Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ahzab ayat 53 - الأحزَاب - Page - Juz 22
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَدۡخُلُواْ بُيُوتَ ٱلنَّبِيِّ إِلَّآ أَن يُؤۡذَنَ لَكُمۡ إِلَىٰ طَعَامٍ غَيۡرَ نَٰظِرِينَ إِنَىٰهُ وَلَٰكِنۡ إِذَا دُعِيتُمۡ فَٱدۡخُلُواْ فَإِذَا طَعِمۡتُمۡ فَٱنتَشِرُواْ وَلَا مُسۡتَـٔۡنِسِينَ لِحَدِيثٍۚ إِنَّ ذَٰلِكُمۡ كَانَ يُؤۡذِي ٱلنَّبِيَّ فَيَسۡتَحۡيِۦ مِنكُمۡۖ وَٱللَّهُ لَا يَسۡتَحۡيِۦ مِنَ ٱلۡحَقِّۚ وَإِذَا سَأَلۡتُمُوهُنَّ مَتَٰعٗا فَسۡـَٔلُوهُنَّ مِن وَرَآءِ حِجَابٖۚ ذَٰلِكُمۡ أَطۡهَرُ لِقُلُوبِكُمۡ وَقُلُوبِهِنَّۚ وَمَا كَانَ لَكُمۡ أَن تُؤۡذُواْ رَسُولَ ٱللَّهِ وَلَآ أَن تَنكِحُوٓاْ أَزۡوَٰجَهُۥ مِنۢ بَعۡدِهِۦٓ أَبَدًاۚ إِنَّ ذَٰلِكُمۡ كَانَ عِندَ ٱللَّهِ عَظِيمًا ﴾
[الأحزَاب: 53]
﴿ياأيها الذين آمنوا لا تدخلوا بيوت النبي إلا أن يؤذن لكم إلى﴾ [الأحزَاب: 53]
Khaled Ibrahim Betala “E inu amene mwakhulupirira! Musalowe m’nyumba za Mneneri pokhapokha chilolezo chitaperekedwa kwa inu kukadya, osati kukhala nkuyembekezera kupsa kwa chakudya. Koma mukaitanidwa, lowani. Ndipo mukamaliza kudya, balalikani; ndiponso musakambe nkhani zocheza. Chifukwa kutero kumavutitsa Mneneri. Ndipo iye amakuchitirani manyazi (kuti akutulutseni); koma Allah alibe manyazi ponena choona. Ndipo inu mukamawafunsa (akazi ake) za ziwiya, afunseni uku muli kuseri kwa Chotsekereza. Zimenezo ndi zoyera zedi ku mitima yanu ndi mitima yawo. Sikoyenera kwa inu kumvutitsa Mtumiki wa Allah, ndiponso nkosayenera kwa inu kukwatira akazi ake pambuyo pa imfa yake mpaka muyaya. Ndithu kutero ndi tchimo lalikulu kwa Allah |