×

Ndipo, ndithudi, tidawapanga iwo kukhala amphamvu zoposa zanu. Ndipo Ife tidawapatsa makutu, 46:26 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Al-Ahqaf ⮕ (46:26) ayat 26 in Chichewa

46:26 Surah Al-Ahqaf ayat 26 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ahqaf ayat 26 - الأحقَاف - Page - Juz 26

﴿وَلَقَدۡ مَكَّنَّٰهُمۡ فِيمَآ إِن مَّكَّنَّٰكُمۡ فِيهِ وَجَعَلۡنَا لَهُمۡ سَمۡعٗا وَأَبۡصَٰرٗا وَأَفۡـِٔدَةٗ فَمَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُمۡ سَمۡعُهُمۡ وَلَآ أَبۡصَٰرُهُمۡ وَلَآ أَفۡـِٔدَتُهُم مِّن شَيۡءٍ إِذۡ كَانُواْ يَجۡحَدُونَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ ﴾
[الأحقَاف: 26]

Ndipo, ndithudi, tidawapanga iwo kukhala amphamvu zoposa zanu. Ndipo Ife tidawapatsa makutu, maso ndi mitima koma palibe china chilichonse chimene makutu awo, maso awo ndi mitima yawo idawathandiza chifukwa iwo adakana kumvera chivumbulutso cha Mulungu ndipo icho chimene anali kuchinyoza chidawapeza iwo

❮ Previous Next ❯

ترجمة: ولقد مكناهم فيما إن مكناكم فيه وجعلنا لهم سمعا وأبصارا وأفئدة فما, باللغة نيانجا

﴿ولقد مكناهم فيما إن مكناكم فيه وجعلنا لهم سمعا وأبصارا وأفئدة فما﴾ [الأحقَاف: 26]

Khaled Ibrahim Betala
“Ndipo ndithu tidawapatsa mphamvu (yochitira zinthu ndi kukhala ndi chuma chambiri ndi moyo wautali) zomwe sitidakupatseni inu (Aquraish) ndipo tidawapatsa makutu ndi maso ndi mitima, koma makutu awo ndi maso awo ndi mitima yawo sizidawapindulire chilichonse chifukwa chotsutsa Ayah za Allah; ndipo zidawazinga zomwe adali kuzichitira chipongwe
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek