَنُبَيِّتَنَّهُ وَأَهْلَهُ ثُمَّ لَنَقُولَنَّ لِوَلِيِّهِ مَا شَهِدْنَا مَهْلِكَ أَهْلِهِ وَإِنَّا لَصَادِقُونَ (49)
Iwo adati, “Tiyeni tonse tilumbire, dzina la Mulungu, kuti timuphe nthawi ya usiku pamodzi ndi a pabanja lake lonse. Ndipo tidzawauza abale ake kuti, “Ife kudalibe pamene iwo anali kuphedwa. Ndipo zimene tili kunena ndi zoona zokhazokha.”
وَمَكَرُوا مَكْرًا وَمَكَرْنَا مَكْرًا وَهُمْ لَا يَشْعُرُونَ (50)
Iwo adachita chiwembu ndipo nafenso tidachita chiwembu iwo osadziwa chilichonse
فَانظُرْ كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ مَكْرِهِمْ أَنَّا دَمَّرْنَاهُمْ وَقَوْمَهُمْ أَجْمَعِينَ (51)
Ndipo taona zotsatira zake za chiwembu chawo. Ife tidawaonongeratu pamodzi ndi anthu awo onse
فَتِلْكَ بُيُوتُهُمْ خَاوِيَةً بِمَا ظَلَمُوا ۗ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَةً لِّقَوْمٍ يَعْلَمُونَ (52)
Chifukwa chakuti iwo adalakwa, nyumba zawo zimene anali kukhalamo tsopano ndi mabwinja. Ndithudi m’zimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira
وَأَنجَيْنَا الَّذِينَ آمَنُوا وَكَانُوا يَتَّقُونَ (53)
Ndipo Ife tidapulumutsa anthu onse okhulupirira ndipo anali kuopa Mulungu
وَلُوطًا إِذْ قَالَ لِقَوْمِهِ أَتَأْتُونَ الْفَاحِشَةَ وَأَنتُمْ تُبْصِرُونَ (54)
Loti kwa anthu ake, “Kodi inu mukuchita zinthu zochititsa manyazi pamene muli kuona?”
أَئِنَّكُمْ لَتَأْتُونَ الرِّجَالَ شَهْوَةً مِّن دُونِ النِّسَاءِ ۚ بَلْ أَنتُمْ قَوْمٌ تَجْهَلُونَ (55)
“Kodi inu muli kuchita chiwerewere ndi amuna anzanu pokwaniritsa zilakolako zanu ndi kusiya akazi? Inu ndinu mbuli basi.”
۞ فَمَا كَانَ جَوَابَ قَوْمِهِ إِلَّا أَن قَالُوا أَخْرِجُوا آلَ لُوطٍ مِّن قَرْيَتِكُمْ ۖ إِنَّهُمْ أُنَاسٌ يَتَطَهَّرُونَ (56)
“Yankho lawo silidali lina koma kuti, “Chotsani anthu a Loti mu mzinda wanu. Awa ndi anthu amene afuna kudziyeretsa.”
فَأَنجَيْنَاهُ وَأَهْلَهُ إِلَّا امْرَأَتَهُ قَدَّرْنَاهَا مِنَ الْغَابِرِينَ (57)
Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi anthu ake kupatula mkazi wake amene adatsalira m’chilango
وَأَمْطَرْنَا عَلَيْهِم مَّطَرًا ۖ فَسَاءَ مَطَرُ الْمُنذَرِينَ (58)
Ndipo tidawalasa iwo ndi mvula ya miyala imene idagwa pa iwo. Ndi mvula yoipa imene idagwera iwo amene adachenjezedwa
قُلِ الْحَمْدُ لِلَّهِ وَسَلَامٌ عَلَىٰ عِبَادِهِ الَّذِينَ اصْطَفَىٰ ۗ آللَّهُ خَيْرٌ أَمَّا يُشْرِكُونَ (59)
Nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu ndipo mtendere ukhale pa Atumwi ake amene Iye wawasankha. Kodi wabwino ndani Mulungu kapena mafano amene amawapembedza yoonjezera pa Mulungu?”
أَمَّنْ خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ وَأَنزَلَ لَكُم مِّنَ السَّمَاءِ مَاءً فَأَنبَتْنَا بِهِ حَدَائِقَ ذَاتَ بَهْجَةٍ مَّا كَانَ لَكُمْ أَن تُنبِتُوا شَجَرَهَا ۗ أَإِلَٰهٌ مَّعَ اللَّهِ ۚ بَلْ هُمْ قَوْمٌ يَعْدِلُونَ (60)
Kapena wabwino ndi Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi kukutumizirani mvula kuchokera kumwamba ndi kubweretsa minda ya chisangalalo? Iwo sangathe kumeretsa mitengo. Kodi pali milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni? Koma iwo ndi anthu amene amafanizira ena ake kukhala ofanana ndi Mulungu
أَمَّن جَعَلَ الْأَرْضَ قَرَارًا وَجَعَلَ خِلَالَهَا أَنْهَارًا وَجَعَلَ لَهَا رَوَاسِيَ وَجَعَلَ بَيْنَ الْبَحْرَيْنِ حَاجِزًا ۗ أَإِلَٰهٌ مَّعَ اللَّهِ ۚ بَلْ أَكْثَرُهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (61)
Kapena Iye amene adakhazikitsa dziko ndi kulithirira ilo ndi mitsinje ya madzi oyenda; ndipo wakhazikitsa mapiri pa dziko ndipo waika malire pakati pa nyanja ziwiri. Kodi pali mulungu wina woonjezera pa Mulungu weniweni? Koma ambiri a iwo ndi osadziwa
أَمَّن يُجِيبُ الْمُضْطَرَّ إِذَا دَعَاهُ وَيَكْشِفُ السُّوءَ وَيَجْعَلُكُمْ خُلَفَاءَ الْأَرْضِ ۗ أَإِلَٰهٌ مَّعَ اللَّهِ ۚ قَلِيلًا مَّا تَذَكَّرُونَ (62)
Kapena Iye amene amayankha mapemphero a munthu opanikizika pamene amupempha Iye ndipo amamuchotsera mavuto. Ndiyetu amene wakupatsani dziko lapansi kuti muzikhalamo. Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Ndi zazing’ono zimene mumakumbukira
أَمَّن يَهْدِيكُمْ فِي ظُلُمَاتِ الْبَرِّ وَالْبَحْرِ وَمَن يُرْسِلُ الرِّيَاحَ بُشْرًا بَيْنَ يَدَيْ رَحْمَتِهِ ۗ أَإِلَٰهٌ مَّعَ اللَّهِ ۚ تَعَالَى اللَّهُ عَمَّا يُشْرِكُونَ (63)
Kapena ndi Iye amene amakutsogolerani mu mdima pa mtunda kapena pa nyanja ndipo amatumiza mphepo ngati yonyamula uthenga wabwino wa chisomo chake. Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Mulungu ndi wapamwamba kuposa zimene amamufanizira nazo
أَمَّن يَبْدَأُ الْخَلْقَ ثُمَّ يُعِيدُهُ وَمَن يَرْزُقُكُم مِّنَ السَّمَاءِ وَالْأَرْضِ ۗ أَإِلَٰهٌ مَّعَ اللَّهِ ۚ قُلْ هَاتُوا بُرْهَانَكُمْ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (64)
Kapena Iye amene poyambirira adapanga zolengedwa ndiponso amene adzatidzutsanso kukhala ndi moyo m’moyo umene uli nkudza ndiponso amene amakupatsani chakudya kuchokera ku nthaka ndi kumwamba? Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Nena, “Tionetseni chizindikiro chanu ngati zimene mukunenazi ndi zoonadi.”
قُل لَّا يَعْلَمُ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ الْغَيْبَ إِلَّا اللَّهُ ۚ وَمَا يَشْعُرُونَ أَيَّانَ يُبْعَثُونَ (65)
Nena, “Palibe amene ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene amadziwa zobisika kupatula Mulungu. Ndiponso anthu sadziwa nthawi imene adzaukitsidwa kukhalanso ndi moyo.”
بَلِ ادَّارَكَ عِلْمُهُمْ فِي الْآخِرَةِ ۚ بَلْ هُمْ فِي شَكٍّ مِّنْهَا ۖ بَلْ هُم مِّنْهَا عَمُونَ (66)
Kodi kuzindikira kwawo m’moyo umene uli nkudza kwakwaniritsidwa? Iwo ndi okaika pa zamoyo umene uli nkudza ndipo maso awo ndi otsekeka pa za iwo
وَقَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا أَإِذَا كُنَّا تُرَابًا وَآبَاؤُنَا أَئِنَّا لَمُخْرَجُونَ (67)
Anthu osakhulupirira adati, “Kodi pamene ife ndi makolo anthu, tisanduka dothi tidzaukitsidwanso?”
لَقَدْ وُعِدْنَا هَٰذَا نَحْنُ وَآبَاؤُنَا مِن قَبْلُ إِنْ هَٰذَا إِلَّا أَسَاطِيرُ الْأَوَّلِينَ (68)
“Ndithudi ife tidalonjezedwa ndiponso makolo athu. Ichi si china ayi koma nkhani zopanda pake za anthu akale.”
قُلْ سِيرُوا فِي الْأَرْضِ فَانظُرُوا كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الْمُجْرِمِينَ (69)
Nena, “Pitani pa dziko lonse lapansi ndipo mukaone zimene zidawaonekera anthu ochimwa.”
وَلَا تَحْزَنْ عَلَيْهِمْ وَلَا تَكُن فِي ضَيْقٍ مِّمَّا يَمْكُرُونَ (70)
Usachite chisoni kapena kuvutika mu mtima chifukwa cha ziwembu zimene apanga
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا الْوَعْدُ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (71)
Ndipo iwo amati, “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati zimene muli kunenazi ndi zoona?”
قُلْ عَسَىٰ أَن يَكُونَ رَدِفَ لَكُم بَعْضُ الَّذِي تَسْتَعْجِلُونَ (72)
Nena, “Mwina gawo lina la zimene muli kufuna kuti zidze msanga zili pafupi kudza.”
وَإِنَّ رَبَّكَ لَذُو فَضْلٍ عَلَى النَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَشْكُرُونَ (73)
Ndipo, ndithudi, Ambuye wako ndi wokoma mtima kwa anthu, koma ambiri a iwo sathokoza ayi
وَإِنَّ رَبَّكَ لَيَعْلَمُ مَا تُكِنُّ صُدُورُهُمْ وَمَا يُعْلِنُونَ (74)
Ndipo, ndithudi, Ambuye wako amadziwa zonse zimene zimabisika m’mitima mwawo ndiponso zonse zimene amaulula
وَمَا مِنْ غَائِبَةٍ فِي السَّمَاءِ وَالْأَرْضِ إِلَّا فِي كِتَابٍ مُّبِينٍ (75)
Kulibe chinsinsi kumwamba kapena padziko lapansi chimene sichidalembedwe mu Buku lake lolemekezeka
إِنَّ هَٰذَا الْقُرْآنَ يَقُصُّ عَلَىٰ بَنِي إِسْرَائِيلَ أَكْثَرَ الَّذِي هُمْ فِيهِ يَخْتَلِفُونَ (76)
Buku la Korani lili kuwauza ana a Israyeli zambiri zimene iwo amatsutsana
وَإِنَّهُ لَهُدًى وَرَحْمَةٌ لِّلْمُؤْمِنِينَ (77)
Ndipo limeneli ndi chenjezo ndiponso madalitso kwa anthu okhulupirira m’choonadi
إِنَّ رَبَّكَ يَقْضِي بَيْنَهُم بِحُكْمِهِ ۚ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْعَلِيمُ (78)
Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo ndi chiweruzo chake. Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini kudziwa za chinthu china chilichonse
فَتَوَكَّلْ عَلَى اللَّهِ ۖ إِنَّكَ عَلَى الْحَقِّ الْمُبِينِ (79)
Kotero iwe ika chikhulupiriro chako mwa Mulungu chifukwa iwe uli pa choonadi chenicheni
إِنَّكَ لَا تُسْمِعُ الْمَوْتَىٰ وَلَا تُسْمِعُ الصُّمَّ الدُّعَاءَ إِذَا وَلَّوْا مُدْبِرِينَ (80)
Ndithudi iwe siungathe kumupanga munthu wakufa kuti amve ndiponso siungathe kumupanga munthu osamva kuti amve kuitana kwako pamene iye atembenuka
وَمَا أَنتَ بِهَادِي الْعُمْيِ عَن ضَلَالَتِهِمْ ۖ إِن تُسْمِعُ إِلَّا مَن يُؤْمِنُ بِآيَاتِنَا فَهُم مُّسْلِمُونَ (81)
Si udindo wako kutsogolera anthu a khungu kuti aleke kusochera. Palibe munthu amene adzakumvera kupatula okhawo amene amakhulupirira mu chivumbulutso chathu ndipo amadzipereka kwathunthu
۞ وَإِذَا وَقَعَ الْقَوْلُ عَلَيْهِمْ أَخْرَجْنَا لَهُمْ دَابَّةً مِّنَ الْأَرْضِ تُكَلِّمُهُمْ أَنَّ النَّاسَ كَانُوا بِآيَاتِنَا لَا يُوقِنُونَ (82)
Patsiku limene chiweruzo chathu chidzayandikira kwa osakhulupirira, Ife tidzawabweretsera chinyama chimene chidzayankhula nawo kuchokera ku dziko lapansi chifukwa munthu sanakhulupirire chivumbulutso chathu
وَيَوْمَ نَحْشُرُ مِن كُلِّ أُمَّةٍ فَوْجًا مِّمَّن يُكَذِّبُ بِآيَاتِنَا فَهُمْ يُوزَعُونَ (83)
Patsiku limeneli, tidzasonkhanitsa kuchokera ku mtundu uliwonse gululaanthuamenesadakhulupirirechivumbulutsochathu. Iwo adzasonkhanitsidwa ndi kuikidwa m’mizere
حَتَّىٰ إِذَا جَاءُوا قَالَ أَكَذَّبْتُم بِآيَاتِي وَلَمْ تُحِيطُوا بِهَا عِلْمًا أَمَّاذَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (84)
Mpaka pamene adzafike pamalo a chiweruzo, Mulungu adzati, “Kodi inu mudakana chivumbulutso changa ngakhale kuti inu simumadziwa chilichonse cha chivumbulutsocho? Kodi ndi chiyani mumachita?”
وَوَقَعَ الْقَوْلُ عَلَيْهِم بِمَا ظَلَمُوا فَهُمْ لَا يَنطِقُونَ (85)
Chionongeko chidzadza pa iwo chifukwa cha zoipa zawo ndipo iwo adzasowa chowiringula
أَلَمْ يَرَوْا أَنَّا جَعَلْنَا اللَّيْلَ لِيَسْكُنُوا فِيهِ وَالنَّهَارَ مُبْصِرًا ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يُؤْمِنُونَ (86)
Kodi iwo saona mmene tidakonzera usiku kuti ukhale mpumulo ndi masana kuti uziwapatsa kuwala? Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira
وَيَوْمَ يُنفَخُ فِي الصُّورِ فَفَزِعَ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَمَن فِي الْأَرْضِ إِلَّا مَن شَاءَ اللَّهُ ۚ وَكُلٌّ أَتَوْهُ دَاخِرِينَ (87)
Patsikulimeneli, lipengalidzalizidwandipoonseamene amakhala kumwamba ndi padziko lapansi adzagwidwa ndi mantha kupatula okhawo amene Mulungu adzafuna kuwapatula mu zimene zi. Onse adzabwera kwa Iye modzichepetsa
وَتَرَى الْجِبَالَ تَحْسَبُهَا جَامِدَةً وَهِيَ تَمُرُّ مَرَّ السَّحَابِ ۚ صُنْعَ اللَّهِ الَّذِي أَتْقَنَ كُلَّ شَيْءٍ ۚ إِنَّهُ خَبِيرٌ بِمَا تَفْعَلُونَ (88)
Iwe udzaona mapiri ndi kuwaganizira kuti ndi okhazikika koma iwo adzayenda ngati mmene mitambo imachitira. Uwu ndi mchitidwe wa Mulungu amene wakonza bwino lomwe chinthu chilichonse. Ndithudi Iye amadziwa bwino zonse zomwe mumachita
مَن جَاءَ بِالْحَسَنَةِ فَلَهُ خَيْرٌ مِّنْهَا وَهُم مِّن فَزَعٍ يَوْمَئِذٍ آمِنُونَ (89)
Iwo amene achita zabwino adzalandira mphotho imene ili yabwino ndipo adzakhala osakhudzidwa ndi zochititsa mantha za tsiku limeneli
وَمَن جَاءَ بِالسَّيِّئَةِ فَكُبَّتْ وُجُوهُهُمْ فِي النَّارِ هَلْ تُجْزَوْنَ إِلَّا مَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (90)
Koma iwo amene achita zoipa adzaduduluzidwa pa mphumi zawo kunka ku moto. “Kodi inu simudzalandira malipiro ofanana ndi ntchito zanu?”
إِنَّمَا أُمِرْتُ أَنْ أَعْبُدَ رَبَّ هَٰذِهِ الْبَلْدَةِ الَّذِي حَرَّمَهَا وَلَهُ كُلُّ شَيْءٍ ۖ وَأُمِرْتُ أَنْ أَكُونَ مِنَ الْمُسْلِمِينَ (91)
Nena, “Ine ndalamulidwa kutumikira Ambuye wa mzinda uno umene waupanga kuti ukhale Woyera. Zinthu zonse ndi zake. Ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi mwa odzipereka.”
وَأَنْ أَتْلُوَ الْقُرْآنَ ۖ فَمَنِ اهْتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهْتَدِي لِنَفْسِهِ ۖ وَمَن ضَلَّ فَقُلْ إِنَّمَا أَنَا مِنَ الْمُنذِرِينَ (92)
Ndipo ndalamulidwa kuwerenga Buku la Korani. Aliyense amene atsatira njira yoyenera atero podzithandiza yekha. Kwa iye amene asochera nena “Ine si ndine kanthu kena koma mmodzi wa iwo ochenjeza anthu.”
وَقُلِ الْحَمْدُ لِلَّهِ سَيُرِيكُمْ آيَاتِهِ فَتَعْرِفُونَهَا ۚ وَمَا رَبُّكَ بِغَافِلٍ عَمَّا تَعْمَلُونَ (93)
Ndipo nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu! Iye adzakulangizani zizindikiro zake ndipo inu mudzazizindikira. Ambuye wanu saiwala zimene mumachita.”
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas