×

oh inu anthu a m’Buku! Musadutse malire a chipembedzo chanu kapena kunena 4:171 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah An-Nisa’ ⮕ (4:171) ayat 171 in Chichewa

4:171 Surah An-Nisa’ ayat 171 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah An-Nisa’ ayat 171 - النِّسَاء - Page - Juz 6

﴿يَٰٓأَهۡلَ ٱلۡكِتَٰبِ لَا تَغۡلُواْ فِي دِينِكُمۡ وَلَا تَقُولُواْ عَلَى ٱللَّهِ إِلَّا ٱلۡحَقَّۚ إِنَّمَا ٱلۡمَسِيحُ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ رَسُولُ ٱللَّهِ وَكَلِمَتُهُۥٓ أَلۡقَىٰهَآ إِلَىٰ مَرۡيَمَ وَرُوحٞ مِّنۡهُۖ فَـَٔامِنُواْ بِٱللَّهِ وَرُسُلِهِۦۖ وَلَا تَقُولُواْ ثَلَٰثَةٌۚ ٱنتَهُواْ خَيۡرٗا لَّكُمۡۚ إِنَّمَا ٱللَّهُ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞۖ سُبۡحَٰنَهُۥٓ أَن يَكُونَ لَهُۥ وَلَدٞۘ لَّهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۗ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ وَكِيلٗا ﴾
[النِّسَاء: 171]

oh inu anthu a m’Buku! Musadutse malire a chipembedzo chanu kapena kunena zokhudza Mulungu kupatula choonadi. Messiya Yesu, mwana wa Maria, sadali wina aliyense koma Mtumwi wa Mulungu ndi Mawu ake amene adanena kwa Maria, ndi Mzimu wolengedwa ndi Iye. Kotero khulupirirani mwa Mulungu ndi Atumwi ake. Ndipo musanene kuti: “Atatu.” Siyani! Zidzakhala bwino kwa inu. Chifukwa Mulungu ndi mmodzi yekha. Ulemerero ukhale kwa Iye. Iye sangakhale ndi mwana. Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndipo Mulungu ndi okwana kukhala Mtetezi wodalirika

❮ Previous Next ❯

ترجمة: ياأهل الكتاب لا تغلوا في دينكم ولا تقولوا على الله إلا الحق, باللغة نيانجا

﴿ياأهل الكتاب لا تغلوا في دينكم ولا تقولوا على الله إلا الحق﴾ [النِّسَاء: 171]

Khaled Ibrahim Betala
“E inu anthu a buku! Musamalumphe malire pa chipembedzo chanu. Ndipo musamamnenere Allah koma zowona (zokhazokha). Ndithu Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, ndi mtumiki wa Allah (ndiponso ndi munthu wolengedwa) ndi liwu Lake lomwe adaliyika mwa Mariya ndiponso (ali) ndi mzimu (moyo) wochokera kwa Iye (Allah, monga mizimu ina yonse imachokera kwa Iye). Choncho Khulupirirani Allah ndi atumiki Ake. Musamanene: “Utatu wa Mulungu;” siyani, (zikhululupiliro za utatu wa Mulungu), kutero ndibwino kwa inu. Ndithudi, Allah ndi Mulungu m’modzi (basi). Ulemelero wake ngotukuka kutali ndi kukhala ndi mwana. Nzake zonse za kumwamba ndi pansi. Ndipo Allah ndiMtetezi Wokwanira
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek